Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kuchokera ku Seder Kumka ku Chipulumutso
    Nsanja ya Olonda—1990 | February 15
    • 13, 14. Kodi ndimotani mmene mwazi wa Yesu uliri wopulumutsa moyo ndi wofunika kaamba ka chipulumutso? (Aefeso 1:13)

      13 Mwazi ngwophatikizidwanso m’chipulumutso lerolino​—mwazi wokhetsedwa wa Yesu. Pamene “paskha, phwando la Ayuda, linali pafupi” mu 32 C.E., Yesu anauza unyinji wa omvetsera kuti: “Iye wakudya thupi langa ndi wakumwa mwazi wanga ali nawo moyo wosatha; ndipo ine ndidzamuukitsa tsiku lomaliza. Pakuti thupi langa ndichakudya ndithu, ndi mwazi wanga ndichakumwa ndithu.” (Yohane 6:4, 54, 55) Amvetseri ake onse Achiyuda akakumbukira Paskha yoyandikirayo ndi kuti mwazi wa mwana wankhosa unagwiritsiridwa ntchito mu Igupto.

      14 Pamenepo Yesu sanali kulankhula za zizindikiro zogwiritsiridwa ntchito pa Mgonero wa Ambuye. Phwando latsopano limenelo la Akristu silinayambitsidwe kufikira chaka chimodzi pambuyo pake, chotero ngakhale atumwi amene adamva Yesu mu 32 C.E. sanadziwe konse za iro. Chikhalirechobe, Yesu ankasonyeza kuti mwazi wake unali wofunika kaamba ka chipulumutso chosatha. Paulo analongosola kuti: “Tiri ndi mawomboledwe m’mwazi wake, chikhululukiro cha zochimwa, monga mwa kulemera kwa chisomo chake.” (Aefeso 1:7) Kokha mwa kukhululukidwa pamaziko a mwazi wa Yesu kuti tingathe kukhala ndi moyo kosatha.

  • Kuchokera ku Seder Kumka ku Chipulumutso
    Nsanja ya Olonda—1990 | February 15
    • 15. Kwa Ahebri mu Igupto, kodi nchipulumutso chotani ndi mwaŵi zimene zinali zothekera, ndipo kodi nchiyani chimene sichinali chotheka? (1 Akorinto 10:1-5)

      15 Chipulumutso chokhala ndi polekezera chabe chinaphatikizidwa m’Igupto wakale. Palibe aliyense amene anatuluka m’Igupto anayembekezeredwa kupatsidwa moyo wosatha pambuyo pa Kutulukako. Zowona, Mulungu adaika Alevi kukhala ansembe a mtunduwo, ndipo ena a fuko la Yuda anakhala mafumu akanthaŵi, komatu onsewo akamwalira. (Machitidwe 2:29; Ahebri 7:11, 23, 27) Pamene kuli kwakuti ‘gulu losanganizikana’ limenenso linatuluka m’Igupto linalibe mwaŵi wotero, iwo, limodzi ndi Ahebri, anayembekezera kukafika ku Dziko Lolonjezedwa ndi kusangalala ndi moyo wanthaŵi zonse akumalambira Mulungu. Ndiponso, atumiki a Yehova a Chikristu chisanakhale adali ndi maziko a kuyembekezerera kuti, m’nthawi yokwanira, iwo akasangalala ndi moyo wamuyaya padziko lapansi, kumene Mulungu analinganizira anthu kukhala. Ichi chikakhala chogwirizana ndi lonjezo la Yesu pa Yohane 6:54.

      16. Kodi nchipulumutso chotani chimene atumiki akalekale a Mulungu adayembekezera?

      16 Mulungu anagwiritsira ntchito ena a atumiki ake akale kulemba mawu ouziridwa onena za dziko lapansi kukhala litalengedwera kukhalamo anthu ndi onena za olungama kukhalamo kosatha. (Salmo 37:9-11; Miyambo 2:21, 22; Yesaya 45:18) Komabe, kodi ndimotani mmene alambiri owona amenewo akapezera chipulumutso choterocho ngati anafa? Mwa kubwezeretsedweranso kwawo ku moyo padziko lapansi ndi Mulungu. Mwachitsanzo, Yobu, analongosola chiyembekezo chakuti akakumbukiridwa ndi kubwezeretseredwanso ku moyo. (Yobu 14:13-15; Danieli 12:13) Momvekera, mtundu wina wa chipulumutso ndiwo moyo wosatha padziko lapansi.​—Mateyu 11:11.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena