Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ŵerengani Mawu a Mulungu ndi Kumtumikira M’choonadi
    Nsanja ya Olonda—1996 | May 15
    • 5. Kodi nchiyani chimene chikufunika ngati titi tipeze choonadi cha Mulungu?

      5 Choonadi cha Mulungu ndicho chuma chamtengo wosayerekezereka. Kuchipeza kumafuna kukumba, kusanthula Malemba kwakhama. Ndi kukhala monga ana ophunzira a Mlangizi Wamkulu kokha kumene tingapeze nako nzeru ndi kufikira pa kuzindikira kuwopa Yehova kwaulemu. (Miyambo 1:7; Yesaya 30:20, 21) Zoonadi, tiyenera kutsimikizira zinthu mwa Malemba. (1 Petro 2:1, 2) Ayuda ku Bereya “anali mfulu koposa a m’Tesalonika, popeza analandira mawu ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m’malembo masiku onse, ngati zinthu [zonenedwa ndi Paulo] zinali zotero.” Iye anayamikira m’malo mwa kudzudzula Abereya chifukwa cha kuchita zimenezi.​—Machitidwe 17:10, 11.

  • Ŵerengani Mawu a Mulungu ndi Kumtumikira M’choonadi
    Nsanja ya Olonda—1996 | May 15
    • 7. Kodi nchiyani chimene chikufunika kuti tikulitse kumvetsetsa Baibulo, ndipo chifukwa ninji?

      7 Kuti tikulitse kumvetsetsa kwathu Baibulo, tifunikira chitsogozo cha mzimu wa Mulungu, kapena mphamvu yogwira ntchito. “Mzimu [u]santhula zonse, zakuya za Mulungu zomwe” kuti tidziŵe tanthauzo lake. (1 Akorinto 2:10) Akristu ku Tesalonika anafunikira ‘kuyesa zonse’ pa ulosi uliwonse umene anamva. (1 Atesalonika 5:20, 21) Pamene Paulo analembera Atesalonika (cha ku ma 50 C.E.), mbali yokha ya Malemba Achigiriki imene inali italembedwa kale inali Uthenga Wabwino wa Mateyu. Chotero Atesalonika ndi Abereya akanatha kutsimikiza zinthu zonse, mwachionekere mwa kupenda matembenuzidwe a Septuagint yachigiriki ya Malemba Achihebri. Anafunikira kuŵerenga ndi kuphunzira Malemba, ndipo nafenso tifunikira kutero.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena