Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 9/15 tsamba 10-15
  • Akulu—Chinjirizani Choikiziridwa Chanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Akulu—Chinjirizani Choikiziridwa Chanu
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Chinaikizidwiranji kwa Inu?
  • Mmene Mungachinjirizire Choikiziridwa Chanu
  • Peŵani Mbuna
  • “Tadzichenjerani Nokha”
  • Chisangalalo Chimachokera m’Kuchinjiriza Choikiziridwa Chanu
  • Amuna Amene Angakuthandizeni Kuchita Bwino
    Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo
  • Abusa, Tsanzirani Abusa Aakulu
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Mverani Atsogoleri
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kodi Muli Woyeneretsedwa Kutumikira?
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 9/15 tsamba 10-15

Akulu​—Chinjirizani Choikiziridwa Chanu

“Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo mzimu woyera [u]nakuikani oyang’anira, kuti muŵete [mpingo, “NW”] wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa [Mwana wake, “NW”].”​—MACHITIDWE 20:28.

1. Kodi nchiyani chimene choikiziridwa Chachikristu chimaphatikizapo?

YEHOVA MULUNGU wapereka kwa awo okhala m’gulu lake la padziko lapansi choikiziridwa chabwino kwambiri. Koma kodi choikiziridwa nchiyani? Chiri chinachake cha mtengo chopatsidwa kwa munthu yemwe afunikira kuŵerengera. Choikiziridwa Chachikristu chimaphatikizapo “chitsanzo cha mawu a moyo,” chowonadi choperekedwa kupyolera mwa Malemba ndipo choperekedwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” monga “zakudya pa nthaŵi yake.” (2 Timoteo 1:13, 14; Mateyu 24:45-47) Choikiziridwa chimenechi chimaphatikizapo utumiki wogwirizanitsidwa ndi chowonadi, womwe uyenera kulalikidwa mkati ndi kunja kwa mpingo. (2 Timoteo 4:1-5) Alengezi a Ufumu, kuphatikizapo akulu oikidwa ndi mzimu, ayenera kuwona choikiziridwachi kukhala cha mtengo wapamwamba.

2. Kodi akulu ali ndi choikiziridwa chowonjezereka chotani, ndipo kodi nchiyani chimene Petro ananena ponena za icho?

2 Akulu Achikristu ali ndi choikiziridwa chowonjezereka​—thayo la kuŵeta gulu la Mulungu. Pa mfundoyi, mtumwi Petro analemba kuti: “Akulu tsono mwa inu ndiwadandaulira, ine mkulu mnzanu ndi mboni ya zowawa za Kristu, ndinenso wolawana nawo ulemerero udzavumbulutsikawo: Wetani gulu la Mulungu liri mwa inu, ndi kuliyang’anira, osati mokangamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu; osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo. Ndipo pakuwonekera Mbusa wamkulu, mudzalandira korona wa ulemerero, wosafota.”​—1 Petro 5:1-4.

3. Kodi akulu Achikristu ayenera kukhala magwero a chiyani?

3 Akulu Achikristu “[ayenera kutsimikizira kukhala, NW] pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m’malo owuma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.” (Yesaya 32:1, 2) Ichi chimatanthauza kuti akulu ayenera kukhala magwero a chisungiko, mtendere, ndi kukhazikika ku gulu la atumiki onga nkhosa la Mulungu. “Zowonjezereka” zimafunika kwa akulu, kapena abusa aang’ono, a gulu chifukwa chakuti iwo “[aikiziridwa] zambiri.” (Luka 12:48) Ndipo iwo alidi ndi choikiziridwa chamtengo wapatali chimene chiyenera kuchinjirizidwa.

Kodi Chinaikizidwiranji kwa Inu?

4. Kodi nchifukwa ninji akulu ochulukira akufunika?

4 Kukhalapo kwa mipingo yoposa 60,000 ya Mboni za Yehova padziko lonse lapansi kumafunikiritsa amuna oyeneretsedwa mwauzimu zikwi makumi ambiri kusamalira gulu la Mulungu. M’dziko lirilonse muli akulu ambiri, ndipo ichi chiri magwero a chisangalalo. Dziko lonse lapansi pali avereji ya chifupifupi alengezi a Ufumu 60 mu mpingo uliwonse. Chotero, pali ntchito yaikulu imene akulu afunikira kuichita.​—1 Akorinto 15:58.

5. Kodi ndi pamaziko otani pamene mwaŵi wa kutumikira monga mkulu umaperekedwera kwa mwamuna?

5 Ngati ndinu mkulu, nchifukwa ninji mwaŵi wadalitso umenewu unapatsidwa kwa inu? Chifukwa chakuti munachita zinthu zina, ndipo muli ndi ziyeneretso zauzimu. Mwachitsanzo, muyenera kukhala mutaphunzira Mawu a Mulungu mwakhama. (Yoswa 1:7, 8) Muyenera kukhala mutagaŵanamo mwachangu mu utumiki wa kumunda, ndiponso kuthandiza ena kukhala alengezi a Ufumu. Pokhala “[mutayesedwa] ponena za kuyenera choyamba,” inu munatumikira mokhulupirika monga mtumiki wotumikira. Inu ‘munakalamira,’ kapena kufunafuna kuyeneretsedwa, kukhala mkulu, mukumazindikira kuti kukhala mkulu ndiko “ntchito yabwino.” (1 Timoteo 3:1, 10, NW) Mofanana ndi Timoteo, munali ndi “umboni wabwino [wa] abale.” (Machitidwe 16:2) Mwachiwonekere pamene munavomerezedwa kukhala mkulu, inu munali chakumapeto kwa zaka zanu za ma 20 kapena kuposerapo ndipo munali ndi chidziŵitso m’moyo. Mpingo unafikira pakukulemekezani monga mbale wachikulire mwauzimu, wofikirika woyenerera kupereka uphungu wogwira mtima Wamalemba ndi kusunga chinsinsi.​—Miyambo 25:9, 10.

Mmene Mungachinjirizire Choikiziridwa Chanu

6, 7. Kodi Timoteo Woyamba 4:13-15 amapereka uphungu wotani kuthandiza mwamuna kuchinjiriza choikiziridwa chake monga mkulu?

6 Inde, ngati ndinu mkulu, panali chifukwa chabwino chimene uyang’aniro Wachikristu unaikiziridwa kwa inu. Ndipo mwadziwona kukhala wamwaŵi chotani nanga! Koma kodi ndimotani mmene mungachinjirizire choikiziridwa chanu?

7 Njira imodzi ya kuchinjirizira choikiziridwa chanu monga mkulu iri kukhala wotsimikiza ndi wakhama m’kusamalira mathayo anu. Tonsefe tagaŵiridwa mathayo osiyanasiyana m’gulu la Yehova. Chotero, sungani malo anu, ndipo khalani okhutira ‘kudzisamalira monga wam’ng’ono.’ (Luka 9:46-48; yerekezani ndi Oweruza 7:21.) Wonani mwaŵi wanu kukhala wamtengo wapatali, ndipo ‘musagwire ntchito konse ndi dzanja laulesi.’ (Miyambo 10:4) Musakhale malo amodzi, koma mwachithandizo cha Yehova, pangani kupita patsogolo m’mbali zonse za utumiki. Ndithudi, labadirani uphungu woperekedwa ndi Paulo kwa Timoteo uwu: “Usamalire kuŵerenga, kuchenjeza, kulangiza. Usanyalapsye mphatsoyo iri mwa iwe, yopatsidwa kwa iwe mwa chinenero, pamodzi ndi kuika kwa manja a akulu. Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako kuwonekere kwa onse.”​—1 Timoteo 4:13-15.

8. Kodi nchiyani chimene chidzathandiza mkulu kupereka uphungu wolama ndi kupereka chinachake cholemeretsa mwauzimu pa misonkhano?

8 Tsimikizirani kuti mukusunga programu yabwino, yopindulitsa ya phunziro laumwini. Monga mkulu, mukuyembekezeredwa moyenera kupereka uphungu wolama Wamalemba. Kuti mudzikonzekeretse kaamba ka thayo limeneli, kodi mwaŵerenga Baibulo lonse mosinkhasinkha, mwinamwake nthaŵi zambiri? (Miyambo 15:28) Bwanji ponena za magawo anu a pa pulatifomu? Akonzekereni bwino lomwe, mukumafunafuna thandizo la Yehova mwapemphero kotero kuti mupereke chinthu chopindulitsa mwauzimu kwa ofika pa misonkhano yathu. Makamaka akulu ayenera ‘kunena zinthu zabwino ndi zolimbikitsa kuti zipereke chisomo kwa iwo akumva.’​—Aefeso 4:29; Aroma 1:11.

9. Mogwirizana ndi 2 Timoteo 4:2, kodi mkulu ayenera kuchita chiyani?

9 Monga mkulu, labadirani uphungu wa Paulo wakuti: “Lalikira mawu; chita nawo pa nthaŵi yake, popanda nthaŵi yake; tsutsa, dzudzula, chenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso.” (2 Timoteo 4:2) Paulo anali wodera nkhaŵa za mpatuko chifukwa chakuti ena mu mpingo ‘anachita makani ndi mawu,’ naphatikizidwa mu ‘mafunso opusa,’ ndipo ‘anali kutsutsa chowonadi.’ (2 Timoteo 2:14-18, 23-25; 3:8-13; 4:3, 4) Komabe, kaya mpingo unali kukumana ndi nyengo yovuta kapena yachiyanjo, Timoteo anafunikira “kulalikira mawu.” Kutero kukalimbikitsa okhulupirira anzake kutsutsa mpatuko. Mofananamo lerolino, akulu ayenera kulalikira Mawu anzeru, kapena uthenga, wa Mulungu, umene umafikira mtima ndi kulimbikitsa kumamatira ku miyezo ya Yehova.​—Ahebri 4:12.

10. Kodi nchifukwa ninji mkulu ayenera kugwira ntchito mokhazikika mu utumiki wa kumunda ndi ziŵalo za banja lake ndi ena?

10 Kuti alankhule mwaukumu, mkulu ayenera kukhala ndi moyo mogwirizana ndi Mawu a Mulungu. Komatu iye sakuchinjiriza mokwanira choikiziridwa chake ngati iye ‘alalikira mawu’ kokha pa pulatifomu mkati mwa mpingo. M’mawu ozungulira lembali amodzimodziwo Paulo analimbikitsa Timoteo kuti: “Chita ntchito ya mlaliki wa Uthenga Wabwino.” ‘Kukwaniritsa uminisitala wanu mokwanira’ monga mkulu, muyenera kulalikira Mawu a Mulungu “poyera ndi kunyumba ndi nyumba.” (2 Timoteo 4:5; Machitidwe 20:20, 21, NW) Chotero, gwirani ntchito mu utumiki wa kumunda ndi ziŵalo za banja lanu. Zimenezi zingathandizire ku chomangira chauzimu pakati pa inu ndi mkazi wanu ndipo zidzapindulitsa ana anu kwambiri. Theraninso nthaŵi ina, kugawanamo m’ntchito yolalikira ndi ziŵalo zina za mpingo. Ichi chimalimbitsa zomangira zauzimu ndi kuwonjezera chikondi chaubale. (Yohane 13:34, 35) Ndithudi, mkulu ayenera kuyesayesa kukhala wokhazikika m’kugawa nthaŵi yofunikirayo pakati pa banja lake ndi mpingo. Kugwiritsira ntchito luntha kudzamthandiza kusapereka nthaŵi yochulukitsitsa ku chinthu chimodzi, pamene chinacho chinyalanyazidwa ndi kuwonongeka.

11. Kodi nchifukwa ninji mkulu ayenera kugwira ntchito zolimba kuwonjezera maluso ake monga mphunzitsi?

11 Kuti muchinjirize choikiziridwa chanu monga mkulu, gwiraninso ntchito zolimba kuwonjezera luso lanu monga mphunzitsi. “Iye wakuphunzitsa, akhale kukuphunzitsako,” anatero Paulo, “kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako.” (Aroma 12:7, 8) Popeza kuti mphunzitsi amaimirira pamaso pa ena monga mlangizi, iwo ali ndi kuyenera kwa kuyembekezera zochulukira kwa iye. Ngati mkulu angaphophonye kwambiri m’chiphunzitso chake ndipo ngati chipangitsa mavuto kwa okhulupirira anzake, iye amafunikira kuweruzidwa ndi Mulungu. Inde, aphunzitsi “[a]dzalangika koposa.” (Yakobo 3:1, 2; Mateyu 12:36, 37) Chotero akulu afunikira kukhala ophunzira osamalitsa a Mawu a Mulungu ndipo ayenera kuwagwiritsira ntchito m’moyo. Ndiyeno chiphunzitso chawo Chamalemba, chochirikizidwa ndi kuwagwiritsira ntchito kwawo, chidzayamikiridwa kwambiri ndi okhulupirira anzawo. Chidzachinjirizanso mpingo ku zisonkhezero zoipitsitsa, kuphatikizapo mpatuko.

Peŵani Mbuna

12. Kodi ndi uphungu wotani umene nthaŵi zina unafalitsidwa m’magazini ano womwe udzathandiza mkulu kupeŵa kugwiritsira ntchito lirime molakwa?

12 Ndiponso, chinjirizani choikiziridwa chanu monga mkulu, mwa kupeŵa mbuna. Imodzi ya zimenezi ndiyo kugwiritsidwa ntchito kwa lilime molakwa monga mphunzitsi. Kufunika kwa kusamala pa mfundoyi kwagogomezeredwa kale ndi gulu la Yehova. Mwachitsanzo, m’kope lake la May 15, 1897, magazini ino inalongosola Yakobo 3:1-13 ndipo inati makamaka ponena za akulu: “Ngati iwo ali ndi lilime labwino iro lingakhale ngalande ya madalitso okulira, kukopera ziŵerengero zokulira kwa Ambuye, ku chowonadi ndi ku njira ya chilungamo; kapena, kumbali ina, ngati liri loipitsidwa ndi mphulupulu, lilime lingachite chifupifupi chivulazo chosaneneka​—chivulazo ku chikhulupiriro, ku makhalidwe, ku ntchito zabwino. Ziridi zowona, kuti aliyense wogwiritsira ntchito mphatso ya kuphunzitsa amadzinyamulira thayo lowonjezereka pamaso pa Mulungu ndi anthu. . . . Aliyense amene angakhale kasupe woyendamo Mawu a Mulungu, wonyamula dalitso ndi chitsitsimulo ndi nyonga, ayenera kutsimikizira kuti madzi oŵaŵa, ziphunzitso zonama zimene zingapangitse temberero, kuvulala​—kuchitira Mulungu mwano ndi kuipitsa Mawu ake​—sizipezanso mwa iwo ngalande yolankhulira. Posankha atsogoleri amisonkhano chiyeneretso cha ‘lilime,’ monga momwe chalembedwera panopa sichiyenera kunyalanyazidwa. A lilime lopyoza sayenera kusankhidwa, koma ofatsa, odekha amene, ‘amalamulira’ malilime awo ndi kuyesayesa kwambiri ‘kulankhula monga oimira Mulungu’ okha.” Nkofunika chotani nanga kuti mkulu agwiritsire ntchito lilime lake molondola!

13. Kodi akulu afunikira kusonyeza kusamala kotani m’nkhani ya zosangulutsa?

13 Zosangulutsa zopambanitsa zirinso mbuna yofunikira kupeŵa. Zosangulutsa ziyenera kutsitsimula ndi kulimbikitsa, osati kutopetsa ndi kuchenjeneketsa Mkristu. Ndiponso, oyang’anira ayenera kukhala “osapambanitsa m’zizoloŵezi.” (1 Timoteo 3:2, NW) Ngati kusapambanitsa kumalamulira zimene muchita m’nkhani za zosangulutsa, zimenezi zidzakuchinjirizani ndi banja lanu ndipo zidzapereka chitsanzo chabwino ku mpingo. Simudzakhala mukupereka chitsanzo chabwino konse ngati, munapita mobwerezabwereza, ku zosangulutsa kumapeto a mlungu pamene okhulupirira anzanu anali kukhala ndi phande mokangalika mu utumiki wa kumunda. Mbiri yabwino iyenera kulalikidwa, ndipo akulu ayenera kutsogoza m’ntchito imeneyi monga alengezi okangalika a Ufumu.​—Marko 13:10; Tito 2:14.

14. (a) Kodi ndi zitsanzo zotani Zamalemba zimene zimagogomezera kufunika kwa akulu kupeŵa chisembwere cha kugonana? (b) Kodi akulu sayenera kunyalanyaza uphungu wobwerezedwabwerezedwa uti pakuthandiza alongo auzimu?

14 Chisembwere cha kugonana chiri mbuna ina yofunikira kupeŵedwa. Kuwola kwa makhalidwe a dziko kungayambukire ngakhale mkulu ngati iye sakaniza mayeso ogwiritsidwa ntchito ndi Satana m’kuyesayesa kwake kwa kuswa umphumphu wa anthu a Mulungu. (Yerekezani ndi Mateyu 4:1-11; 6:9, 13.) Kumbukirani kuti mneneri Balamu, atalephera m’zoyesayesa zake zakutemberera Aisrayeli, analingalira kuti Yehova iyemwini akawatemberera ngati iwo akanyengedwa kuphatikizidwa m’kulambira mpheto. Chotero Balamu anaphunzitsa mfumu ya Moabu Balaki “kuika chokhumudwitsa pamaso pa ana a Israyeli, kuti adye zinthu zoperekedwa nsembe ku mafano ndi kuchita chigololo.” Kodi iwo anapeŵa mbuna imeneyo? Ayi, popeza kuti Aisrayeli 24,000 anafa mu mliri wochokera kwa Yehova chifukwa chakuti anachita chisembwere ndi akazi a ku Moabu ndipo anagwadira milungu yawo. (Chibvumbulutso 2:14; Numeri 25:1-9) Kumbukiraninso, kuti ngakhale Davide, ‘wapamtima pa Mulungu,’ anagwera m’mbuna ya chisembwere cha kugonana. (1 Samueli 13:14; 2 Samueli 11:2-4) Pamenepo, monga mkulu, labadirani uphungu wobwerezedwabwerezedwa wa “mdindo wokhulupirika” kusathandiza konse mlongo wauzimu mulinokha koma kukhala ndi mkulu wina posamalira thayo limeneli.​—Luka 12:42.

15. Kodi ndimotani mmene banja la mkulu lingamthandizire kupeŵa mbuna za kukondetsa zinthu zakuthupi?

15 Kukonda zinthu zakuthupi ndiko mbuna ina imene mkulu afunikira kupeŵa. Khalani wokhutira ndi zimene muli nazo, mukumadziŵa kuti Yehova adzagaŵira zofunika zokwanira. (Mateyu 6:25-33; Ahebri 13:5) Phunzitsani banja lanu kuchita unkhwima, popeza kuti kuwawanya kumaba nthaŵi ndi chuma zimene zingagwiritsiridwe ntchito kuthandiza banja, limodzi ndi kugaŵanamo mu utumiki wa kumunda, kulimbitsa mpingo, ndi kupititsa patsogolo zabwino za Ufumu. Mkulu amapindula ndi kugwirizanika kwa banja lake pa nkhaniyi ndipo amakhala wosangalala kuti samamkakamiza kufuna zinthu zimene kwenikweni siziri zofunika. M’chenicheni, “zapang’ono, uli kuwopa Yehova, zipambana ndi katundu wambiri pokhala phokoso.”​—Miyambo 15:16.

“Tadzichenjerani Nokha”

16. Kodi ndiuphungu wotani umene Paulo anapereka kwa oyang’anira a ku Efeso?

16 Ngati akulu ati achinjirize choikiziridwa chawo, iwo ayenera kugwiritsira ntchito uphungu wa Paulo kwa oyang’anira a ku Efeso. Iye anawauza kuti: “Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera [u]nakuikani oyang’anira, kuti muŵete [mpingo, NW] wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa [Mwana wake, NW]. Ndidziŵa ine kuti, nditachoka ine, idzaloŵa mimbulu yosautsa, yosalekerera gululo; ndipo mwa inu nokha adzauka anthu, olankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate, Chifukwa chake dikirani, nimukumbukire kuti zaka zitatu sindinaleka usiku ndi usana kuchenjeza yense wa inu ndi misozi.”​—Machitidwe 20:28-31.

17, 18. Kodi ndiuphungu uti wofalitsidwa m’magazini ano zaka 80 zapitazo umene udakagwirabe ntchito kwa akulu Achikristu?

17 Zoposa zaka 80 zapitazo, The Watchtower (March 1, 1909) inagwira mawu uphungu wapamwambapawo wa Paulo kwa akulu anzake ndi kuchitira ndemanga kuti: “Akulu kulikonse afunikira kulabadira mwapadera; chifukwa chakuti m’chiyeso chirichonse munthu woyanjidwa koposa ndi wotchuka koposa amakanthidwa ndi nkhonya ndi ziyeso zazikulu koposa. Chifukwa chake [Yakobo] akuchenjeza kuti, ‘Musakhale aphunzitsi ambiri a inu, abale, podziŵa kuti munthu akalandira kuyesedwa koipitsitsa.’ Ife, mofananamo, tikuchenjeza Akulu onse amene mu mtima ali oyera, opanda dyera, kuti asakhale ndi chinthu china chirichonse koma kokha chikondi ndi mafuno abwino kaamba ka anthu onse, ndi kuti adzazidwe mowonjezerekawonjezereka ndi zipatso ndi zisomo za Mzimu woyera, akumasamaliranso gulu. Kumbukirani, kuti gulu liri la Ambuye ndi kuti muli ndi thayo kwa Ambuye, ndi kwa ilo. Kumbukirani, kuti mufunikira kuyang’anira miyoyo yawo (ubwino wawo) monga awo ayenera kuŵerengera kwa Mbusa Wamkulu. Kumbukirani, kuti chinthu chachikulu koposa zonse ndicho Chikondi; ndipo pamene kuli kwakuti simukunyalanyaza ziphunzitso, labadirani mwapadera kugwira ntchito kwapadera kwa Mzimu wa Ambuye pakati pa ziŵalo zosiyanasiyana za Thupi lake, kuti mwakutero zikakhale ‘zokwanira kaamba ka choloŵa cha oyera m’kuwunika,’ ndipo, mogwirizana ndi chifuno cha Mulungu, musavutike ndi kukhumudwa m’tsiku iri loipa, koma, pokhala mutachita zonse, kuima okwanira mwa Kristu, Thupi lake, Ziŵalo zake, Ansembe Anzake, Oloŵa Nyumba Anzake.”

18 Mawu amenewo analunjikitsidwa kwa akulu odzozedwa ndi mzimu ndi okhulupirira anzawo m’chigwirizano ndi kumvetsetsa ndi mikhalidwe ya gulu la Yehova m’masiku oyambirira amenewo. Komabe, uphunguwo umagwira ntchito bwino chotani nanga lerolino! Kaya ziyembekezo zawo ziri zakumwamba kapena zapadziko lapansi, akulu Achikristu ayenera kupereka chisamaliro kwa iwo eni, kuchinjiriza choikiziridwa chawo, ndi kusamalira mwachikondi zabwino za gulu la Mulungu.

Chisangalalo Chimachokera m’Kuchinjiriza Choikiziridwa Chanu

19, 20. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti pamakhala chotulukapo chachisangalalo pamene akulu achinjiriza choikiziridwa chawo?

19 Chimwemwe​—m’chenicheni, chisangalalo chochokera mu mtima​—chimadza kuchokera ku kuchinjiriza choikiziridwa chanu monga mkulu Wachikristu. Pali chisangalalo m’kusenza bwino lomwe thayo lokulirako. Chotero khalani ochenjera, mwa pemphero, mwachangu. Chinjirizani choikiziridwa chanu monga mkulu ndipo yang’anirani m’tsogolo ku nthaŵi pamene mungakhoze kunena, monga momwe anachitira mwamuna wokhala ndi cholembera cha mlembi kuti: “Ndachita monga munandilamulira ine.”​—Ezekieli 9:3, 4, 11.

20 Inde, gwirani ntchito mokhulupirika monga mkulu kotero kuti kunganenedwe za inu monga momwe zinaliri kwa Nowa: “Momwemonso anachita.” (Genesis 6:22) Kuchokera ku utumiki wachangu wotero, mpingo umapindula m’njira zambiri. Koposa zonse, Yehova amalemekezedwa ndi mipingo yamphamvu, yokangalika yotumikiridwa ndi akulu okhulupirika amene amachinjiriza choikiziridwa chawo. Koma kwenikweni zambiri zimafunika ngati mudzati muwuzidwe kuti: “Chabwino, kapolo wabwino iwe.” (Luka 19:17) Monga mkulu, inu muyeneranso kusamalira gulu la Mulungu ndi kukoma mtima.

Kodi Nchiyani Chimene Munganene?

◻ Kodi ndi choikiziridwa chowonjezerka chotani chimene akulu Achikristu ali nacho?

◻ Kodi mkulu angatenge masitepi otsimikizirika otani kuchinjiriza choikiziridwa chake?

◻ Kuti achinjirize choikiziridwa chake, kodi ndi mbuna zotani zimene mkulu ayenera kupeŵa?

◻ Kodi nchifukwa ninji chisangalalo chimatulukapo pamene akulu achinjiriza choikiziridwa chawo?

[Chithunzi patsamba 10]

Akulu Achikristu ayenera kukhala ngati “pousira chimphepo”

[Chithunzi patsamba 12]

Monga mkulu, gawananimo mokhazikika mu utumiki wa kumunda ndi ziŵalo za banja lanu ndi ena

[Chithunzi patsamba 13]

Ngati muchinjiriza choikiziridwa chanu monga mkulu, mpingo udzapindula m’njira zambiri

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena