Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Nthaŵi Yonse Palibe Munthu Analankhula Chotero”
    Nsanja ya Olonda—2002 | September 1
    • 6. Perekani chitsanzo cha mmene Yesu anafotokozera zinthu zosavuta kumva koma za tanthauzo lalikulu.

      6 Nthaŵi zambiri Yesu anali kufotokoza zinthu zosavuta kumva koma za tanthauzo lalikulu pogwiritsa ntchito mawu afupiafupi, omveka bwino. Nthaŵi imeneyo mabuku anali asanayambe kusindikizidwa, koma mwa kugwiritsa ntchito mawu osavuta, iye anasindikiza uthenga wake m’maganizo ndi m’mitima ya omvera ake moti sakanaiwala. Taonani zitsanzo izi: “Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye aŵiri: . . . simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.” “Musaweruze, kuti mungaweruzidwe.” “Pa zipatso zawo mudzawazindikira iwo.” “Olimba safuna sing’anga ayi, koma odwala.” “Onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.” “Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu.” “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”c (Mateyu 6:24; 7:1, 20; 9:12; 26:52; Marko 12:17; Machitidwe 20:35) Mpaka pano, mawu amphamvu amenewo savuta kuwakumbukira ngakhale kuti papita zaka pafupifupi 2,000 kuchokera pamene Yesu anawalankhula.

  • “Nthaŵi Yonse Palibe Munthu Analankhula Chotero”
    Nsanja ya Olonda—2002 | September 1
    • c Mawu omalizaŵa amene ali pa Machitidwe 20:35, anawagwira mawu ndi mtumwi Paulo yekha, ngakhale kuti mfundo ya mawuwo imapezeka m’Mauthenga Abwino. Mwina Paulo anamva mawu ameneŵa kwa munthu wina (mwina wophunzira amene anamva Yesu akunena zimenezi kapena anamva kwa Yesu woukitsidwa) kapena Mulungu anam’vumbulutsira.​—Machitidwe 22:6-15; 1 Akorinto 15:6, 8.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena