Waluso wonyalanyazidwa koposa m’Nthaŵi Yathu
“Chilengedwe ndicho luso la Mulungu.”—Bwana Thomas Browne, sing’anga wa m’zaka za zana la 17.
LEONARDO DA VINCI, Rembrandt, van Gogh—ameneŵa ndi maina odziŵika kwa anthu ambiri. Ngakhale kuti simunaonepo zojambula zawo zoyamba, amuna ameneŵa mumawadziŵa monga aluso kwambiri. Tinganene kuti, luso lawo lawachititsa kusafa.
Iwo anajambula pa nsalu nkhope ya munthu akumwetulira yovuta kuzindikira, chithunzithunzi chochititsa chidwi, mbali yaing’ono ya kukongola kwa chilengedwe, zimene zimatenga mtima wa wozipenya. Timakopedwa ndi zimene zinawakopa—ngakhale kuti anakhalako zaka mazana zapitazo.
Mwina sitingakhale aluso kapena ofufuza kwambiri za luso, koma tingaonebe kukongola kwa luso. Monga waluso amene timakhumba ntchito yake, nafenso timazindikira kukongola. Mwina sitimaganizirapo kwambiri pa kuzindikira kwathu maonekedwe, maumbidwe, mitundu ndi kuŵala kosonyezedwa pa chithunzithunzi, koma kuli mbali ya moyo wathu. Mosakayikira timakonda kukometsa nyumba zathu ndi zinthu kapena zithunzithunzi zimene zimakondweretsa maso. Ngakhale kuti zimene aliyense amakonda zimasiyana, mphamvu ya kuzindikira kukongola imeneyi ili mphatso imene anthu ambiri alinayo. Ndipo ili mphatso imene ingatiyandikizitse kwa Mlengi wathu.
Mphatso ya Kukongola
Kuzindikira kukongola kuli imodzi ya mikhalidwe imene imasiyanitsa anthu ndi zinyama. Buku lakuti Summa Artis—Historia General del Arte (Comprehensive Treatise of Art—A General History of Art) limanena kuti “munthu angafotokozedwe kukhala nyama imene ili ndi nzeru yozindikira kukongola.” Chifukwa ndife osiyana ndi nyama, timaona chilengedwe mosiyana. Kodi galu amasangalala ndi kuloŵa kwa dzuŵa kokongola?
Kodi ndani anatipanga motero? Baibulo limafotokoza kuti “Mulungu ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adamlenga iye.” (Genesis 1:27) Sikuti makolo athu oyamba anaoneka ngati Mulungu. M’malo mwake Mulungu anawapatsa mikhalidwe imene iye mwiniyo ali nayo. Umodzi wa imeneyi ndiwo kukhoza kusangalala ndi kukongola.
Mwa njira yosadziŵika bwino, ubongo wa munthu umazindikira kukongola. Choyamba, ziŵalo zathu zimatumiza uthenga ku ubongo ponena za mawu osiyanasiyana, mafungo, maonekedwe, ndi mapangidwe a zinthu zimene timakopeka nazo. Koma kukongola kumapambana unyinji wonse wa mauthenga a magetsi ndi a makhemikolo amenewo, amene amangotidziŵitsa zimene zikuchitika pamalo otizinga. Sitimaona mtengo, duŵa, kapena mbalame mmene nyama imazionera. Ngakhale kuti zinthu zimenezi sizingatipindulitse pamenepo, izo zimatipatsabe chisangalalo. Ubongo wathu umatikhozetsa kuona kukongola kwake.
Mphamvu imeneyi imakhudza mtima wathu ndipo imalemeretsa moyo wathu. Mary, amene amakhala ku Spain, akukumbukira bwino kwambiri madzulo ena m’November zaka zambiri zapitazo pamene anaima m’mbali mwa nyanja ina ndi kumapenya kuloŵa kwa dzuŵa. “Akakoŵa ambiri anadza akumaulukira cha kumene ine ndinali akumaitanana,” iye akutero. “Mbalame zikwi zambiri zinali yangalala m’mwamba mofiiriramo. Ulendo wawo wa pachaka wosamukira kuchokera ku Russia ndi Scandinavia unazibweretsa kuno ku malo opumirako Achispanya. Zimene ndinaona zinali zokongola kwambiri kwakuti zinandichititsa kulira.”
Kodi Chifuno cha Mphatso ya Kukongola Nchiyani?
Kwa ambiri nzeru yakuzindikira kukongola imasonyeza bwino kukhalapo kwa Mlengi wachikondi, amene amafuna zolengedwa zake za luntha kusangalala ndi luso lake. Nkoyenera ndi kokhutiritsa chotani nanga kunena kuti nzeru yathu yozindikira kukongola imachokera kwa Mlengi wathu wachikondi. Baibulo limafotokoza kuti “Mulungu ndiye chikondi,” ndipo mzimu wake wa chikondi ndiwo kugaŵana. (1 Yohane 4:8; Machitidwe 20:35) Yehova ali wosangalala kugaŵana nafe luso lake la kulenga. Ngati kuti nyimbo yabwino kwambiri sinamvedwepo kapena chithunzithunzi chojambulidwa sichinaonedwepo, kukongola kwake kungakhale kopanda tanthauzo. Luso limachitidwa kuti anthu alione ndi kusangalala nalo—nlopanda pake popanda openyerera.
Inde, Yehova mofananamo analenga zinthu zokongola ndi chifuno—kuti anthu aziziona ndi kusangalala nazo. Indetu, mudzi wa makolo athu oyamba unali paki yaikulu ya paradaiso yotchedwa Edene—limene limatanthauza “Chisangalalo.” Mulungu sanadzaze dziko lapansi ndi luso lake chabe koma wapatsanso anthu mphamvu ya kuliona ndi kuliyamikira. Ndipo pali zinthu zokongola zochuluka chotani nanga zoti tizione! Monga momwe Paul Davies ananenera, “nthaŵi zina kumaoneka ngati kuti chilengedwe ‘chimayesayesa mwapadera’ kupanga chilengedwe chonse kukhala chokondweretsa ndi chothandiza.” Timaona chilengedwe chonse kukhala chokondweretsa ndi chothandiza chifukwa Yehova ‘anayesayesa mwapadera’ kutilenga ndi nzeru ya kuchiphunzira ndi kusangalala nacho.
Nchifukwa chake si kodabwitsa kuti anthu amafuko onse kuyambira kwa ojambula zithunzi m’mapanga, kufika kwa odziŵa luso la Impressionism amazindikira kukongola kwa chilengedwe ndipo ali ndi chikhumbo cha kukujambula. Zaka zikwi zapitazo, nzika za kumpoto kwa Spain zinajambula zithunzithuzi zooneka bwino kwambiri za zinyama m’mapanga a Altamira, Cantabria. Koposa zaka zana zapitazo, odziŵa za Impressionism anatuluka m’nyumba zawo zojambulira ndi kuyesa kujambula maonekedwe oŵala m’munda wa maluŵa kapena kusintha kwa maonekedwe a kuunika pa madzi. Ngakhale ana ngatcheru kwambiri ndi zinthu zokongola. Ndipo, ambiri a iwo atapatsidwa makrayoni amaonekedwe osiyanasiyana ndi pepala amakonda kujambula kalikonse komwe aona komwe kakopa malingaliro awo.
Masiku ano, anthu ambiri achikulire amakonda kutenga pikicha kuti azikumbukira malo okongola amene anawasangalatsa. Koma ngakhale popanda kamera, maganizo athu akhoza kukumbuka zithunzithunzi zokongola zimene tinaona zaka makumi zapitazo. Ndithudi, Mulungu anatipanga ndi kukhoza kwa kusangalala ndi mudzi wathu wa dziko lapansi, umene waukongoletsa kwambiri. (Salmo 115:16) Komabe, palinso chifukwa china chimene Mulungu anatipatsira mphamvu ya kuzindikira kukongola.
‘Mikhalidwe Yake Ioneka Bwino’
Kukulitsa chiyamikiro chathu kaamba ka luso m’chilengedwe kungatithandize kudziŵa Mlengi wathu, amene ntchito zake zatizinga. Nthaŵi ina Yesu anauza ophunzira ake kuyang’anitsitsa maluŵa a mthengo omera m’Galileya. “Tapenyetsani maluŵa akuthengo,” iye anatero, “makulidwe awo; sagwiritsa ntchito kapena sapota; koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanavala monga limodzi la ameneŵa.” (Mateyu 6:28, 29) Kukongola kwa duŵa laling’ono kungatikumbutse kuti Mulungu sali wosasamala zofuna za banja la munthu.
Yesu ananenanso kuti mungadziŵe munthu ndi “zipatso” zake, kapena ntchito. (Mateyu 7:16-20) Motero, tingayembekeze kuti luso la Mulungu lidzatipatsa chidziŵitso pa umunthu wake. Kodi ina ya ‘mikhalidwe yake imene ioneka bwino chilengedwere dziko lapansi’ njotani?—Aroma 1:20 (NW).
“Ntchito zanu zichulukadi, Yehova!” anatero wamasalmo. “Munazichita zonse mwanzeru.” (Salmo 104:24) Nzeru za Mulungu zingaonedwe m’maonekedwe amene anagwiritsira ntchito “kupaka utoto” zomera ndi zinyama za dziko lapansi. “Maonekedwe amasangalatsa kwambiri mtima ndi maso,” anatero Fabris ndi Germani m’buku lawo lakuti Colore, Disegno ed estetica nell’arte grafica (Color—Design and Aesthetics in Graphic Art). Maonekedwe ogwirizana ndi osiyanasiyana, amene amasangalatsa maso ndi kukondweretsa mtima, ali ponseponse. Koma mwinamwake okongola kwambiri ndi maonekedwe aja amene amasinthasintha chifukwa cha kuunika—maonekedwe abwino onga a utawaleza—umboni wamphamvu wakuti analinganizidwa mwanzeru.
Maonekedwe osinthasintha ngofala makamaka pakati pa mbalame za hummingbird.a Kodi nchiyani chimene chimachititsa nthenga zawo kuwala motero? Nthenga zawo zapadera zambiri zapamwamba zimachititsa kuunika kwa dzuŵa kuoneka m’maonekedwe osiyanasiyana a utawaleza—monga mmene prism imachitira. Maina ofala a ma hummingbird, monga ngati ruby, sapphire, ndi emerald, amasonyeza bwino lomwe maonekedwe ofiira, a bluu, ndi obiriŵira amene amakometsa mbalamezi zonga majuwelo. “Kodi chifuno cha kukongolaku kwa mbalame zabwino zimenezi nchiyani?” akufunsa motero Sara Godwin m’buku lake lakuti Hummingbirds. “Sayansi imangopeza kuti palibe chifuno chilichonse koma kudabwitsa wozipenya,” akuyankha. Mosakayikira, palibe munthu waluso amene anapangapo maonekedwe okongola otero!
Tingaone mphamvu ya Mulungu m’mathithi a mkokomo, mafunde omaŵinduka, mafunde amphamvu omafika kugombe, kapena mitengo yaitali ya m’nkhalango yomandenguma ndi mphepo yamphamvu. Luso lamphamvu limeneli lingakhale losangalatsa ngati malo abata. Wodziŵa za chilengedwe wotchuka wa ku America John Muir anafotokozapo zimene mkuntho umachita pa mitengo ya Douglas fir m’mapiri a Sierra Nevada ku California:
“Ngakhale inali yaing’ono, inali yaitali pafupifupi [mamita 33], nthambi zake zosalimba zinali kugwedera ndi kukhota mosangalala. . . . Nthambi zake zakunsonga zosalimba zinagwedera ndi mvula yaikuluyo, zikumakhota ndi kuweyuka mobwerezabwereza, zikumazungulirazungulira.” Monga momwe wamasalmo analembera zaka zikwi zapitazo, ‘mphepo ya namondwe ilemekeza Yehova’—imatisonyeza mphamvu yake yapadera.—Salmo 148:7, 8.
Kwa nthaŵi yaitali mbalame ina yakhala chizindikiro cha chikondi kwa Ajapani. Ndiyo kakoŵa Wachijapani wokongolayo amene kuchecherera kwake nkokongola ngati kuvina kwabwino kulikonse. Mbalame zovina zimenezi nzolemekezedwa kwambiri kwakuti ku Japan zaikidwa monga “chikumbukiro chapadera chachibadwa.” Popeza akakoŵa amakhala aŵiriaŵiri kwa moyo wonse ndipo amakhala ndi moyo kwa zaka 50 ndi kuposapo, Ajapani amaziona kukhala chizindikiro chachikulu cha kukhulupirika kwa mu ukwati.
Bwanji ponena za chikondi cha Mulungu? Mokondweretsa, Baibulo limayerekezera chitetezo chachikondi cha Yehova pa okhulupirika ake ndi chija cha mbalame ya ana yogwiritsira ntchito mapiko ake kutetezera ana ake ku machedwe oipa. Deuteronomo 32:11 amanena za mphungu imene ‘ikasula chisa chake, nikapakapa pa ana ake, iyala mapiko ake, niwalandira, niwanyamula pa mapiko ake.’ Mphungu yokhala ndi ana imachita zinthu zimenezi kulimbikitsa ana ake kuchoka m’chisa ndi kuuluka. Ngakhale simaonedwa kaŵirikaŵiri, nthaŵi zina zamveka kuti mphungu yathandiza ana ake mwa kuwanyamula pa mapiko ake.—Salmo 17:8.
Pamene tiyang’ana zinthu zotizungulira zachilengedwe, timaona malamulo ena akugwira ntchito amenenso amavumbula mbali zina za umunthu wa Mulungu.
Kusiyanasiyana Kuli Chokometsera Moyo
Kusiyanasiyana kwa ntchito ya Mulungu kuli koonekeratu. Kusiyanasiyana kwa zomera, mbalame, nyama, ndi tizilombo nkodabwitsa. Hekitala imodzi chabe ya nkhalango ingakhale ndi mitundu ya mitengo yosiyanasiyana 300 ndi mitundu ya tizilombo 41,000; malo a makilomita atatu mbali zonse angakhale phanga la mitundu 1,500 ya agulugufe; ndipo mtengo umodzi ungakhale chisa cha mitundu 150 ya akafalubvu! Ndipo monga momwe zakhalira kuti palibe anthu aŵiri ofanana ndendende, zimenezo zinganenedwenso ponena za mitengo ya oak kapena nyama zotchedwa tiger. Kusonyeza zenizeni, mkhalidwe wofunika kwambiri pakati pa anthu aluso, kuli mbali yachibadwa ya chilengedwe.
Zoonadi, tangotchula mwachidule mbali zochepa za luso la chilengedwe. Mwakuchiyang’anitsitsa, tingaone mbali zambiri za umunthu wa Mulungu. Koma kuti titero, tiyenera kugwiritsira ntchito nzeru yathu ya kuzindikira kukongola yopatsidwa ndi Mulungu. Kodi ndimotani mmene tingaphunzirire kuyamikira bwinopo luso la Waluso wamkulu koposa wa dziko lonse lapansi?
[Mawu a M’munsi]
a Agulugufe ambiri, onga ngati ma morpho a bluu okongolawo a ku malo otentha a ku America, ali ndi mamba a maonekedwe omwe amasintha pa mapiko ake.
[Bokosi patsamba 23]
Tiyenera Kudziŵa Amene Anatiika Pano
Mtembenuzi wa Baibulo Ronald Knox anakhalapo ndi makambitsirano a zachipembedzo ndi wasayansi John Scott Haldane. “M’chilengedwe chokhala ndi mamiliyoni a mapulaneti,” anatero Haldane, “kodi sikotheka kuti imodzi ya iwo ingakhale ndi moyo?”
“Bwana,” anayankha motero Knox, “ngati Scotland Yard inapeza thupi m’bokosi lanu loikamo katundu, kodi mungawauze kuti: ‘Pali mabokosi mamiliyoni ambiri oikamo katundu pa dziko lapansi—mosakayikira lina liyenera kukhala ndi thupi?’ Ndiganiza kuti angafunebe kudziŵa amene analiikamo.”—The Little, Brown Book of Anecdotes.
Kuwonjezera pa kukhutiritsa chidwi chathu, pali chifukwa chinanso chimene tiyenera kudziŵira amene anatiika pano—kuti timpatse Iye chiyamiko chomuyenera. Kodi waluso wodziŵa kwambiri angamve motani ngati wopenda wouma mutu anena kuti ntchito yake inangokhalako chifukwa cha ngozi ya mosungira utoto? M’njira imodzimodziyo, kodi ndi chipongwe chotani chimene tingachitire Mlengi wa chilengedwe chonse kuposa kunena kuti luso lake linangochitika mwamwaŵi?
[Mawu a Chithunzi]
Mwa chilolezo cha ROE/Anglo-Australian Observatory, chotengedwa ndi David Malir
[Zithunzi patsamba 24]
Akakoŵa ali kuuluka
Zithunzithunzi za m’mapanga ku Altamira, Spain
[Zithunzi patsamba 25]
Ma dolphin, ma hummingbird, ndi mathithi zonse zimavumbula mbali za umunthu wa Waluso Wamkulu
[Mawu a Chithunzi]
Godo-Foto
G. C. Kelley, Tucson, AZ
Godo-Foto