Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 3/1 tsamba 30-31
  • Munthu Wamkulu Koposa Onse Achita Utumiki Wodzichepetsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Munthu Wamkulu Koposa Onse Achita Utumiki Wodzichepetsa
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Phunziro la Kudzichepetsa
  • Phunziro kwa Ife
  • Anawaphunzitsa Kudzichepetsa pa Pasika Womaliza
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kudzichepetsa pa Paskha Womalizira
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kudzichepetsa pa Paskha Womalizira
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Yesu Anatipatsa Chitsanzo cha Kudzichepetsa
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 3/1 tsamba 30-31

Anachita Chifuniro cha Yehova

Munthu Wamkulu Koposa Onse Achita Utumiki Wodzichepetsa

YESU anadziŵa kuti maola omaliza kukhala pamodzi ndi atumwi ake akakhala amtengo wapatali kwambiri. Posachedwa, akagwidwa, ndiponso chikhulupiriro chake chikayetsedwa koposa kale lonse. Yesu ankadziŵanso kuti madalitso aakulu anali m’tsogolo. Posachedwa anali kukakwezedwa kudzanja lamanja la Mulungu ndi kupatsidwa “dzina limene liposa mayina onse, kuti m’dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m’mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko.”​—Afilipi 2:9, 10.

Komabe, nkhaŵa ya imfa yake yomwe inali pafupiyi kapena chilakolako cha mphoto imene analonjezedwa sinamuiŵalitse zosoŵa za atumwi ake. Pambuyo pake Yohane analemba mu Uthenga wake Wabwino kuti, iye “anawakonda kufikira chimaliziro.” (Yohane 13:1) Ndipo m’maola omaliza a moyo wake monga munthu wangwiro ovutaŵa, Yesu anawaphunzitsa atumwi ake phunziro lofunika kwambiri.

Phunziro la Kudzichepetsa

Yesu ndi atumwi ake anali m’chipinda chapamwamba ku Yerusalemu kukachita phwando la Paskha. Papitapo, Yesu anawamva akukangana ponena za amene anali wamkulu pakati pawo. (Mateyu 18:1; Marko 9:33, 34) Anali atakambirana nawo nkhani imeneyi ndipo anayesetsa kuwadzudzula malingaliro awo. (Luka 9:46) Tsopano, nthaŵi ino, Yesu anagogomezera maphunzirowo mwa kugwiritsa ntchito njira ina. Iye sanawauze kokha za kudzichepetsa koma anawaonetsa chitsanzo cha kudzichepetsa.

Yesu “ananyamuka pamgonero, navula malaya ake,” akulemba motero Yohane. “Ndipo mmene adatenga chopukutira, anadzimanga m’chuuno. Pomwepo anathira madzi m’nsambidwe, nayamba kusambitsa mapazi a akuphunzira ake, ndi kuwapukuta ndi chopukutira, chimene anadzimanga nacho.”​—Yohane 13:4, 5.

Nthaŵi yotentha ku Middle East wakale, kaŵirikaŵiri anthu ankavala sandasi poyenda m’misewu yafumbi. Akafika pa nyumba ya munthu wamba, woitana alendoyo ndiye ankawalandira, komanso ndi iye ankapereka mosambira ndi madzi oti asambe mapazi awo. M’nyumba zopeza bwino, kapolo ndiye ankasambitsa anthu mapazi.​—Oweruza 19:21; 1 Samueli 25:40-42.

M’chipinda chapamwamba, Yesu ndi atumwi ake sanali alendo a wina aliyense. Panalibe wolandira alendo woti abweretse mosambira, ndiponso panalibe akapolo osambitsa anthu mapazi. Pamene Yesu anayamba kusambitsa mapazi awo, atumwi anachita manyazi kwambiri. Pano, Amene anali wamkulu pakati pawo anachita ntchito yodzichepetsa kwambiri!

Poyamba, Petro anakana kuti Yesu amusambitse mapazi ake. Koma Yesu anamuuza kuti: “Ngati sindikusambitsa iwe ulibe cholandira pamodzi ndi Ine.” Pamene Yesu anamaliza kusambitsa atumwi ake onse mapazi, anati: “Nanga chimene ndakuchitirani inu, muchizindikira kodi? Inu munditcha Ine Mphunzitsi, ndi Ambuye: ndipo munena bwino; pakuti ndine amene. Chifukwa chake, ngati Ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi wina ndi mnzake. Pakuti ndakupatsani inu chitsanzo, kuti, monga Ine ndakuchitirani inu, inunso muchite.”​—Yohane 13:6-15.

Yesu sanali kuyambitsa mwambo wosambitsa mapazi. Komano, anali kuthandiza atumwi ake kusintha maganizo awo​—kuti akhale ndi maganizo odzichepetsa ndi ofunitsitsa kuchita ntchito zonyozeka m’malo mwa abale awo. Mwachionekere, anamvetsa cholinga cha chochitikachi. Lingalirani zimene zinachitika patapita zaka zambiri pamene funso la mdulidwe linabuka. Ngakhale panali “mafunsano ambiri,” anthu opezekapo anasunga bata ndipo anamvetsera molemekeza malingaliro a wina ndi mnzake. Komanso, kukuoneka kuti amene anali kutsogolera msonkhanowu anali wophunzira Yakobo​—osati mmodzi wa atumwi, monga tingaganizire, popeza analinso pomwepo. Mfundo imeneyi m’nkhani ya m’Machitidwe imasonyeza kuti atumwiwo anali atakulitsa kwambiri kudzichepetsa.​—Machitidwe 15:6-29.

Phunziro kwa Ife

Mwa kusambitsa ophunzira ake mapazi, Yesu anapereka phunziro lofunika kwambiri la kudzichepetsa. Inde, Akristu sayenera kudziona kukhala ofunika kwambiri akumafuna ena kuwatumikira nthaŵi zonse, komanso sayenera kukhumba malo aulemu ndi kutchuka. M’malo mwake, ayenera kutsatira chitsanzo cha Yesu, amene “sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.” (Mateyu 20:28) Ndithudi, otsatira a Yesu ayenera kukhala ofunitsitsa kuchitirana mautumiki odzichepetsa kwambiri wina ndi mnzake.

Pachifukwa chabwino Petro analemba kuti: “Muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.” (1 Petro 5:5) Liwu lachigiriki “muvale” lachokera ku liwu lotanthauza “epuloni ya kapolo,” yomwe amaimanga kunja kwa chovala chotakasuka. Kodi Petro angakhale anali kunena za chochitika cha Yesu chodzimanga chopukutira m’chuuno n’kusambitsa atumwi ake mapazi? Zimenezi sizinganenedwe motsimikizirika. Komabe, utumiki wodzichepetsa wa Yesu unali wosaiwalika mumtima wa Petro. Ndi mmenenso uyenera kukhalira m’mitima ya onse amene ali otsatira Kristu.​—Akolose 3:12-14.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena