-
“Yakani ndi Mzimu”Nsanja ya Olonda—2009 | October 15
-
-
9. N’chifukwa chiyani Paulo anayerekezera Akhristu obadwa ndi mzimu, ndi ziwalo za thupi?
9 Werengani Aroma 12:4, 5, 9, 10. Paulo anayerekezera Akhristu odzozedwa ndi ziwalo za thupi zimene zikutumikira mogwirizana pansi pa Khristu, amene ali Mutu wawo. (Akol. 1:18) Iye anakumbutsa Akhristu obadwa ndi mzimu kuti thupi limakhala ndi ziwalo zambiri zimene zimagwira ntchito zosiyanasiyana ndiponso kuti iwowo, ‘ngakhale kuti ndi ambiri, ali thupi limodzi mwa Khristu.’ Pamfundo yomweyi, Paulo analimbikitsa Akhristu odzozedwa a ku Efeso kuti: “Tiyeni tikule m’zinthu zonse, kudzera m’chikondi, pansi pa iye amene ali mutu, Khristu. Kuchokera kwa iye, thupi lonselo limakula podzimanga lokha mwachikondi, pokhala lolumikizika bwino ndi logwirizana mwa mfundo iliyonse yogwira ntchito yake yofunikira, malinga ndi ntchito yoyenerera ya chiwalo chilichonse.”—Aef. 4:15, 16.
-
-
“Yakani ndi Mzimu”Nsanja ya Olonda—2009 | October 15
-
-
11. Kodi mgwirizano wathu umazikidwa pa chiyani, nanga Paulo anapereka malangizo enanso otani?
11 Mgwirizano umenewo umazikidwa pa chikondi, chimene ndi “chomangira umodzi changwiro.” (Akol. 3:14) M’chaputala 12 cha Aroma, Paulo anagogomezera mfundo imeneyi ponena kuti chikondi chathu “chisakhale cha chiphamaso” ndiponso kuti ‘posonyezana chikondi chaubale tikhale ndi chikondi chenicheni kwa wina ndi mnzake.’ Kuchita zimenezi kumathandiza kuti tizilemekezana. Mtumwiyu ananena kuti: “Posonyezana ulemu wina ndi mnzake, khalani patsogolo.” Komabe, tisaganize kuti chikondi chimatanthauza kumangolekerera zinthu. Tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti mpingo ukhalebe woyera. Popereka malangizo ake okhudza chikondi, Paulo anapitiriza kuti: “Nyansidwani ndi choipa, gwiritsitsani chabwino.”
-