-
Kodi Yesu Ali Ndi Makhalidwe Otani?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
6. Yesu ndi wopatsa
Ngakhale kuti Yesu analibe zinthu zambiri zakuthupi, ankakonda kugawira ena zomwe anali nazo. Iye amafuna kuti nafenso tizikhala opatsa. Werengani Machitidwe 20:35, kenako mukambirane funso ili:
Malinga ndi zimene Yesu ananena, tizichita chiyani kuti tizikhala osangalala?
Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:
Kodi tingasonyeze bwanji mtima wopatsa ngakhale titakhala kuti tilibe zinthu zambiri?
-
-
Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani ya Ntchito Komanso NdalamaMungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
3. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife owolowa manja pogwiritsa ntchito ndalama zathu?
Yehova ndi Mulungu wowolowa manja ndipo tingasonyeze kuti tikumutsanzira pokhala “owolowa manja, okonzeka kugawira ena.” (1 Timoteyo 6:18) Tingachite zimenezi popereka ndalama zathu kuti zithandize pampingo ndiponso pothandiza amene akuvutika makamaka abale ndi alongo athu. Yehova amasangalala kwambiri akamaona cholinga chimene timaperekera ndalama zathu, osati kuchuluka kwa ndalamazo. Tikamapereka ndalama zathu mowolowa manja, timakhala osangalala komanso timasangalatsa Yehova.—Werengani Machitidwe 20:35.
-