Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bt mutu 4 tsamba 28-35
  • “Osaphunzira Ndiponso Anthu Wamba”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Osaphunzira Ndiponso Anthu Wamba”
  • ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Sitinamuchiritse “ndi Mphamvu Zathu” (Machitidwe 3:11-26)
  • “Ife Sitingasiye Kulankhula” (Machitidwe 4:1-22)
  • “Anafuula kwa Mulungu” (Machitidwe 4:23-31)
  • Tisamangochita Zinthu Kuti Tisangalatse “Anthu, Koma Mulungu” (Machitidwe 4:32–5:11)
  • Mbuye Wake Anam’phunzitsa Kufunika Kokhala Wokhululuka
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Mbuye Wake Anam’phunzitsa Kukhululukira Ena
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Anathetsa Mantha Ndiponso Mtima Wokayikira
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Anakhalabe Wokhulupirika pa Nthawi Yovuta
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
Onani Zambiri
‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
bt mutu 4 tsamba 28-35

MUTU 4

“Osaphunzira Ndiponso Anthu Wamba”

Atumwi anachita zinthu molimba mtima ndipo Yehova anawadalitsa

Nkhaniyi yachokera pa Machitidwe 3:1–5:11

1, 2. Kodi Petulo ndi Yohane anachita chozizwitsa chiti pafupi ndi khomo la kachisi?

MASANA dzuwa litachepa mphamvu, Ayuda ambiri okhulupirika komanso ophunzira a Khristu, ankapita kukachisi chifukwa “nthawi yokapemphera” inali itatsala pang’ono kukwana.a (Mac. 2:46; 3:1) Pagululo panalinso Petulo ndi Yohane ndipo ankalowera cha kukhomo lotchedwa Geti Lokongola. Ngakhale kuti anthu ankachita phokoso, panamvekanso mawu a munthu wina wa zaka za m’ma 40 wopemphetsa, amene anabadwa wolumala.​—Mac. 3:2; 4:22.

2 Pamene Petulo ndi Yohane anayandikira, munthu wopemphetsayo anafuula monga mwa masiku onse kuti amupatse ndalama. Pamenepo atumwiwo anaima ndipo munthuyo ananyadira chifukwa ankayembekezera kuti alandira ndalama. Ndiyeno Petulo ananena kuti: “Siliva ndi golide ndilibe, koma ndikupatsa chimene ndili nacho: M’dzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti, yenda!” Tangoganizirani mmene gulu la anthuwo linadabwira pamene Petulo anamugwira dzanja, ndipo kwa nthawi yoyamba m’moyo wake, munthuyo anaimirira. (Mac. 3:6, 7) Ganiziraninso mmene zinthu zinalili pamene munthuyo anaimirira n’kumayang’anitsitsa miyendo yake yochiritsidwayo kenako n’kuyamba kuyeserera kuyenda kwa nthawi yoyamba. M’pake kuti anayamba kudumphadumpha ndi kutamanda Mulungu mofuula.

3. Kodi Petulo anapereka mphatso yofunika kwambiri iti kwa munthu yemwe anali wolumala uja ndiponso kwa anthu ena onse?

3 Gulu la anthuwo, lomwe linasangalala kwambiri, linathamangira pakhonde la zipilala la Solomo kumene kunali Petulo ndi Yohane. Petulo anauza anthuwo tanthauzo lenileni la zimene zinachitikazo ali pakhondeli, ndipo m’pamenenso nthawi ina Yesu anaimapo n’kumaphunzitsa anthu. (Yoh. 10:23) Iye anapereka mphatso yoposa siliva kapena golide kwa gululo komanso munthu amene anali wolumala uja. Mphatsoyo inali yofunika kwambiri kuposa kuchiritsidwa. Petulo anapatsa anthuwo mwayi woti alape ndi kukhululukidwa machimo awo, ndiponso kuti akhale otsatira a Yesu Khristu, amene Yehova anamusankha kukhala “Mtumiki Wamkulu wa moyo.”​—Mac. 3:15.

4. (a) Kodi anthu audindo anayamba kuchita chiyani Petulo ndi Yohane atachiritsa munthu mozizwitsa? (b) Kodi tikambirana mafunso awiri ati?

4 Zimene zinachitika pa tsikuli zinali zosaiwalika. Munthu wolumala anachiritsidwa ndipo anayamba kuyenda bwinobwino. Anthu enanso ambirimbiri anapatsidwa mwayi woti achiritsidwe mwauzimu kuti aziyenda mogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna. (Akol. 1:9, 10) Komanso, zimene zinachitika pa tsiku limeneli zinachititsa kuti anthu audindo azilimbana ndi anthu okhulupirika otsatira Khristu poyesa kuwaletsa kumvera lamulo la Yesu lakuti azilalikira uthenga wa Ufumu. (Mac. 1:8) Ngakhale kuti Petulo ndi Yohane anali “osaphunzira ndiponso anthu wamba,” kodi tingaphunzire chiyani kuchokera pa zimene anachita polalikira gulu la anthulo?b (Mac. 4:13) Ndipo kodi tingatani kuti titsanzire njira imene iwowo komanso ophunzira ena anatsatira pamene ankatsutsidwa?

Sitinamuchiritse “ndi Mphamvu Zathu” (Machitidwe 3:11-26)

5. Kodi tikuphunzira chiyani tikaona mmene Petulo analankhulira ndi gulu la anthu?

5 Petulo ndi Yohane anaimirira n’kulankhula ndi gululo ngakhale kuti ankadziwa kuti masiku angapo m’mbuyomo, ena mwa anthuwo ankafuula kuti Yesu apachikidwe. (Maliko 15:8-15; Mac. 3:13-15) Tangoganizani kulimba mtima kumene Petulo anasonyeza pamene analankhula mopanda mantha kuti munthu wolumalayo wachiritsidwa m’dzina la Yesu. Iye sanalankhule mozungulira poopa kukhumudwitsa anthuwo. Iye anadzudzula anthuwo mosapita m’mbali kuti anali ndi mlandu wopha nawo Khristu. Komabe Petulo sanawasungire chakukhosi chifukwa anthuwo ‘anachita zinthu mosazindikira.’ (Mac. 3:17) M’malomwake, iye analankhula nawo monga abale ake ndipo anawalimbikitsa ndi mfundo zabwino za uthenga wa Ufumu. Ngati anthuwo akanalapa ndi kukhulupirira Khristu, “nyengo zotsitsimutsa” zochokera kwa Yehova zikanafika kwa iwo. (Mac. 3:19) Ifenso tiyenera kukhala olimba mtima ndipo tizilankhula mosapita m’mbali tikamalengeza uthenga wokhudza chiweruzo cha Mulungu chimene chikubwerachi. Koma tiyenera kupewa kulankhula mwachipongwe kapena kuweruziratu anthu amene tikuwalalikirawo ndipo tiziwaona kuti akhoza kukhala abale athu auzimu. Mofanana ndi Petulo, tizikambirana nawo kwambiri mfundo zolimbikitsa za uthenga wa Ufumu.

6. Kodi Petulo ndi Yohane anasonyeza bwanji kuti anali odzichepetsa?

6 Atumwiwo anali anthu odzichepetsa kwambiri. Iwo sanadzitamande n’kumati anachiritsa munthu uja chifukwa cha mphamvu zawo. Petulo anafunsa anthuwo kuti: “N’chifukwa chiyani mukutiyang’anitsitsa ngati kuti tamuyendetsa ndi mphamvu zathu, kapena chifukwa cha kudzipereka kwathu kwa Mulungu?” (Mac. 3:12) Petulo komanso atumwi enawo ankadziwa kuti chinthu chilichonse chabwino chimene anachita mu utumiki wawo, chinatheka ndi mphamvu za Mulungu osati zawo. Choncho iwo ankadzichepetsa n’kumauza anthu kuti asamawatamande chifukwa cha zimene achita, koma azitamanda Yehova ndi Yesu.

7, 8. (a) Kodi ndi mphatso iti imene tingapatse anthu? (b) Kodi lonjezo la “kubwezeretsa zinthu zonse” likukwaniritsidwa bwanji masiku ano?

7 Ifenso tiyenera kukhala odzichepetsa tikamagwira ntchito yolalikira za Ufumu. N’zoona kuti masiku ano mzimu wa Mulungu supereka mphamvu kwa Akhristu zochiritsira anthu mozizwitsa. Ngakhale zili choncho, tingathandize anthu kuti azikhulupirira Mulungu ndi Khristu ndiponso kuti alandire mphatso imene Petulo anapereka kwa gulu la anthu aja, yomwe ndi mwayi woti alape n’cholinga choti machimo awo akhululukidwe ndiponso kuti atsitsimulidwe ndi Yehova. Chaka chilichonse, anthu masauzande ambiri amalandira mwayi umenewu ndipo amabatizidwa n’kukhala ophunzira a Khristu.

8 N’zoonadi, tikukhala m’masiku amene Petulo anawatchula kuti “nthawi yobwezeretsa zinthu zonse.” Ndipo pokwaniritsa mawu amene “Mulungu ananena kudzera mwa aneneri ake oyera akale,” Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba m’chaka cha 1914. (Mac. 3:21; Sal. 110:1-3; Dan. 4:16, 17) Zimenezi zitangochitika, Khristu anayamba kuyang’anira ntchito yobwezeretsa kulambira koona padziko lapansi. Chifukwa cha zimenezi, anthu mamiliyoni ambiri abwera m’paradaiso wauzimu ndipo akugonjera Ufumu wa Mulungu. Iwo anavula umunthu wawo wakale umene unali woipa ndi kuvala “umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.” (Aef. 4:22-24) Mofanana ndi kuchiritsidwa kwa munthu wolumala amene anali wopemphetsa uja, ntchito yaikuluyi ikuchitika osati ndi mphamvu za anthu, koma ndi mzimu wa Mulungu. Mofanana ndi Petulo, tizigwiritsa ntchito Mawu a Mulungu molimba mtima ndiponso mwaluso pophunzitsa ena. Zilizonse zimene tingakwanitse kuchita pothandiza anthu kuti akhale ophunzira a Khristu, zimatheka ndi mphamvu ya Mulungu, osati ndi mphamvu zathu.

“Ife Sitingasiye Kulankhula” (Machitidwe 4:1-22)

9-11. (a) Kodi atsogoleri a Chiyuda anatani atamva zimene Petulo ndi Yohane ankaphunzitsa? (b) Kodi atumwiwo anatsimikiza mtima kuchita chiyani?

9 Zimene Petulo analankhula komanso zimene munthu yemwe anali wolumala uja anachita, monga kukuwa ndi kudumphadumpha, zinayambitsa chipwirikiti. Ataona zimenezi, woyang’anira kachisi, amene ntchito yake inali yoonetsetsa kuti pakachisi pali mtendere, ndiponso ansembe aakulu anathamangira komweko kuti akafufuze chimene chinachitika. Zikuoneka kuti anthu amenewa anali Asaduki, omwe anali gulu la anthu olemera ndiponso andale amene ankayesetsa kuti azigwirizana ndi Aroma. Iwo ankakana malamulo a pakamwa amene Afarisi ankawakonda ndiponso ankanyoza chikhulupiriro chakuti anthu akufa adzauka.c Anthu amenewa ayenera kuti anakwiya kwambiri ataona Petulo ndi Yohane m’kachisi, akuphunzitsa molimba mtima kuti Yesu anaukitsidwa.

10 Anthu otsutsa omwe anali atakwiya kwambiri anagwira Petulo ndi Yohane n’kuwatsekera m’ndende, ndipo tsiku lotsatira, anawatengera ku Khoti Lalikulu la Ayuda. Atsogoleriwo, omwe ankadziona kuti ndi anthu apamwamba, ankaona kuti Petulo ndi Yohane anali “osaphunzira ndiponso anthu wamba” ndipo analibe ufulu wophunzitsa m’kachisi. Iwo sanapite kusukulu iliyonse yapamwamba yophunzitsa zachipembedzo. Koma khotilo linadabwa litaona kuti iwo akuphunzitsa mogwira mtima ndiponso mochokera pansi pa mtima. N’chifukwa chiyani Petulo ndi Yohane ankatha kuphunzitsa chonchi? Chifukwa chimodzi chinali chakuti “ankayenda ndi Yesu.” (Mac. 4:13) Mbuye wawo ankaphunzitsa monga munthu waulamuliro, osati ngati alembi.​—Mat. 7:28, 29.

11 Khotilo linalamula atumwiwo kuti asiye kulalikira. Pa nthawi imeneyo, khotilo linali ndi mphamvu zambiri. Milungu ingapo m’mbuyomo, khoti lomweli linagamula kuti Yesu anali ‘woyenera kufa basi.’ (Mat. 26:59-66) Komabe, Petulo ndi Yohane sanachite mantha. Ataimirira pamaso pa anthu amenewa omwe anali olemera, ophunzira kwambiri ndiponso otchuka, Petulo ndi Yohane analankhula mopanda mantha koma mwaulemu kuti: “Weruzani nokha, ngati n’zoyenera pamaso pa Mulungu kumvera inu m’malo momvera Mulunguyo. Koma ife sitingasiye kulankhula za zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.”​—Mac. 4:19, 20.

MKULU WA ANSEMBE KOMANSO ANSEMBE AAKULU

Mkulu wa ansembe ankatsogolera anthu polambira Mulungu. M’nthawi ya atumwi, iye analinso mkulu wa Khoti Lalikulu la Ayuda. M’khoti limeneli, iye ankakhalanso ndi ansembe aakulu, amene analinso atsogoleri a Chiyuda. Pagulu la ansembe aakulu limeneli, pankakhalanso munthu amene anakhalapo mkulu wa ansembe, monga Anasi komanso akuluakulu ochokera m’mabanja mwina 4 kapena 5 amene ankasankhamo akulu a ansembe. Katswiri wina wa mbiri ya Chiyuda dzina lake Emil Schürer, analemba kuti: “Munthu amene anali wochokera m’mabanjawa, omwe anali olemekezeka, anthu ankamulemekeza kwambiri.”

Malemba amasonyeza kuti mkulu wa ansembe ankakhala pa udindowu kwa moyo wake wonse. (Num. 35:25) Koma m’nthawi ya atumwi, abwanamkubwa a Chiroma komanso mafumu amene ankalamulira mololedwa ndi ufumu wa Roma, ankasankha mkulu wa ansembe komanso kumuchotsa nthawi iliyonse imene afuna. Komabe zikuoneka kuti olamulira amenewa, omwe ankalambira milungu yabodza, ankasankha akulu a ansembewo kuchokera m’banja la Aroni.

12. N’chiyani chingatithandize kuti tizilalikira molimba mtima komanso mogwira mtima kwambiri?

12 Kodi inuyo mumalimba mtima ngati mmene atumwiwo anachitira? Kodi mumamva bwanji mumtima mwanu mukakhala ndi mwayi wolalikira anthu olemera, ophunzira kwambiri kapena otchuka amene ali m’dera lanu? Nanga bwanji ngati abale anu, anzanu akusukulu kapena akuntchito amakunyozani chifukwa cha zimene mumakhulupirira? Kodi mumachita mantha? Ngati mumatero, n’zotheka kuthana ndi vuto limeneli. Pamene anali padziko lapansi, Yesu anaphunzitsa atumwi ake mmene angayankhire molimba mtima komanso mwaulemu ngati ena atatsutsa zimene amakhulupirira. (Mat. 10:11-18) Yesu ataukitsidwa, analonjeza ophunzira ake kuti adzapitiriza kukhala nawo “masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:20) Motsogoleredwa ndi Yesu, “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru” masiku ano amatiphunzitsa mmene tingafotokozere zimene timakhulupirira ngati anthu ena akutitsutsa. (Mat. 24:45-47; 1 Pet. 3:15) Timaphunzira zimenezi pamisonkhano ya mpingo pogwiritsa ntchito malangizo opezeka mu Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu, komanso nkhani za pa webusaiti ya jw.org za mutu wakuti “Kuyankha Mafunso a M’Baibulo.” Kodi inuyo mumagwiritsa ntchito zinthu zimenezi? Mukamachita zimenezi, mudzatha kulalikira molimba mtima komanso mogwira mtima kwambiri. Ndipo mofanana ndi atumwi, simudzalola chinthu chilichonse kuti chikulepheretseni kulankhula mfundo zosangalatsa za choonadi zimene munaziona ndi kuzimva.

Mlongo akulalikira nzake wakuntchito pa nthawi yopuma.

Musalole kuti chilichonse chikulepheretseni kulankhula mfundo zosangalatsa za choonadi zimene mwaphunzira

“Anafuula kwa Mulungu” (Machitidwe 4:23-31)

13, 14. Kodi tiyenera kuchita chiyani anthu ena akamatitsutsa, nanga n’chifukwa chiyani?

13 Petulo ndi Yohane atangotulutsidwa m’ndende, anakumana ndi mpingo wonse. Onse pamodzi, “anafuula kwa Mulungu” ndipo anapemphera kuti awathandize kukhala olimba mtima n’cholinga choti apitirize kulalikira. (Mac. 4:24) Petulo ankadziwa bwino kuti ndi kupusa kwambiri kudalira mphamvu zako pochita chifuniro cha Mulungu. Iye ankadziwa zimenezi chifukwa milungu ingapo m’mbuyomo, anauza Yesu modzitama kuti: “Ngakhale ena onse atathawa n’kukusiyani, ine ndekha sindingathawe!” Koma monga mmene Yesu ananenera, Petulo anaopa anthu ndipo anakana Yesu, amene anali mnzake ndiponso mphunzitsi wake. Komabe, Petulo anaphunzirapo kanthu pa zimene analakwitsazi.​—Mat. 26:33, 34, 69-75.

14 Kukhala ndi mtima wofunitsitsa kutumikira Yehova, pakokha sikungakuthandizeni kukwaniritsa ntchito imene mumafunikira kugwira kuti mukhale mboni ya Khristu. Anthu akamakutsutsani n’cholinga choti akusiyitseni zimene mumakhulupirira kapena ntchito yolalikira, muzitsatira chitsanzo cha Petulo ndi Yohane. Muzipemphera kwa Yehova kuti akupatseni mphamvu. Muzipempha ena mumpingo kuti akuthandizeni. Muziuza akulu komanso anthu ena olimba mwauzimu mavuto amene mukukumana nawo. Mapemphero a anthu ena angakhale othandiza kwambiri.​—Aef. 6:18; Yak. 5:16.

15. N’chifukwa chiyani anthu amene nthawi ina anasiya kulalikira sayenera kutaya mtima?

15 Ngati nthawi ina munasiya kulalikira chifukwa chotsutsidwa, musataye mtima. Kumbukirani kuti atumwi onse anasiya kulalikira kwa kanthawi Yesu atangophedwa, koma kenako anayambiranso kulalikira mwakhama. (Mat. 26:56; 28:10, 16-20) M’malo mokhumudwa ndi zimene munalakwitsapo m’mbuyomu, mukhoza kuphunzirapo kanthu pa zimenezo komanso kuzigwiritsa ntchito polimbikitsa ena.

16, 17. Kodi tingaphunzire chiyani tikaganizira pemphero limene otsatira a Khristu anapemphera ku Yerusalemu?

16 Anthu olamulira akamatizunza, kodi tiyenera kutchula mfundo zotani popemphera? Onani kuti ophunzira a Yesu sanapemphere kwa Yehova kuti awateteze kuti asakumane ndi chizunzo. Iwo ankakumbukira bwino mawu a Yesu akuti: “Ngati anazunza ine, inunso adzakuzunzani.” (Yoh. 15:20) M’malomwake, ophunzira okhulupirika amenewa anapempha Yehova kuti ‘amve’ mmene anthu otsutsawo ankawaopsezera. (Mac. 4:29) Ophunzirawo anamvetsa bwino nkhani yonse, ndipo ankadziwa kuti akuzunzidwa pokwaniritsa ulosi. Monga mmene Yesu ananenera pamene ankawaphunzitsa kupemphera, iwo ankadziwa kuti chifuniro cha Mulungu ‘chidzachitika padziko lapansi,’ ngakhale anthu olamulira atayesetsa kuwatsutsa.​—Mat. 6:9, 10.

17 Kuti akwanitse kuchita chifuniro cha Mulungu, ophunzirawo anapemphera kwa Yehova kuti: “Tithandizeni ife akapolo anu kuti tipitirize kulankhula mawu anu molimba mtima.” Kodi Yehova anawayankha bwanji nthawi yomweyo? “Malo amene anasonkhanawo anagwedezeka. Kenako onse anadzazidwa ndi mzimu woyera ndipo anayamba kulankhula mawu a Mulungu molimba mtima.” (Mac. 4:29-31) Palibe chimene chingalepheretse Mulungu kukwaniritsa chifuniro chake. (Yes. 55:11) Ngakhale zinthu zitaoneka ngati n’zovuta kwambiri, kapena anthu amene amatitsutsa atakhala amphamvu kwambiri, tikapemphera kwa Mulungu, tingakhale otsimikiza kuti iye adzatipatsa mphamvu kuti tipitirize kulalikira mawu ake molimba mtima.

Tisamangochita Zinthu Kuti Tisangalatse “Anthu, Koma Mulungu” (Machitidwe 4:32–5:11)

18. Kodi anthu a mumpingo ku Yerusalemu ankathandizana bwanji?

18 Pasanapite nthawi, mpingo umene unali utangoyamba kumene ku Yerusalemu unakula kwambiri ndipo unali ndi anthu oposa 5,000.d Ngakhale kuti ophunzirawo anali ochokera m’madera osiyanasiyana, iwo anali ndi “mtima umodzi ndi maganizo amodzi” ndipo ankagwirizana. (Mac. 4:32; 1 Akor. 1:10) Ophunzirawo ankachita zinthu zambiri kuwonjezera pa kupemphera kwa Yehova kuti adalitse ntchito yawo. Iwo ankathandizana mwauzimu komanso mwakuthupi ngati panafunika kutero. (1 Yoh. 3:16-18) Mwachitsanzo, wophunzira wina dzina lake Yosefe, amene atumwi anam’patsa dzina lakuti Baranaba, anagulitsa malo ake ndipo anapereka ndalama zonse kuti athandizire anthu ochokera kutali amene anatsalira ku Yerusalemu kuti apitirize kuphunzira zambiri zokhudza chikhulupiriro chawo chatsopanocho.

19. N’chifukwa chiyani Yehova anapha Hananiya ndi Safira?

19 Hananiya ndi mkazi wake Safira nawonso anagulitsa munda wawo n’kupereka ndalama zothandizira Akhristu anzawo. Iwo ananama kuti apereka ndalama zonse zimene analandira atagulitsa mundawo, koma “anachotsapo ndalama zina n’kubisa.” (Mac. 5:2) Yehova anapha banjali, osati chifukwa choti anapereka ndalama zochepa, koma chifukwa choti anali ndi zolinga zoipa komanso anali anthu achinyengo. Sikuti iwo ananamiza “anthu, koma Mulungu.” (Mac. 5:4) Mofanana ndi anthu achinyengo amene Yesu anawadzudzula, Hananiya ndi Safira ankafuna kuti anthu aziwatama, osati kusangalatsa Mulungu.​—Mat. 6:1-3.

20. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani yopereka zinthu zathu kwa Yehova?

20 Masiku anonso, a Mboni za Yehova mamiliyoni ambiri amatsanzira mtima wopatsa umene ophunzira a Yesu oyambirira a ku Yerusalemu anali nawo ndipo amathandiza pa ntchito yolalikira padziko lonse popereka ndalama mwa kufuna kwawo. Palibe amene amakakamizidwa kupereka ndalama kapena nthawi yake pothandiza pa ntchito imeneyi. Ndithudi, Yehova safuna kuti tizimutumikira monyinyirika kapena mokakamizika. (2 Akor. 9:7) Yehova amasangalala ndi cholinga chimene tikuperekera zinthu kwa iye, osati ndi kuchuluka kwa zinthuzo. (Maliko 12:41-44) Tisayerekeze n’komwe kukhala ndi mtima ngati wa Hananiya ndi Safira, wotumikira Mulungu n’cholinga choti titchuke kapena kuti ena azititama. M’malomwake, nthawi zonse tizitumikira Yehova Mulungu chifukwa chomukondadi ndiponso chifukwa chokonda anthu ngati mmene anachitira Petulo, Yohane ndi Baranaba.​—Mat. 22:37-40.

PETULO ANASIYA KUPHA NSOMBA N’KUKHALA MTUMWI WODALIRIKA

M’Baibulo, Petulo amatchulidwa ndi mayina 5. Iye amadziwika ndi dzina la Chiheberi lakuti Sumiyoni lomwe ndi lofanana ndi la Chigiriki lakuti Simoni. Amadziwikanso ndi dzina lakuti Petulo, lomwe ndi lofanana ndi dzina la Chiaramu lakuti Kefa. Mtumwiyu amadziwikanso ndi dzina lophatikiza mayina awiri lakuti Simoni Petulo.​—Mat. 10:2; 16:16; Yoh. 1:42; Mac. 15:14.

Mtumwi Petulo wanyamula dengu la nsomba.

Petulo anali wokwatira ndipo anatenga apongozi ake aakazi ndiponso mchimwene wake n’kumakhala nawo kunyumba kwake. (Maliko 1:29-31) Iye anali msodzi ndipo kwawo kunali ku Betsaida, tauni imene inali kumpoto kwa nyanja ya Galileya. (Yoh. 1:44) Kenako iye anasamuka n’kumakhala m’tauni ina yapafupi yotchedwa Kaperenao. (Luka 4:31, 38) Pa nthawi ina Yesu anakhala mubwato la Petulo n’kumalalikira gulu la anthu limene linasonkhana m’mbali mwa nyanja ya Galileya. Yesu atamaliza kulalikira, Petulo anapha nsomba zambirimbiri mozizwitsa chifukwa anatsatira zimene Yesu anamuuza. Kenako Petulo anachita mantha ndipo anagwada, koma Yesu anamuuza kuti: “Usachite mantha. Kuyambira lero uzisodza anthu amoyo.” (Luka 5:1-11) Petulo ankagwira ntchito yausodzi pamodzi ndi mchimwene wake Andireya komanso ndi Yakobo ndi Yohane. Anthu 4 onsewa anavomera, Yesu atawaitana kuti akhale otsatira ake ndipo anasiya ntchito yawo yausodzi. (Mat. 4:18-22; Maliko 1:16-18) Patapita pafupifupi chaka chimodzi, Petulo anali m’gulu la anthu 12 amene Yesu anawasankha kuti akhale “atumwi” ake.​—Maliko 3:13-16.

Pochita zinthu zina zapadera, Yesu ankakonda kusankha Petulo, Yakobo ndi Yohane kuti ayende naye. Atumwi atatuwa anaona Yesu atasintha maonekedwe, anamuona akuukitsa mwana wamkazi wa Yairo komanso pamene Yesu ankavutika ndi chisoni m’munda wa Getsemane, atumwi amenewa analipo ndipo nawonso anavutika kwambiri. (Mat. 17:1, 2; 26:36-46; Maliko 5:22-24, 35-42; Luka 22:39-46) Atumwi atatuwa, pamodzi ndi Andireya, anafunsa Yesu kuti awauze chizindikiro cha kukhalapo kwake.​—Maliko 13:1-4.

Petulo anali munthu wosabisa mawu ndiponso anali wodalirika, koma nthawi zina ankachita zinthu mopupuluma kwambiri. Zikuoneka kuti nthawi zambiri ankalankhula moyambirira anzake asanalankhule. Mawu a Petulo amene analembedwa m’mabuku a Uthenga Wabwino ndi ochuluka kwambiri kuposa mawu onse a atumwi ena 11 aja tikawaphatikiza pamodzi. Komanso Petulo ankafunsa mafunso koma atumwi enawo ankangokhala chete. (Mat. 15:15; 18:21; 19:27-29; Luka 12:41; Yoh. 13:36-38) Pa nthawi ina, Petulo anakana kuti Yesu amusambitse mapazi, koma atamudzudzula, iye anapempha Yesuyo kuti amusambitsenso manja ndi m’mutu.​—Yoh. 13:5-10.

Chifukwa choti ankamukonda kwambiri Yesu, Petulo anayesa kumunyengerera kuti asalole kuti azunzidwe ndiponso kuphedwa. Koma Yesu anamudzudzula mwamphamvu chifukwa maganizo akewa sanali oyenera. (Mat. 16:21-23) Pa usiku umene Yesu anagwidwa ndi adani ake, Petulo ananena modzitama kuti ngakhale atumwi ena onse atathawa n’kumusiya Yesu, iye sangamusiye. Yesu atamangidwa ndi adani ake, Petulo anasonyeza kulimba mtima pogwiritsa ntchito lupanga kuti amuteteze, kenako anatsatira Yesu mpaka kukafika kunyumba ya mkulu wa ansembe. Koma usiku womwewo, Petulo anakana Mbuye wake katatu konse ndipo kenako analira mopwetekedwa mtima kwambiri atazindikira kuti wachita zinthu zolakwika.​—Mat. 26:31-35, 51, 52, 69-75.

Yesu atatsala pang’ono kuti aonekere koyamba kwa atumwi ake ku Galileya pambuyo poukitsidwa, Petulo anauza anzakewo kuti akupita kukapha nsomba, ndipo atumwi enawo anamutsatira. Atazindikira kuti munthu amene ankamuona m’mphepete mwa nyanja anali Yesu, nthawi yomweyo Petulo anadumphira m’madzi n’kuyamba kusambira kupita kumtunda. Pa nthawi imene atumwiwo ankadya nsomba zimene Yesu anawakonzera monga chakudya cham’mawa, Yesu anafunsa Petulo ngati ankamukonda kuposa “izi,” kutanthauza nsombazo. Pamenepa Yesu ankalimbikitsa Petulo kuti asankhe kutsatira iyeyo nthawi zonse m’malo mogwira ntchito ina, monga yausodzi.​—Yoh. 21:1-22.

Cha m’ma 62 C.E. mpaka 64 C.E., Petulo analalikira uthenga wabwino ku Babulo, komwe pano ndi ku Iraq, kumene kunkakhala Ayuda ochuluka. (1 Pet. 5:13) Pa nthawi imene anali ku Babulo, Petulo analemba kalata youziridwa yoyamba, ndipo mwinanso yachiwiri. Makalata amenewa amadziwika ndi dzina lake. Yesu “anapatsa Petulo mphamvu yokhala mtumwi kwa anthu odulidwa.” (Agal. 2:8, 9) Petulo anagwira ntchito imeneyi mwachifundo ndiponso mwakhama.

YOHANE ANALI WOPHUNZIRA AMENE YESU ANKAMUKONDA KWAMBIRI

Mtumwi Yohane anali mwana wa Zebedayo ndipo anali mchimwene wake wa mtumwi Yakobo. Zikuoneka kuti amayi ake dzina lawo linali Salome, ndipo n’kutheka kuti anali mchemwali wa Mariya, amayi a Yesu. (Mat. 10:2; 27:55, 56; Maliko 15:40; Luka 5:9, 10) Choncho, n’kutheka kuti Yohane ndi Yesu anali anthu apachibale. Zikuoneka kuti Yohane ankachokera ku banja lolemera chifukwa bizinezi ya Zebedayo inali yaikulu ndithu moti anali ndi aganyu amene ankamuthandiza. (Maliko 1:20) Salome ankayenda ndi Yesu ndipo ankamutumikira pa nthawi imene anali ku Galileya. Kenako Yesu ataphedwa, Salome anabweretsa zonunkhiritsa kuti apake mtembo wake pokonzekera kumuika m’manda. (Maliko 16:1; Yoh. 19:40) Zikuonekanso kuti Yohane anali ndi nyumba yakeyake.​—Yoh. 19:26, 27.

Mtumwi Petulo wanyamula dengu la nsomba.

Poyamba, mwina Yohane anali wophunzira wa Yohane M’batizi, ndipo anaima ndi Andireya pamene Yohane M’batiziyo anayang’ana Yesu n’kunena kuti: “Onani, Mwanawankhosa wa Mulungu!” (Yoh. 1:35, 36, 40) Yohane mwana wa Zebedayo atamva zimenezi, anayamba kutsatira Yesu ndipo anali naye limodzi pa ulendo wa ku Kana kumene anaona Yesuyo akuchita chozizwitsa chake choyamba. (Yoh. 2:1-11) M’buku lake la Uthenga Wabwino, Yohane anafotokoza mwatsatanetsatane ndiponso momveka bwino zimene Yesu anachita ku Yerusalemu, ku Samariya ndi ku Galileya ndipo zimenezi zikusonyeza kuti mwina iye analipo pamene zinthu zimenezi zinkachitika. N’zoonekeratu kuti Yohane anali ndi chikhulupiriro cholimba chifukwa Yesu atamuitana kuti akhale wotsatira wake, sanazengereze kusiya maukonde ophera nsomba, bwato ndiponso zonse zimene ankachita. Izi ndi zimenenso Yakobo, Petulo ndi Andireya anachita Yesu atawaitana.​—Mat. 4:18-22.

Tikawerenga nkhani za m’mabuku a Uthenga Wabwino, zikuoneka kuti Yohane sanatchulidwe kwambiri poyerekeza ndi Petulo. Komabe, nayenso Yohane anali wolimba mtima ndipo zimenezi zikuonekera bwino ndi dzina limene Yesu anam’patsa pamodzi ndi m’bale wake Yakobo. Iye anawapatsa dzina lakuti a Boanege, kutanthauza “Ana a Bingu.” (Maliko 3:17) Poyamba, Yohane anali ndi mtima wofuna kwambiri udindo moti iye ndi mchimwene wake anatuma mayi awo kuti akapemphe Yesu kuti adzapereke udindo wapamwamba kwa ana awowo mu Ufumu wake. Ngakhale kuti zimenezi zinasonyeza kuti iwo anali ndi mtima wodzikonda, zinasonyezanso kuti anali ndi chikhulupiriro cholimba choti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni. Zimene Yohane ndi mchimwene wakeyo anachita zinapereka mpata kwa Yesu wophunzitsa atumwi ake onsewo kufunika kokhala anthu odzichepetsa.​—Mat. 20:20-28.

Yohane anasonyeza kuti anali wolimba mtima pamene anafuna kuletsa munthu wina amene sanali m’gulu la otsatira a Yesu kuti asamatulutse ziwanda m’dzina la Yesu. Pa nthawi ina, Yohane anafuna kuitanitsa moto kuchokera kumwamba kuti uwononge anthu amene ankakhala m’mudzi winawake wa ku Samariya chifukwa anthuwo anakana kuchita zimene Yesu anatuma amithenga ake. Koma Yesu anadzudzula Yohane chifukwa cha maganizo ake olakwikawo. N’zoonekeratu kuti patapita nthawi, Yohane anaphunzira kuona zinthu m’njira yoyenera ndiponso anaphunzira kuchitira ena chifundo. (Luka 9:49-56) Ngakhale kuti nthawi zina Yohane ankalakwitsa zinthu, iye anali “wophunzira amene [Yesu] ankamukonda.” Choncho Yesu atatsala pang’ono kufa, anapatsa Yohane udindo woti azisamalira mayi ake, Mariya.​—Yoh. 19:26, 27; 21:7, 20, 24.

Yohane anali mtumwi yekhayo amene anakhala ndi moyo nthawi yaitali atumwi ena onse atamwalira, monga mmene Yesu analoserera. (Yoh. 21:20-22) Yohane anatumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka pafupifupi 70. Chakumapeto kwa moyo wake, mu ulamuliro wa mfumu ya Chiroma Domitani, Yohane anamangidwa ndipo anakamuika pachilumba cha Patimo “chifukwa cholankhula za Mulungu ndi kuchitira umboni za Yesu.” Pamene anali pachilumbacho, cha m’ma 96 C.E., Yohane anaona masomphenya amene iye anawalemba m’buku la Chivumbulutso. (Chiv. 1:1, 2, 9) Anthu ambiri amakhulupirira kuti Yohane atamasulidwa, anapita ku Efeso, ndipo ali kumeneko, analemba buku la Uthenga Wabwino limene lili ndi dzina lake ndipo analembanso makalata atatu odziwika ndi dzina lake. Anthuwo amakhulupiriranso kuti iye anamwalira ali ku Efeso komweko cha m’ma 100 C.E.

a Anthu ankapemphera kukachisi pa nthawi yopereka nsembe yam’mawa komanso yamadzulo. Nsembe yamadzulo inkaperekedwa cha m’ma “3 koloko masana,” kapena kuti pa ola la 9.

b Onani bokosi lakuti “Petulo Anasiya Kupha Nsomba N’kukhala Mtumwi Wodalirika,” ndi lakuti “Yohane Anali Wophunzira Amene Yesu Ankamukonda Kwambiri.”

c Onani bokosi lakuti “Mkulu wa Ansembe Komanso Ansembe Aakulu.”

d Zikuoneka kuti mu 33 C.E., ku Yerusalemu kunali Afarisi okwana 6,000 okha ndi Asaduki ochepa kwambiri. Zimenezi zingasonyeze chifukwa china chimene magulu awiriwa ankachitira mantha kwambiri ndi zimene ophunzirawo ankaphunzitsa zokhudza Yesu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena