Kodi Tidzaŵawonanso Nkomwe?
“Inu mwatisiya ife kosatha. Chinali chosayembekezereka kwenikweni. Koma mosasamala kanthu za mabala akuya amene imfa yanu yasiya kumbuyo, m’mitima yathu inu mudzakhala nafe nthaŵi zonse. Sitidzaiwala konse zaka zabwino zimene tasangalala nanu osatinso kuleka kuyembekezera kukuwonaninso tsiku lina.”
MU Grand Duchy ya ku Luxembourg, mabanja okhalabe ndi moyo ndi mabwenzi mobwerezabwereza amalongosola malingaliro onga awa m’zidziŵitso za kukumbukira akufa m’nyuzipepala zofalitsidwa pambuyo pa imfa ya wokondedwa. Malingaliro ofananawo ali m’maganizo a ena kuzungulira dziko lonse, malingaliro ochoka ku mtima a chikumbukiro, limodzi ndi kufooketsedwa kwa kuthedwa nzeru kwa kutaikiridwa kwawo—chiyembekezo chosakanizana ndi kusatsimikizirika. Inu mungakhale munakhalapo ndi kudzimva koteroko kapena kumva za iko kuchokera kwa bwenzi pambuyo pa imfa ya wokondedwa.
Kwa anthu ambiri, chiyembekezo cha kuwonanso okondedwa awo akufa chiri chosokonezeka ndi chosamvekera. Zifukwa ziri zosavuta. Choyambirira nacho, palibe ndi mmodzi yense masiku ano yemwe m’chenicheni amatenga nthaŵi kuzidziŵitsa iyemwini pa nkhaniyo. Ndipo pamene winawake ayesera kutero, chidziŵitso choperekedwa ndi zipembedzo zambiri pa funsolo chiri chosamvekera kwenikweni kapena chachilendo kukhala chokhutiritsa.
Monga momwe mungakhale mukudziŵira, kwa ambiri “moyo wa mtsogolo” wokha kaamba ka akufa uli kupitirizabe kwa mizera ya banja lawo. Inu mungakhale munamvapo lingaliro lakuti anthu ‘amakhalabe ndi moyo mwa ana awo.’ Koma kodi “moyo” woterowo umabweretsa phindu la chikumbumtima lirilonse kwa akufawo kapena chiyembekezo chirichonse kaamba ka opulumuka awo kuwawonanso iwo? Kutalitali! Chotero palidi chitonthozo chochepera m’lingaliro loterolo!
M’chikondwerero cha okondedwa athu, ponse paŵiri omwe anafa ndi awo omwe akali ndi moyo, tifunikira mayankho ku mafunso akuti: Ngati winawake amene timakonda amwalira, kodi tidzamuwonanso ameneyo? Ngati yankho liri lakuti inde, ndi liti ndipo nkuti komwe chidzachitikira? Kumwamba? Kapena ngakhale pano pa dziko lapansi? Ndithudi, kodi nchiyembekezo chotani chomwe chiriko mtsogolo kaamba ka okondedwa akufa ndi ife?
Kunena zowonadi, pali mbiri yabwino yonena za mafunso amenewa. Iyo iri yabwino m’lingaliro lakuti pali chiyembekezo chotsimikizirika, chosangalatsa. Iyo iri mbiri chifukwa chakuti iri uthenga wosiyana ndi umene anthu ambiri amva, ngakhale kuchokera ku magwero a chipembedzo.
M’zana loyamba la Nyengo yathu ya Chisawawa, pamene m’mishonale Wachikristu Paulo anali mu Atene, Grisi, iye analankhula ponena za chiyembekezo cha m’Malemba kaamba ka akufa. Amvetseri ena anali ofunitsitsa kudziŵa, koma ena anamva ndi kunyalanyaza. Anthanthi ena anafuna kupitiriza kukambitsirana kokangana ndi iye, ndipo iwo anati: “Ichi nchiyani afuna kunena wobwetuka uyu?” Ena anadzinenera kuti iye anali “wonga wolalikira [milungu yachilendo, NW] chifukwa analalikira Yesu ndi kuwuka kwa akufa.” (Machitidwe 17:18) Inde, mbiri yabwino imene Paulo anainena inaphatikizapo chiwukiriro!
Ndimotani momwe mukawonera nkhani yonena za chiwukiriro cha mtsogolo—ya kuwona akufa akukhalanso amoyo? Kodi ichi chikawoneka kukhala kubwetuka kopanda pake? Kapena, chifukwa cha maphunziro anu achipembedzo ndi lingaliro lanu laumwini, kodi uthenga wa Malemba Opatulika wonena za chiyembekezo kaamba ka akufa umawoneka kukhala watsopano ndi wachilendo kwa inu, monga ngati unali kuchokera kwa ‘mlungu wachilendo’?
Kwa Paulo, anthu a ku Atene ananena kuti: “Ufika nazo ku makutu athu zachilendo: tifuna tsono kudziŵa, izi zitani?” (Machitidwe 17:20) Kodi inu nanunso mukukhumba kuphunzira zowonjezereka ponena za chiyembekezo cha Baibulo kaamba ka akufa athu, ndi kaamba ka ife omwe tiri ndi moyo? Ngati ndi tero, nkhani yotsatira idzakusangalatsani.