-
Kutchinjiriza Chikhulupiriro ChathuNsanja ya Olonda—1998 | December 1
-
-
12. Kodi ndi mikhalidwe yotani imene inapangitsa Paulo ndi Barnaba kulankhula molimba mtima ku Ikoniyo?
12 Lingaliraninso chitsanzo cha Paulo ndi Barnaba. Machitidwe 14:1, 2 amati: “Kunali pa Ikoniyo kuti analoŵa pamodzi m’sunagoge wa Ayuda, nalankhula kotero, kuti khamu lalikulu la Ayuda ndi Ahelene anakhulupira. Koma Ayuda osamvera anautsa mitima ya Ahelene kuti aipse abale athu.” The New English Bible limati: “Koma Ayuda osatembenuka anautsa mitima ya Akunja ndi kuipitsa maganizo awo pa Akristu.” Posakhutira ndi kuti iwo akana uthengawo, Ayuda otsutsa anayamba kufalitsa mphekesera zoipa, akumayesa kupangitsa anthu Akunja kuti akhale ndi maganizo oipa ponena za Akristu.a Iwo anadadi Chikristu! (Yerekezerani ndi Machitidwe 10:28.) Apa Paulo ndi Barnaba anaona kuti inali “mphindi yakulankhula,” apo ayi ophunzira atsopanowo ataya mtima ponyozedwa ndi anthu. “Chifukwa chake [Paulo ndi Barnaba] anakhala nthaŵi yaikulu nanenetsa zolimba mtima mwa Ambuye,” amene anasonyeza kuwavomereza kwake mwa kuwapatsa mphamvu yochita zizindikiro zozizwitsa. Zimenezi zinagaŵanitsa anthu, ena “anali ndi Ayuda, koma ena anali ndi atumwi.”—Machitidwe 14:3, 4.
-
-
Kutchinjiriza Chikhulupiriro ChathuNsanja ya Olonda—1998 | December 1
-
-
a Matthew Henry’s Commentary on the Whole Bible limati Ayuda otsutsa “anaipanga kukhala ntchito yawo yopita mwadala kwa anthu [Akunja] amene anali atazoloŵerana nawo, ndi kukawauza zonse zimene apeka, kuti awapatse malingaliro osati kokha olakwika komanso oipa onena za Chikristu.”
-