Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 5/8 tsamba 31-32
  • Kodi Akristu Amaiona Bwanji Misa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Akristu Amaiona Bwanji Misa?
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Malemba Amatchula za Misa?
  • Kodi Kristu Amaperekedwa Nsembe Kangati?
  • Misa
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Mumachita Mwambo wa Mgonero wa Ambuye Mosiyana ndi Zipembedzo Zina?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Zoona Zake za Mwambo wa Ukalisitiya
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Mgonero wa Ambuye uli ndi Tanthauzo Lalikulu kwa Inu
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 5/8 tsamba 31-32

Lingaliro la Baibulo

Kodi Akristu Amaiona Bwanji Misa?

MALINGA ndi mmene magazini ya The New York Times inanenera posachedwapa, Akatolika odzipereka anagwirizana ndi Papa Yohane Paulo Wachiŵiri, pamfundo yakuti “tchalitchi chimaona kuti ngati M’katolika waphonya Misa, ndiye kuti wachimwa.” Kodi Misa n’chiyani? Kodi zimene matchalitchi amanena ndi zimene Baibulo limanena, zimagwirizana pankhani imeneyi?

M’buku lakuti Things Catholics Are Asked About (Zinthu Zimene Akatolika Amafunsidwa), wansembe wina wachikatolika, Martin J. Scott, anatanthauzira Misa motere: “Misa imatanthauza kupereka nsembe Thupi ndi Magazi a Kristu popanda magazi. Pa Golgota m’pamene panaperekedwa nsembe ya Kristu yamagazi. Misa n’njofanana ndithu ndi nsembe ya pamtanda ija. Mawu ameneŵa si ophiphiritsira, si mawu ofanizira, kapena osinjirira ayi.” Iyeyo anatinso: “Misa imam’tsitsira Mwana wa Mulungu pa maguwa athu kuti tim’perekenso nsembe kwa Mulungu.”

Kodi Malemba Amatchula za Misa?

Akatolika enieni amakhulupirira kuti Malemba amaphunzitsadi za Misa. Umboni wawo amatenga mawu a Yesu amene ananena pa chochitika chimene ambiri amachitcha Mgonero wa Ambuye. Yesu popereka kwa ophunzira ake mkate ndi vinyo, za mkate anati: “Ichi ndi thupi langa.” Za vinyo anati: “Ichi ndicho mwazi wanga.” (Mateyu 26:26-28)a Akatolika amakhulupirira kuti pamene Yesu ananena mawu amenewo anali atasandutsadi mkatewo ndi vinyoyo kukhala thupi lake lenileni ndi magazi ake enieni. Komabe, buku lotchedwa New Catholic Encyclopedia (1967) linachenjeza kuti: “Mawu akuti ‘ichi ndi thupi langa’ kapena akuti “Ichi ndicho mwazi wanga” sitiyenera kuwaona ngati mawu chabe oti akungotanthauza zomwezo basi. Chifukwa mawu akuti ‘kututa ndicho chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano’ (Mat. 13:39) kapena kuti ‘Ine ndine mpesa weniweni’ (Yoh. 15:1) [mneni wakuti “ndi”] amangonena tanthauzo la chinthu china kapena kuimira chinthu chinachake.” Choncho, ngakhale buku lolongosola za Chikatolika limeneli, limavomereza kuti mawu a pa Mateyu 26:26-28 satanthauza kuti pa Mgonero wa Ambuyepo Yesu anasintha mkate ndi vinyo n’kukhala thupi lake lenileni ndi magazi ake enieni ayi.

Mwina mukukumbukira kuti Yesu anati: “Mkate wamoyo wotsika kumwamba ndine amene. . . . Munthu wina akadyako mkate umene[wu], adzakhala ndi moyo kosatha.” (Yohane 6:51) Anthu ena amene ankamvetsera mawu a Yesuwo anali kuganiza kuti ali ndi tanthauzo lomwelodi ndipo anawadabwitsa kwambiri (Yohane 6:60) Komabe tifunse chonchi, Kodi Yesu anasandutsadi thupi lake n’kukhala mkate tsiku limene lija? Kutalitali! Anali kuyankhula mophiphiritsa. Anadziyerekezera ndi mkate chifukwa anali kuyembekezera kudzapatsa anthu moyo kudzera mwa nsembe yake. Yohane 6:35, 40 amasonyeza bwino kuti kudya ndi kumwa kumeneku kudzachitika mwa kukhulupirira Yesu Kristu.

Popeza kuti Tchalitchi cha Katolika chimaphunzitsa za Misa monga mwambo wawo waukulu, mwina wina angaganize kuti Malemba nawo amachichirikiza chiphunzitso chimenecho. Koma satero ayi. Buku lakuti The Catholic Encyclopedia (1913) linafotokoza chifukwa chake, kuti: “Magwero aakulu achiphunzitso chathu, . . . ndiwo mwambo, umene kuyambira nthaŵi zakalekale umalengeza kufunika kwakupempha Nsembe ya Misa.” Indedi, Misa ya Aroma Katolika n’nja mwambo, si yochokera m’Baibulo iyayi.

Zilibe kanthu kuti mwambowo anthu amauona ngati wabwino, koma ngati sugwirizana ndi Baibulo, Mulungu amadana nawo. Yesu anakalipira atsogoleri achipembedzo akale, kuti: “Mupeputsa mawu a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu.” (Mateyu 15:6) Popeza kuti Yesu ankakonda Malemba kwambiri, tiyeni tione mmene Malemba Opatulika amachifotokozera chiphunzitso chimenechi cha Misa .

Kodi Kristu Amaperekedwa Nsembe Kangati?

Tchalitchi cha Katolika chimaphunzitsa kuti nthaŵi zonse akamachita phwando la Misa, amam’pereka Yesu nsembe, ngakhale kuti amanenanso kuti Yesuyo safadi ndiponso kuti nsembeyo imakhala yopanda magazi. Kodi Baibulo limachitira umboni zimenezo? Onani zimene Ahebri 10:12, 14 amanena: “M’mene [Yesu] adapereka nsembe imodzi chifukwa cha machimo, anakhala pa dzanja lamanja la Mulungu chikhalire. Pakuti ndi chipereko chimodzi anawayesera angwiro chikhalire iwo oyeretsedwa.”

Komabe, Mkatolika weniweni angatsutse zimenezo, kuti: ‘Kodi sikungafunike kuti Yesu adzipereke kaŵirikaŵiri? Tonse timachimwa nthaŵi zambiri.’ Baibulo limayankha ndi mawu ali pa Ahebri 9:25, 26, kuti: “Kosati kuti [Kristu] adzipereke yekha kaŵirikaŵiri. . . . Koma tsopano kamodzi pa chitsiriziro cha nthaŵizo waonekera kuchotsa uchimo mwa nsembe ya Iye yekha.” Tawamveni bwino mawuŵa: Kristu ‘sadzipereka yekha kaŵirikaŵiri.’ Pa Aroma 5:19, mtumwi Paulo anafotokoza chifukwa chake, kuti: “Monga ndi kusamvera kwa munthu mmodzi [Adamu] ambiri anayesedwa ochimwa, chomwecho ndi kumvera kwa mmodzi [Yesu] ambiri adzayesedwa olungama.” Kusamvera kwa Adamu kunatipha tonsefe; mmene Yesu watiwombolamu, ndiye kuti watipatsa mwayi tonsefe okhulupirira nsembe imeneyo, kuti tikhululukidwe machimo athu tsopano lino ndi kutinso tidzakhale ndi moyo wosatha m’tsogolo muno.

Makamaka kodi n’chiyani chimene chili mfundo yaikulu pankhaniyi, yoti kaya Yesu anaperekedwa nsembe kamodzi kapena kuti amaperekedwabe nsembe kaŵirikaŵiri? Mfundo n’njakuti tiyenera kuyamikira nsembe ya Yesu. Imeneyi ndi mphatso yaikulu kwambiri imene tapatsidwa—mphatso yamtengo wapatali zedi, yangwiro, yoti sitidzafunikiranso kuilandira kaŵiri.

Ndithudi nsembe ya Yesu tiyenera kumaikumbukira. Komabe pali kusiyana pakati pa kukumbukira chochitika chinachake ndi kuchibwereza. Mwachitsanzo, mwamuna ndi mkazi wake angakumbukire tsiku laukwati wawo popanda kubwerezanso mwambo waukwati. Chaka chilichonse, a Mboni za Yehova amakumbukira tsiku la imfa ya Yesu, amachitadi monga mmene Yesuyo analamulira—“chikumbukiro,” osati kum’perekanso nsembe. (Luka 22:19) Komanso, chaka chilichonse, Akristu ameneŵa amayesetsa kukhala pamtendere ndi Yehova Mulungu kudzera mwa Yesu Kristu, mwa kuchita ntchito zabwino ndi kukhulupirira zinthu zimene Malemba Opatulika amaphunzitsa.

Nthaŵi zonse, amafunikira kusintha maganizo awo. Koma Mbonizo zimakondwera kudziŵa kuti zikamamvera Mawu a Mulungu mokhulupirika m’malo momvera miyambo ya anthu, zidzadalitsidwa. Ndiponso zikamakhulupirira mwazi wa Yesu womwe unaperekedwa nsembe kamodzi kokha, pafupifupi zaka zikwi ziŵiri zapitazo, nsembeyo idzawayeretsa pamachimo onse.—1 Yohane 1:8, 9.

Ngati mungafune kudziŵa zambiri kapena kuti wina aziphunzira nanu Baibulo panyumba panu kwaulere, lemberani ku Watch Tower, Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku adiresi yoyenera pa maadiresi osonyezedwa patsamba 2.

[Mawu a M’munsi]

a Malemba onse ogwidwa mawu m’nkhani ino n’nga mu New Jerusalem Bible, lachikatolika.

[Chithunzi patsamba 31]

Misa ya ku St. Giles

[Mawu a Chithunzi]

Erich Lessing/Art Resource, NY

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena