Koposa Mdani Wankhanza
KUPWETEKA kosatha kungawononge miyoyo ya anthu. Kumawabera mtendere, chisangalalo, ndi ndalama, kukumapangitsa moyo kukhala wovuta kwambiri kwakuti ena amafunafuna mpumulo kupyolera mwa kudzipha. Wodzipereka pa ntchito zachipatala Albert Schweitzer anati: “Kupweteka ndiko mbuye woipitsitsa wa mtundu wa anthu kuposa imfa yeniyeniyo.”
Kwenikweni mamiliyoni mazana amavutika moipitsitsa. ‘Tikanalenjekeka mumlengalenga mopanda malekezero pamwamba pa phompho limene munamveka dziko lapansi lomazungulira,’ dokotala wa opaleshoni wa ku France anatero, ‘tikanamva namalowe wa mbumo wa zoŵaŵa womveka monga liwu limodzi wochitidwa ndi mtundu wa anthu wovutika.’
Ndithudi, zimene mtumwi Wachikristu Paulo analemba zaka zoposa 1,900 zapitazo zakhaladi zamphamvu kwambiri lerolino: “Cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zoŵaŵa pamodzi kufikira tsopano.”—Aroma 8:22.
Mavuto Aakulu Athanzi
Mmodzi mwa anthu 8 a ku America amamva kupweteka kwakukulu kwa osteoarthritis, mtundu wa kutupa mu mfundo wodziŵika koposa. Anthu ambiridi amamva kupweteka kwa msana kwakukulu. Ena afunikira kupirira ndi ziyambukiro zopweteka za kansa ndi nthenda ya mtima.
Mamiliyoni owonjezereka amavutika ndi kupweteka kwa mutu kwakukulu kwambiri, m’mano, m’khutu, mafundo, ndi nthenda zina ndi zopweteka zambiri. Mposadabwitsa kuti m’chaka chaposachedwapa, anthu a ku America anathera $2,100,000,000 pa mankhwala oletsa kupweteka okha osafuna chilangizo cha dokotala, ndipo kupweteka kumeneko kumatchedwa “mliri wobisika wa America.”
John J. Bonica, mwinamwake amene ali katswiri wamkulu pa nkhani za kupweteka, anati: “Polingalira za madola ndi masenti, ndi polingalira za mavuto a munthu, kupweteka kosatha ndiko kodetsa nkhaŵa kuposa mavuto ena onse azathanzi ngati ataikidwa pamodzi.”
Moyo Wopanda Zoŵaŵitsa?
Poyang’anizana ndi zoipa zenizeni zotero, kungaonekere ngati kuti kuperekera lingaliro la kuthekera kwa moyo wopanda zoŵaŵitsa ndiko kufulumira. Chifukwa chake, zimene Baibulo limanena zingakhale ngati zapatali, ndiko kuti: “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; . . . sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa.”—Chivumbulutso 21:4.
Chikhalirechobe, kuthekera kwa moyo wopanda choŵaŵitsa sikuli kwapatali. Koma taganizani kwakanthaŵi. Kodi lembalo limatanthauzanji kwenikweni? Lerolino pali anthu amene samamva kupweteka. Amabadwa alibe. Kodi tiyenera kuwasirira? Katswiri wa kapangidwe kathupi Allan Basbaum anati: “Kusamva kupweteka kulikonse nkwangozi.”
Ngati munali wosakhoza kumva kupweteka, mwinamwake simukanadziŵa kuti muli ndi thudza kufikira pamene likanakhala chilonda chonyeka moipa. Malinga ndi kunena kwa lipoti la nyuzi, makolo a msungwana wina amene sanali kumva ululu “nthaŵi zina anali kumva kununkha kwa thupi lomapsa ndi kumpeza ataŵeramira pa chitofu mosatekeseka.” Motero, kupweteka kuli koposa mdani wankhanza. Kungakhalenso dalitso.
Nangano, bwanji za lonjezo la Baibulo lakuti: “Sipadzakhalanso . . . chowawitsa”? Kodi limeneli lili lonjezo limene tingafunedi kuti likwaniritsidwe?
Moyo Wopanda Misozi?
Onani kuti mawu a nkhani ya vesili akutinso: “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo.” (Chivumbulutso 21:4) Zimenezi zili ndi tanthauzo, popeza kuti misozi n’njofunika. Imatitetezera, monga momwe mkhalidwe wa kupweteka umachitira.
Misozi imapangitsa maso athu kukhala ndi madzi ndi kuletsa kukhulana kwa diso ndi chikope. Imatsukanso zinthu zosafunika m’maso mwathu. Ndiponso, ili ndi mankhwala opha tizilombo otchedwa lysozyme, amene amayeretsa maso ndi kuletsa matenda. Motero kukhoza kukhetsa misozi kuli mbali yapadera ya matupi athu olinganizidwa modabwitsa, monga momwe zilili ndi mkhalidwe wathu wa kumva kupweteka.—Salmo 139:14.
Komabe, misozi ili yogwirizanitsidwanso kwambiri ndi chisoni, kupweteka kwa mtima, ndi nsautso. “Ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse,” anadandaula motero Mfumu Davide wa nthaŵi za Baibulo. “Mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.” (Salmo 6:6) Ngakhale Yesu “analira” pa imfa ya bwenzi. (Yohane 11:35) Poyambirira Mulungu sanalinganize kuti anthu adzigwetsa misozi ya chisoni yotero. Uchimo wa munthu woyamba, Adamu, ndiwo unachititsa kupanda ungwiro, mkhalidwe wa kufa wa banja la umunthu. (Aroma 5:12) Motero, ili misozi imene imagwa chifukwa cha kupanda ungwiro kwathu, mkhalidwe wakufa imene sidzakhalakonso.
Popeza kuti Baibulo limatchula za mtundu wina wa misozi umene udzachotsedwa, kodi ndimotani mmene lonjezo lakuti zoŵaŵitsa sizidzakhalakonso lidzakwaniritsidwira? Kodi anthu, pa nthaŵi ina, sadzavutika ndi zoŵaŵitsa zimene zimachititsa chisoni ndi kulira?