Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 6/1 tsamba 15-20
  • Ugwiritsireni Ntchito Mwanzeru Ufulu Wanu Wachikristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ugwiritsireni Ntchito Mwanzeru Ufulu Wanu Wachikristu
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Odzozedwera Kulalikira’
  • ‘Chitirani Mfumu Ulemu’
  • ‘Kondani Abale’
  • Mawonekedwe ndi Zosangulutsa
  • Sumikani Maganizo pa Ufulu wa Ana a Mulungu Ukudzawo
  • Anthu Aufulu Koma Oŵerengeredwa Thayo
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Musaphonye Chifuno cha Ufulu Woperekedwa ndi Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Tizitumikira Yehova Mulungu Amene Amapereka Ufulu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Ufulu Womwe Olambira Yehova Amakhala Nawo
    Lambirani Mulungu Woona Yekha
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 6/1 tsamba 15-20

Ugwiritsireni Ntchito Mwanzeru Ufulu Wanu Wachikristu

“[Khalani] monga mfulu, . . . koma ngati akapolo a Mulungu.”​—1 PETRO 2:16.

1. Kodi ndiufulu wotani umene Adamu anautaya, ndipo kodi ndiufulu wotani umene Yehova adzabwezeretsera anthu?

PAMENE makolo athu oyamba anachimwa m’munda wa Edene, anataira ana awo choloŵa chaulemerero​—ufulu ku uchimo ndi chivundi. Monga chotulukapo, tonsefe tinabadwa tiri akapolo a chivundi ndi imfa. Komabe, nzodzetsa chimwemwe kuti Yehova ali ndi chifuno chakubwezeretsera anthu ufulu wabwino koposa. Lerolino, owongoka mtima akudikira ndi chidwi chachikulu ‘vumbulutso la ana a Mulungu’ pamene ‘adzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ana a Mulungu.’​—Aroma 8:19-21.

‘Odzozedwera Kulalikira’

2, 3. (a) Kodi “ana a Mulungu” ndani? (b) Kodi iwo ali ndi unansi wabwino wotani, ndipo umawapatsanso thayo lotani?

2 Kodi “ana a Mulungu” ameneŵa ndani? Ali abale a Yesu odzozedwa ndi mzimu omwe adzakhala olamulira pamodzi naye mu Ufumu wakumwamba. Oyamba a iwoŵa anakhalapo m’zaka za zana loyamba C.E. Iwo analandira chowonadi chomasula chimene Yesu anaphunzitsa, ndipo kuyambira pa Pentekoste wa 33 C.E., anakhala ndi mwaŵi waulemerero umene Petro ananena powalembera kuti: ‘Inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake.’​—1 Petro 2:9a; Yohane 8:32.

3 Eya, kukhala anthu apadera a Mulungu​—ndidalitso lotani nanga! Ndipo otsalira amakono a ana a Mulungu odzozedwa ameneŵa ali muunansi wodalitsika wofananawo ndi Mulungu. Koma mwaŵi wolemekezeka woterowo umabweretsa mathayo. Petro anasonyeza limodzi la mathayo ameneŵa pamene anapitiriza kumati: “Mukalalikire zoposazo za iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, muloŵe kuunika kwake kodabwitsa.”​—1 Petro 2:9b.

4. Kodi ndimotani mmene Akristu odzozedwa akwaniritsira thayo limene ufulu Wachikristu umaika pa iwo?

4 Kodi Akristu odzozedwa akwaniritsa thayo limeneli lakulalikira zoposazo za Mulungu? Inde atero. Polosera za odzozedwa odzakhalapo kuchokera mu 1919 kumka kutsogolo, Yesaya anati: ‘Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mawu abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am’nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m’ndende; ndikalalikire chaka chokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu.’ (Yesaya 61:1, 2) Lerolino, otsalira odzozedwa, otsatira chitsanzo cha Yesu, amene lembali likusonyako kwenikweni, amalengeza mwachangu mbiri yabwino ya ufulu kwa ena.​—Mateyu 4:23-25; Luka 4:14-21.

5, 6. (a) Kodi kulalikira kwachangu kwa Akristu odzozedwa kwakhala ndi zotulukapo zotani? (b) Kodi ndimwaŵi ndi matayo otani amene akhamu lalikulu ali nawo?

5 Monga chotulukapo cha kulalikira kwawo kwachangu, khamu lalikulu la nkhosa zina lawonekera padziko lapansi m’masiku ano otsiriza. Akhamulo achokera m’mitundu yonse kudzagwirizana ndi odzozedwa m’kutumikira Yehova, ndipo chowonadi chawamasula iwonso. (Zekariya 8:23; Yohane 10:16) Mofanana ndi Abrahamu iwo amalengezedwa olungama pamaziko a chikhulupiriro ndipo aloŵa unansi wathithithi ndi Yehova Mulungu. Ndipo mofanana ndi Rahabi kukhala kwawo olengezedwa olungama kumawaika pamzera wakupulumuka​—koma iwo, ndikupulumuka Armagedo. (Yakobo 2:23-25; Chivumbulutso 16:14, 16) Koma mwaŵi wolemekezeka woterowo umadzetsanso thayo lakuuza ena ponena za ulemerero wa Mulungu. Nchifukwa chake Yohane anawawona akutamanda Yehova poyera ‘akufuula ndi mawu aakulu, nanena, Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pampando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.’​—Chivumbulutso 7:9, 10, 14.

6 Chaka chatha khamu lalikulu, tsopano loposa mamiliyoni anayi, pamodzi ndi Akristu odzozedwa ochepawo, anathera maola pafupifupi okwanira biliyoni imodzi akulengeza ponseponse zoposa za Yehova. Iyi inali njira yabwino koposa yogwiritsirira ntchito ufulu wawo wauzimu.

‘Chitirani Mfumu Ulemu’

7, 8. Kodi ufulu Wachikristu umadzetsa thayo lotani kulinga kwa olamulira adziko, ndipo pazimenezi, kodi ndimzimu wolakwa wotani umene tiyenera kupeŵa?

7 Ufulu wathu Wachikristu umadzetsa mathayo. Petro anasonyeza ena a mathayowo pamene analemba kuti: ‘Chitirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Opani Mulungu, chitirani mfumu ulemu.’ (1 Petro 2:17) Kodi mawu akuti ‘chitirani mfumu ulemu’ amatanthauzanji?

8 ‘Mfumu’ panopa ndiwo olamulira akudziko. Lerolino, mzimu wakusalemekeza olamulira wakula m’dziko, ndipo zimenezi zingawayambukire mosavuta Akristu. Mkristu angalingaliretu kuti nchifukwa ninji ayenera kulemekeza ‘mfumu,’ popeza kuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Polingalira za mawu ameneŵa, iye angasankhe kuswa malamulo owoneka kukhala ovuta kwa iye ndi kuzemba misonkho ngati angathe kuipeŵa. Koma zimenezi zikasemphana ndi lamulo la Yesu lachindunji la ‘kupatsa kwa Kaisara zake za Kaisara.’ Kuteroko, kukatanthauza ‘kukhala nawo ufulu monga chobisira choipa.’​—Mateyu 22:21; 1 Petro 2:16.

9. Kodi nzifukwa zabwino ziŵiri zotani zimene tiyenera kukhalira omvera kwa olamulira akudziko?

9 Akristu ali ndi thayo lakulemekeza olamulira ndi kuwagonjera​—ngakhale kuti ayenera kutero mwanjira yokhala ndi polekezera. (Machitidwe 5:29) Chifukwa ninji? Pa 1 Petro 2:14, 15, Petro akusonyeza zifukwa zitatu pamene akunena kuti akazembe ‘amatumidwa ndi [Mulungu] kukalanga ochita zoipa, koma kusimba ochita zabwino.’ Kuwopa chilango kuli chifukwa chabwino chomverera olamulira. Kukakhala kochititsa manyazi chotani nanga ngati mmodzi wa Mboni za Yehova alipiritsidwa faindi kapena kuponyedwa m’ndende pamlandu wakuvulaza munthu, kuba, kapena upandu wakutiwakuti! Talingalirani mmene ena angakhalire okondwa kufalitsa nkhani yoteroyo! Kumbali ina, pamene tikukulitsa dzina labwino la kumvera malamulo a boma, timatamandidwa ndi olamulira amaganizo abwino. Tingapatsidwedi ufulu wokulirapo wakuchita ntchito yathu yakulalikira mbiri yabwino. Ndipo ‘mwakuchita zabwino timatontholetsa chipulukiro cha anthu opusa.’ (1 Petro 2:15b) Ichi ndicho chifukwa chachiŵiri chomverera olamulira.​—Aroma 13:3.

10. Kodi nchifukwa chachikulu koposa chotani chimene tiyenera kumverera olamulira akudziko?

10 Koma chiripo chifukwa chokulirapo. Olamulirawo alipo mwachilolezo cha Yehova. Monga momwe Petro akunenera kuti, olamulira andale zadziko ‘atumizidwa’ ndi Yehova, ndipo ‘chifuniro cha Mulungu chitere’ kuti Akristu agonjere kwa iwo. (1 Petro 2:15a) Mofananamo, mtumwi Paulo akunena kuti: ‘Maulamuliro . . . amene alipo aikidwa ndi Mulungu.’ Chifukwa chake, chikumbumtima chathu chophunzitsidwa ndi Baibulo chimatisonkhezera kumvera olamulira. Ngati tikana kuwagonjera ‘tikaniza choikika ndi Mulungu.’ (Aroma 13:1, 2, 5) Kodi ndani pakati pathu amene angafune kutsutsana ndi makonzedwe a Mulungu? Ha, kumeneko kukakhala kuugwiritsira ntchito molakwa chotani nanga ufulu Wachikristu!

‘Kondani Abale’

11, 12. (a) Kodi ufulu wathu Wachikristu umadzetsa thayo lotani kulinga kwa okhulupirira anzathu? (b) Kodi ndani makamaka amene timafunikira kuwasonyeza chikondi chathu, ndipo chifukwa ninji?

11 Petro ananenanso kuti Mkristu ayenera ‘kukonda abale.’ (1 Petro 2:17) Ili ndithayo lina lobwera ndi ufulu Wachikristu. Ambirife ndife ziŵalo za mpingo. Ndithudi, tonsefe ndife mbali ya ubale wa mitundu yonse, kapena gulu, la abale. Kusonyeza chikondi kwa ameneŵa ndiko kugwiritsira ntchito mwanzeru ufulu wathu.​—Yohane 15:12, 13.

12 Mtumwi Paulo anatchula gulu la Akristu amene makamaka amafunikira chikondi chathu. Iye anati: ‘Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuŵerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.’ (Ahebri 13:17) Akulu ndiwo amene amatsogolera mumpingo. Nzowona, amuna ameneŵa saali angwiro. Komabe, amaikidwa mwachitsogozo cha Bungwe Lolamulira. Iwo amatsogolera mwakupereka chitsanzo ndi kulingalira ena, ndipo ali ndi thayo lakuyang’anira miyoyo yathu. Ha, ndithayo lolemera chotani nanga! (Ahebri 13:7) Mwachimwemwe, mipingo yambiri iri ndi mzimu wabwino wogwirizana, ndipo akulu amakondwa kugwira nawo ntchito. Kumakhala kovuta kwambiri pamene ena samafuna kugwirizanika. Inde, mkulu amachitabe ntchito yake, koma monga momwe Paulo ananenera, amaichita ‘mwachisoni.’ Ndithudi, sitimafuna kuchititsa akulu chisoni! Timafuna kuti apeze chimwemwe m’ntchito yawo kotero kuti atimangirire.

13. Kodi ndinjira zina zotani zimene tingagwirizanire ndi akulu?

13 Kodi ndinjira zina ziti zimene tingagwirizanire ndi akulu? Imodzi ya izo ndiyo kuthandiza kusamalira ndi kuyeretsa Nyumba Yaufumu. Ina ndiyo kugwirizana m’kuchezera odwala ndi kuthandiza osatha kudzichitira zinthu. Ndiponso, tingakalimire kukhalabe olimba kuuzimu, kotero kuti tisakhale chothodwetsa. Mbali yofunikira kwambiri kugwirizana ndiyo kusunga chiyero cha makhalidwe ndi cha uzimu wa mpingo, ponse paŵiri mwa mayendedwe athu ndi mwakuulula tchimo lalikulu limene tingalidziŵe.

14. Kodi tingasonyeze motani kugwirizanika pakachitidwe kachilango ka akulu?

14 Nthaŵi zina, akulu amatchotsa wochimwa wosalapa kotero kuti asunge mpingo kukhala woyera. (1 Akorinto 5:1-5) Kachitidweka kamatetezera mpingo. Ndipo kangathandizenso wochimwayo. Kaŵirikaŵiri, chilango choterocho chathandiza kubwezeretsa malingaliro abwino kwa wochimwayo. Komabe, bwanji ngati wochotsedwayo ndibwenzi lapamtima kapena wachibale? Tinene kuti ndiatate athu enieniwo kapena amayi kapena mwana. Kodi timalemekezabe kachitidwe ka akulu? Nzowona, zingakhale zovuta zimenezo. Koma kukakhala kugwiritsira ntchito ufulu wathu molakwa chotani nanga ngati tikaikira chosankha cha akulu ndi kumapitiriza kuyanjana mwauzimu ndi munthu amene wadzisonyeza kukhala wopereka chisonkhezero choipa mumpingo! (2 Yohane 10, 11) Anthu a Yehova pamodzi ayenera kuthokozedwa chifukwa cha kugwirizana kwawo m’nkhani zoterozo. Monga chotulukapo, gulu la Yehova limakhalabe losadetsedwa m’dziko lino lovunda.​—Yakobo 1:27.

15. Ngati munthu achita tchimo lalikulu, kodi ayenera kuchitanji mwamsanga?

15 Koma bwanji ngati ifeyo tachita tchimo lalikulu? Mfumu Davide analongosola za awo amene Yehova amawayanja pamene anati: ‘Adzakwera ndani m’phiri la Yehova? Nadzaima m’malo ake oyera ndani? Woyera m’manja, ndi wowona mtima, ndiye; iye amene sanakweza moyo wake kutsata zachabe, ndipo salumbira monyenga.’ (Salmo 24:3, 4) Ngati kaamba ka chifukwa chinachake ‘sitikhalanso oyera m’manja, ndi wowona mtima,’ tiyenera kuchitapo kanthu mofulumira. Moyo wathu wosatha umakhala paupandu.

16, 17. Kodi nchifukwa ninji munthu wokhala ndi liŵongo la tchimo lalikulu sayenera kuchita ndi nkhaniyo payekha?

16 Ena akhala ndi lingaliro lakubisa machimo aakulu, mwinamwake akuganiza kuti: ‘Ndinaulula kwa Yehova ndi kulapa. Motero nkuwaloŵetseramonji akulu?’ Wochimwayo angachite manyazi kapena kuwopa zimene akulu angachite. Komabe, ayenera kukumbukira kuti ngakhale kuti Yehova ndiye yekha angatiyeretse machimo athu, Iye wapatsa akulu thayo lakusungitsa chiyero cha mpingo. (Salmo 51:2) Iwo amachiritsa, ‘kukonzera oyera mtima.’ (Aefeso 4:12) Kusawafikira pamene tifunikira chithandizo chauzimu kufanana ndi kusapita kwa dokotala pamene tidwala.

17 Ena amene amayesa kuchita ndi nkhaniyo pawokha amapeza kuti pambuyo pa miyezi kapena zaka, chikumbumtima chawo chimawavutitsabe kwambiri. Choposapo kuipa, ena amene amabisa tchimo lalikulu amachimwanso kachiŵiri ndipo ngakhale kachitatu. Pomalizira pake pamene nkhaniyo idziŵika kwa akulu, amapeza kuti nditchimo lochitidwa mobwerezabereza. Nkwabwinopo chotani nanga kutsatira uphungu wa Yakobo! Iye analemba kuti: ‘Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu a mpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m’dzina la [Yehova, NW].’ (Yakobo 5:14) Fikani kwa akulu ikadalipo nthaŵi yakuchira. Ngati tiyembekeza mopambanitsa, tingakhale akhutu kumve panjira yathu yochimwa.​—Mlaliki 3:3; Yesaya 32:1, 2.

Mawonekedwe ndi Zosangulutsa

18, 19. Kodi nchifukwa ninji wansembe wina analankhula moyanja Mboni za Yehova?

18 Zaka zisanu zapitazo, wansembe wina Wachikatolika ku Italiya ananena moyanja Mboni za Yehova m’magazini a tchalitchi.a Iye anati: “Ine pandekha, ndimazikonda Mboni za Yehova; Ndikunena mosabisa. . . . Zimene ndimazidziŵa nzaulemu kwambiri, zofatsa . . . [ndipo] zokhutiritsa. Kodi tidzadziŵa liti kuti chowonadi chimafunikira mawonekedwe abwino? Kuti awo olengeza chowonadi samafunikira kukhala amitima iŵiri, onyenga, opanda chilongosoko, ovala mosadekha?”

19 Malinga ndi mawu ameneŵa, wansembeyo anasangalatsidwa ndi mmene Mbonizo zinavalira ndi mawonekedwe awo ndi mbali zina zakenso. Mwachidziŵikire, Mboni zimene adazidziwazo zidamvera uphungu woperekedwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kwa zaka zambiri. (Mateyu 24:45) Baibulo limanena kuti chovala cha mkazi chiyenera kukhala ‘choyenera, ndi chamanyazi.’ (1 Timoteo 2:9) M’nthaŵi zino zovuta, uphunguwo ngofunikira kwa amuna nawonso. Kodi sikwanzeru kuti oimira Ufumu wa Mulungu ayenera kukhala amawonekedwe oyenera kwa akunja?

20. Kodi nchifukwa ninji Mkristu nthaŵi zonse ayenera kukhala wosamala ponena za mavalidwe ake?

20 Ena angavomereze kuti pamisonkhano ndi muutumiki wakumunda, ayenera kukhala osamala ndi mavalidwe awo, koma angalingalire kuti miyezo ya Baibulo simagwira ntchito nthaŵi zina. Koma kodi timaleka nthaŵi zina kukhala oimira a Ufumu wa Mulungu? Nzowona kuti mikhalidwe imasiyana. Ngati tikugwira ntchito yomanga Nyumba Yaufumu, tidzavala mosiyana ndi mmene timavalira pamisonkhano mu Nyumba Yaufumu imodzimodziyo. Pamene tikusanguluka, mwachiwonekere sitidzavala motchena kwenikweni. Koma nthaŵi zonse pamene tiwonedwa ndi ena, mavalidwe athu ayenera kukhala oyenera ndi aulemu.

21, 22. Kodi takhala otetezeredwa motani ponena za kusanguluka kwaupandu, ndipo kodi tiyenera kuuwona motani uphungu wa zimenezo?

21 Mbali ina yofunikira chisamaliro ndiyo zosangulutsa. Anthu​—makamaka achichepere​—amafunikira kusanguluka. Sitchimo kapena kutaya nthaŵi kukhala ndi makonzedwe akusanguluka kwa banja. Ngakhale Yesu anauza ophunzira ake ‘kupumula kamphindi.’ (Marko 6:31) Koma samalani kuti kusanguluka sikululuza mkhalidwe wanu wauzimu. Tikukhala m’dziko limene zosangulutsa zimagogomezera chisembwere, chiwawa chachikulu, zowopsa, ndi kukhulupirira mizimu. (2 Timoteo 3:3; Chivumbulutso 22:15) Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amakhala maso ku maupandu oterowo ndipo nthaŵi zonse amatichenjeza. Kodi mumawona zikumbutso zimenezi kukhala zopondereza ufulu wanu? Kapena kodi mumayamikira kuti gulu la Yehova limakusamalani pomakukumbutsani nthaŵi zonse za maupandu amenewo?​—Salmo 19:7; 119:95.

22 Komabe musaiŵale kuti ngakhale kuti ufulu wathu umachokera kwa Yehova, thayo limakhala lathu la mmene timaugwiritsirira ntchito. Ngati tinyalanyaza uphungu wabwino ndi kupanga zosankha zolakwa, sitingaloze tchala munthu winawake. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Munthu aliyense wa ife adzadziŵerengera mlandu wake kwa Mulungu.”​—Aroma 14:12; Ahebri 4:13.

Sumikani Maganizo pa Ufulu wa Ana a Mulungu Ukudzawo

23. (a) Kodi ndimadalitso otani a ufulu amene tsopano tikusangalala nawo? (b) Kodi ndimadalitso otani amene tikuwayembekezera mwachidwi?

23 Ifetu ndife anthu odalitsidwa. Tinamasulidwa ku chipembedzo chonyenga ndi malaulo. Chifukwa cha nsembe ya dipo, tikhoza kumfikira Yehova ndi chikumbumtima choyera, omasuka m’njira yauzimu ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. Ndipo posachedwapa padzakhala ‘vumbulutso la ana a Mulungu.’ Pa Armagedo, abale a Yesu muulemerero wawo wakumwamba adzavumbulidwa kwa anthu monga owononga adani a Yehova. (Aroma 8:19; 2 Atesalonika 1:6-8; Chivumbulutso 2:26, 27) Pambuyo pake, ana a Mulungu ameneŵa adzavumbulidwa monga njira zimene anthu adzalandilira madalitso ochokera ku mpando wachifumu wa Mulungu. (Chivumbulutso 22:1-5) Pomalizira pake, vumbulutso la ana a Mulungu limeneli lidzatulukira m’kudalitsidwa kwa anthu okhulupirika ndi kulandira ufulu waulemerero wa ana a Mulungu. Kodi mumailakalaka nthaŵi imeneyo? Pamenepo gwiritsirani ntchito ufulu wanu Wachikristu mwanzeru. Khalani akapolo a Mulungu tsopano, ndipo mudzasangalala ndi ufulu wodabwitsa umenewo ku umuyaya wonse!

[Mawu a M’munsi]

a Pambuyo pake wansembeyo anachotsamo chithokozo chake, mwachiwonekere chifukwa chokakamizidwa ndi ena.

Mbali Yakupenda

◻ Kodi ndimotani mmene odzozedwa ndi nkhosa zina alemekezera Yehova?

◻ Kodi nchifukwa ninji Akristu ayenera kulemekeza olamulira akudziko?

◻ Kodi Mkristu angakhale wogwirizanika motani kwa akulu?

◻ Ponena za kuvala, kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova ziri zosiyana ndi ambiri m’dziko?

◻ Kodi tiyenera kupeŵanji ponena za kusanguluka?

[Chithunzi patsamba 17]

Akulu makamaka amafunikira chikondi ndi chigwirizano chathu

[Zithunzi patsamba 18]

Chovala cha Mkristu chiyenera kukhala choyenera, ndi chaulemu panthaŵi iriyonse

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena