Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kudzichepetsa pa Paskha Womalizira
PETRO ndi Yohane, mwakulangizidwa ndi Yesu, afika kale m’Yerusalemu kukakonzekera Paskha. Mwachiwonekere, Yesu pamodzi ndi atumwi khumi enawo, akufika mochedwa masana. Dzuŵa likuloŵa m’chizimezime pamene Yesu ndi gulu lake akutsika pa Phiri la Azitona ndi kudutsa Chigwa cha Kedroni. Ili ndi tsiku lomalizira lowona mzinda la Yesu kufikira pambuyo pa kuukitsidwa kwake.
Mofulumira Yesu ndi gulu lake afika mu mzindawo nkupita kunyumba kumene akachitira phwando la Paskha. Iwo akwera makwerero onkira kuchipinda chachikulu chapamwamba, komwe akupeza kuti zonse zakonzekeretsedwa kaamba ka phwando lawo lachinsinsi la Paskha. Yesu ankayembekezera chochitikachi, monga momwe iye akunenera kuti: “Ndinalakalaka ndithu kudya Paskha uwu pamodzi ndinu, ndisanayambe kusautsidwa.”
Mwamwambo, zikho zinayi za vinyo zamwedwa kale ndi otengamo phande a Paskhayo. Pambuyo polandira chomwe chikuwonekera kukhala chikho chachitatu, Yesu ayamika ndi kuti: ‘Landirani ichi, muchigawane mwa inu nokha; pakuti ndinena kwa inu, kuyambira tsopano Ine sindidzamwako chipatso cha mpesa, kufikira Ufumu wa Mulungu udzafika.’
Nthaŵi ina mkati mwa chakudyacho, Yesu anyamuka, navula malaya ake, natenga chopukutira, nathira madzi m’nsambidwe. Mwachibadwa, wochereza akatsimikizira kuti mapazi a alendo asambitsidwa. Koma popeza kuti pa chochitikachi palibe wochereza, Yesu akusamalira ntchito yaumwiniyi. Aliyense wa atumwiwo akadatenga mwaŵi wa kuchita ichi; komabe, mwachiwonekere popeza kuti padali kukangana pakati pawo, palibe yemwe akuchita tero. Tsopano akuchititsidwa manyazi pamene Yesu akuyamba kusambitsa mapazi awo.
Pamene Yesu adza kwa Petro, iye akana motere: “Simudzasambitsa mapazi anga ku nthawi yonse.”
‘Ngati sindikusambitsa iwe ulibe cholandira pamodzi ndi Ine,’ atero Yesu.
“Ambuye,” Petro ayankha motero, “si mapazi anga okha, komanso manja ndi mutu.”
Yesu anena naye kuti, “Amene anatha kusamba alibe kusowa koma kusamba mapazi, koma ayera monse: ndipo inu ndinu oyera, koma si nonse ai.” Iye akunena izi chifukwa chakuti akudziŵa kuti Yudase Isikariote akukonzekera kumpereka.
Pamene Yesu wasambitsa mapazi a 12 onsewo, kuphatikizapo mapazi a wompereka wake, Yudase, iye avala malaya ake naseyama kachiŵirinso. Pamenepo iye akufunsa kuti: ‘Nanga chimene ndakuchitirani inu, muchizindikira kodi? Inu mundicha Ine Mphunzitsi, ndi Ambuye: ndipo munena bwino; pakuti ndine amene. Chifukwa chake, ngati Ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi wina ndi mnzake. Pakuti ndakupatsani inu chitsanzo, kuti, monga Ine ndakuchitirani inu, inunso muchite. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake; kapena mtumwi sali wamkulu ndi womtuma iye. Ngati mudziwa izi, odala inu ngati muzichita.’
Ndi phunziro labwino chotani nanga la kuchita utumiki wodzichepetsa! Atumwiwo sayenera kufunafuna malo oyamba, akumalingalira kuti ngofunika kwambiri kwakuti ena akayenera kuwatumikira nthaŵi zonse. Iwo afunikira kutsatira chitsanzo chokhazikitsidwa ndi Yesu. Ichi sichimodzi cha miyambo ya kusambitsa mapazi. Ayi, koma nchakufunitsitsa kwa kutumikira popanda tsankho, mosasamala kanthu za kutsika kapena kusasangalatsa kumene ntchitoyo ingakhalire. Mateyu 26:20, 21; Marko 14:17, 18; Luka 22:14-18; 7:44; Yohane 13:1-17.
◆ Kodi nchiyani chimene chiri chapadera ponena za kuwona Yerusalemu kwa Yesu pamene akuloŵa kukachita phwando la Paskha?
◆ Mkati mwa Paskha, kodi nchikho chiti chimene Yesu mwachiwonekere akupatsa atumwi 12 pambuyo pakuyamika?
◆ Kodi ndi utumiki waumwini uti umene unali mwambo woperekedwa kwa alendo pamene Yesu anali padziko lapansi, ndipo kodi nchifukwa ninji iwo sunaperekedwe mkati mwa phwando la Paskha lochitidwa ndi Yesu ndi atumwi ake?
◆ Kodi nchiti chimene chinali chifuno cha Yesu chakuchitira utumiki wapansi wosambitsa mapazi a atumwi ake?