Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 12/1 tsamba 30
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Nkhani Yofanana
  • Kulimbana ndi Mphamvu ya Uchimo pa Thupi Lochimwa
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Samalirani Mzimu ndi Kukhala ndi Moyo!
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Yendani Mogwirizana ndi Mzimu Kuti Mupeze Moyo ndi Mtendere
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Tifunika Kukhala Odziletsa
    Imbirani Yehova
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 12/1 tsamba 30

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

◼ Pa Aroma 8:27, New World Translation imamasulira liwu Lachigiriki lakuti phroʹne·ma monga “tanthauzo,” koma m’mavesi 6 ndi 7, lamasuliridwa monga “kusamalira.” Kodi nchifukwa ninji liwu Lachigiriki limodzimodzili latembenuzidwa mosiyana?

Mawu apatsogolo ndi apambuyo amavomereza mamasuliridwe aŵiri osankhidwawo.

Mawu Oyamba a New World Translation of the Christian Greek Scriptures (1950) analongosola motere: “Ku liwu lirilonse lalikulu tapereka tanthauzo limodzi ndipo tamamatira ku tanthauzo limenelo kuukulu umene mawu apatsogolo ndi apambuyo a lembalo alola.” Ena sangalingalire phroʹne·ma kukhala liwu lalikulu, popeza kuti likuwoneka nthaŵi zinayi zokha. Komabe, ilo nlogwirizana ndi mawu amene agwiritsiridwa ntchito mobwerezabwereza. Limodzi ndi phro·neʹo, lotanthauza “kuganiza, kusamaliridwa mwanjira yakutiyakuti.” (Mateyu 16:23; Marko 8:33; Aroma 8:5; 12:3; 15:5) Mawu ena Achigiriki ogwirizana nalo amapereka lingaliro lakugwiritsira ntchito nzeru, kulingalira, kapena kuzindikira.​—Luka 1:17; 12:42; 16:8; Aroma 11:25; Aefeso 1:8.

The Kingdom Interlinear Translation of the Greek Scriptures imasonyeza kuti phroʹne·ma imawoneka nthaŵi zinayi pa Aroma 8:6, 7, 27 ndikuti tanthauzo lake lenileni losasintha ndilo “kusamalira.” Akatswiri Achigiriki Bauer, Arndt, ndi Gingrich akulongosola phroʹne·ma monga: ‘njira ya kuganiza, (kusumika) maganizo, cholinga, chonulirapo, kukalamira.’​—A Greek-English Lexicon of the New Testament and Other Early Christian Literature.

Mu Aroma mutu 8, mtumwi Paulo analangiza Akristu kusayenda mogwirizana ndi thupi lopanda ungwiro. Kuti apambane kuchita zimenezi, iwo ayenera kuchenjera ndi zikhoterero kapena zisonkhezero zathupi, limodzinso ndi zolingalira za mtima wopanda ungwiro. ‘Kusumika maganizo awo’ pa zinthu zogwirizana ndi mzimu woyera wa Mulungu kukawathandiza m’zimenezi.​—Aroma 8:1-5.

Paulo anapereka mawu osiyanitsa awa: ‘Chisamaliro cha thupi chiri imfa; koma chisamaliro cha mzimu chiri moyo ndi mtendere. Chifukwa chisamaliro cha thupi chidana ndi Mulungu; pakuti sichigonja ku chilamulo cha Mulungu.’ (Aroma 8:6, 7) Anthu ndiwo akufotokozedwa m’mavesi aŵiriwa. Anthu, makamaka Akristu, sayenera kusumika maganizo awo, kapena ‘kusamalira,’ zinthu za thupi lochimwa. M’malo mwake, iwo ayenera kusumika maganizo awo, kapena ‘kusamalira,’ zinthu zogwirizana ndizosonkhezeredwa ndi mzimu.

Mosiyana, vesi 27 (NW) likunena za Mulungu iyemwini. Tikuwerenga motere: “Komabe iye [Yehova] amene asanthula mitima adziŵa chimene chiri tanthauzo la mzimu, chifukwa uchonderera mogwirizana ndi Mulungu kaamba ka oyera mtima.” Inde, “iye” panopa ndi Yehova, Wakumva pemphero.

Liwu lakuti phroʹne·ma m’vesi 27 likanamasulidwa monga ‘kusamalira.’ Koma mzimu woyera simunthu kuti umaganiza kapena kukhala ndi malingaliro akeake. Mzimu ndiwo mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu, amene amadziŵa mmene mzimu wake woyera umagwirira ntchito kukwaniritsa chifuniro chake. Kuwonjezera apa, tanthauzo la vesili nlosiyana ndi lija la pa Aroma 8:6, 7. Mavesi oyambirirawo akugogomezera kufunika kwa anthu kulamulira kulingalira ndi zochita zawo. Koma Yehova satofunikira kuyesayesa, kapena kulimbikira, kuti adzilamulire yekha. Iye amadziŵa zimene zinalembedwa mouziridwa m’Baibulo, monga ngati mawu Abaibulo osonyeza chifuno chake kaamba ka atumiki ake apadziko lapansi. Dr. Heinrich Meyer akuthirira ndemanga pa Aroma 8:27 motere: “Mulungu angadziŵe m’chochitika chirichonse chifuno cha Mzimu.”

Chotero, kumasulira kwakuti “tanthauzo” n’kogwirizana ndi mawu apatsogolo ndi apambuyo kapena tanthauzo la Aroma 8:27, ndipo nkovomerezeka ndi Chigiriki. The Translator’s New Testament limalimasulira motere: “Iye amene asanthula m’mitima adziŵa chimene Mzimu umatanthauza.”

◼ Kodi Nchifukwa Ninji New World Translation Nthaŵi Zina Imamasulira Liwu Lachigiriki Lakuti Pi·steuʹo Monga “Kukhulupirira” (mofanana ndi matembenuzidwe ambiri) Ndipo Nthaŵi Zina Monga “Kusonyeza [Kapena Kuika] Chikhulupiriro Mwa”?

Ichi chimachitidwa kufuna kusonyeza matanthauzo osiyanasiyana amene amalongosoledwa ndi liwu Lachigiriki lakuti pi·steuʹo.

Mwachitsanzo, A Grammar of New Testament Greek, lolembedwa ndi James Moulton, limadziŵitsa kuti Akristu oyambirira anazindikira bwino lomwe “kufunika kwa kusiyana pakati pa chikhulupiriro wamba . . . ndi kukhulupirira kwa munthu payekha.” Malingaliro aŵiri onseŵa angalongosoledwe mwakugwiritsira ntchito liwu Lachigiriki lakuti pi·steuʹo.

Kaŵirikaŵiri, matanthauzo osiyanasiyana a tanthauzo la pi·steuʹo ayenera kuzindikiridwa m’mawu apatsogolo ndi apambuyo a lembalo. Komabe, nthaŵi zina kalembedwe ka galamala kosiyanasiyana kamatithandiza kuwona zimene wolembayo ankaganiza. Mwachitsanzo, ngati liwu lakuti pi·steuʹo latsatiridwa ndi liwu lolongosola chinthu m’kalembedwe kosalongosola mneni wachindunji, New World Translation kaŵirikaŵiri imalimasulira monga “kukhulupirira”​—kusiyapo kokha ngati mawu apatsogolo ndi apambuyo pa lembalo akusonyeza chinachake chosiyana. (Mateyu 21:25, 32; koma onani Aroma 4:3.) Ngati liwu lakuti pi·steuʹo latsatiridwa ndi liwu lakuti e·piʹ, “pa,” mwachisawawa limamasuliridwa kukhala “khulupirirani pa.” (Mateyu 27:42; Machitidwe 16:31, NW) Ngati latsatiridwa ndi liwu lakuti eis, “ku,” kaŵirikaŵiri limatembenuzidwa kukhala “kusonyeza chikhulupiriro mwa.”​—Yohane 12:36; 14:1, NW.

Kumasulira komaliziraku (kumene kumatikumbutsa kuti liwu lakuti pi·steuʹo nlofanana ndi liwu Lachigiriki lakuti piʹstis, “chikhulupiriro”) nkogwirizana ndi ndemanga yopezeka mu An Introductory Grammar of New Testament Greek, lolembedwa ndi Paul Kaufman. Bukhu limeneli likunena kuti: “Kalembedwe kena kamene nkofala m’Chipangano Chatsopano (makamaka mu Uthenga Wabwino wa Yohane) ndiko πιστεύω [pi·steuʹo] ndi εἰς [eis] ndi kalembedwe kolongosola mneni wachindunji . . . Kalembedwe konse ka εἰς kuphatikizapo kalembedwe kosalongosola mneni wachindunji kayenera kutembenuzidwa m’malo moyesera kutembenuza liwu losonyeza kumene chinthu chinachitikira εἰς monga liwu lapalokha. Chikhulupiriro chimalingaliridwa kukhala ntchito, chinachake chimene anthu amachita, uku ndiko kuti kuika chikhulupiriro mwa munthu wina.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena