Mutu 22
Kudziwa Chipembedzo Chowona
1. Kodi ndani amene anali kutsatira chipembedzo chowona m’zaka za zana loyamba?
SIPANGAKHALE kukayikira ponena za amene anali kutsatira chipembedzo chowona m’zaka za zana loyamba. Anali atsatiri a Yesu Kristu. Amenewa onse anali a gulu limodzi Lachikristu. Bwanji ponena za lerolino? Kodi awo amene akutsatira chipembedzo chowona angadziwidwe motani?
2. Kodi awo otsatira chipembedzo chowona angadziwidwe motani?
2 Pofotokoza mmene tingachitire zimenezi, Yesu anati: “Mudzawazindikira ndi zipatso zawo. . . . Mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa. . . . Inde chomwecho pa zipatso zawo mudzawazindikira iwo.” (Mateyu 7:16-20) Kodi mukayembekezere alambiri owona a Mulungu kubala zipatso zabwino zotani? Kodi iwo ayenera kukhala akunena ndi kuchita chiyani tsopano?
KUYERETSA DZINA LA MULUNGU
3, 4. (a) Kodi pempho loyamba loperekedwa m’Pemphero Lachitsanzo la Yesu linali lotani? (b) Kodi Yesu anayeretsa dzina la Mulungu motani?
3 Olambira owona a Mulungu akachita mogwirizana ndi Pemphero Lachitsanzo limene Yesu anapatsa atsatiri ake. Chinthu choyamba chimene Yesu anatchula m’menemo chinali ichi: “Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.” Kutembenuza kwina Kwabaibulo kumaika mawu amenewa motere: “Dzina lanu liwonedwetu kukhala loyera.” (Mateyu 6:9, Jerusalem Bible) Kodi kuyeretsa, kapena kuwona kukhala loyera, dzina la Mulungu kumatanthauzanji? Kodi Yesu anakuchita motani?
4 Yesu anasonyeza mmene anakuchitira pamene ananena m’pemphero kwa Atate wake kuti: “Ndaliwonetsera dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa Ine m’dziko lapansi.” (Yohane 17:6) Inde, Yesu analengeza dzina la Mulungu, Yehova, kwa ena. Iye sanalephere kugwiritsira ntchito dzina limenelo. Yesu anadziwa kuti chinali chifuno cha Atate wake kuti dzina Lawo lilemekezedwe m’dziko lonse lapansi. Motero iye anapereka chitsanzo m’kulengeza dzina limenelo ndi kuliwona kukhala loyera.—Yohane 12:28; Yesaya 12:4, 5.
5. (a) Kodi mpingo Wachikristu ukugwirizanitsidwa ndi dzina la Mulungu motani? (b) Kodi tiyenera kuchitanji ngati titi tipeze chipulumutso?
5 Baibulo limasonyeza kuti kukhalako kwenikweniko kwa mpingo Wachikristu kukugwirizanitsidwa ndi dzina la Mulungu. Mtumwi Petro anafotokoza kuti Mulungu “anatembenuzira maso ake kwa amitundu kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake.” (Machitidwe 15:14, NW) Motero anthu a Mulungu ayenera kuwona dzina lake kukhala loyera ndi kulilengeza m’dziko lonse lapansi. Kunena zowona, kudziwa dzina limenelo nkofunikira kaamba ka chipulumutso, monga momwe Baibulo likunenera kuti: “Pakuti ‘aliyense amene aitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa.’”—Aroma 10:13, 14, NW.
6. (a) Kodi matchalitchi onse akuwona dzina la Mulungu kukhala loyera? (b) Kodi pali alionse amene akuchitira umboni dzina la Mulungu?
6 Tsopano, pamenepa, kodi ndani lerolino amene amawona dzina la Mulungu kukhala loyera ndipo analilengeza padziko lonse lapansi? Matchalitchi onse amapewa kugwiritsiridwa ntchito kwa dzinalo Yehova. Ena alichotsadi m’matembenuzidwe awo a Baibulo. Komabe, ngati mukanamalankhula ndi anansi anu ndipo mukutchula Yehova kawirikawiri, mukumagwiritsira ntchito dzina lake, kodi muganiza kuti iwo akanakugwirizanitsani ndi gulu liti? Pali anthu amodzi okha amene akutsatiradi chitsanzo cha Yesu m’mbali imeneyi. Chifuno chawo chachikulu m’moyo ndicho kutumikira Mulungu ndi kuchitira umboni dzina lake, monga momwedi anachitira Yesu. Motero iwo atenga dzina Lamalembalo “Mboni za Yehova.”—Yesaya 43:10-12.
KULENGEZA UFUMU WA MULUNGU
7. Kodi Yesu anasonyeza motani kufunika kwa ufumu wa Mulungu?
7 M’Pemphero Lachitsanzo limene Yesu anapereka, iye anasonyezanso kufunika kwa ufumu wa Mulungu. Iye anaphunzitsa anthu kupemphera kuti: “Ufumu wanu udze.” (Mateyu 6:10) Mobwerezabwereza Yesu anagogomezera Ufumu kukhala chothetsera chokha cha mavuto a anthu. Iye ndi atumwi ake anachita zimenezi mwa kulalikira kwa anthu ponena za ufuu umenewo “kumudzi ndi mudzi” ndi “kunyumba ndi nyumba.” (Luka 8:1; Machitidwe 5:42; 20:20, NW) Ufumu wa Mulungu unali mutu wankhani wa kulalikira ndi kuphunzitsa kwawo.
8. Kodi Yesu anasonyeza motani chimene chikakhala uthenga waukulu wa atsatiri ake owona “m’masiku otsiriza” ano?
8 Bwanji ponena za nthawi yathu? Kodi nchiyani chimene chiri chuphunzitso chachikulu cha gulu lowona Lachikristu la Mulungu? M’kulosera “masiku otsiriza” ano, Yesu anati: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14, NW) Motero Ufumu uyenera kukhala uthenga waukulu wa anthu a Mulungu lerolino.
9. Kodi ndianthu ati lerolino amene akulalikira uthenga Waufumu?
9 Dzifunseni kuti: Ngati munthu afika pakhomo panu ndipo akunena za ufumu wa Mulungu kukhala chiyembekezo chowona cha anthu, kodi inu mumagwirizanitsa munthu ameneyo ndi gulu liti? Kodi anthu a chipembedzo chirichonse kusiyapo Mboni za Yehova alankhula nanu ponena za ufumu wa Mulungu? Eya, owerengeka kwambiri a iwo amadziwadi chimene uwo uli! Iwo samanena chirichonse ponena za boma la Mulungu. Chikhalirechobe boma limenelo ndilo mbiri yogwedeza dziko. Mneneri Danieli ananeneratu kuti ufumu umenewu ‘ukaphwanya ndi kutha maboma ena onse ndipo uwo wokha ukalamulira dziko lapansi.’—Danieli 2:44.
ULEMU KAAMBA KA MAWU A MULUNGU
10. Kodi Yesu analemekeza motani Mawu a Mulungu?
10 Njira ina mu imene awo amene akutsatira chipembedzo chowona angadziwidwire ndiyo mwa lingaliro lawo ku Baibulo. Yesu pa nthawi iriyonse analemekeza Mawua Mulungu. Iye anapita ku iwo mobwerezabwereza monga ulamuliro wotsiriza pa zinthu. (Mateyu 4:4, 7, 10; 19:4-6) Yesu analemekezanso Baibulo mwa kukhala ndi moyo mogwirizana ndi ziphunzitso zake. Iye sanaluluze Baibulo. M’malo mwake, iye anatsutsa awo amene analephera kuphunzitsa mogwirizana ndi Baibulo ndi amene anayesa kufooketsa mphamvu ya ziphunzitso zake mwa kupereka malingaliro awo a iwo eni.—Marko 7:9-13.
11. Kodi matchalitchi kawirikawiri amasonyeza lingaliro lotani ku Mawu a Mulungu?
11 Kodi matchalitchi a Dziko Lachikristu amatsatira motani chitsanzo cha Kristu m’mbali imeneyi? Kodi iwo analemekeza kwambiri Baibulo? Atsogoleri ambiri achipembedzo lerolino samakhulupirira cholembedwa Chabaibulo cha kulowa kwa Adamu mu uchimo, chigumula cha nthawi ya Nowa, Yona ndi chinsomba, ndi zina. Iwo amanenanso kuti munthu anafika pano mwa chisinthiko, osati mwa kulenga kwachindunji kwa Mulungu. Kodi iwo mwa njira imeneyo akulimbikitsa kulemekeza Mawu a Mulungu? Ndiponso, atsogoleri ena amatchalitchi amanena kuti kugonana kosakhala kwa muukwati sikuli kolakwa, kapena kuti ngakhale kugonana kwa ofanana ziwalo kapena mitala zingakhale zoyenera. Kodi munganene kuti iwo akulimbikitsa anthu kugwiritsira ntchito Baibulo monga chitsogozo chawo? Iwo sakutsatiradi chitsanzo cha Mwana wa Mulungu ndi atumwi ake.—Mateyu 15:18, 19; Aroma 1:24-27.
12. (a) Kodi nchifukwa ninji kulambira kwa ambiri amene alidi ndi Baibulo sikokondweretsa Mulungu? (b) Ngati ochita zoipa adala aloledwa kukhalabe m’kaimidwe kabwino m’tchalitchi, kodi tiyenera kunenanji?
12 Pali ziwalo zamatchalitchi zimene ziri ndi Baibulo ndipo zimaliphunziranso, koma njira imene izo zimakhalira imasonyeza kuti izo sizikulitsatira. Ponena za anthu onga amenewo, Baibulo limati: “Abvomereza kuti adziwa Mulungu, koma ndi ntchito zawo amkana Iye.” (Tito 1:16; 2 Timoteo 3:5) Ngati ziwalo zamatchalitchi zimene zimachova juga, zimaledzera kapena kuchita zolakwa zina zikuloledwa kukhalabe m’kaimidwe kabwino mkati mwa tchalitchi chawo, kodi zimenezi zimasonyezanji? Ndizo umboni wakuti gulu lawo lachipembedzo silikuvomerezedwa ndi Mulungu.—1 Akorinto 5:11-13.
13. Kodi munthu ayenera kupanga chosankha chachikulu chotani ngati iye wapeza kuti ziphunzitso za tchalitchi chake chonse sizikugwirizana ndi Baibulo?
13 Ngati mwalingalira mitu yapitayo ya bukhu lino, mukumawerenga malemba Abaibulo opezekamo, mwafika pa kudziwa ziphunzitso zazikulu za Mawu a Mulungu. Koma bwanji ngati ziphunzitso za gulu lachipembedzo limene mukugwirizana nalo ziri zosagwirizana ndi zija za Mawu a Mulungu? Pamenepo mukukhala ndi vuto lalikulu. Ndilo vuto la kusankha kaya kulandira kunena zowona za Baibulo kapena kukukana mochirikiza ziphunzitso zimene Baibulo silimachirikiza. Zimene mukuchita, ndithudi, ziyenera kukhala chosankha chanuchanu. Komabe, muyenera kupima zinthuzo mosamala. Zimenezi ziri chifukwa chakuti chosankha chimene mukupanga chidzayambukira kaimidwe kanu ndi Mulungu ndi ziyembekezo zanu za kukhala ndi moyo kosatha m’paradaiso padziko lapansi.
KUKHALA WOLEKANA NDI DZIKO
14. (a) Kodi chizindikiro china chodziwikitsa chipembedzo chowona nchotani? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwambiri kuti alambiri owona akwaniritse chofunika chimenechi?
14 Komabe chizindikiro china chodziwikitsa cha awo amene akutsatira chipembedzo chowona nchakuti, monga momwe Yesu ananenera, “iwo sali mbali ya dziko.” (Yohane 17:14, NW) Zimenezi zikutanthauza kuti olambira owona amakhala olekana ndi dziko loipa ndi zochita zake. Yesu Kristu anakana kukhala wolamulira wandale zadziko. (Yohane 6:15) Mungazindikire chifukwa chake kukhala wolekana ndi dziko kuli kofunika kwambiri pamene mukumbukira kuti Baibulo limanena kuti Satana Mdyerekezi ndiye wolamulira wa dziko. (Yohane 12:31; 2 Akorinto 4:4) Kuwopsa kwa nkhani imeneyi kukuwoneka mowonjezereka kuchokera m’mawu Abaibulowo: “Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani ndi Mulungu.”—Yakobo 4:4.
15. (a) Kodi kwenikweni matchalitchi amene mukuwadziwa “sali mbali ya dziko”? (b) Kodi mukudziwa chipembedzo chimene chikukwaniritsa chofunika chimenechi?
15 Kodi zenizeni zimasonyeza kuti matchalitchi m’chitaganya chanu amalabandira nkhani imeneyi? Kodi atsogoleri achipembedzo kuphatikizapo ziwalo za mipingo salidi “mbali ya dziko”? Kapena kodi iwo alowerera kwambiri mu utundu, ndale zadziko ndi nkhondo zamagulu za dziko? Mafunso amenewa siovuta kuyankha, popeza kuti zochita za machalitchi nzodziwika mofala. Ndiponso, kulinso kwapafupi kupenda zochita za Mboni za Yehova. Mwa kutero, mudzawona kuti izo zikutsatiradi chitsanzo cha Kristu ndi atsatiri ake oyambirira mwa kukhala olekana ndi dziko, zochita zake zandale zadziko ndi njira zake zadyera, zoipa ndi ziwawa.—2 Yohane 2:15-17.
CHIKONDI PAKATI PA IWO OKHA
16. Kodi njira yofunika imene ophunzira owona a Kristu angadziwidwire njotani?
16 Njira yaikulu koposa mu imene ophunzira enieni a Kristu angadziwidwire ndiyo mwa chikondi chimene iwo ali nacho pakati pa iwo okha. Yesu anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Kodi magulu achipembedzo amene mukuwadziwa ali ndi chikondi chimenechi? Kodi iwo amachitanji, mwa chitsanzo, pamene maiko mu amene akukhala akumenyana lina ndi linzake?
17. Kodi magulu achipembedzo ndi ziwalo zawo amachita motani m’kukwaniritsa chofunika cha kusonyeza chikondi pakati pa iwo okha?
17 Mukudziwa zimene kawirikawiri zimachitika. Molamulidwa ndi anthu adziko ziwalo za magulu achipembedzo osiyanasiyana zimapita kubwalo lankhondo ndi kupha akhulupiriri anzawo a dziko lina. Motero Mkatolika amapha Mkatolika, Mprotesitanti amapha Mprotesitanti ndipo Msilamu amapha Msilamu. Kodi mukuganiza kuti njira yoteroyo njogwirizana ndi Mawu a Mulungu ndipo imasonyezadi mzimu wa Mulungu?—1 Yohane 3:10-12.
18. Kodi Mboni za Yehova zikuchita motani m’nkhani imeneyi ya kusonyezana chikondi?
18 Kodi ndimotani mmene Mboni za Yehova zimakwaniritsira m’nkhani imeneyi ya kusonyezana chikondi? Izo sizimatsatira njira ya zipembedzo zadziko. Izo sizimapha akhulupiriri anzawo pamabwalo ankhondo. Izo sizinakhale ndi liwongo la kuchita bodza mwa kuti, “Ndikonda Mulungu,” pamene akuda mbale wawo wa dziko lina, fuko kapena mtundu. (1 Yohane 4:20, 21) Koma izo zimasonyezanso chikondi m’njira zina. Motani? Mwa njira imene izo zimachitira ndi anansi awo ndi mwa zoyesayesa zawo zachikondi za kuthandiza ena kudziwa Mulungu.—Agalatiya 6:10.
CHIPEMBEDZO CHIMODZI CHOWONA
19. Kodi nchifukwa ninji kuli ponse koyenera ndi Kwamalemba kunena kuti pali chipembedzo chowona chimodzi chokha?
19 Kuli kokha koyenera kuti payenera kukhala chipembedzo chimodzi chowona. Zimenezi nzogwirizana ndi chenicheni chakuti Mulungu wowona sali Mulungu “wa chisokonezo koma wa mtendere.” (1 Akorinto 14:33) Kwenikweni Baibulo limanena kuti kuli “chikhulupiriro chimodzi” chokha. (Aefeso 4:5) Pamenepa, kodi anthu amene akupanga gulu la alambiri owona lerolino ndani?
20. (a) Mothandizidwa ndi umboni, kodi bukhu lino likusonyeza yani kukhala alambiri owona lerolino? (b) Kodi zimenezo ndizo zimene inu mukukhulupirira? (c) Kodi njira yabwino koposa yodziwira bwino lomwe Mboni za Yehova njotani?
20 Sitikayikira kunena kuti iwo ndiwo Mboni za Yehova. Kuti inu mukhutiritsidwe maganizo za zimenezi tikukupemphani kuti muzolowerane nazo kwambiri. Njira yabwino koposa yochitira zimenezi ndiyo kufika pa misonkhano yawo pa Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova. Popeza kuti Baibulo limasonyeza kuti kutsatira chipembedzo chowona kumapereka chikhutiro chachikulu tsopano ndipo kumatsegula njira ya kulandira moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi, kudzakhaladi kokupindulitsani kupanga kufufuza koteroko. (Deuteronomo 30:19, 20) Mukupemphedwa mwachikondi ndi ife kuti mutero. Bwanji osafufuza tsopano?
[Chithunzi patsamba 185]
Ngati mukanati mulankhule ndi munthu wina ponena za Yehova ndi ufumu wake, kodi anthu akanakugwirizanitsani ndi chipembedzo chiti?
[Zithunzi patsamba 186]
Kodi munthu amalemekeza Mawu a Mulungu ngati iye alephera kuwatsatira?
[Chithunzi pamasamba 188, 189]
Yesu anakana kukhala wolamulira wandale zadziko
[Chithunzi patsamba 190]
Mukupemphedwa mwachikondi kufika pa misonkhano ya Mboni za Yehova