-
Kodi “Makiyi a Ufumu” N’chiyani?Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
-
-
Nthawi zina mawu akuti “Makiyi a Ufumu,” m’Mabaibulo ena amatchedwanso “Makiyi olowera mu ufumu.” Mawuwa amatanthauza udindo wothandiza anthu kuti ‘akalowe mu ufumu wa Mulungu.’ (Mateyu 16:19;The New American Bible; Machitidwe 14:22)a Yesu anapatsa Petulo “makiyi a ufumu wakumwamba.” Zimenezi zikutanthauza kuti Petulo anapatsidwa udindo wotsegulira anthu okhulupirika mwayi wolandira mzimu woyera wa Mulungu kuti anthuwo adzathe kulowa mu Ufumu wakumwamba.
-
-
Kodi “Makiyi a Ufumu” N’chiyani?Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
-
-
Kodi ‘kulowa mu Ufumu’ kumatanthauza chiyani?
Anthu amene ‘amalowa mu Ufumu,’ adzalamulira limodzi ndi Yesu kumwamba. Baibulo linaneneratu kuti anthuwa adzakhala “m’mipando yachifumu” ndipo “adzakhala mafumu olamulira dziko lapansi.”—Luka 22:29, 30; Chivumbulutso 5:9, 10.
-