Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Dalirani Yehova
    Nsanja ya Olonda—2003 | September 1
    • N’chifukwa Chiyani Yehova Amalola Kuti Anthu Azivutika?

      10, 11. (a) Malinga ndi Aroma 8:19-22, n’chiyani chinachitikira “cholengedwa chonse”? (b) Kodi tingadziŵe bwanji amene anagonjetsera cholengedwa ku utsiru?

      10 Ndime ina ya kalata imene Paulo analembera Aroma imatithandiza kumvetsa nkhani yofunika kwambiri imeneyi. Iye analemba kuti: “Chiyembekezetso cha cholengedwa chilindira vumbulutso la ana a Mulungu. Pakuti cholengedwacho chagonjetsedwa kuutsiru, chosafuna mwini, koma chifukwa cha iye amene anachigonjetsa, ndi chiyembekezo kuti cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu. Pakuti tidziŵa kuti cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zowawa pamodzi kufikira tsopano.”​—Aroma 8:19-22.

      11 Kuti timvetse mfundo ya mavesi ameneŵa, choyamba tifunika kuyankha mafunso ena ofunika kwambiri. Mwachitsanzo, Ndani anagonjetsera cholengedwa ku utsiru? Ena amanena kuti ndi Satana ndipo ena amati ndi Adamu. Koma Satana ndi Adamu sakanachita zimenezo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti amene wagonjetsera cholengedwa ku utsiru wachita zimenezo “ndi chiyembekezo.” Inde, amapereka chiyembekezo chakuti m’kupita kwanthaŵi anthu okhulupirika ‘adzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi.’ Adamu kapena Satana sakanapereka chiyembekezo choterocho. Yehova yekha ndi amene akanatha kutero. Motero, n’zoonekeratu kuti ndi Yehova amene anagonjetsera cholengedwa ku utsiru.

      12. Kodi pali maganizo osiyana ati pankhani yakuti “cholengedwa chonse” n’chiyani, ndipo tingayankhe bwanji funso limeneli?

      12 Koma kodi “cholengedwa chonse” chimene achitchula m’ndime imeneyi n’chiyani? Ena amanena kuti “cholengedwa chonse” chimenechi ndi chinthu chilichonse chimene chili m’dzikoli, kuphatikizapo nyama ndi zomera. Koma kodi nyama ndi zomera zimayembekezera kuloŵa “ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu”? Ayi. (2 Petro 2:12) Motero, “cholengedwa chonse” chimene akunena apa ndi anthu okha basi. Chimenechi ndicho cholengedwa chimene chakhudzidwa ndi uchimo ndi imfa chifukwa cha kupanduka kumene kunachitika mu Edene ndipo n’chimene chimafuna kwambiri chiyembekezo.​—Aroma 5:12.

      13. N’chiyani chachitikira anthu chifukwa cha kupanduka kumene kunachitika mu Edene?

      13 Kodi n’chiyani kwenikweni chachitikira anthu chifukwa cha kupanduka kumeneku? Paulo anafotokoza zimene zachitika chifukwa cha kupandukako ndi mawu amodzi akuti: utsiru.a Malinga ndi buku lina laumboni, liwu limene analimasulira kuti utsiru limatanthauza “kupanda pake kwa chinthu chimene sichikugwira ntchito imene anachikonzera kuti chizigwira.” Anthu anawalenga kuti akhale ndi moyo kosatha, kuchitira zinthu limodzi monga banja langwiro, logwirizana, posamalira dziko la paradaiso. Koma m’malomwake, anthu amangokhala ndi moyo kwa nthaŵi yochepa ndipo moyo wake umakhala wopweteka ndiponso nthaŵi zambiri wokhumudwitsa. Monga mmene Yobu ananenera, “munthu wobadwa ndi mkazi ngwa masiku oŵerengeka, nakhuta mavuto.” (Yobu 14:1) Kupanda pakedi kwenikweni!

      14, 15. (a) Kodi tikupeza umboni wotani woti Yehova anaweruza anthu mwachilungamo? (b) N’chifukwa chiyani Paulo ananena kuti cholengedwa chinagonjetsedwa ku utsiru “chosafuna mwini”?

      14 Tsopano tikufika pa funso lofunika kwambiri lakuti: N’chifukwa chiyani “Woweruza wa dziko lonse lapansi” anagonjetsera anthu ku moyo wopweteka, wokhumudwitsa woterewu? (Genesis 18:25) Kodi anasonyeza chilungamo pochita zimenezi? Chabwino, takumbukirani zimene makolo athu oyambawo anachita. Popandukira Mulungu, iwo anakhala kumbali ya Satana yemwe anakayikira kwambiri zoti Yehova ndiye woyenera kulamulira. Mwa zimene anachita, analimbikitsa mfundo yakuti anthu zingawayendere bwino popanda Yehova, koma kuti azidzilamulira okha motsogoleredwa ndi cholengedwa chauzimu chopanduka. Yehova poweruza opandukawo, kwenikweni anawapatsa zimene iwo ankafuna. Analola kuti anthu adzilamulire okha motsogozedwa ndi Satana. Malinga ndi mmene zinalilimu, kodi pakanakhalanso chigamulo china cholungama kwambiri kuposa kuwagonjetsera anthu ku utsiru koma ndi chiyembekezo?

      15 Komabe, izi zinachitika ngakhale kuti cholengedwa ‘sichinafune’ kuti zitero. Timabadwa tili akapolo a uchimo ndi chivundi popanda kuchitira mwina. Koma Yehova mwachifundo chake analola kuti Adamu ndi Hava akhale ndi moyo ndi kubereka ana. Ngakhale kuti mbadwa zawofe tagonjetsedwa ku utsiru wa uchimo ndi imfa, tili ndi mwayi wochita zimene Adamu ndi Hava analephera kuchita. Tingamvere Yehova ndi kudziŵa kuti ulamuliro wake ndi wolungama ndiponso wangwiro, pamene ulamuliro wa anthu osadalira Yehova umangobweretsa zopweteka, zokhumudwitsa ndi zinthu zopanda pake. (Yeremiya 10:23; Chivumbulutso 4:11) Ndipo zochita za Satana zikungopangitsa kuti zinthu ziipireipire. Zimene zachitikira anthu zikutsimikizira mfundo zoona zimenezi.​—Mlaliki 8:9.

      16. (a) N’chifukwa chiyani tingatsimikize kuti si Yehova amene amachititsa kuvutika kumene tikukuona m’dzikoli? (b) Kodi Yehova wapereka chiyembekezo chotani mwachikondi kwa anthu okhulupirika?

      16 Mwachionekere, Yehova anali ndi zifukwa zolungama zimene anagonjetsera anthu ku utsiru. Koma kodi zimenezo zikutanthauza kuti Yehova ndi amene wachititsa kuti anthufe tizivutika masiku ano? Taganizirani woweruza amene wapereka chigamulo cholungama kwa munthu wolakwa. Wolakwayo angavutike ndithu pamene akugwira ukaidi wake, koma kodi zingakhale zoona kunena kuti woweruzayo ndi amene wachititsa kuti iye avutike? Ayi. Ndiponso, si Yehova amene amachititsa zoipa zimene zikuchitikazi. Lemba la Yakobo 1:13 limati: “Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu.” Ndiponso tiyenera kukumbukira kuti Yehova anapereka chiweruzo pamodzi “ndi chiyembekezo.” Iye mwachikondi wakonza zoti mbadwa zokhulupirika za Adamu ndi Hava zidzaone kutha kwa utsiru ndi kusangalala ndi “ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.” Kwa nthaŵi yomka muyaya, anthu okhulupirika sadzakhala ndi nkhaŵa yakuti cholengedwa chonse chingadzabwererenso ku utsiru wopweteka. Kuchita zinthu molungama kwa Yehova kudzatsimikizira kuti iye ndiye woyenera kulamulira mpaka kalekale.​—Yesaya 25:8.

  • Dalirani Yehova
    Nsanja ya Olonda—2003 | September 1
    • a Liwu la Chigiriki limene Paulo analigwiritsa ntchito limene lamasuliridwa kuti “utsiru” ndi limenenso analigwiritsa ntchito m’Baibulo la Septuagint ya Chigiriki pomasulira mawu amene Solomo anawagwiritsa ntchito mobwerezabwereza m’buku la Mlaliki, monga pa mawu akuti ‘zonse ndi chabe.’​—Mlaliki 1:2, 14; 2:11, 17; 3:19; 12:8.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena