Kusunga Khalidwe Labwino m’Dziko Lodzala ndi Makhalidwe Oipa
“Chitani zonse kopanda madandaulo ndi makani, kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chirema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka.”—AFILIPI 2:14, 15.
1, 2. Kodi nchifukwa ninji Mulungu anafuna kuti Akanani afafanizidwe?
MALAMULO a Yehova ngosasinthika. Aisrayeli anali pafupi kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa pamene mneneri Mose anawauza kuti: “Muwawononge konse Ahiti, ndi Aamori, Akanani, ndi Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi; monga Yehova Mulungu wanu anakulamulirani.”—Deuteronomo 7:2; 20:17.
2 Nangano popeza Yehova ndi Mulungu wachifundo, kodi nchifukwa ninji anafuna kuti okhala m’Kanani afafanizidwe? (Eksodo 34:6) Chifukwa china chinali ‘kuti Akanani angaphunzitse Aisrayeli kuchita monga mwa zonyansa zawo zonse, anazichitira milungu yawo; nachimwire Yehova Mulungu.’ (Deuteronomo 20:18) Mose anatinso: “Yehova awapitikitsa pamaso panu chifukwa cha zoipa za amitundu awa.” (Deuteronomo 9:4) Akanani ndiwo anali okanga pamakhalidwe oipa. Kulambira kwawo kunali kodzala ndi chisembwere chosaneneka ndi kulambira mafano. (Eksodo 23:24; 34:12, 13; Numeri 33:52; Deuteronomo 7:5) Kugonana kwapachibale, kugonana amuna okhaokha, ndi kugona nyama ndizo zinali “machitidwe a dziko la Kanani.” (Levitiko 18:3-25) Ana osadziŵa kalikonse ankawapereka nsembe mwankhanza ku milungu yonyenga. (Deuteronomo 18:9-12) Ndiye chifukwa chake Yehova anati kukhalapo kokhako kwa mitundu imeneyi kungawononge ubwino wakuthupi, wamakhalidwe, ndi wauzimu wa anthu ake!—Eksodo 34:14-16.
3. Kodi nchiyani chinachitika chifukwa chakuti Aisrayeli sanatsatire malangizo onse a Mulungu onena za okhala m’Kanani?
3 Chifukwa chakuti Aisrayeli sanatsatire kwenikweni malangizo a Mulungu polanda Dziko Lolonjezedwa, ambiri okhala m’Kanani anapulumuka. (Oweruza 1:19-21) M’kupita kwa nthaŵi, chisonkhezero cha Akanani chinayamba kumveka pang’onopang’ono, ndipo kunanenedwa kuti: “[Aisrayeli] anakaniza malemba ake [a Yehova], ndi chipangano anachichita ndi makolo awo, ndi mboni zake anawachitira umboni nazo, natsata zopanda pake, nasanduka opanda pake, natsata amitundu owazinga, amene Yehova adawalamulira nawo, kuti asachite monga iwowa.” (2 Mafumu 17:15) Inde, pazaka zotsatirapo Aisrayeli ambiri anakhala ndi makhalidwe oipa amodzimodziwo amene anachititsa Mulungu kulamula kuti Akanani afafanizidwe—kulambira mafano, chisembwere chosaneneka, ndipo ngakhale kupereka ana nsembe!—Oweruza 10:6; 2 Mafumu 17:17; Yeremiya 13:27.
4, 5. (a) Kodi nchiyani chinachitikira Israyeli ndi Yuda osakhulupirikawo? (b) Kodi nchilimbikitso chotani chimene chikuperekedwa pa Afilipi 2:14, 15, ndipo pakubuka mafunso otani?
4 Chotero mneneri Hoseya analengeza kuti: “Imvani mawu a Yehova, inu ana a Israyeli; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi okhala m’dziko, popeza palibe choonadi, kapena chifundo, kapena kudziŵa Mulungu m’dziko. Koma kulumbira, ndi kunama, ndi kupha, ndi kuba, ndi kuchita chigololo; aboola, ndi mwazi ukhudzana nawo mwazi. Chifukwa chake dziko lidzachita chisoni, ndi aliyense wokhalamo adzalefuka, pamodzi ndi nyama zakuthengo, ndi mbalame za mumlengalenga; ndi nsomba za m’nyanja zomwe zidzachotsedwa.” (Hoseya 4:1-3) Mu 740 B.C.E., Asuri anangonjetsa ufumu wa Israyeli woipawo wa kumpoto. Patapita zaka zoposa ngati zana limodzi, ufumu wosakhulupirika wa kummwera wa Yuda unagonjetsedwa ndi Babulo.
5 Zochitikazi zikusonyeza ngozi ya kulekerera makhalidwe oipa pakati pathu. Mulungu amanyansidwa ndi chisalungamo ndipo sadzachilekerera pakati pa anthu ake. (1 Petro 1:14-16) Nzoona kuti tikukhala “m’nyengo ya pansi pano ino yoipa,” m’dziko limene likuipiraipira. (Agalatiya 1:4; 2 Timoteo 3:13) Ngakhale zili choncho, Mawu a Mulungu amalimbikitsa Akristu onse kupitirizabe kukhala “osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chirema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene [aonekera] monga mauniko m’dziko lapansi.” (Afilipi 2:14, 15) Koma kodi khalidwe labwino tingalisunge motani m’dziko lodzala ndi makhalidwe oipa? Kodi kuteroko nkothekadi?
Dziko Lachiroma Lodzala Ndi Makhalidwe Oipa
6. Kodi nchifukwa ninji Akristu a m’zaka za zana loyamba anavutika kusunga khalidwe labwino?
6 Akristu a m’zaka za zana loyamba anavutika kusunga khalidwe labwino chifukwa chakuti mbali iliyonse ya moyo wachiroma inali yodzala ndi makhalidwe oipa. Wafilosofi wachiroma Seneca anati za anthu a m’nthaŵi yake: “Amuna akupikisana koopsa pazoipa. Tsiku lililonse chilakolako cha kulakwa chikukulirakulira, mantha a kulakwa acheperachepera.” Iye anayerekezera mkhalidwe wachiroma ndi “mkhalidwe wa zilombo zakuthengo.” Choncho, nkosadabwitsa kuti Aroma ankafunafuna mipikisano yankhanza yomenyana mpaka wina afe ndi maseŵero onyansa kuti asanguluke.
7. Kodi Paulo anafotokoza motani makhalidwe oipa amene anali ofala pakati pa ambiri m’zaka za zana loyamba C.E.?
7 Mtumwi Paulo ayenera kuti anali kuganizira za khalidwe lonyansa la anthu a m’zaka za zana loyamba pamene analemba kuti: “Mulungu anawapereka iwo ku zilakolako zamanyazi: pakuti angakhale akazi awo anasandutsa machitidwe awo a chibadwidwe akhale machitidwe osalingana ndi chibadwidwe: ndipo chimodzimodzinso amuna anasiya machitidwe a chibadwidwe cha akazi, natenthetsana ndi cholakalaka chawo wina ndi mnzake, amuna okhaokha anachitirana chamanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho yakuyenera kulakwa kwawo.” (Aroma 1:26, 27) Pokhala otsimikiza kulondola zilakolako zodetsedwa za thupi, makhalidwe achiroma anangodzaza ndi makhalidwe oipa.
8. Kodi nthaŵi zambiri ana anali kuwawononga motani pakati pa Agiriki ndi Aroma?
8 Mbiri yakale simafotokoza zonse ponena za kufala kwa mathanyula pakati pa Aroma. Komabe, mosakayikira, iwo anasonkhezeredwa ndi owayambira awo, Agiriki, ambiri amene ankachita mathanyula. Chinali chizoloŵezi kwa amuna akulu kupotola maganizo a anyamata aang’ono, kuwatenga kuti awaphunzitse nakhala monga wophunzira ndi mphunzitsi wake, zimene nthaŵi zambiri zinachititsa anawo kukhala ndi khalidwe lolobodoka pa zakugonana. Mosakayikira, Satana ndi ziŵanda zake ndiwo anachititsa zoipa zimenezi ndi kuwononga ana.—Yoweli 3:3; Yuda 6, 7.
9, 10. (a) Kodi 1 Akorinto 6:9, 10 anatsutsa motani makhalidwe oipa amitundu yosiyanasiyana? (b) Kodi moyo wakale wa ena mumpingo wa ku Korinto unali wotani, ndipo anasintha motani?
9 Polemba mouziridwa ndi Mulungu, Paulo anauza Akristu a ku Korinto kuti: “Kapena simudziŵa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna, kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu. Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m’dzina la Ambuye Yesu Kristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.”—1 Akorinto 6:9-11.
10 Choncho kalata youziridwa ya Paulo inatsutsa chisembwere, niiti “adama” “sadzalandira ufumu wa Mulungu.” Komabe, atandandalika zoipa zingapo, Paulo anati: “Ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa.” Kunali kotheka kuti olakwa nkukhala oyera pamaso pa Mulungu ndi thandizo lake.
11. Kodi zinawakhalira bwanji Akristu a m’zaka za zana loyamba pakati pa anthu a makhalidwe oipawo a m’tsiku lawo?
11 Inde, khalidwe labwino lachikristu linaliko ngakhale m’dziko lodzala ndi makhalidwe oipa a m’zaka za zana loyamba. Okhulupirira ‘ankasandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wawo.’ (Aroma 12:2) Iwo anasiya “makhalidwe [awo] oyamba” ‘nakhala atsopano mumzimu wa mtima wawo.’ Choncho anathaŵa makhalidwe oipa a dziko “[navala] munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.”—Aefeso 4:22-24.
Dziko Lamakono Lodzala ndi Makhalidwe Oipa
12. Kodi pakhala kusintha kotani m’dziko chiyambire 1914?
12 Bwanji za tsiku lathu? Dziko limene tikukhalamoli nlodzaliratu ndi makhalidwe oipa kuposa nkale lonse. Makamaka chiyambire 1914 pakhala kunyonyotsoka kwa makhalidwe padziko lonse. (2 Timoteo 3:1-5) Poti akana njira zamwambo za khalidwe labwino, ulemu, ndi kakhalidwe, ambiri akhala ongoganizira za iwo eni ndipo “sazindikiranso makhalidwe.” (Aefeso 4:19, NW) Magazini ya Newsweek inati: “Tikukhala m’nyengo imene khalidwe labwino limadalira pakaonedwe ka munthu mwini,” niiwonjezera kuti makhalidwe amene alipo tsopano “asintha malingaliro onse a chabwino ndi choipa kukhala nkhani ya chokonda chake cha munthu, chosankha cha mtima wake kapena chosankha chamwambo.”
13. (a) Kodi zosangulutsa zambiri zamakono zimachirikiza motani makhalidwe oipa? (b) Kodi zosangulutsa zoipa zingasonkhezere motani anthu kuchita zoipa?
13 Monga m’zaka za zana loyamba, zosangulutsa zonyansa nzofala lerolino. Wailesi yakanema, wailesi wamba, mafilimu, ndi mavidiyo nthaŵi zonse zimakhala ndi nkhani zochirikiza kugonana. Makhalidwe oipa aloŵa ngakhale pa makompyuta. Malinga ndi kufufuza kwa payunivesite ina, zamaliseche za pakompyuta tsopano zakhala “imodzi ya ntchito zazikulu koposa zopereka zosangulutsa (ngati sindiyo yokha yaikulu koposa) kwa ogwiritsira ntchito makompyuta.” Kodi zonsezi zachititsanji? Wolemba m’nyuzipepala wina akuti: “Pamene mwazi ndi kulemaza ena dala ndi kugonana koluluzika zichuluka m’chikhalidwe chathu chotchuka, timazoloŵera mwazi ndi kulemaza ena dala ndi kugonana koluluzika. Sizimakhalanso kanthu kwa ife. Timayamba kulekerera zopotoka zochuluka chifukwa chakuti zinthu zowonjezereka sizimakhalanso zamalodza kwa ife.”—Yerekezerani ndi 1 Timoteo 4:1, 2.
14, 15. Kodi pali umboni wotani wakuti khalidwe la zakugonana laipa padziko lonse?
14 Lingalirani za lipoti ili la mu The New York Times: “Zinthu zimene zikanakhala zamalodza zaka 25 zapitazo tsopano zakhala njira yamoyo yovomerezeka. Chiŵerengero cha amuna ndi akazi osankha kungokhalira limodzi m’malo mokwatirana chinakwera kufika pa 80 peresenti [mu United States] pakati pa 1980 ndi 1991.” Mkhalidwe wachilendowu si wa ku North America chabe ayi. Magazini ya Asiaweek ikuti: “M’maiko onse a mu [Asia] muli mkangano wa chikhalidwe. Nkhani yake ndi ufulu wakugonana motsutsana ndi mwambo wa khalidwe, ndipo okakamiza kusintha akuwonjezereka nthaŵi zonse.” Ziŵerengero zikusonyeza kuti m’maiko ambiri anthu owonjezereka akuvomereza chigololo ndi kugonana ukwati usanakhale.
15 Baibulo linaneneratu kuti zochita zausatana zidzachuluka m’tsiku lathu. (Chivumbulutso 12:12) Ndiye chifukwa chake sitiyenera kudabwa kuti makhalidwe oipa achuluka koopsa. Mwachitsanzo, kugona ana kwafika poti nkukhala mliri.a United Nations Children’s Fund ikuti “malonda a kugonana akuwononga ana pafupifupi m’dziko lililonse la dziko lapansi.” Chaka chilichonse “ana oposa miliyoni imodzi padziko lonse amawakakamiza kukhala mahule, kuwazembetsa ndi kuwagulitsa kuti aziwagona, ndi kuwagwiritsira ntchito kufalitsa zamaliseche za ana.” Nawonso mathanyula afala, ndipo andale ena ndi atsogoleri achipembedzo ali patsogolo kuwachirikiza namati ndi “njira ina yamoyo.”
Kukana Zoipa za Dziko
16. Kodi Mboni za Yehova zimaliona motani khalidwe la zakugonana?
16 Mboni za Yehova sizimagwirizana ndi awo amene amavomereza miyezo yolekerera zinthu pakhalidwe la zakugonana. Tito 2:11, 12 amati: “Chaonekera chisomo cha Mulungu chakupulumutsa anthu onse, ndi kutiphunzitsa ife kuti, pokana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m’dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza.” Inde, timakulitsa chidani chenicheni, kunyansidwa ndi makhalidwe oipawa monga kugonana kwa osakwatira, chigololo, ndi mathanyula.b (Aroma 12:9; Aefeso 5:3-5) Paulo anapereka chilimbikitso ichi chakuti: “Adzipatule kwa chosalungama yense wakutchula dzina la Ambuye.”—2 Timoteo 2:19.
17. Kodi Akristu oona amakuona motani kumwa moŵa?
17 Akristu oona amakana kaonedwe ka dziko ka zimene zimaoneka ngati zoipa zazing’ono. Mwachitsanzo, anthu ambiri lerolino amaona kumwetsa moŵa ngati kosangalatsa. Koma anthu a Yehova amalabadira uphungu wa pa Aefeso 5:18 wakuti: “Musaledzere naye vinyo, mmene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu.” Ngati Mkristu wasankha kumwa, amatero mosapambanitsa.—Miyambo 23:29-32.
18. Kodi mapulinsipulo a Baibulo amawatsogoza motani atumiki a Yehova pakachitidwe kawo ndi a m’banja?
18 Pokhala atumiki a Yehova, timakananso lingaliro la ena m’dziko lakuti kukuwira ndi kuzazira mnzako wa muukwati ndi ana ako kapena kuwatukwana ndi khalidwe lololeka. Pokhala otsimikiza kulondola khalidwe labwino, amuna achikristu okwatira ndi akazi awo onse amayesetsa kugwiritsira ntchito uphungu wa Paulo wakuti: “Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse. Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Kristu anakhululukira inu.”—Aefeso 4:31, 32.
19. Kodi makhalidwe oipa afala motani m’zamalonda?
19 Kusaona mtima, chinyengo, kunama, machenjera achinyengo pamalonda, ndi kuba nazonso nzofala lerolino. Nkhani ina m’magazini ya zamalonda ya CFO ikuti: “Kufufuza antchito 4,000 . . . kunapeza kuti 31 peresenti ya ofunsidwawo anali ataonapo ‘kupulupudza koopsa’ m’chaka chapitacho.” Kupulupudza kumeneko kunaphatikizapo kunama, kulemba zabodza, kuvuta akazi kapena amuna, ndi kuba. Ngati tikufuna kukhala ndi khalidwe loyera pamaso pa Yehova, tiyenera kupeŵa khalidwe lotere ndi kukhala oona mtima pamalonda athu.—Mika 6:10, 11.
20. Kodi nchifukwa ninji Akristu sayenera kukhala ndi “chikondi cha pandalama”?
20 Talingalirani zimene zinachitikira mwamuna wina amene anaganiza kuti adzakhala ndi nthaŵi yaikulu yotumikira Mulungu atapanga phindu lalikulu kwambiri pamalonda ena ake. Anakopa ena kuti aikize ndalama zawo m’malonda ena mwa kukokomeza mapindu amene iwo adzapeza. Pamene analephera kupeza mapinduwo, anada nkhaŵa kwambiri kuti adzazibweza bwanji ndalama zambirizo zimene zinatayika kwakuti anaba ndalama zimene ena anamuikiza. Chifukwa cha zochita zake ndi mzimu wosalapa, anachotsedwa mumpingo wachikristu. Nloonadi chenjezo la Baibulo lakuti: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi mumsampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko. Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.”—1 Timoteo 6:9, 10.
21. Kodi amuna ambiri okhala ndi ulamuliro m’dziko ali ndi khalidwe lotani, koma kodi okhala ndi udindo mumpingo wachikristu ayenera kukhala ndi khalidwe lotani?
21 Amuna akudziko amene ali ndi mphamvu ndi chisonkhezero nthaŵi zambiri samakhala ndi khalidwe labwino ndipo amasonyeza choonadi cha mwambi wakuti ‘Mphamvu imaipitsa.’ (Mlaliki 8:9) M’maiko ena, ziphuphu ndi mitundu ina ya chinyengo ndizo moyo wa ena mwa oweruza, apolisi, ndi andale. Komabe, otsogolera mumpingo wachikristu ayenera kukhala ndi khalidwe labwino ndipo sayenera kuchita ufumu pa ena. (Luka 22:25, 26) Akulu limodzinso ndi atumiki otumikira, samatumikira kuti ‘atsate phindu lonyansa.’ Iwo ayenera kukaniratu zoyesayesa kukhotetsa kapena kusonkhezera chiweruzo chawo mwa kuwalonjeza chuma.—1 Petro 5:2; Eksodo 23:8; Miyambo 17:23; 1 Timoteo 5:21.
22. Kodi nkhani yotsatira idzafotokozanji?
22 Monga gulu, Akristu akupambana nkhondo yamakonoyi yakusunga khalidwe labwino m’dziko lathuli lodzala ndi makhalidwe oipa. Komabe, khalidwe labwino sindilo kungopeŵa zoipa basi. Nkhani yotsatira idzafotokoza zenizeni zimene zimafunika pokulitsa khalidwe labwino.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani zakuti “Tetezerani Ana Anu!,” zopezeka mu Galamukani! ya October 8, 1993.
b Awo amene achitapo mathanyula kumbuyoku angasinthe khalidwe lawo, monga momwenso ena a m’zaka za zana loyamba anachitira. (1 Akorinto 6:11) Chidziŵitso chothandiza chinaperekedwa mu Galamukani! ya April 8, 1995, masamba 21-3.
Mfundo Zopenda
◻ Kodi nchifukwa ninji Yehova analamula kuti Akanani afafanizidwe?
◻ Kodi ndi zoipa zotani zimene zinali zofala m’zaka za zana loyamba, ndipo kodi Akristu zinawakhalira bwanji pakati pa anthu amakhalidwe oipa ameneŵa?
◻ Kodi pali umboni wotani wakuti khalidwe laipa padziko lonse lapansi chiyambire 1914?
◻ Kodi anthu a Yehova ayenera kukana makhalidwe oipa otani ofala?
[Chithunzi patsamba 9]
Akristu a m’zaka za zana loyamba anali ndi khalidwe labwino, ngakhale ankakhala m’dziko lodzala ndi makhalidwe oipa
[Chithunzi patsamba 10]
Zoipa zaloŵa ngakhale pamakompyuta, kuchititsa kuti achinyamata ambiri ndi ena azipenyerera zamaliseche
[Chithunzi patsamba 12]
Akristu ayenera kusungabe khalidwe labwino, osatsanzira machenjera osaona mtima a ena