-
Kodi Yesu Ndi Ndani?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
6. Kuphunzira zokhudza Yesu kumatithandiza kwambiri
Baibulo limatilimbikitsa kuti tiyenera kuphunzira zokhudza Yesu komanso udindo umene Mulungu anamupatsa. Werengani Yohane 14:6 ndi 17:3, kenako mukambirane funso ili:
Kodi kuphunzira zokhudza Yesu n’kofunika chifukwa chiyani?
Yesu anatsegula njira yotithandiza kuti Mulungu akhale mnzathu. Iye anaphunzitsa choonadi chonena za Yehova komanso kudzera mwa Yesuyo tikhoza kudzapeza moyo wosatha
-