Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 5/15 tsamba 8-9
  • Funso la Utate

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Funso la Utate
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhani Yofanana
  • Nkhani ya Utate
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Kodi Atate Wawo Anali Abulahamu Kapena Mdyerekezi?
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Abulahamu Anali “Bwenzi” la Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Kodi Abulahamu Anali Ndani?
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 5/15 tsamba 8-9

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Funso la Utate

MKATI mwa Phwando la Misasa la 32 C.E., kukambitsirana kwa Yesu ndi atsogoleri Achiyuda kwafika poipa. “Ndidziŵa kuti muli mbewu ya Abrahamu,” Yesu akuvomereza, “koma mufuna kundipha ine, chifukwa mawu anga alibe malo mwa inu. Zimene ndinawona ine kwa Atate, ndilankhula. Ndipo inunso muchita chimene mudamva kwa atate wanu.”

Ngakhale kuti sakudziŵikitsa atate wawo, Yesu akuchimveketsa kuti atate wawo ali wosiyana ndi atate ake. Osadziŵa za amene Yesu ali naye m’malingaliro, atsogoleri Achiyuda akuyankha: “Atate wathu ndiye Abrahamu.” Iwo akudzimva kuti ali ndi chikhulupiriro chofanana ndi cha Abrahamu, yemwe anali bwenzi la Mulungu.

Ngakhale kuli tero, Yesu akuwadabwitsa iwo ndi yankho iri: “Ngati muli ana a Abrahamu, mukadachita ntchito za Abrahamu.” Ndithudi, mwana weniweni amatsanzira atate ake. “Koma tsopano mufuna kundipha ine,” Yesu akutero, “ndine munthu amene ndinalankhula ndi inu chowonadi chimene ndinamva kwa Mulungu. Ichi Abrahamu sanachita.” Chotero Yesu akunenanso kuti: “Inu muchita ntchito za atate wanu.”

Kufikira tsopano iwo sakumvetsetsabe amene Yesu akulankhula ponena za iye. Iwo akusungirira kuti ali ana enieni a Abrahamu, akumanena kuti: “Sitinabadwa ife m’chigololo.” Chotero akumadzinenera kukhala alambiri enieni monga Abrahamu, iwo akuti: “Tiri naye Atate mmodzi, Mulungu.”

Koma kodi Mulungu ndithudi ndiye Atate wawo? “Mulungu akadakhala atate wanu,” Yesu akuyankha, “mukadakonda ine, pakuti ine ndinatuluka ndi kuchokera kwa Mulungu. Pakuti sindinadza kwa ine ndekha, koma Iyeyu anandituma ine. Simuzindikira malankhulidwe anga chifukwa ninji?”

Yesu wayesera kusonyeza atsogoleri achipembedzo amenewo zotulukapo za kumkana kwawo iye. Koma tsopano iye mwachindunji akunena kuti: “Inu muli ochokera mwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita.” Kodi ndi atate a mtundu wanji amene Mdyerekezi ali? Yesu anamzindikiritsa iye monga wambanda ndiponso ananena kuti: “Iye ali wabodza ndi atate wake wa bodza.” Chotero Yesu akumaliza: “Iye wochokera kwa Mulungu amva zonena za Mulungu. Inu simumva chifukwa chakuti simuli a kwa Mulungu.”

Okwiitsidwa ndi chitsutso cha Yesu, Ayuda ayankha: “Kodi sitinenetsa kuti inu ndinu Msamariya, ndipo muli ndi chiwanda?” Liwu lakuti “Msamariya” likugwiritsiridwa ntchito monga kalongosoledwe ka kuputa ndi kutonza, Asamariya akumakhala anthu odedwa ndi Ayuda.

Akumanyalanyaza kalankhulidwe kawo kotonza konena za kukhala Msamariya, Yesu akuyankha: “Ndiribe chiwanda ine, koma ndilemekeza Atate wanga, ndipo inu mundipeputsa.” Akupitiriza, Yesu akupanga lonjezo lozizwitsa: “Munthu akasunga mawu anga, sadzawona imfa nthaŵi yonse.” Ndithudi, Yesu sanatanthauze kuti awo onse amene akutsatira iye m’chenicheni sadzawona imfa. M’malomwake, iye akutanthauza kuti iwo sadzawona chiwonongeko chotheratu, kapena “imfa yachiŵiri,” kuchokera ku imene kulibe chiwukiriro.

Ngakhale kuli tero, Ayuda akutenga mawu a Yesu m’lingaliro lenileni. Chotero, iwo akunena kuti: “Tsopano tizindikira kuti muli ndi chiwanda. Abrahamu anamwalira, ndi aneneri; ndipo inu munena, ‘Munthu akasunga mawu anga, sadzalaŵa imfa ku nthaŵi yonse.’ Kodi inu ndinu wamkulu ndi atate wathu Abrahamu, amene anamwalira? Ndipo aneneri anamwalira: mudziyesera nokha muli yani?”

M’kukambitsirana konseku, chiri chodziŵikiratu kuti Yesu akulozera anthuwa ku chenicheni chakuti iye ali Mesiya wolonjezedwa. Koma m’malo mwakuyankha mwachindunji mafunso awo ponena za chizindikiritso chake, Yesu akunena kuti: “Ngati ine ndidzilemekeza ndekha, ulemerero wanga uli wachabe. Atate wanga ndiye wondilemekeza ine, amene munena za iye kuti ndiye Mulungu wanu; ndipo inu simunamdziŵa iye. Koma ine ndimdziŵa iye. Ndipo ngati ndinena kuti sindimdziŵa iye, ndidzakhala wonama chimodzimodzi inu.”

Akupitiriza, Yesu akulozeranso kwa Abrahamu wokhulupirika, akumanena kuti: “Atate wanu Abrahamu anakondwera kuwona tsiku langa, ndipo anawona, nasangalala.” Inde, ndi maso a chikhulupiriro, Abrahamu anayang’ana kutsogolo ku kufika kwa Mesiya wolonjezedwa. M’kusakhulupirira, Ayuda, akuyankha: “Simunafikire zaka makumi asanu, ndipo munawona Abrahamu kodi?”

“Indetu indetu, ndinena kwa inu,” Yesu akuyankha, “asanayambe kukhala Abrahamu ndipo ine ndiripo.” Yesu, m’chenicheni, akulozera ku kukhalapo kwake asanakhale munthu monga munthu wauzimu wamphamvu kumwamba.

Okwiitsidwa ndi kudzinenera kwa Yesu kwakukhalapo asanakhale Abrahamu, Ayuda atola miyala kuti amponye nayo. Koma iye abisala ndi kuchoka m’kachisi osavulazidwa. Yohane 8:37-59; Chivumbulutso 3:14; 21:8.

◆ Ndimotani mmene Yesu akusonyezera kuti iye ndi adani ake ali ndi atate osiyana?

◆ Nchiyani chimene chiri nsonga ya Ayuda m’kutchula Yesu kukhala Msamariya?

◆ Ndi mlingaliro lotani mmene Yesu akutanthauza kuti atsatiri ake sadzawona imfa?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena