Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Kodi Akristu a zaka za zana loyamba anakhulupirira kuti mapeto a dongosolo loipa lino akabwera m’nthaŵi ya moyo wawo?
Otsatira a Yesu m’zaka za zana loyamba anali olakalaka kwambiri kuti mapeto afike. Monga momwe tidzawonera, ena a iwo anatsimikizira kuti mapeto anayandikira, kufika nthaŵi yomweyo. Lingaliro lawo linafunikira kuwongoleredwa. Koma sikulidi koipa kwa Akristu, panthaŵiyo kapena tsopano, kukhulupirira mowona mtima kuti mapeto onenedweratuwo ayenera kuwonedwa kukhala pafupi ndi kukhala ndi moyo wa tsiku ndi tsiku mogwirizana ndi chidziŵitso chimenecho.
Poyankha funso la ophunzira ake lonena za “chizindikiro” cha kukhalapo kwake, Yesu anawachenjeza kuti: “Dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake lakufika Ambuye wanu.” (Mateyu 24:3, 42) Kudikira koteroko kuyenera kuyambukira machitidwe awo, popeza Kristu anawonjezera kuti: “Koma mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa . . . Koma inu dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso Mwana wa munthu.”—Luka 21:34-36.
Wonani kuti Yesu anapereka uphungu uwu mwamsanga atamaliza kusanja zochitika zimene zikapanga “chizindikiro.” Chotero atumwiwo anachenjezedwa pa chenicheni chakuti zinthu zina zikachitika mogwirizana ndi mbiri mapeto asanadze. Komabe, milungu yochepera pambuyo pake, iwo anafunsa Yesu wowukitsidwayo kuti: “Ambuye, kodi nthaŵi ino mubwezera ufumu kwa Israyeli?” Iye anayankha: “Sikuli kwa inu kudziŵa nthaŵi kapena nyengo, zimene Atate anaziika m’ulamuliro wake wa iye yekha.”—Machitidwe 1:6, 7.
Tingawone kuchokera ku mawuwa kuti atsatiri a Yesu oyandikana naye koposa anali ofunitsitsa kwambiri kuti mapeto afike mofulumira kotero kuti iwo ananyalanyaza zimene anali atawawuza osati kale kwambiri zonena za maumboni owoneka okachitika m’nthaŵi ya kukhalapo kwake mapeto asanafike.
Tikupeza chisonyezero china cha kulakalaka kwawo m’kalata ya mtumwi Paulo kwa Akristu a ku Tesalonika. Chifupifupi 50 C.E. iye analemba kuti: “Koma za nthaŵiyo ndi nyengozo, abale, sikufunika kuti tidzakulembereni. Pakuti inu nokha mudziŵa bwino kuti tsiku la [Yehova] lidzadza monga mbala usiku. Chifukwa chake tsono tisagone monga otsalawo, komatu tidikire, ndipo tisaledzere.” (1 Atesalonika 5:1, 2, 6) Ena a Akristu odzozedwa ndi mzimu amenewo anatenga chimenecho kutanthauza kuti kukhalapo kwa Yesu (ndi tsiku la Yehova la kuwononga oipa) linali kudza nthaŵi yomweyo, ndipo mwamsangadi.
Komatu sichoncho. Ndiiko komwe, Paulo anawalembera m’kalata yachiŵiri kuti: “Ndipo tikupemphani, abale, chifukwa cha kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi kusonkhana pamodzi kwathu kwa iye; kuti musamagwedezeka mtima msanga ndi kutaya maganizo anu, kapena kuwopsyedwa, mwa mzimu kapena mwa mawu; kapena mwa kalata, monga wolembedwa ndi ife, monga ngati tsiku la [Yehova] lafika; munthu asakunyengeni konseko; kuti silifika, koma chiyambe chifike chipatukocho, navumbulutsike munthu wosayeruzika, mwana wa chiwonongeko.”—2 Atesalonika 2:1-3.
Zimenezi sizinatanthauze kuti iwo akakhala osadikira ponena za kukhalapo kwa Yesu ndi mapeto a dongosolo la zinthu. Ndi kupita kwa chaka chirichonse, chenjezo la Yesu linakhala lofulumirirapo mowonjezerekawonjezereka: “Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake lakufika kwa Ambuye wanu.”
Motero, chifupifupi zaka zisanu pambuyo pa kulemba Atesalonika Wachiŵiri, Paulo analemba kuti: “Tsopano ndiyo nthaŵi yabwino yakuuka kutulo; pakuti tsopano chipulumutso chanu chiri pafupi koposa pamene tinayamba kukhulupirira. Usiku wapita, ndi dzuŵa layandikira; chifukwa chake ntivule ntchito za mdima, ntivale chamuna cha kuunika.” (Aroma 13:11, 12) Pambuyo pa zaka zina zisanu, Paulo analangiza Akristu a ku Ahebri kuti: “Pakuti chikusoŵani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano. Pakuti katsala kanthaŵi kakang’onong’ono, ndipo wakudzayo adzafika, wosachedwa.” (Ahebri 10:36, 37) Kenaka, m’vesi lotsatiridwa ndi lomalizira la Chibvumbulutso, mtumwi Yohane analemba kuti: “Iye wakuchitira umboni izi, anena, indetu; ndiza msanga. Ameni; idzani, Ambuye Yesu.”—Chibvumbulutso 22:20.
Mosakaikira, Mkristu kalelo sanali wopanda nzeru kuti ankalingalira kuti mapeto akafika m’nthaŵi ya moyo wake. Ndipo ngati kupyolera m’zochitika za ngozi kapena zachibadwa, iye akanayenera kufa mapeto asanafike, akamwalira atakhala ndi moyo ndi lingaliro labwino la kufulumira limene Yesu ndi Malemba owuziridwa anapereka.
Zonsezi ziridi zogwira ntchito koposerapo kwa ife, pa nthaŵi yomalizira imene tikukhalamo. Kutanthauzira mawu a Paulo, sitingakane kuti ‘tsopano chipulumutso chathu chayandikira koposa nthaŵi iriyonse pamene Akristu oyambirira anakhulupirira ndiponso kuposadi pamene ife enife tinayamba kukhulupirira. Usiku wapita; usana wayandikiradi.’
Takhala okhoza kuwona m’mbiri kuyamba ndi Nkhondo ya Dziko ya I umboni wowoneka ndimaso ukuunjikana kwambiri, umboni umene umatsimikizira kuti tiri kumapeto kwa dongosolo la zinthu. M’malo mwa kutanganitsidwa ndi kuyerekezera pamene mapeto adzafika, tiyenera kutanganitsidwa ndi kulalikira mbiri yabwino, imene ingapulumutse miyoyo yathu ndi miyoyo ya ena ambiri.—1 Timoteo 4:16.
Tiri ndi zifukwa zokwanira kuyembekezera kuti kulalikira kumeneku kudzamalizidwa m’nthaŵi yathu. Kodi zimenezo zitanthauza usanathe mwezi uno, chisanathe chaka, zisanathe zaka khumi, zisanathe zaka zana limodzi? Palibe amene adziŵa, popeza Yesu ananena kuti ‘chinkana angelo akumwamba’ sanadziŵe zimenezo. (Mateyu 24:36) Ndiponso, ife sitifunikira kudziŵa pokhala tikumapitirizabe kuchita zimene Ambuye akutilamula kusumikapo maganizo. Chofunika koposa ndicho kuchitidwa kwa chifuniro ndi ntchito ya Mulungu ndi kuti tigawanemo mokwanira. Mwakutero tingakhoze “kupulumuka zonse zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wamunthu.”—Luka 21:36.