Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Aliyense Adzakhala Paufulu
    Nsanja ya Olonda—1999 | May 1
    • “Vumbulutso la ana a Mulungu”

      Yehova anagonjetsa chilengedwe kuutsiru “ndi chiyembekezo” chakuti tsiku lina mtundu wa anthu udzakhalanso paufulu kupyolera muntchito ya “ana a Mulungu.” Kodi “ana a Mulungu” ameneŵa ndi ayani? Ndi ophunzira a Yesu Kristu amene, monga anthu ena onse ‘obadwa mwa [munthu],’ amabadwa ndi uchimo komanso opanda ungwiro. Pobadwa amakhala opanda malo m’banja loyera ndi langwiro lachilengedwe chonse cha Mulungu. Komabe, Yehova amawachitira chinthu china chapadera. Kupyolera mu nsembe ya dipo ya Yesu Kristu, Iye amawamasula kuukapolo womwe anabadwa nawo wa uchimo ndipo amawayesa “olungama,” kapena oyera mwauzimu. (1 Akorinto 6:11) Ndiyeno amawatenga monga “ana a Mulungu,” ndi kuwabwezeranso m’banja lake lachilengedwe chonse.​—Aroma 8:14-17.

      Monga ana otengedwa a Yehova, adzakhala ndi mwayi waulemerero. Adzakhala “ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo achita ufumu padziko” pamodzi ndi Yesu Kristu monga mbali ya Ufumu kapena Boma lakumwamba la Mulungu. (Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1-4) Limeneli ndi boma lokhazikitsidwa zolimba pa malamulo aufulu ndi achilungamo​—osati otsendereza ndi ankhanza. (Yesaya 9:6, 7; 61:1-4) Mtumwi Paulo ananena kuti ana a Mulungu ameneŵa ali anzake a Yesu, ‘mbewu ya Abrahamu’ yolonjezedwa kalekale. (Agalatiya 3:16, 26, 29) Chotero, iwonso, ali ofunika kwambiri pokwaniritsa lonjezo limene Mulungu analonjeza bwenzi lake Abrahamu. Mbali ya lonjezo limenelo inali yakuti kupyolera mwa mbewu ya Abrahamu (kapena, mwana), “mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa.”​—Genesis 22:18.

  • Aliyense Adzakhala Paufulu
    Nsanja ya Olonda—1999 | May 1
    • Kodi “vumbulutso la ana a Mulungu” lidzayamba liti? Posachedwapa tsopano, pamene Yehova adziŵikitsa anthu onse amene ali ana a Mulungu. Izi zidzachitika pamene “ana” ameneŵa, oukitsidwira kumwamba, pamodzi ndi Yesu Kristu adzayeretsa dziko loipa ndi lopondereza lino pankhondo ya Mulungu ya Harmagedo. (Danieli 2:44; 7:13, 14, 27; Chivumbulutso 2:26, 27; 16:16; 17:14; 19:11-21) Tikuona umboni wochuluka paliponse wakuti tili mkati mwenimweni mwa “masiku otsiriza,” pamene Mulungu sadzalekereranso chipanduko ndi kuipa kumene chinabweretsa monga mmene wachitira kwanthaŵi yaitali.​—2 Timoteo 3:1-5; Mateyu 24:3-31.

  • Aliyense Adzakhala Paufulu
    Nsanja ya Olonda—1999 | May 1
    • Pamene ‘mukulindira vumbulutso la ana a Mulungu,’ muyenera kukulitsa chidaliro chimene mtumwi Paulo anali nacho mu chisamaliro ndi chichirikizo cha Kristu, ngakhale pamene mavuto ndi chisalungamo zikuoneka kukhala zosapiririka. Atakambirana za kuvumbulutsidwa kwa ana a Mulungu, Paulo anafunsa kuti: “Adzatisiyanitsa ndani ndi chikondi cha Kristu? Nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiwa, kapena zoopsa kapena lupanga kodi?” (Aroma 8:35) Inde, kugwira mawu a Rousseau, Akristu a m’tsiku la Paulo anali adakali “paukapolo” chifukwa cha kuponderezedwa. Anali “kuphedwa dzuŵa lonse” monga “nkhosa zakupha.” (Aroma 8:36) Kodi zimenezi zinawafooketsa?

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena