Achichepere Akufunsa Kuti
Umathanyula—Kodi Ngwoipa Kwambiridi?
“Chiyambire pamene ndinali mwana, ndakhala ndi zikhumbo za mathanyula. Chifukwa cha kusazizindikira, sindinatenge njira yodzitetezera. Zimenezi zinanditsogolera m’kuchita chinthu choipa kwambiri ndi mnzanga wina. Ndinali ndi liwongo lalikulu, ndipo ndinalingalira kuti Yehova sadzandikhululukira.”
“TV Ikuyesa Kunyengerera Ana Athu Kuloŵa m’Mathanyula.” Umenewu unali mutu wa nkhani yolembedwa ndi wolemba nkhani ndi kuzigulitsa kwa osindikiza manyuzipepala. Wolembayo anati: “Oonerera wailesi yakanema amachititsidwa kuonerera maprogramu ochulukitsitsa amene amakonda kusonyeza moyo waumathanyula.” Komabe, TV yangokhala imodzi ya njira zambiri zimene zikugwiritsiridwa ntchito masiku ano kuchirikizira umathanyula pakati pa achichepere. Manenanena ochirikiza umathanyula akuchirikizidwanso ndi aphunzitsi, ausinkhu wawo, mafilimu, mabuku, ndi magazini.
Akatswiri azamankhwala nawonso agwirizana nawo pankhaniyi. Mwamwambo, kale madokotala anaona umathanyula kukhala matenda. Koma mu 1973, American Psychiatric Association inalengeza kuti umathanyula sudzalingaliridwanso kukhala kusokonezeka kwa maganizo. Kuyambira pamenepo, akatswiri ambiri azamankhwala asonyeza pafupifupi kuvomereza mokwanira moyo waumathanyula. Mwachitsanzo, katswiri wochiritsa kusokonezeka maganizo Albert Ellis, analengeza kuti maunansi aumathanyula “sali oipa kwenikweni koma ngakhalidwe labwino laumunthu la kugonana. . . . Ngati muwafuna sangalalani nawo, ndipo musalole aliyense kukubwatikani kuti mukhulupirire kuti ‘ngolakwika’ kapena kuti kuli ‘kusokonezeka maganizo.’”
Malingaliro otero ali owanda kwambiri kwakuti magazini a Newsweek akusimba kuti: “Posonkhezeredwa ndi zithunzithunzi za ofalitsa nkhani ndi mkhalidwe watsopano wa kuvomereza, achichepere akuyesa poyera mowonjezereka mkhalidwe wa umathanyula ndi kukondana ndi aziŵalo zonse.” Pamene kuli kwakuti m’nthaŵi zapitazo achichepere anatsutsa mwamphamvu kugonana ndi aziŵalo zofanana nawo, sikuwonjezera mawu kunena kuti chiŵerengero chomakula cha achichepere tsopano chimakuona kukhala “fashoni.” Kaŵirikaŵiri ngakhale achichepere amene samachita mathanyula amakhala ololera ena amene amatero. “Ndiganiza kuti ngati bwenzi langa lindiuza kuti ndi lamathanyula, ndingakhalabe bwenzi lake,” akutero wachichepere wina wotchedwa Darren. Wophunzira wachichepere wina wapakoleji anasonyezadi nkhaŵa yakuti mwina ali wolemala popeza kuti “amakonda atsikana okha”!
Motero mkhalidwe womasuka wa lerolino ungakhale wosokoneza Akristu achichepere—makamaka awo amene kaamba ka chifukwa china chake amakopeka ndi ofanana nawo ziŵalo.a Amadziŵa kuti umathanyula umanyansa Mulungu, ndipo moona mtima amafuna kuupeŵa. Komabe, nthaŵi zina nkhondo yolamulira malingaliro awo ingakhale yothetsa mphamvu kwakuti angayambe kukayikira ngati lingaliro la Baibulo lili loyenera ndi lanzeru. ‘Kodi umathanyula ulidi woipa?’ iwo angadabwe motero.
Zimene Mawu a Mulungu Amanena
Kuti mupeze yankho, dziŵerengereni zimene mtumwi Paulo ananena pa 1 Akorinto 6:9, 10: “Kapena simudziŵa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena [amuna osungidwira zifuno zachilendo, NW] [“mahule achimuna,” New International Version; “mwamuna wachikazi,” King James Version], kapena akudziipsa ndi amuna [“asodomu,” Jerusalem Bible; “amathanyula oluluzika,” Today’s English Version], kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.” Onani kuti Paulo akutchula kwenikweni awo amene mwachionekere amatenga mbali ya kugonedwa kolobodoka ndi awo amene amatenga mbali ya “amuna” m’maunansi awo onyansawo. Motero iye ananena mosabisa kuti Mulungu amanyansidwa ndi machitachita onse amathanyula.
Zimenezi nzoonekanso m’mawu a Paulo pa Aroma 1:18-27: “Mkwiyo wa Mulungu, wochokera Kumwamba, uonekera pa chisapembedzo chonse ndi chosalungama cha anthu, amene akanikiza pansi choonadi m’chosalungama chawo . . . Mulungu anawapereka iwo m’zilakolako za mitima yawo, kuzonyansa, kuchititsana matupi awo wina ndi mnzake zamanyazi . . . Chifukwa cha ichi Mulungu anawapereka iwo ku zilakolako zamanyazi: pakuti angakhale akazi awo anasandutsa machitidwe awo a chibadwidwe akhale machitidwe osalingana ndi chibadwidwe: ndipo chimodzimodzinso amuna anasiya machitidwe a chibadwidwe cha akazi, natenthetsana ndi cholakalaka chawo wina ndi mnzake, amuna okhaokha anachitirana chamanyazi.” Pano Paulo anatsutsa mwachindunji umathanyula wa amuna ndi wa akazi womwe. Iye anatsutsa machitachita amathanyula kukhala osalingana ndi chibadwidwe ndi kukhala “chamanyazi.”
Ndi Kudwala Kapena Umoyo?
Mwina mwake ambiri angayankhe funsoli mwa kunena kuti lingaliro la Baibulo nlachikale, lotha ntchito. Koma pamene muganiza za ilo, kodi ndani amene amadziŵa bwino kwambiri mpangidwe wathu wakuthupi, wamaganizo, wamalingaliro ndi wauzimu kuposa Mlengi wathu? Mulungu anapanga mwamuna ndi mkazi, ndipo mwa iwo anaikamo mkhalidwe wa kukopeka kwa wina ndi mnzake. (Genesis 1:27, 28) Sanawapange kuti akopeke m’kugonana ndi munthu wa ziŵalo zofanana naye. Ndiponso, Mulungu analamula kuti maunansi a kugonana pakati pa mwamuna ndi mkazi azichitika muukwati mokha.—Ahebri 13:4.
Zimenezi sizimatipatsa mavuto. Pa Yesaya 48:17, Yehova Mulungu amanena kuti iye ndiye ‘amene akuphunzitsani kupindula.’ Inde, iye amadziŵa chimene chimatithandiza ndi chimene chimativulaza. Ngakhale kuti kwa ena ziphunzitso za Baibulo zingaonekere kukhala zovuta kutsatira, izo nthaŵi zonse zili “chiphunzitso cholamitsa,” ndiko kuti, zimapindulitsa maganizo ndi thupi. (Tito 2:1) Tsono, umathanyula umangoika pangozi thupi la munthuwe, malingaliro, ndi mkhalidwe wauzimu.
Vuto la AIDS ndi chitsanzo chimodzi cha mmene moyo wamathanyula ulili woipa. Ku North America, amuna amathanyula ali ndi kuthekera kwakukulu kwa kutenga nthendayi. Koma AIDS yangokhala imodzi ya nthenda zambiri—hepatitis, nthenda yachiŵindi, chinzonono, chindoko, ndi tizilombo ta m’matumbo—zimene amathanyula amagwidwa nazo kaŵirikaŵiri. Kodi nchiyani chimene chimasonkhezera kuwanda kwa matenda kumeneku? Dr. Joseph Nicolosi akufotokoza kuti: “Chikoka ndi kumwerekeretsa kwa moyo waumathanyula kwalembedwa ndi olemba ambiri.” Kupenda kwina kwakukulu kunavumbula kuti “28 peresenti ya amuna amathanyula [anali] atagonana ndi mabwenzi awo okwanira chikwi chimodzi kapena kuposa pamenepo. . . . Pafupifupi theka la amuna achiyera amathanyula . . . ananena kuti anali ndi mabwenzi ogonana nawo osiyanasiyana pafupifupi 500.”
Buku lakuti Homosexual Behavior likufotokoza kuti pakati pa amathanyula ambiri “pali mantha a kuloŵa mu unansi wa kulonjezana kukhulupirika, kuyandikirana, kapena kukhala ndi thayo . . . Nthaŵi zina chikhumbo cha kugonana kosakhala kwachibadwa chili ndi mphamvu yaikulu. Ena a anthu ameneŵa angakhale atadziloŵetsa m’kugonana ndi anthu khumi kapena kuposa pamenepo patsiku kapena usiku umodzi.” Kodi khalidwe losalamulirika lotero lingakhale umoyo? M’malo mwake kodi sikudwala ndi kululuzika? Awo amene amadziloŵetsa mu khalidwe losadzisunga lalikulu lotero mwachionekere ali “akapolo a chivundi.”—2 Petro 2:19.
Ndiponso, kugonana kwa mathanyula kochuluka nkwa nkhalwe, kwachiwawa, ndi kwauchiwanda. Mtumwi Paulo anati: “Zochitidwa nawo mseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi.” (Aefeso 5:12) Chiwawa chotero chimasonyeza mkwiyo ndi ululu zimene zimabisika m’moyo wolingaliridwa kukhala wachimwemwewo. Zoonadi, amathanyula ena amanena kuti sali osadzisungira. Koma amathanyula “ogonana ndi munthu mmodzi” ngochepa kwambiri—ndipo kaŵirikaŵiri maunansi awo sakhalitsa. Ngakhale pamene chibwenzi cha aziŵalo zofanana chikhalitsa, sichimakhalapo chifukwa cha chikondi chimene chimafotokozedwa m’Baibulo. Chikondi chimenecho “sichichita zosayenera.”—1 Akorinto 13:4, 5.
Zotulukapo Zake
Paulo pa Aroma 1:27 akunena kuti: “Amuna ndi amuna anachita zamanyazi zonyansa zimenezi, akumalandiradi mwa iwo okha zotulukapo za kuipa kwa kugonana.” (The New Testament in Modern English, lolembedwa ndi J. B. Phillips) M’njira zotani? Choyamba buku lakuti Homosexual Behavior likusimba kuti: “Akazi amathanyula amavutika kwambiri ndi kumwetsa moŵa ndi uchidakwa kuposa akazi ogonana ndi amuna.” Ofufuza ena amanenanso kuti kuyesa kudzipha nkofala pakati pa anyamata amathanyula.
Chowononga munthu kuposa zonse ndicho chiyambukiro cha zotulukapo zake pa mkhalidwe wauzimu. Amathanyula amapeza kuti ali “odetsedwa m’nzeru zawo, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu.” (Aefeso 4:18) Koma bwanji ponena za achichepere owopa Mulungu amene, mosasamala kanthu za kudziŵa kwawo malamulo a mkhalidwe a Baibulo, amakopeka ndi aziŵalo zofanana nawo? Mwachionekere, iwo ali pa nkhondo yeniyeni. Zoonadi, kudziŵa mmene Mulungu amaonera umathanyula kumathandiza otero ‘kudana nacho choipa.’ (Aroma 12:9) Palinso njira zambiri zothandiza zimene angatenge kuti apeŵe kugonjera ku zikhumbo zoipa. Imeneyi ndi nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Onani “Achichepere Akufunsa Kuti . . . Kodi Nchifukwa Ninji Ndimamva Motere?” m’nkhani yathu yapapitayo.
[Chithunzi patsamba 21]
Moyo wamathanyula umasonyezedwa ndi kusadzisungira, kupsinjika maganizo, ndi nthenda