Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lff phunziro 16
  • Kodi Yesu Anachita Zotani Ali Padzikoli?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Yesu Anachita Zotani Ali Padzikoli?
  • Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • FUFUZANI MOZAMA
  • ZOMWE TAPHUNZIRA
  • ONANI ZINANSO
  • Kodi pa Zozizwitsa za Yesu Mungaphunzirepo Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kodi Tingaphunzire Chiyani pa Zozizwitsa za Yesu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Kodi Yesu Ndi Ndani?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Yesu Ali Ndi Makhalidwe Otani?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
lff phunziro 16
Phunziro 16. Yesu akuphunzitsa gulu la amuna ndi akazi omwe akhala paphiri.

PHUNZIRO 16

Kodi Yesu Anachita Zotani Ali Padzikoli?

Losindikizidwa
Losindikizidwa
Losindikizidwa

Anthu ambiri akaganizira za Yesu amamukumbukira ngati mwana wakhanda atagonekedwa modyeramo ziweto. Ena amamukumbukira ngati mneneri wanzeru, pamene ena amakumbukira mmene anafera. Koma kodi kuphunzira zokhudza moyo wa Yesu ali padziko lapansi kungatithandize bwanji kumudziwa bwino? M’phunziroli tikambirana zinthu zina zofunika kwambiri zimene Yesu anachita komanso mmene zingakuthandizireni.

1. Kodi ntchito yofunika kwambiri yomwe Yesu ankagwira inali yotani?

Ntchito yofunika kwambiri yomwe Yesu ankagwira inali ‘yolengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.’ (Werengani Luka 4:​43.) Iye ankalalikira uthenga wabwino wakuti Mulungu adzakhazikitsa ufumu, kapena kuti boma, lomwe lidzathetse mavuto onse amene anthu akukumana nawo padzikoli.a Yesu anagwira mwakhama ntchito youza anthu uthenga wolimbikitsawu kwa zaka zitatu ndi hafu.​—Mateyu 9:​35.

2. N’chifukwa chiyani Yesu ankachita zozizwitsa?

Baibulo limafotokoza kuti ‘Mulungu anagwiritsa ntchito Yesu pochita ntchito zamphamvu, zodabwitsa komanso zizindikiro.’ (Machitidwe 2:22) Mulungu anapatsa Yesu mphamvu zotha kulamulira mphepo, kudyetsa anthu masauzande ambirimbiri, kuchiritsa odwala, ngakhalenso kuukitsa anthu amene anamwalira. (Mateyu 8:23-27; 14:15-21; Maliko 6:56; Luka 7:11-17) Zozizwitsa zimene Yesu ankachita ndi umboni woti iye anachita kutumidwa ndi Mulungu komanso wakuti Yehova ali ndi mphamvu zothetsa mavuto athu onse.

3. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Yesu?

Yesu ankamvera Yehova pa chilichonse. (Werengani Yohane 8:​29.) Yesu ankachita chilichonse chimene Atate wake amutuma. Iye ankachita zimenezi pa nthawi yonse yomwe anali ndi moyo padziko lapansi ngakhale kuti anthu ena ankafuna kumulepheretsa. Zimene anachitazi zikusonyeza kuti n’zotheka kuti anthu azitumikirabe Mulungu mokhulupirika ngakhale kuti akukumana ndi mavuto. Choncho, Yesu ‘anatisiyira chitsanzo kuti titsatire mapazi ake mosamala kwambiri.’​—1 Petulo 2:21.

FUFUZANI MOZAMA

Fufuzani kuti muone zimene Yesu ankachita kuti alalikire uthenga wabwino komanso mmene anachitira zozizwitsa.

4. Yesu ankalalikira uthenga wabwino

Yesu ankayenda mitunda italiitali kwambiri m’misewu yafumbi, n’cholinga choti akalalikire uthenga wabwino kwa anthu ambiri. Werengani Luka 8:1, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi Yesu ankalalikira kwa anthu okhawo amene asonkhana kuti amvetsere ulaliki wake?

  • Kodi Yesu ankachita chiyani kuti afikire anthu kulikonse komwe ali?

Mulungu ananeneratu kuti Mesiya adzalalikira uthenga wabwino. Werengani Yesaya 61:1, 2, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi Yesu anakwaniritsa bwanji ulosi umenewu?

  • Kodi mukuona kuti masiku ano anthu akufunika kumva uthenga wabwinowu?

Yesu akulowa m’mudzi ndi ophunzira ake ena.

5. Yesu anaphunzitsa mfundo zothandiza

Kuwonjezera pa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu Yesu ankaphunzitsa mfundo zothandiza. Tiyeni tikambirane zitsanzo zingapo zosonyeza mmene Yesu ankachitira zimenezi pa ulaliki wina wotchuka wotchedwa Ulaliki Wapaphiri. Werengani Mateyu 6:14, 34 ndi 7:12, kenako mukambirane mafunso awa:

  • M’mavesiwa kodi Yesu anapereka malangizo othandiza ati?

  • Kodi mukuona kuti malangizo amenewa angatithandize masiku ano?

Yesu akuphunzitsa gulu la amuna, akazi komanso ana pa Ulaliki Wapaphiri.

6. Yesu anachita zozizwitsa

Yehova anapatsa Yesu mphamvu zochita zozizwitsa zambiri. Kuti muone chitsanzo chimodzi, werengani Maliko 5:25-34 kapena onerani VIDIYO. Kenako mukambirane mafunso otsatirawa.

VIDIYO: Yesu Anachiritsa Mzimayi (5:10)

  • Muvidiyoyi, kodi mayi wodwalayu ankakhulupilira zotani?

  • N’chiyani chimene chikukusangalatsani mukaganizira chozizwitsa chimenechi?

Werengani Yohane 5:36, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi zozizwitsa zimene Yesu anachita ‘zinamuchitira umboni’ wotani?

Yesu wagwada ndipo akulankhula ndi mayi yemwe akuchita mantha pambuyo poti wachiritsidwa ku nthenda yake yakukha magazi.

Kodi mukudziwa?

Zinthu zambiri zokhudza moyo wa Yesu zimapezeka m’mabuku 4 a m’Baibulo otchedwa Uthenga Wabwino. Mabukuwa ndi Mateyu, Maliko, Luka ndi Yohane. Aliyense wa olemba mabukuwa anafotokoza mfundo zokhudza Yesu m’njira zosiyanasiyana. Choncho tikamawerenga mabukuwa timamvetsa bwino zomwe zinachitika pa moyo wa Yesu.

  • MATEYU

    ndi amene anayamba kulemba buku loyamba la Uthenga Wabwino. Bukuli limatiuza zambiri zimene Yesu anaphunzitsa makamaka zokhudza Ufumu wa Mulungu.

  • MALIKO

    ndi amene analemba buku lalifupi kwambiri pa mabuku a Uthenga Wabwino. Bukuli limatiuza zinthu zambiri zochititsa chidwi.

  • LUKA

    anafotokoza kuti Yesu ankaona kuti pemphero ndi lofunika kwambiri komanso kuti ankachita zinthu mwachifundo ndi akazi.

  • YOHANE

    ndi amene anafotokoza makhalidwe ambiri a Yesu. Tikutero chifukwa chakuti analemba zinthu zambiri zomwe Yesu ankakambirana ndi anzake apamtima komanso anthu ena.

ZIMENE ENA AMANENA: “Yesu anangokhala munthu wabwino chabe.”

  • Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Yesu ankalalikira zokhudza Ufumu wa Mulungu, ankachita zozizwitsa komanso ankamvera Yehova pa chilichonse.

Kubwereza

  • Kodi ndi ntchito yofunika kwambiri iti yomwe Yesu ankagwira ali padziko lapansi?

  • Kodi zozizwitsa zimene Yesu anachita zinkasonyeza chiyani?

  • Kodi ndi mfundo zothandiza ziti zimene Yesu anaphunzitsa?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Kodi nkhani imene Yesu ankakonda kukambirana ndi anthu inali yokhudza chiyani?

“Yesu Ankaona Kuti Ufumu wa Mulungu Ndi Wofunika Kwambiri” (Nsanja ya Olonda, October 1, 2014)

Fufuzani kuti muone chifukwa chake sitikayikira kuti Yesu anachitadi zozizwitsa.

“Kodi pa Zozizwitsa za Yesu Mungaphunzirepo Chiyani?” (Nsanja ya Olonda, July 15, 2004)

Werengani nkhaniyi kuti muone mmene munthu wina yemwe anali ndi khalidwe lodzikonda anasinthira potengera chitsanzo cha Yesu.

“Ndinali Munthu Wodzikonda Kwambiri” (Nsanja ya Olonda, October 1, 2014)

Onani zochitika zikuluzikulu zokhudza utumiki wa Yesu malinga ndi nthawi imene zinachitika.

“Zochitika Zikuluzikulu M’moyo wa Yesu Padziko Lapansi” (Kabuku Kothandiza Kuphunzira Mawu a Mulungu, tsamba 18-33)

a Nkhani yokhudza Ufumu wa Mulungu idzafotokozedwa bwino kwambiri m’phunziro 31 mpaka 33.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena