-
“Lirani ndi Anthu Amene Akulira”Nsanja ya Olonda (Yophunzira)—2017 | July
-
-
14. Kodi tingalimbikitse bwanji anthu amene aferedwa?
14 Kunena zoona, n’zovuta kudziwa mawu amene tinganene kwa munthu amene akumva chisoni kwambiri. Komabe Baibulo limanena kuti “lilime la anthu anzeru limachiritsa.” (Miy. 12:18) Ena amapeza mfundo zolimbikitsa m’kabuku kakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira.c Koma nthawi zambiri chomwe chimafunika ndi ‘kulira ndi anthu amene akulira.’ (Aroma 12:15) Mlongo wina dzina lake Gaby, yemwe mwamuna wake anamwalira, ananena kuti: “Ine ndimaona kuti kulira kumathandiza kuti anthu ena adziwe mmene ndikumvera. Choncho anzanga akamalira nane zimandilimbikitsa. Ndimaona kuti sindikumva ndekha chisonicho.”
-
-
“Lirani ndi Anthu Amene Akulira”Nsanja ya Olonda (Yophunzira)—2017 | July
-
-
20. N’chifukwa chiyani tinganene kuti malonjezo a Yehova ndi olimbikitsa kwambiri?
20 Timalimbikitsidwa kwambiri tikaganizira kuti Yehova adzathetseratu chisoni chathu pamene “onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu [a Khristu] ndipo adzatuluka.” (Yoh. 5:28, 29) Mulungu yemwe ndi Ambuye Wamkulu Koposa walonjeza kuti ‘adzameza imfa kwamuyaya ndiponso adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.’ (Yes. 25:8) Pa nthawiyo, sipadzakhalanso ‘zolira ndi anthu amene akulira,’ m’malomwake ‘tizidzasangalala ndi anthu amene akusangalala.’—Aroma 12:15.
-