Yehova ndi Kristu Olankhula Opambana
‘[Mfumu, “NW”] Ambuye Yehova sadzachita kanthu osaulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.’—AMOSI 3:7.
1. Kodi ndinjira zotani za kulankhulana zimene zimagwiritsiridwa ntchito lerolino?
LEROLINO kulankhulana kuli bizinesi ya madola mamiliyoni ambirimbiri. Mabuku onse omwe amafalitsidwa, manyuzipepala ndi magazini onse amene amasindikizidwa mosalekeza, maprogramu onse a wailesi yamawu ndi wailesi yakanema amene amaulutsidwa, limodzinso ndi zithunzithunzi zonse zoyenda ndi maseŵera apapulatifomu, ziri zoyesayesa za kulankhulana. Zimenezo ziri zowona ponena za makalata onse olembedwa ndi kutumizidwa limodzinso ndi matelefoni onse. Zonsezo ndi zoyesayesa za kulankhulana.
2. Kodi ndizitsanzo zina zotani za kupita patsogolo kumene anthu akupanga m’luso la kulankhulana?
2 Kupita patsogolo kumene anthu akupanga m’mbali ya maluso akulankhulana kuli kodabwitsa. Mwachitsanzo, nsambo za fiber-optic, zomwe ziri zabwinopo kuposa nsambo za mkuwa, zikhoza kunyamula makambitsirano apatelefoni okwanira zikwi makumi ambirimbiri panthaŵi imodzi. Ndiyeno pali masetilaiti olankhulirana, omwe amazungulira dziko lapansi m’thambo ndipo ali ndi ziŵiya zoperekera zizindikiro za telefoni, telegraph, wailesi yamawu, ndi wailesi yakanema. Setilaiti imodzi yoteroyo ikhoza kusamalira mauthenga a telefoni okwanira 30,000 panthaŵi imodzi!
3. Kodi nchiyani chimene chimachitika pamene pali mipata yoletsa kulankhulana?
3 Koma mosasamala kanthu za njira zolankhulirana zonsezi, padakali chisoni chachikulu m’dziko chifukwa cha kusoŵeka kwa kulankhulana pakati pa anthu. Chotero, tikuuzidwa kuti “pali mpata womakulakula—‘mpata woletsa kulankhulana’ womafutukuka—pakati pa olamulira ndi olamulidwa.” Ndipo kodi ndiuti umene uli mpata wambadwo wotchulidwa mofala? Kodi sindiwo kulephera kwa makolo kulankhulana ndi ana awo mwachipambano? Aphungu aukwati amasimba kuti vuto lalikulu koposa m’maukwati ndilo kulephera kulankhulana kwa pakati pa mwamuna ndi mkazi. Kusoŵeka kwa kulankhulana kwabwino kungachititse imfa. Kuchiyambi kwa 1990, anthu 73 anamwalira m’kugwa kwa ndege, mwachiwonekere chochititsa chinali kulephera kulankhulana kwa pakati pa woulutsa ndege ndi wopereka malangizo wapansi. Mutu wanyuzipepala unalengeza kuti: “Kulephera Kulankhulana Kunapangitsa Ngozi.”
4. (a) Kodi liwu lakuti “kulankhulana” limatanthauzanji? (b) Kodi kulankhulana Kwachikristu kuli ndi chonulirapo chotani?
4 Kodi kulankhulana nchiyani m’makhazikitsidwe Achikristu? Malinga ndi dikishonale ina, “kulankhulana” kumatanthauza “kupereka chidziŵitso, maganizo, kapena malingaliro kotero kuti alandiridwe kapena kumvetsetsedwa mokhutiritsa.” Dikishonale ina imakumasulira kukhala “luso lofotokozera malingaliro mogwira mtima.” Onani mamasuliridwe akuti ‘kufotokoza malingaliro mogwira mtima.’ Kulankhulana Kwachikristu kuyeneradi kukhala kogwira mtima chifukwa chakuti chonulirapo chake ndicho kufikira mitima ya anthu ndi chowonadi chochokera m’Mawu a Mulungu kotero kuti, anthuwo angagwirire ntchito pa zimene aphunzira. Mwapadera, kumasonkhezeredwa ndi kupanda dyera, ndi chikondi.
Yehova Monga Wolankhula
5. Kodi ndiiti imene ili imodzi ya njira zoyambirira zimene Yehova Mulungu analankhulana ndi anthu?
5 Mosakaikira Yehova Mulungu ali Wolankhula wamkulu koposa. Popeza kuti anatilenga m’chifaniziro ndi m’chikhalidwe chake, iye ali wokhoza kulankhulana nafe, ndipo kuli kotheka kuti ifeyo tilankhulane ndi ena ponena za iye. Chiyambire kulengedwa kwa munthu, Yehova walankhula ndi zolengedwa zapadziko lapansi ponena za iyemwini. Njira imodzi imene wachitira zimenezi ndiyo mwa chilengedwe chake chowoneka. Chotero, wamasalmo akutiuza kuti: ‘Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake. Usana ndi usana uchulukitsa mawu, ndipo usiku ndi usiku uonetsa nzeru.’ (Salmo 19:1, 2) Ndipo Aroma 1:20 amatidziŵitsa kuti ‘chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka’ za Mulungu. “Zaoneka bwino” kusonyeza kulankhulana kogwira mtima!
6. Kodi Yehova analankhula chiyani kwa zolengedwa zake zapadziko lapansi pamene zinali m’munda wa Edene?
6 Amene samakhulupirira Mulungu ndi vumbulutso lake laumulungu angatipangitse kukhulupirira kuti munthu ayenera kudalira chidziŵitso chake kutsimikizira chifukwa cha kukhalapo kwake. Koma Mawu a Mulungu amamveketsa bwino kuti Mulungu analankhula ndi munthu kuchokera pachiyambi. Chotero, Mulungu anapatsa mwamuna ndi mkazi oyamba lamulo la kubala ili: ‘Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire . . . pa zamoyo zonse.’ Mulungu anawapatsanso ufulu wakudya zipatso za m’mundamo—kupatulapo chimodzi chokha. Ndiyeno, pamene Adamu ndi Hava sanamvere, Yehova analankhula za lonjezo Laumesiya loyamba, akumapatsa anthu chiyembekezo ichi: ‘Ndidzaika udani pakati pa iwe [njokayo] ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.’—Genesis 1:28; 2:16, 17; 3:15.
7. Kodi bukhu la Genesis limavumbula chiyani ponena za kulankhula kwa Yehova ndi atumiki ake?
7 Pamene Kaini, mwana wa Adamu anadzazidwa ndi njiru yakupha, Yehova Mulungu analankhula naye, akumanena kuti: ‘Samalira! Ukuloŵa m’vuto!’ Koma Kaini sanalabadire chenjezo limenelo ndipo anapha mbale wake. (Genesis 4:6-8) Ndiyeno, pamene dziko lapansi linadzazidwa ndi chiwawa ndi kuipa, Yehova analankhula ndi Nowa wolungama za chifuno Chake chakuchotsa padziko lapansi zonyansa zonse. (Genesis 6:13–7:5) Pambuyo pa Chigumulacho, pamene Nowa ndi banja lake anatuluka m’chingalawa, Yehova analankhula nawo za chifuno chake ponena za kupatulika kwa moyo ndi mwazi, ndipo kupyolera mwa utaŵaleza anapereka chitsimikiziro chakuti sakawononganso zamoyo zonse ndi chigumula. Zaka mazana angapo pambuyo pake, Yehova analankhula ndi Abrahamu za chifuno Chake chakuti mabanja onse a anthu adzadzidalitse kupyolera mwa Mbewu ya Abrahamu. (Genesis 9:1-17; 12:1-3; 22:11, 12, 16-18) Ndipo pamene Mulungu analamula kuti akawononga anthu oluluzika a mu Sodomu ndi Gomora, mwachikondi analankhula mfundo imeneyo kwa Abrahamu, akumati: ‘Kodi ndidzabisira Abrahamu chimene ndichita?’—Genesis 18:17.
8. Kodi ndi m’njira zinayi zotani zimene Yehova analankhulira ndi atumiki ake padziko lapansi?
8 Kuyambira ndi Mose, Yehova anagwiritsira ntchito aneneri ambiri kulankhula ndi Israyeli. (Ahebri 1:1) Nthaŵi zina anagwiritsira ntchito kulankhulana kwapakamwa, monga pamene anamuuza Mose kuti: ‘Ulembe mawu awa.’ (Eksodo 34:27) Mobwerezabwereza Yehova analankhula ndi omlankhulira mwa masomphenya, monga momwe anachitira ndi Abrahamu.a Yehova anagwiritsiranso ntchito maloto kulankhula ndi anthu, ndipo osati ndi atumiki ake okha komanso awo amene anali ndi zochita ndi atumiki ake. Mwachitsanzo, Yehova analotetsa aŵiri a akaidi anzake a Yosefe, maloto omwe Yosefe anawamasulirira. Yehova analotetsanso Farao ndi Nebukadinezara, maloto omwe atumiki ake Yosefe ndi Danieli anawamasulirira. (Genesis 40:8–41:32; Danieli, mitu 2 ndi 4) Ndiponso, pazochitika zambiri Yehova anagwiritsira ntchito amithenga aungelo kulankhula ndi atumiki ake.—Eksodo 3:2; Oweruza 6:11; Mateyu 1:20; Luka 1:26.
9. Kodi nchiyani chimene chinasonkhezera Yehova kulankhula ndi anthu ake Israyeli, monga momwe kukuwonekera m’mawu ake ati?
9 Kulankhula kwa Yehova konseko kupyolera mwa aneneri ake kunasonyeza chikondi chake kaamba ka anthu ake Israyeli. Chotero, iye anafotokoza kupyolera mwa mneneri wake Ezekieli kuti: ‘Sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo; bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji inu nyumba ya Israyeli?’ (Ezekieli 33:11) Yehova anali Wolankhula woleza mtima ndi wopirira kwa anthu ake akale achipanduko, monga momwe zikuwonekera mu 2 Mbiri 36:15, 16: ‘Yehova Mulungu wa makolo awo anatumiza kwa iwo ndi dzanja la mithenga yake, nalaŵirira mamawa kuituma, chifukwa anamvera chifundo anthu ake, ndi pokhala pake; koma . . . anapeputsa mawu ake, naseka aneneri ake . . . mpaka panalibe cholanditsa.’
10. Kodi ndimotani mmene Yehova amalankhulira ndi anthu ake lerolino, ndipo kodi iye ali Mulungu wolankhula kufikira pamlingo wotani?
10 Lerolino, tiri ndi Mawu ouziridwa a Mulungu, Baibulo Lopatulika, mwa limene Yehova amalankhula nafe za chidziŵitso chonena za iyemwini, zifuno zake, ndi chifuniro chake kaamba ka ife. (2 Timoteo 3:16, 17) Kwenikwenidi, monga Wolankhula Wamkulu, Yehova amalengeza kuti: ‘[Mfumu, NW] Ambuye Yehova sadzachita kanthu osaulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.’ (Amosi 3:7) Iye amadziŵitsa atumiki ake zimene akufuna kuchita.
Mwana wa Mulungu Monga Wolankhula
11. Kodi ndani amene ali chiŵiya choyambirira cha Yehova cholankhulira ndi anthu, ndipo kodi nchifukwa ninji dzina lake laulemu lakuti ‘Mawu’ liri loyenerera?
11 Pa atumiki onse amene Yehova anagwiritsirapo ntchito kulankhula za chifuniro Chake, wamkulu koposa ndiye Mawu, Logosi, amene anakhala Yesu Kristu. Kodi kutchedwa kwake Mawu, kapena Logosi kumatanthauzanji? Kumatanthauza kuti ali Wolankhulira Wamkulu wa Yehova. Ndipo kodi wolankhulira ndiye yani? Munthu yemwe amalankhula zimene munthu wina afuna kunena. Chotero Logosi anakhala wolankhula mawu a Yehova Mulungu kwa zolengedwa Zake zaluntha zapadziko lapansi. Thayo limenelo liri lofunika kwambiri kotero kuti akutchedwa Mawu.—Yohane 1:1, 2, 14.
12. (a) Kodi Yesu anadza kudziko lapansi kaamba ka chifuno chotani? (b) Kodi nchiyani chimene chimachitira umboni kukwaniritsa kwake mokhulupirika chifuno chimenecho?
12 Yesu iyemwini anauza Pontiyo Pilato kuti cholinga chake chachikulu chimene anadzera kudziko lapansi chinali kulankhula chowonadi kwa anthu nati: ‘Ndinabadwira ichi ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi chowonadi.’ (Yohane 18:37) Ndipo cholembedwa cha m’Mauthenga Abwino chimatiuza mmene anachitira bwino lomwe thayo limenelo. Ulaliki wake wa pa Phiri umazindikiridwa kukhala ulaliki wabwino koposa womwe sunalalikidwepo ndi munthu aliyense. Iye analankhula bwino chotani nanga kupyolera mu ulalikiwo! ‘Makamu a anthu [amene anamva ulalikiwo] anazizwa ndi chiphunzitso chake.’ (Mateyu 7:28) Ponena za chochitika china, timaŵerenga kuti: ‘Anthu a makamuwo anakondwa kumva iye.’ (Marko 12:37) Pamene nduna zina zinatumidwa kukagwira Yesu, zinabwerera popanda iye. Chifukwa ninji? Iwo anawayankha Afarisiwo kuti: ‘Nthaŵi yonse palibe munthu analankhula chotero.’—Yohane 7:46.
Ophunzira a Kristu Anatumidwa Kukhala Olankhula
13. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti Kristu sanali wokhutira ndi kukhala wolankhula mmodzi yekha?
13 Posakhutira kukhala wolankhula mmodzi yekha, choyamba Yesu anatuma atumwi 12 ndiyeno alaliki 70 kupita monga olankhula mbiri yabwino ya Ufumu. (Luka 9:1; 10:1) Ndiyeno mwamsanga asanakwere kumwamba, iye anatuma ophunzira ake kuchita ntchito yapadera. Ntchito yotani? Monga momwe tikuŵerengera pa Mateyu 28:19, 20, iye anawalangiza kukhala olankhula; ndipo iwo anayenera kuphunzitsanso ena kukhala olankhula.
14. Kodi olankhula Achikristu oyambirira anali ogwira mtima motani?
14 Kodi ophunzirawo anali olankhula ogwira mtima? Iwo analidi! Monga chotulukapo cha kulalikira kwawo patsiku la Pentekoste wa 33 C.E., anthu 3,000 anawonjezeredwa ku mpingo Wachikristu wopangidwa chatsopanowo. Posakhalitsa chiŵerengerocho chinawonjezeka kufika ku amuna 5,000. (Machitidwe 2:41; 4:4) Nkosadabwitsa kuti adani awo Achiyuda anawaimba mlandu wakudzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chawo ndipo pambuyo pake anadandaula kuti anasanduliza dziko lapansi lokhalidwa ndi anthu ndi kulalikira kwawo!—Machitidwe 5:28; 17:6.
15. Kodi ndichiŵiya chotani chimene Yehova amagwiritsira ntchito kulankhulira ndi anthu m’nthaŵi zamakono?
15 Bwanji ponena za nthaŵi zamakono? Monga momwe kunanenedweratu pa Mateyu 24:3, 45-47, Mbuyeyo, Yesu Kristu, waika “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” wopangidwa ndi Akristu odzozedwa, kusamalira banja lake lonse padziko lapansi mkati mwa tsiku la kukhalapo kwake. Lerolino kapolo wokhulupirika ndi wanzeru ameneyo amaimiridwa ndi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, lomwe liri ndi Watch Tower Bible and Tract Society monga chiŵiya chake cholengezera. Moyenerera kwenikweni, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru ameneyo watchedwanso ngalande yolankhulira ya Mulungu. Nayenso, amatilimbikitsa kukhala olankhula abwino. Kwenikwenidi, kope loyambirira lenileni la Zion’s Watch Tower and Herald of Christ’s Presence linalangiza oŵerenga ake kuti: “Ngati muli ndi mnansi kapena bwenzi amene mukuganiza kuti angakondweretsedwe kapena kupindula ndi malangizo a [magaziniwa], mungawasonyeze; mwakutero kulalikira Mawu ndi kuchita zabwino kwa anthu onse pamene mupeza mpata.”
16. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti zowonjezereka zimafunikira kuposa Baibulo lokha kuti Mulungu alankhule mogwira mtima ndi atumiki ake apadziko lapansi?
16 Komabe, kungokhala nawo kokha Mawu a Mulungu ndikuwaŵerenga tokha sikuli kokwanira kupeza chidziŵitso cholongosoka chimene chimaika munthu pa msewu wopita ku moyo. Kumbukirani nduna ya ku Aitopiya imene inali kuŵerenga ulosi wa Yesaya koma sinamvetsetse zimene inali kuŵerenga. Filipo mlalikiyo anamfotokozera ulosiwo, pambuyo pake anali wokonzeka kubatizidwa monga wophunzira wa Kristu. (Machitidwe 8:27-38) Chenicheni chakuti zowonjezereka zimafunikira kuposa kungodziŵerengera Baibulo chikuwonekera bwino pa Aefeso 4:11-13, pamene Paulo akusonyeza kuti Kristu sanangopatsa ena kukhala atumwi ouziridwa ndi aneneri komanso anapatsa ena monga ‘alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi; kuti akonzere oyera mtima ku ntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Kristu; kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso cha Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro.’
17. Kodi tingazizindikire motani nthumwi zimene Yehova akugwiritsira ntchito lerolino kulankhula zifuno zake kwa anthu?
17 Kodi tingaŵazindikire motani amene Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu akuwagwiritsira ntchito kuthandiza anthu amene angakhale Akristu kufikira kukhala munthu wangwiro? Malinga ndi kunena kwa Yesu, chizindikiro chimodzi chikakhala chikondi chimene iwo amasonyeza kwa wina ndi mnzake monga momwe Yesu anakondera otsatira ake. (Yohane 13:34, 35) Chizindikiro china nchakuti: Iwo sakakhala mbali ya dziko, monga momwedi Yesu sanali mbali ya dziko. (Yohane 15:19; 17:16) Chizindikiro chinanso chikakhala chakuti akazindikira Mawu a Mulungu kukhala chowonadi, monga momwe anachitira Yesu, akumasonya ku ukumu wake mosalekeza. (Mateyu 22:29; Yohane 17:17) Kudziŵikitsa dzina la Mulungu monga momwe anachitira Yesu kukakhala chizindikiro china. (Mateyu 6:9; Yohane 17:6) Ndipo chizindikiro chinanso chikakhala kutsatira chitsanzo cha Yesu m’kulalikira Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 4:17; 24:14) Pali gulu limodzi lokha limene limakwaniritsa ziyeneretso zimenezi, ilo ndi gulu lamitundu yonse la olankhula odziŵika monga Mboni Zachikristu za Yehova.
18. Kodi ndimbali zitatu ziti za kulankhulana zimene zidzafotokozedwa m’nkhani zotsatira?
18 Komabe, kulankhulana kumatanthauza thayo kwa anthu ena. Kodi Akristu ali ndi thayo lakulankhulana ndi yani? Kwakukulukulu, pali mbali zitatu zimene Akristu ayenera kuzisamalira kusunga njira zolankhulirana zotseguka: m’banja, mumpingo Wachikristu, ndi muutumiki wakumunda Wachikristu. Nkhani zotsatira zidzafotokoza mbali zimenezi za nkhani yathu.
[Mawu a M’munsi]
a Onani Genesis 15:1; 46:2; Numeri 8:4; 2 Samueli 7:17; 2 Mbiri 9:29; Yesaya 1:1; Ezekieli 11:24; Danieli 2:19; Obadiya 1; Nahumu 1:1; Machitidwe 16:9; Chibvumbulutso 9:17.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndichivulazo chotani chimene chingatulukepo ngati palibe kulankhulana?
◻ Kodi ndani omwe ali olankhula aŵiri aakulu koposa?
◻ Kodi ndinjira zosiyanasiyana zotani zimene Mulungu wagwiritsira ntchito kulankhula ndi anthu?
◻ Kodi Yesu anapambana motani monga wolankhula?
◻ Kodi Akristu oyambirira anali achipambano motani m’kulankhulana?
[Chithunzi patsamba 18]
Mofanana ndi Atate wake wakumwamba, Yesu anali wolankhula wachifundo