-
Mphatso Zoyenera Kupatsa MfumuNsanja ya Olonda—2015 | March 1
-
-
Kodi zonunkhira zomwe zinkachokera ku mayiko ena, zinkachokera mayiko ati? Aloye, kasiya ndi sinamoni ankachokera kudera lomwe masiku ano ndi China, India ndi Sri Lanka. Mule ndi lubani ankachokera m’dera lachipululu lomwe linkayambira kum’mwera kwa Arabia mpaka kukafika ku Somalia, komwe ndi ku Africa. Ndipo nado wambiri ankachokera ku India, kumapiri a Himalaya.
-