Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Tonse Tagwirizana”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
    • 9. Kodi maganizo amene Yakobo anapereka anathandiza bwanji?

      9 Kodi maganizo a Yakobo amenewa anali abwino? N’zoonekeratu kuti anali abwino chifukwa atumwi komanso akulu atakambirana, anagwirizana nawo. Kodi zimenezi zinathandiza bwanji? Choyamba, zimene anagwirizanazo zinathandiza kuti ‘asavutitse’ Akhristu a mitundu ina powakakamiza kuti azitsatira Chilamulo cha Mose. (Mac. 15:19) Chachiwiri, zimenezi zinasonyeza kuti akulemekeza chikumbumtima cha Akhristu a Chiyuda, amene kwa zaka zambiri ankamva ‘mawu ochokera m’mabuku a Mose, akuwerengedwa mokweza m’masunagoge sabata lililonse.’b (Mac. 15:21) Zimene anagwirizanazo zinathandiza kuti Akhristu a Chiyuda ndi a mitundu ina azigwirizana kwambiri. Komanso chofunika kwambiri n’chakuti zinasangalatsa Yehova Mulungu chifukwa zinali zogwirizana ndi chifuniro chake. Imeneyitu inali njira yabwino kwambiri yothetsera nkhani imene ikanasokoneza mgwirizano komanso mtendere wa anthu a Mulungu mumpingo. Chimenechi ndi chitsanzo chabwino kwambiri ku mpingo wa Chikhristu masiku ano.

  • “Tonse Tagwirizana”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
    • b Mwanzeru, Yakobo anatchula mabuku a Mose mmene simumangopezeka Chilamulo chokha, koma mumapezekanso zinthu zina zimene Mulungu anachita. Mabukuwa amanenanso zimene Mulungu anachita posonyeza chifuniro chake asanapereke Chilamulo kwa anthu ake. Mwachitsanzo, m’buku la Genesis tingaone mosavuta kuti Mulungu amadana ndi anthu achigololo, olambira mafano komanso ogwiritsa ntchito magazi molakwika. (Gen. 9:3, 4; 20:2-9; 35:2, 4) Choncho Yehova anapereka mfundo zimene zimagwira ntchito kwa anthu onse, kaya ndi Ayuda kapena a mitundu ina.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena