-
Kodi Satana Tizimuopa?Nsanja ya Olonda—2014 | November 1
-
-
Watipatsa zitsanzo. Lemba la Machitidwe 19:19 limanena zimene anthu a ku Efeso anachita atangokhala Akhristu. Limati: “Ambiri ndithu amene anali kuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku awo pamodzi ndi kuwatentha pamaso pa onse. Ndipo atawonkhetsa mitengo yake, anapeza ndalama zasiliva zokwana 50,000.”a Akhristu amenewa anawotcha chilichonse chogwirizana ndi zamizimu, ngakhale kuti zinthuzo zinali za ndalama zambiri. Chitsanzo chawochi chingatithandize kwambiri masiku ano. M’dzikoli anthu ambiri amakhulupirira zamizimu komanso nkhani zokhudza ufiti. Kukhala ndi chilichonse chokhudza zamizimu komanso kuchita zamizimu kungapangitse kuti munthu azivutitsidwa ndi ziwanda. Choncho ndi bwino kupewa chilichonse chokhudzana ndi mizimu.—Deuteronomo 18:10-12.
-
-
Kodi Satana Tizimuopa?Nsanja ya Olonda—2014 | November 1
-
-
a Ngati ndalama zasiliva zomwe zatchulidwa palembali zinali madinari achiroma, ndiye kuti zinali ndalama zochuluka kwambiri chifukwa zinali zofanana ndi ndalama zimene anthu 50,000 ankalandira akagwira ntchito tsiku lonse.
-