-
Tizichotsa Maganizo Alionse Otsutsana ndi Kudziwa MulunguNsanja ya Olonda (Yophunzira)—2019 | June
-
-
1. Kodi Paulo anapereka chenjezo liti kwa Akhristu odzozedwa?
MTUMWI PAULO analembera Akhristu oyambirira kuti: “Musamatengere nzeru za nthawi ino.” (Aroma 12:2) N’chifukwa chiyani analemba zimenezi kwa Akhristu amene anali atadzipereka kwa Mulungu komanso anali odzozedwa ndi mzimu woyera?—Aroma 1:7.
2-3. (a) Kodi Satana amagwiritsa ntchito zinthu ziti pofuna kuti tisiye kutumikira Yehova? (b) N’chiyani chingatithandize kuchotsa zinthu zolakwika zimene zinazikika molimba m’maganizo athu?
2 Paulo anali ndi nkhawa chifukwa zikuoneka kuti Akhristu ena ankatengera maganizo komanso nzeru zosathandiza zam’dziko la Satanali. (Aef. 4:17-19) Zimenezi zikhoza kutichitikiranso ifeyo. Satana, yemwe ndi Mulungu wa nthawi ino, ali ndi zinthu zambiri zimene amagwiritsa ntchito pofuna kuti tisiye kutumikira Yehova. Mwachitsanzo, iye akhoza kupezerapo mwayi ngati tili ndi kamtima kodziona kuti ndife ofunika kwambiri. Akhozanso kugwiritsa ntchito zinthu zina zokhudza kumene tinakulira, chikhalidwe chathu kapena maphunziro athu kuti tiziyendera maganizo ake.
-
-
Tizichotsa Maganizo Alionse Otsutsana ndi Kudziwa MulunguNsanja ya Olonda (Yophunzira)—2019 | June
-
-
‘SINTHANI MAGANIZO ANU’
4. Kodi ambirife tinafunika kusintha zinthu ziti titayamba kuphunzira choonadi?
4 Kodi ndi zinthu ziti zimene munafunika kusintha mutaphunzira Mawu a Mulungu n’kusankha zoti muyambe kutumikira Yehova? Ambirife tinafunika kusintha makhalidwe ena oipa. (1 Akor. 6:9-11) Ndipo timayamikira kuti Yehova anatithandiza kusintha makhalidwewo.
5. Malinga ndi Aroma 12:2, kodi tiyenera kuchita zinthu ziwiri ziti?
5 Komabe sitiyenera kukhutira ndi zimene tinasintha basi. N’zoona kuti tasiya kuchita machimo akuluakulu amene tinkachita tisanabatizidwe. Koma tiyenera kuyesetsa kupewa zinthu zimene zingatichititse kuyambiranso khalidwe loipalo. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Paulo ananena kuti: “Musamatengere nzeru za nthawi ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu.” (Aroma 12:2) Malinga ndi lembali, tifunika kuchita zinthu ziwiri. Choyamba, tiyenera kupewa ‘kutengera nzeru’ za dzikoli. Chachiwiri, tiyenera “kusandulika” mwa kusintha maganizo athu.
6. Kodi mfundo yaikulu pa mawu a Yesu a pa Mateyu 12:43-45 ndi yotani?
6 Mawu a Paulo akuti kusandulika amatanthauza zambiri osati kungosintha maonekedwe. Amatanthauza kusintha mbali zonse za moyo wathu. (Onani bokosi lakuti “Kusandulika Kapena Kudzisandutsa?”) Kusintha maganizo kumatanthauza kusintha mtima wathu, zimene timalakalaka komanso mmene timaonera zinthu. Choncho aliyense ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi munthune ndangosintha pamwambamwamba kapena ndasinthadi kuchokera mumtima?’ Funso limeneli ndi lofunika kwambiri. Yesu ananena zimene tiyenera kuchita pa Mateyu 12:43-45. (Werengani.) Mfundo yaikulu palembali ndi yakuti: Tikachotsa zinthu zolakwika m’maganizo athu, tiyenera kuikamo maganizo a Mulungu.
-