Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Tingatani Kuti Mulungu Azisangalala Ndi Kulambira Kwathu?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • 2. Tizitani kuti Yehova azivomereza kulambira kwathu?

      Yehova amafuna kuti tizilambira iye yekha chifukwa ndiye Mlengi wathu. (Chivumbulutso 4:11) Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kukonda ndi kulambira iye yekha basi, popanda kugwiritsa ntchito mafano, zithunzi kapena chifaniziro china chilichonse.​—Werengani Yesaya 42:8.

      Yehova amafuna kuti tizimulambira m’njira “yoyera ndi yovomerezeka.” (Aroma 12:1) Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kumvera malamulo ake pa moyo wathu. Mwachitsanzo, anthu amene amakonda Yehova amamvera ndi kutsatira malamulo ake pa nkhani yokhudza ukwati. Ndipo amayesetsa kupewa makhalidwe omwe amaika moyo pangozi monga kusuta fodya, kugwiritsa ntchito mankhwala molakwika kapenanso kumwa mowa mwauchidakwa.a

  • Muziona Kuti Moyo Ndi Mphatso Yamtengo Wapatali
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • 3. Muzisamalira thanzi lanu

      Nthawi zonse timayesetsa kuchita zimene Yehova amafuna chifukwa tinamulonjeza kuti tizimutumikira ndi moyo wathu wonse. Tikamachita zimenezi timakhala ngati tikupereka matupi athu nsembe kwa Mulungu. Werengani Aroma 12:1, 2, kenako mukambirane mafunso awa:

      • N’chifukwa chiyani muyenera kusamalira thanzi lanu?

      • Nanga ndi zinthu ziti zomwe mungachite posonyeza kuti mumasamalira thanzi lanu?

      Mzimayi woyembekezera akulankhulana ndi dokotala.
Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena