Kuchitira Umboni ku “Mitundu Yonse”
“Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kuti ikhale umboni ku mitundu yonse; ndiyeno mapeto adzafika.”—MATEYU 24:14, NW.
1. Kodi nchifukwa ninji mawu a Yesu olembedwa pa Mateyu 24:14 ayenera kukhala anali odabwitsa kwa otsatira ake?
MAWU a Yesu amenewo ayenera kukhala anali odabwitsa chotani nanga kwa ophunzira ake Achiyuda! Lingaliro lenileni la Ayuda oyeretsedwa kukhala akupita kukalankhula kwa Akunja “onyansa,” “amitundu,” linali lachilendo kwa Myuda, lonyansadi.a Eya, Myuda wosamalitsa sankalingalira nkomwe zoloŵa m’nyumba ya Wakunja! Ophunzira Achiyuda amenewo anali adakali ndi zambiri zoti aphunzire ponena za Yesu, chikondi chake, ndi ntchito yake. Ndipo anali ndi zambiribe zoti aphunzire ponena za kupanda tsankhu kwa Yehova.—Machitidwe 10:28, 34, 35, 45.
2. (a) Kodi utumiki wa Mboni wakhala wofika patali motani? (b) Kodi ndi zinthu zitatu ziti zimene zachititsa kupita patsogolo kwa Mboni?
2 Mboni za Yehova zalalikira mbiri yabwino pakati pa mitundu, kuphatikizapo Israyeli wamakono, ndipo tsopano zikuilengeza m’mitundu yambiri kuposa ndi kalelonse. Mu 1994 Mboni zoposa mamiliyoni anayi ndi theka zikulalikira m’maiko pafupifupi 230. Izo zikuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba pafupifupi mamiliyoni anayi ndi theka kwa anthu okondwerera. Zimenezi zikuchitidwa mkati mwa kulingaliridwa molakwa kwa padziko lonse, kaŵirikaŵiri kozikidwa pa kusadziŵa ziphunzitso ndi zolinga za Mboni. Monga momwe kunanenedwera kwa Akristu oyambirira, momwemonso kunganenedwenso kwa iwo kuti: “Pakuti za mpatuko uwu, tidziŵa kuti aunenera ponseponse.” (Machitidwe 28:22) Pamenepo kodi tingati chipambano chawo muutumiki chimachokera kuti? Pali pafupifupi zinthu zitatu zimene zimachititsa kupita patsogolo kwawo—kutsatira chitsogozo cha mzimu wa Yehova, kutsanzira njira zogwira ntchito za Kristu, ndi kugwiritsira ntchito ziŵiya zoyenera za kulankhulana kogwira mtima.
Mzimu wa Yehova ndi Mbiri Yabwino
3. Kodi nchifukwa ninji sitingadzitamandire pa zimene zakwaniritsidwa?
3 Kodi Mboni za Yehova zimadzitamandira pa chipambano chawo, monga ngati kuti chimachitika chifukwa cha maluso apadera amene zili nawo? Ayi, popeza kuti mawu a Yesu amagwira ntchito: “Mmene mutachita zonse anakulamulirani, nenani, Ife ndife akapolo opanda pake, tangochita zimene tayenera kuzichita.” Monga Akristu odzipatulira, obatizidwa, Mboni za Yehova zavomereza modzifunira thayo la kutumikira Mulungu, mosasamala kanthu za mikhalidwe yawo yaumwini. Kwa ena, zimenezo zimatanthauza utumiki wanthaŵi yonse monga amishonale kapena odzipereka mwaufulu m’maofesi anthambi ndi nyumba zosindikizira zofalitsidwa Zachikristu. Kwa ena kufunitsitsa Kwachikristu kumeneko kumawatsogolera ku ntchito yomanga nyumba zachipembedzo, kulalikira nthaŵi yonse monga atumiki ochita upainiya, kapena kulalikira mwa kanthaŵi monga ofalitsa mbiri yabwino a mipingo yakumaloko. Palibe aliyense wa ife amene moyenerera angadzitamandire za kuchita ntchito yathu, ‘imene tiyenera kuichita.’—Luka 17:10; 1 Akorinto 9:16.
4. Kodi chitsutso cha padziko lonse pa utumiki Wachikristu chalakidwa motani?
4 Chipambano chilichonse chimene tili nacho chinganenedwe kuti chimachititsidwa ndi mzimu, kapena mphamvu yogwira ntchito ya Yehova. Nkoyenerera kunena lerolino monga momwe kunaliri m’masiku a mneneri Zekariya kuti: “Awa ndi mawu a Yehova kwa Zerubabele, Ndi khamu la nkhondo ayi, ndi mphamvu ayi, koma ndi Mzimu wanga, ati Yehova wa makamu.” Motero, chitsutso chapadziko lonse pa ntchito yolalikira ya Mboni chagonjetsedwa, osati ndi zoyesayesa za anthu, koma ndi chitsogozo ndi chitetezo cha Yehova.—Zekariya 4:6.
5. Kodi ndi mbali yotani imene Yehova amachita m’kufalitsa uthenga wa Ufumu?
5 Ponena za awo amene amavomereza uthenga wa Ufumu, Yesu anati: “Chalembedwa mwa aneneri, Ndipo adzakhala onse ophunzitsidwa ndi Mulungu. Yense amene adamva kwa Atate, naphunzira, adza kwa Ine. . . . Palibe munthu angathe kudza kwa Ine, koma ngati kupatsidwa kwa iye ndi Atate.” (Yohane 6:45, 65) Yehova angaone mitima ndi maganizo, ndipo amadziŵa awo amene angavomereze chikondi chake ngakhale kuti angakhale asanamudziŵebe. Iye amagwiritsiranso ntchito angelo ake kutsogolera utumiki wapadera umenewu. Ndicho chifukwa chake m’masomphenya Yohane anaona kutenga mbali kwa angelo ndi kulemba kuti: “Ndinaona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nawo Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu.”—Chivumbulutso 14:6.
Ozindikira Kusoŵa Kwauzimu
6. Kodi ndi mkhalidwe wamaganizo waukulu wotani umene umafunikira kuti munthu alabadire mbiri yabwino?
6 Chinthu china chimene Yehova amapatsira munthu mwaŵi wakulandira mbiri yabwino ndicho chija chimene chinalongosoledwa ndi Yesu kuti: “Achimwemwe ali awo ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu, popeza kuti ufumu wakumwamba uli wawo.” (Mateyu 5:3, NW) Munthu wodzikhutiritsa maganizo kapena amene sakufunafuna choonadi sangakhale wozindikira kusoŵa kwauzimu. Iye amalingalira za zinthu zooneka ndi zakuthupi. Kukhutira kumakhala chopinga. Chotero, pamene ambiri amene timakumana nawo pamene tipita kunyumba ndi nyumba akana uthengawo, tiyenera kulingalira zifukwa zonse zosiyanasiyana zimene anthu angakhale nazo kaamba ka kuchita kwawoko.
7. Kodi nchifukwa ninji ambiri samalabadira choonadi?
7 Ambiri amakana kumvetsera chifukwa chakuti amamamatira mouma khosi ku chipembedzo chimene anabadwiramo ndipo samafuna kukambitsirana. Ena akopeka ndi chipembedzo chimene chimayenerana ndi umunthu wawo—ena amafuna chipembedzo chamatsenga, ena amakopeka ndi kutengeka maganizo, ena amafunanso zosangulutsa ku tchalitchi chawo. Ambiri lerolino asankha njira ya moyo imene imawombana ndi miyezo ya Mulungu. Mwinamwake akukhala ndi moyo wachiwerewere, umene uli chifukwa chawo chonenera kuti, “Sindili wokondweretsedwa.” Komabe, ena amene amanena kuti ngophunzira ndi odziŵa sayansi, amakana Baibulo akumati ndi lokhweka kwambiri.—1 Akorinto 6:9-11; 2 Akorinto 4:3, 4.
8. Kodi nchifukwa ninji kukana sikuyenera kuchepetsa changu chathu? (Yohane 15:18-20)
8 Kodi kukanidwa ndi anthu ochuluka kuyenera kuchepetsa chikhulupiriro ndi changu chathu muutumiki wopulumutsa moyowu? Tingapeze chitonthozo m’mawu a Paulo kwa Aroma akuti: “Nanga bwanji ngati ena sanakhulupira? Kodi kusakhulupira kwawo kuyesa chabe chikhulupiriko cha Mulungu? Msatero ayi. Koma Mulungu akhale woona, ndimo anthu onse akhale onama; monga kwalembedwa, Kuti Inu mukayesedwe wolungama m’maneno anu, ndi kuti mukalakike mmene muweruzidwa.”—Aroma 3:3, 4.
9, 10. Kodi pali umboni wotani wakuti chitsutso chalakidwa m’maiko ambiri?
9 Tingapeze chilimbikitso kuchokera m’zitsanzo zambiri kuzungulira dziko za maiko amene anaonekera kukhala osalabadira kwambiri ndipo komabe, m’kupita kwa nthaŵi, atsimikizira kukhala osiyana kotheratu. Yehova ndi angelo adziŵa kuti kunali anthu a mtima wabwino amene akapezeka—koma Mboni za Yehova zinayenera kuchita khama ndi kupirira muutumiki wawo. Mwachitsanzo, talingalirani za maiko ena kumene Chikatolika chinaonekera kukhala chopinga chachikulu zaka 50 zapitazo—Argentina, Brazil, Colombia, Ireland, Italy, Mexico, Portugal, ndi Spain. Mboni zinali zochepa kalelo mu 1943, zinalipo 126,000 zokha padziko lonse, ndipo 72,000 za zimenezi zinali mu United States. Kupulukira ndi kulingaliridwa molakwa kumene Mbonizo zinakumana nako kunaonekera ngati khoma la njerwa limene silikanabooledwa. Komabe, lerolino zina za zotulukapo zachipambano koposa za kulalikira zachitika m’maiko ameneŵa. Zofananazo zachitika m’maiko ambiri amene kale anali Achikomyunizimu. Mu 1993 kubatizidwa kwa anthu 7,402 pamsonkhano mu Kiev, Ukraine, kumapereka umboni wa zimenezi.
10 Kodi ndi njira zotani zimene Mbonizo zagwiritsira ntchito kuti zilankhule mbiri yabwino kwa anansi awo? Kodi zagwiritsira ntchito zokopa zooneka kuti zipeze otembenuka, zomwe zili zimene ena anena? Kodi zachezera osauka ndi osaphunzira okha, monga momwe ena anenera?
Njira Zachipambano Zoperekera Mbiri Yabwino
11. Kodi ndi chitsanzo chabwino chotani chimene Yesu anakhazikitsa muutumiki wake? (Onani Yohane 4:6-26.)
11 Yesu ndi ophunzira ake anakhazikitsa chitsanzo chimene Mboni zimatsatira kufikira lerolino m’ntchito yawo yopanga ophunzira. Yesu anapita kulikonse kumene kunali anthu, olemera kapena osauka—kunyumba, m’malo apoyera, m’mphepete mwa nyanja, m’mphepete mwa mapiri, ngakhale ku masunagoge.—Mateyu 5:1, 2; 8:14; Marko 1:16; Luka 4:15.
12, 13. (a) Kodi Paulo anapereka motani chitsanzo kwa Akristu? (b) Kodi Mboni za Yehova zatsatira motani chitsanzo cha Paulo?
12 Ponena za utumiki wake wa iyemwini, mtumwi Paulo moyenerera anati: “Mudziŵa inu kuyambira tsiku loyamba ndinafika ku Asiya, makhalidwe anga pamodzi ndi inu nthaŵi yonse, wotumikira Ambuye . . . ; kuti sindinakubisirani zinthu zopindulira, osazilalikira kwa inu, ndi kukuphunzitsani inu pabwalo ndi m’nyumba m’nyumba.”—Machitidwe 20:18-20.
13 Mboni za Yehova zimadziŵika padziko lonse chifukwa cha kutsatira kwawo chitsanzo cha atumwi, utumiki wakunyumba ndi nyumba. Mmalo mosumika maganizo pa utumiki wowononga ndalama, wopanda chidziŵitso chakuya, wosafika mtima wa pa TV, Mboni zimapita kwa anthu, olemera ndi osauka, ndi kukumana nawo maso ndi maso. Zimafuna kulankhula za Mulungu ndi Mawu ake.b Izo sizimayesa kupanga Akristu m’dzina lokha, mwa kupereka zinthu zakuthupi. Kwa awo amene ali ofunitsitsa kukambitsirana, zimawasonyeza kuti njira yokha yothetsera mavuto a mtundu wa anthu ndiyo ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, umene udzasintha mikhalidwe padziko lathu lapansi kukhala yabwino kwambiri.—Yesaya 65:17, 21-25; 2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:1-4.
14. (a) Kodi amishonale ndi apainiya ambiri ayala motani maziko olimba? (b) Kodi timaphunzira chiyani m’chokumana nacho cha Mboni za Yehova m’Japan?
14 Kuti ntchitoyo ichitidwe m’maiko ochuluka monga momwe kungathekere, amishonale ndi apainiya akhazikitsa maziko m’maiko ambiri. Iwo ayala maziko, ndiyeno Mboni zakumaloko zatsogolera. Motero, sipanafunikire ziŵerengero zazikulu za Mboni zachilendo kuti ntchito yolalikira ipitirizebe kuchitidwa ndi kukhala yolinganizidwa bwino. Chitsanzo chimodzi chapadera ndicho Japan. Kalelo kumapeto kwa ma 1940, kwakukulukulu amishonale a ku Australasia ndi Britain anapita kumeneko, anaphunzira chinenero, nasintha mogwirizana ndi mikhalidwe yachikale ya nyengo ya pambuyo pa nkhondo imeneyo, ndi kuyamba kuchitira umboni kunyumba ndi nyumba. Mkati mwa Nkhondo Yadziko II, Mboni zinali zitaletsedwa ndi kuzunzidwa m’Japan. Chotero amishonalewo anafika ndi kupeza Mboni za ku Japan zokangalika zochepa zokha. Koma lerolino zawonjezeka kuposa pa 187,000 m’mipingo yoposa 3,000! Kodi nchiyani chimene chinali chinsinsi cha chipambano chawo choyambirira? Mmishonale wina amene watumikira kwa zaka zoposa 25 kumeneko anati: “Kunali kofunika koposa kuphunzira kulankhula ndi anthuwo. Mwa kudziŵa chinenero chawo, tinali okhoza kumvana nawo, kumvetsetsa ndi kuyamikira njira yawo ya moyo. Tinayenera kusonyeza kuti timakonda anthu a ku Japan. Tinayesayesa modzichepetsa kukhala mbali ya anthu akumaloko, popanda kulolera molakwa mikhalidwe yathu Yachikristu.”
Mkhalidwe Wachikristu Ulinso Umboni
15. Kodi Mboni zasonyeza motani mkhalidwe Wachikristu?
15 Komabe, anthu sanavomereze uthenga wa Baibulo wokha. Iwo aonanso Chikristu mu ntchito. Iwo aona chikondi, kugwirizana, ndi umodzi wa Mboni ngakhale pansi pa mikhalidwe yopereka chiyeso koposa, monga ngati nkhondo zachiweniweni, kulimbana kwa mafuko, ndi udani wa mitundu. Mbonizo zasunga kaimidwe koonekera bwino ka uchete Wachikristu m’mikangano yonse ndipo zakwaniritsa mawu a Yesu akuti: “Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.”—Yohane 13:34, 35.
16. Kodi ndi chokumana nacho chotani chimene chimasonyeza chikondi Chachikristu chothandiza?
16 Chikondi cha pa mnansi chinasonyezedwa m’nkhani ya mwamuna wina wokalamba amene analembera nyuzipepala yakumaloko ponena za “A Munthu Wabwino ndi Akazi Awo.” Iye analongosola kuti anansi ake anali achifundo kwa iye pamene mkazi wake anali kumwalira. “Kuyambira pamene anamwalira . . . iwo akhala anthu abwino koposa,” iye analemba motero. “Kuyambira pamenepo ‘ananditenga’ . . . , akumachita ntchito zonse zosiyanasiyana ndi kuthandiza kuthetsa mavuto a wopuma ntchito wazaka 74. Zimene zikupangitsa zonsezi kukhala zachilendo ndi zakuti iwo ndi anthu akuda, ndine mzungu. Iwo ndi Mboni za Yehova, ndine Mkatolika wotulukira pazenera.”
17. Kodi ndi njira yotani imene tiyenera kupeŵa?
17 Chokumana nacho chimenechi chikusonyeza kuti tingapereke umboni m’njira zambiri, kuphatikizapo khalidwe lathu la tsiku ndi tsiku. Kwenikweni, pokhapo ngati khalidwe lathu lili longa la Kristu, utumiki wathu udzakhala ngati wa Afarisi, wosagwira mtima. Sitifuna kukhala ngati awo amene Yesu anawafotokoza kuti: “Zinthu zilizonse zimene iwo akauza inu, chitani nimusunge; koma musatsanza ntchito zawo; pakuti iwo amalankhula, koma samachita.”—Mateyu 22:37-39; 23:3.
Gulu la Kapolo Limapereka Ziŵiya Zoyenera
18. Kodi mabuku a Baibulo amatikonzekeretsa motani kuthandiza anthu oona mtima?
18 Chinthu china chofunika m’kulalikira mbiri yabwino ku mitundu yonse chakhala kupezeka kwa mabuku a Baibulo otulutsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society. Tili ndi mabuku, mabrosha, matrakiti, ndi magazini amene angakhutiritse pafupifupi wofunsa woona mtima aliyense. Ngati tikumana ndi munthu wachipembedzo cha Chisilamu, Chihindu, Chibuddah, Chitao, kapena Chiyuda, tingagwiritsire ntchito buku la Mankind’s Search for God kapena matrakiti ndi timabuku tosiyanasiyana kuyambitsa kukambitsirana ndipo mwinamwake phunziro la Baibulo. Ngati wa chisinthiko afunsa ponena za chilengedwe, tingagwiritsire ntchito buku la Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? Ngati munthu wachichepere afunsa kuti, ‘Kodi chifuno cha moyo nchiyani?’ tingatembenukire naye ku buku la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. Ngati wina wayambukiridwa kwambiri ndi vuto laumwini—kupsinjika maganizo, kutopa, kugwiriridwa chigololo, chisudzulo—tili ndi magazini amene alongosola mogwira mtima nkhani zoterozo. Ndithudi, kagulu ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru kamene Yesu analosera kuti kakapereka “zakudya pa nthaŵi yake” kakukwaniritsa ntchito yake.—Mateyu 24:45-47.
19, 20. Kodi ntchito ya Ufumu yafulumizidwa motani ku Albania?
19 Koma pofuna kufikira mitundu, kwakhala koyenera kutulutsa mabuku ameneŵa m’zinenero zambiri. Kodi zatheka motani kumasulira Baibulo ndi mabuku Amalemba m’zinenero zoposa 200? Kupenda mwachidule chitsanzo chimodzi, Albania, kumasonyeza mmene kagulu ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru kakhalira kokhoza kuchirikiza mbiri yabwino mosasamala kanthu za mavuto aakulu ndipo popanda Pentekoste wamakono wopereka mwaŵi wakulankhula zinenero panthaŵi yomweyo.—Machitidwe 2:1-11.
20 Zaka zoŵerengeka zokha zapitazo, Albania anali kuonedwabe monga dziko lokha la Chikomyunizimu losakhulupiriradi kukhalapo kwa Mulungu. Magazini a National Geographic ananena mu 1980 kuti: “Albania amaletsa [chipembedzo], akumadzilengeza mu 1967 ‘kukhala boma loyamba losakhulupirira kukhalapo kwa Mulungu m’dziko.’ . . . Mbadwo watsopano wa ku Albania umadziŵa kusakhulupirira kukhalapo kwa Mulungu kokha.” Tsopano popeza kuti Chikomyunizimu chagwa, anthu a ku Albania amene akuzindikira kusoŵa kwawo kwauzimu akulabadira kulalikira kumene kukuchitidwa ndi Mboni za Yehova. Kagulu kakang’ono ka otembenuza ka Mboni zachichepere zodziŵa Chitaliyana ndi Chingelezi kanapangidwa mu Tiranë mu 1992. Abale achidziŵitso odzacheza kuchokera ku maiko ena anawaphunzitsa kugwiritsira ntchito makompyuta a laptop kulemba mawu m’Chialbania. Iwo anayamba kutembenuza matrakiti ndi magazini a Nsanja ya Olonda. Pamene akuzoloŵera, amayamba kutembenuza zofalitsidwa zina zofunika za Baibulo. Pakali pano kuli Mboni zokangalika pafupifupi 200 m’dziko laling’ono limenelo (la anthu 3,262,000), ndipo 1,984 anafika pa Chikumbutso mu 1994.
Tonsefe Tili ndi Thayo
21. Kodi tikukhala m’nyengo yotani?
21 Zochitika za dziko zikufika pachimake. Pokhala ndi kuwonjezeka kwa upandu ndi chiwawa, kuphana ndi kugwirira chigololo m’nkhondo zakumaloko, mkhalidwe wolekerera wachisembwere womwe ulipo ndi zipatso zake za matenda opatsirana mwakugonana, kusalemekeza ulamuliro wovomerezedwa mwalamulo, dziko likuonekera kukhala losokonezeka, losalamulirika. Tili m’nyengo yofanana ndi nthaŵi za Chigumula chisanadze zolongosoledwa mu Genesis kuti: “Anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu pa dziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha. Ndipo Yehova anamva chisoni chifukwa anapanga munthu pa dziko lapansi, ndipo anavutika m’mtima mwake.”—Genesis 6:5, 6; Mateyu 24:37-39.
22. Kodi ndi thayo Lachikristu lotani limene Mboni za Yehova zonse zili nalo?
22 Mofanana ndi m’tsiku la Nowa, Yehova adzachitapo kanthu. Koma chifukwa cha chilungamo ndi chikondi chake, iye akufuna kuti mbiri yabwino ndi uthenga wochenjeza ulalikidwe choyamba ku mitundu yonse. (Marko 13:10) Chifukwa cha zimenezi Mboni za Yehova zili ndi thayo—kupeza awo amene ali oyenerera mtendere wa Mulungu ndi kuwaphunzitsa njira zake zamtendere. Posachedwapa, m’nthaŵi yoyenera ya Mulungu, ntchito yolalikira idzamalizidwa mwachipambano. “Pomwepo chidzafika chimaliziro.”—Mateyu 10:12, 13; 24:14; 28:19, 20.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mupeze chidziŵitso chowonjezereka ponena za Akunja, onani mutu wakuti “Nations” mu Insight on the Scriptures, Voliyumu II, masamba 472-4, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b Kuti mupeze malingaliro othandiza a utumiki Wachikristu, onani Nsanja ya Olonda ya February 1, 1985, tsamba 15, “Mmene Mungakhalire Aminisitala Ogwira Mtima,” ndi tsamba 21, “Uminisitala Wogwira Mtima Wotsogolera ku Ophunzira Ochulukirapo.”
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi Mboni zamakono zakhala ndi chipambano chotani muutumiki wawo?
◻ Kodi nchifukwa ninji ambiri amakana uthenga Wachikristu?
◻ Kodi ndi njira ya atumwi yakulalikira yotani imene Mboni zimagwiritsira ntchito?
◻ Kodi ndi ziŵiya zotani zimene tili nazo zochitira utumiki wogwira mtima?
◻ Kodi tonsefe tiyenera kuchita chiyani mogwirizana ndi Marko 13:10?
[Bokosi patsamba 19]
DZIKO MBONI ZOKANGALIKA MU 1943 MU 1993
Argentina 374 102,043
Brazil 430 366,297
Chile 72 44,668
Colombia ?? 60,854
France Nkhondo Yadziko II-palibe zolembedwa 122,254
Ireland 150? 4,224
Italy Nkhondo Yadziko II-palibe zolembedwa 201,440
Mexico 1,565 380,201
Peru Palibe zolembedwa za ntchito 45,363
Philippines Nkhondo Yadziko II-palibe zolembedwa 116,576
Poland Nkhondo Yadziko II-palibe zolembedwa 113,551
Portugal Palibe zolembedwa za ntchito 41,842
Spain Palibe zolembedwa za ntchito 97,595
Uruguay 22 9,144
Venezuela Palibe zolembedwa za ntchito 64,081
[Chithunzi patsamba 17]
Mboni za Yehova zikuwonjezereka m’maiko ambiri Achikatolika, monga ngati Spain
[Zithunzi patsamba 18]
Mboni za Yehova zili zokangalika m’maiko padziko lonse