-
“New World Translation”—Yaukatswiri ndi YowonaNsanja ya Olonda—1991 | March 1
-
-
Pa Yohane 1:1 New World Translation imati: “Mawu anali mulungu.” M’matembenuzidwe ambiri ndemangayi imati: “Mawu anali Mulungu” ndipo imagwiritsiridwa ntchito kuchilikiza chiphunzitso cha Utatu. Mosadabwitsa, nchifukwa chake okhulupirira Utatu samakufuna kumasulira kwa New World Translation. Koma Yohane 1:1 sinapotozedwe kotero kuti imutsimikizire Yesu kusakhala Mulungu Wamphamvuyonse. Kalekale New World Translation isanakhalepo, Mboni za Yehova, pakati pa ena ambiri, zinatsutsa kulemba chilembo choyambirira cha liwu lakuti “mulungu” kukhala chachikulu, kumene kuli kuyesayesa kumasulira molongosoka chinenero choyambirira. Ajeremani asanu otembenuza Baibulo mofananamo amagwiritsira ntchito liwu lakuti “mulungu” m’vesi limenelo.b Pafupifupi ena 13 agwiritsira ntchito mawu onga “wa mtundu waumulungu” kapena “waumulungu.” Kumasulira kumeneku kumamvana ndi mbali zina za Baibulo kuvomereza kuti, inde, Yesu kumwamba ali mulungu m’lingaliro lakuti ngwaumulungu. Koma Yehova ndi Yesu sali munthu mmodzimodzi, Mulungu mmodzimodzi.—Yohane 14:28; 20:17.
-
-
“New World Translation”—Yaukatswiri ndi YowonaNsanja ya Olonda—1991 | March 1
-
-
b Jürgen Becker, Jeremias Felbinger, Oskar Holtzmann, Friedrich Rittelmeyer, ndi Siegfried Schulz. Emil Bock amati, “munthu waumulungu.” Onaninso matembenuzidwe Achingelezi aŵa Today’s English Version, The New English Bible, Moffatt, Goodspeed.
-