Choikidwiratu
Tanthauzo: Chochitika chosapeŵeka ndipo kaŵirikaŵiri chatsoka. Choikidwiratu ndiko kukhulupirira kuti zochitika zonse zimatsimikiziridwa ndi chifuniro cha Mulungu kapena ndi mphamvu ina yaikulu kwambiri koposa munthu, kuti chochitika chiri chonse chiyenera kuchitika monga momwe chimachitikira chifukwa chakuti chinalinganizidwiratu. Sindicho liwu kapena chiphunzitso cha Baibulo.
Kodi munthu aliyense ali ndi “nthaŵi yakufa” yoikidwiratu?
Chikhulupiriro chimenechi chinali chofala pakati pa Agiriki ndi Aroma. Mogwirizana ndi kunena kwa nthanthi yachikunja ya Agiriki, Olinganiza zoikidwiratu anali milungu itatu imene inapota ulusi wamoyo, kutsimikiza kutalika kwake, ndi kuudula.
Mlaliki 3:1, 2 amanena za “mphindi yakumwalira.” Koma, kusonyeza kuti imeneyi siri mphindi yoikika yoikidwiratu yamunthuyo, Mlaliki 7:17 amapereka uphungu wakuti: “Usapambanitse kuipa, ngakhale kupusa, uferenji nthaŵi yako isanafike?” Miyambo 10:27 imati: “Kuwopa Yehova kutanimphitsa masiku; koma zaka za oipa zidzafinimpha.” Ndipo Salmo 55:23 limawonjezera kuti: “Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku awo sadzafikira nusu.” Pamenepa, kodi Mlaliki 3:1, 2 amatanthauza chiyani? Akungofotokoza kuchitika kosalekeza kwa kukhala wamoyo ndi imfa m’dongosolo lopanda ungwiro lino lazinthu. Pali nthaŵi imene anthu amabadwa ndi nthaŵi imene amafa—kaŵirikaŵiri pamsinkhu wosaposa zaka 70 kapena 80, koma nthaŵi zina mofulumilirapo ndipo nthaŵi zina mochedwerapo.—Sal. 90:10; wonaninso Mlaliki 9:11.
Ngati nyengo yamunthu aliyense ndi mmene adzafera zinaikidwiratu kale panthaŵi yakubadwa kapena poyambirira, sipakanakhala kufunika kwa kupeŵa mikhalidwe yangozi kapena kusamalira thanzi lako, ndipo kulabadira machenjezo achitetezo sikukanasuntha ziŵerengero za imfa. Koma kodi mukhulupirira kuti bwalo lankhondo mkati mwa nkhondo angakhale malo otetezereka mofanana ndi nyumba yamunthu yokhala kutali ndi malo ankhondowo? Kodi inu mumasamalira thanzi lanu kapena kutengera ana anu kwa dotokola? Kodi nchifukwa ninji osuta fodya amafa ali ocheperapo ndi zaka zitatu kapena zinayi pa avereji, kuposa osasuta fodya? Kodi nchifukwa ninji pali ngozi zakupha zocheperapo pamene apaulendo m’galimoto amavala malamba apampando ndi pamene oyendetsa magalimoto amamvera malamulo apansewu? Mwachiwonekere, kulabadira kuli kopindulitsa.
Kodi kanthu kalikonse kamene kamachitika ndiko “chifuniro cha Mulungu”?
2 Pet. 3:9: “Ambuye . . . aleza mtima kwa inu osafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.” (Koma sionse amene amalabadira kuleza mtima kwake. Mwachiwonekere, sichiri ‘chifuniro cha Mulungu’ pamene ena alephera kulapa. Yerekezerani ndi Chivumbulutso 9:20, 21.)
Yer. 7:23-26: “Chinthu ichi ndinawauza [Israyeli] kuti, Mverani mawu anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga; nimuyende m’njira yonse imene ndakuuzani inu, kuti chikukomereni. Koma sanamvera . . . ndatumiza kwa inu atumiki anga onse, aneneri, tsiku ndi tsiku, kuuka mamaŵa ndi kuwatumiza iwo; koma sanandimvera Ine, sanatchera khutu lawo, koma anaumitsa khosi lawo.” (Mwachiwonekere, kuipa kochitika mu Israyeli sikunali ‘chifuniro cha Mulungu.’)
Marko 3:35: “Aliyense achita chifuniro cha Mulungu, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo, ndi amayi.” (Ngati chirichonse chimene munthu anachita chinali “chifuniro cha Mulungu,” pamenepo aliyense akanakhala ndi unansi ndi Yesu umene anaulongosola panopa. Koma iye anati kwa ena: “Muli ochokera mwa atate wanu Mdyerekezi.”—Yoh. 8:44.)
Kodi nchiyani chimene chimachititsa zinthu zambiri zowonekera kukhala zodabwitsa zimene zimachitika?
Mlal. 9:11: “Nthaŵi ndi chochitika chosawonedweratu [“ngozi,” NE, RS] zimabwerera iwo onse.” (Motero, sichifukwa chakulinganizidwiratu kulikonse kwa moyo wamunthu, koma chifukwa cha ngozi iye angakhale mkhole wamikhalidwe yatsoka.)
Kodi anthu ali ndi thayo la mavuto ambiriwo amene iwo eni amavutika nawo ndi a anthu ena?
Aroma 5:12: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse chifukwa chakuti onse anachimwa.” (Kupanda ungwiro, kuphatikizapo zikhoterero zakuchita cholakwa, ndizo choloŵa cha ife tonse kuchokera kwa Adamu.)
Mlal. 8:9: “Wina apweteka mnzake pomlamulira.”
Miy. 13:1: “Mwana wanzeru amamvera mwambo wa atate; koma wonyoza samvera chidzudzulo.” (Zimene makolo amachita ziri ndi chiyambukiro chachikulu pa miyoyo ya ana awo.)
Agal. 6:7: “Musanyengedwe, Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.” (Ndiponso Miyambo 11:17; 23:29, 30; 29:15; 1 Akorinto 6:18)
Kodi pali mphamvu zoposa za munthu zimene zimachititsanso tsoka kwa anthu?
Chiv. 12:12: “Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.” (Ndiponso Machitidwe 10:38)
Kodi Mulungu amadziŵiratu ndi kulinganiziratu kanthu kali konse?
Yes. 46:9, 10: “Ndine Mulungu, ndipo palibenso wina; ine ndine Yehova ndipo palibenso wina wofana ndi ine; ndilalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthaŵi zakale ndinena zinthu zimene zisanachitidwe, ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse.” (Amaulula chifuno chake, amalinganiziratu zinthu mogwirizana ndi kukwaniritsidwa kwake, ndipo ali ndi mphamvu zonse kutsimikizira kuti zimenezi zidzakwaniritsidwa.)
Yes. 11:1-3: “Padzatuluka mphukira patsinde la Jese, ndi panthambi yotuluka m’mizu yake idzabala zipatso; [Yesu anabadwa m’mzera wa Jese.] ndipo mzimu wa Yehova udzambalira iye, . . . ndipo adzakondwera nako kumuwopa Yehova.” (Yehova akananeneratu mwachidaliro zimenezi ponena za Mwana wake chifukwa chakuti Iye anawona mkhalidwe wake ndi kudzisungira kwake m’miyamba kuyambira chiyambi cha chilengedwe.) (Ponena za kukhalapo kwa Yesu asanakhale munthu wonani tsamba 431, pamutu wakuti “Yesu Kristu.”)
Deut. 31:20, 21: “Pakuti nditakaloŵetsa awa [mtundu wa Israyeli] kudziko limene ndinalumbirira makolo awo, moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ndipo atadya nakhuta, nanenepa, pamenepo adzatembenukira milungu ina, ndi kuitumikira, ndi kundipeputsa ine, ndi kuthyola chipangano changa. Ndipo kudzakhala, zitaŵafikira zoipa ndi zovuta zambiri, nyimbo iyi [yofotokoza mmene adachitira chifukwa cha kulephera kuyamikira chiyanjo cha Mulungu] idzachita mboni pamaso pawo; . . . popeza ndidziŵa zolingalira zawo azichita lerolino, ndisanaŵaloŵetse m’dziko limene ndinalumbira.” (Tawonani kuti mphamvu ya Mulungu ya kuzindikira chotulukapo cha njira yawo siinatanthauze kuti anaichititsa kapena kuti ndizo zimene anafuna kuti iwo achite, koma pamaziko a zimene iwo anali kuchita anali wokhoza kuwoneratu chotulukapo. Mofananamo, pamaziko a zimene zimawonedwa, wodziŵa nyengo anganeneretu nyengo molondola kwambiri, koma iye samaichititsa kapena kwenikweni kuifuna.)
Kodi mphamvu ya Mulungu ya kudziŵiratu ndi kulinganiziratu zochitika imatsimikizira kuti amachita izi pa zochitika zonse za zolengedwa zake?
Chiv. 22:17: “Wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna atenge madzi a moyo kwaulere.” (Chosankha sichiri choikidwiratu; chimasiyidwira kwa munthu aliyense payekha.)
Aroma 2:4, 5: “Kapena upeputsa kodi kulemera kwa ubwino wake, ndi chilekerero ndi chipiriro chake, wosadziŵa kuti ubwino wa Mulungu ukubwezera kuti ulape? Koma molingana ndi kuuma kwako ndi mtima wako wosalapa, uli kudziunjikira wekha mkwiyo padzuŵa lamkwiyo ndi la kuvumbulutsa kuŵeruza kolungama kwa Mulungu.” (Palibe chikakamizo pa anthu alionse paokha chakuti alondole njira yolongosoledwayo. Koma pali kudziyankhira pa zimene munthuyo achita.)
Zef. 2:3: “Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko . . . funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku lamkwiyo wa Yehova.” (Kodi Mulungu wachilungamo ndi wachikondi akalimbikitsa anthu kuchita chimene chiri cholungama, moyembekezera mphotho, ngati iye anadziŵa kuti anaikidwiratu ku kusapeza chipambano?)
Chitsanzo: Mwini rediyo angamvetsere nyuzi za padziko lonse. Koma chenicheni chakuti iye angakhoze kumvetsera ku siteshoni iriyonse sichimatanthauza kuti iye amatero. Choyamba ayenera kutsegula rediyo ndiyeno kusankha siteshoni. Mofananamo, Yehova ali ndi mphamvu ya kudziŵiratu zochitika, koma Baibulo limasonyeza kuti amachita mosankha ndi luntha pogwiritsira ntchito mphamvu, molemekeza ufulu wa kudzisankhira umene iye anapatsa cholengedwa chake chaumunthu.—Yerekezerani ndi Genesis 22:12, 18:20, 21.
Pamene Mulungu analenga Adamu, kodi anadziŵa kuti Adamu akachimwa?
Nazi zimene Mulungu ananena pamaso pa Adamu ndi Hava: “Mubalane, muchuluke, muzadze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m’nyanja, ndi pambalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse za kukwaŵa padziko lapansi.” “Ndipo Yehova Mulungu anauza munthuyo, nati, Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithudi.” (Gen. 1:28; 2:16, 17) Kodi inu mukanalimbikitsa ana anu kuyamba ntchito yokhala ndi mtsogolo mwabwino, mukumadziŵa pachiyambi pomwe kuti idzalephera? Kodi mukawachenjeza za chivulazo, pamene mukudziŵa kuti munali mutalinganiziratu kanthu kalikonse kuti iwo motsimikizirika akamva chisoni? Pamenepa, kodi nkwanzeru kuti ndizo zimene Mulungu anachita?
Mat. 7:11: “Ngati inu, muli oipa [kapena, “oipa monga momwe muliri,” NE], mudziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wakumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha iye?”
Ngati Mulungu analinganiziratu ndipo anadziŵiratu tchimo la Adamu ndi zonse zimene zikatulukapo, kukatanthauza kuti mwa kulenga Adamu, Mulungu mwadala anayambitsa kuipa konse kochitidwa m’mbiri ya anthu. Iye akakhala Magwero a nkhondo zonse, upandu, chisembwere, chitsenderezo, mabodza, chinyengo, ndi nthenda. Koma Baibulo limanena momvekera bwino kuti: “Inu sindinu Mulungu wakukondwera nacho choipa.” (Sal. 5:4) “Moyo wake umuda woipa.” (Sal. 11:5) ‘Mulungu . . . sanganame.’ (Tito 1:2) “Adzawombola [Iye amene anasankhidwa ndi Mulungu monga Mfumu Yaumesiya] moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wamtengo pamaso pake.” (Sal. 72:14) “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yoh. 4:8) “Ndiye wakukonda chilungamo ndi chiweruzo.”—Sal. 33:5.
Kodi Mulungu analinganiziratu Yakobo ndi Esau?
Gen. 25:23: “Yehova ndipo anati kwa iye [Rebeka], mitundu iŵiri iri m’mimba mwako, magulu aŵiri a anthu adzatuluka m’mimba mwako; gulu lina lidzapambana mphamvu ndi linzake; wamkulu [Esau] adzakhala kapolo wa wamng’ono [Yakobo].” (Yehova anali wokhoza kuŵerenga chitsanzo cha majini a amapasa osabadwawo. Iye angakhale atalingalira zimenezi pamene anawoneratu mikhalidwe imene aliyense wa anyamatawo akakulitsa ndi kuneneratu chotulukapo. [Sal. 139:16] Koma panopa palibe chisonyezero chakuti analinganiziratu zoikidwiratu zawo zamuyaya kapena kuti analinganiziratu mmene chochitika chirichonse m’miyoyo yawo chikakhalira.)
Kodi Yudase Isikariote analinganizidwiratu kupereka Yesu?
Sal. 41:9: “Bwenzi langa lenileni, amene ndamkhulupirira, ndi amene adadyako mkate wanga, anandikwezera chidendene chake.” (Tawonani kuti ulosiwo sunalankhule mwachindunji amene akakhala tsamwali ameneyo wa Yesu. Yehova anadziŵa kuti Mdyerekezi anagwiritsira ntchito phungu wa Davide Ahitofeli kumpereka, ndipo Iye anachititsa zimenezo kulembedwa chifukwa chakuti zinasonyeza mmene Mdyerekezi anagwirira ntchito ndi zimene akachita mtsogolo. Sanali Mulungu koma ‘Mdyerekezi . . . amene anaika mu mtima wa Yudase Isikariote, mwana wa Simoni, kumpereka [Yesu].’ [Yoh. 13:2] Mmalo mwa kukaniza, Yudase anagonjera chisonkhezero chauchiŵanda chimenecho.)
Yoh. 6:64: “Pakuti Yesu anadziŵa poyamba . . . amene adzampereka.” (Osati kuyambira pa chiyambi cha chilengedwe, kapena kuyambira nthaŵi ya kubadwa kwa Yudase, koma “kuyambira pachiyambi” cha kuchita kwake mwachiŵembu. Yerekezerani ndi Genesis 1:1; Luka 1:2 ndi 1 Yohane 2:7, 13, mu lirilonse la malembaŵa “pachiyambi” wagwiritsiridwa ntchito m’lingaliro lokhala ndi polekezera. Wonaninso Yohane 12:4-6.)
Kodi mtumwi Paulo samalankhula za Akristu kukhala ‘olinganizidwiratu’?
Aroma 8:28, 29: “Tidziŵa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake. Chifukwa kuti iwo amene iye anawadziŵiratu, iwoŵa anaŵalamuliratu [‘kuwalinganiziratu,’ KJ] afanizidwe ndi chifaniziro cha Mwana wake kuti iye akhale mwana woyamba wa abale ambiri.” (Ndiponso Aefeso 1:5, 11) Komabe, kwa anthu amodzimodzi amenewa, 2 Petro 1:10 amati: “Wonjezani kuchita changu kukhazikitsa maitanidwe ndi masankhulidwe anu; pakuti mukachita izi simudzakhumudwa nthaŵi yonse.” (Ngati anthu anaikidwiratu ku chipulumutso, sikukanatheka kwa iwo kulephera, mosasamala kanthu za chimene anachita. Popeza kuyesayesa kuli kofunika kwa anthu, kuyenera kukhala kagulu kamene kali koikidwiratu. Mulungu analinganiza kuti kagulu kathunthu kakachita mogwirizana ndi chitsanzo choperekedwa ndi Yesu Kristu. Komabe, awo osankhidwa ndi Mulungu kukhala mbali ya kaguluko, ayenera kutsimikizira kukhala okhulupirira ngati ati apezedi mphotho yoikidwa pamaso pawo.)
Aef. 1:4, 5: “Monga anatisankha ife mwa iye [Yesu Kristu] lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima ndi opanda chirema pamaso pake m’chikondi. Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana a iye yekha mwa Yesu Kristu, monga umo kunakomera chifuniro chake.” (Nkokondweretsa kuwona kuti, pa Luka 11:50, 51 Yesu akugwirizanitsa “kukhazikika kwa dziko” ndi nthaŵi ya Abele. Abele ndiye munthu woyamba amene anapitirizabe kukhala ndi chiyanjo cha Mulungu nthaŵi yonse ya moyo wake. Chotero, panali pambuyo pa chipanduko mu Edene, koma Abele asanakhaliridwe pakati pamene Mulungu anapanga chifuno chake cha kutulutsa “mbewu” kupyolera mwa imene chilanditso chikaperekedwa. [Gen. 3:15] Mulungu analinganiza kuti limodzi ndi Mbewu yaikuluyo, Yesu Kristu pakakhala kagulu ka otsatira ake okhulupirika amene akakhala ndi mbali limodzi naye m’boma latsopano lolamulira dziko lapansi, Ufumu Waumesiya.)
Kodi nyenyezi ndi maplaneti zimasonkhezera zochitika m’miyoyo yathu kapena kupereka zizindikiro zimene tiyenera kupenda popanga zosankha?
Kodi ndiati amene ali magwero a kupenda nyenyezi?
“Kupenda nyenyezi kwa maiko Akumadzulo kungalondoledwe m’mbuyo mwachindunji kukafika kunthanthi ndi zizoloŵezi za Akaladayo a m’ma 2000 B.C.”—The Encyclopedia Americana (1977), Vol. 2, p. 557.
“Kupenda nyenyezi kunali kozikidwa pamalingaliro aŵiri Achibabulo: zakuthambo, ndi kulingaliridwa kukhala milungu kwa zakuthambo. . . . Ababulo analingalira kuti maplaneti anali ndi chisonkhezero chimene munthu akayembekezera kwa milungu yawo yosiyanasiyana.”—Great Cities of the Ancient World (New York, 1972), L. Sprague de Camp, p. 150.
“M’Babulo kudzanso m’Suriya monga mphukira yachindunji ya miyambo Yachibabulo . . . kupenda nyenyezi kumapezeka m’mazoma amwambo monga imodzi ya njira ziŵiri zazikulu zogwiritsidwa ntchito ndi ansembe . . . zotsimikizirira chifuniro ndi cholinga cha milungu, ina ikumakhala kupendedwa kwa chiŵindi cha nyama yoperekedwa nsembe. . . . Mayendedwe a dzuŵa, mwezi ndi maplaneti asanu zinaŵerengedwa kukhala zoimira ntchito ya milungu isanu yonenedwayo, limodzi ndi mulungu mwezi Sin ndi mulungu dzuŵa Shamash, pokonzekera kuwonekera padziko lapansi.”—Encyclopædia Britannica (1911), Vol. II, p. 796.
Kodi nchiyani chimene chiri lingaliro la Mlengi wa anthu kulinga ku chizoloŵezi chimenechi?
Deut. 18:10-12: “Asapezeke mwa inu munthu . . . wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga. Popeza yense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye.”
Kwa Ababulo iye anati: “Openda nyenyezi anu, oyang’anitsitsa nyenyezi anu amene amaneneratu mtsogolo mwanu mwezi ndi mwezi, achitetu khama, nakupulumutseni! Koma tawonani, iwo amuka mofanana ndi mungu . . . Chotero kwa amatsenga anu ochulukawo mwatsatsa nawo malonda moyo wanu wonse: akhumudwa, yense panjira yakale, ndipo palibe mmodzi wakukupulumutsani.”—Yes. 47:13-15, NE.