Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 5/1 tsamba 32
  • Kugonjetsa Choipa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugonjetsa Choipa
  • Nsanja ya Olonda—1999
Nsanja ya Olonda—1999
w99 5/1 tsamba 32

Kugonjetsa Choipa

“GALU wakufa uyu atukwaniranji mbuye wanga mfumu? Mundilole ndioloke ndi kudula mutu wake.” Pempho limeneli linaperekedwa ndi Abisai, mkulu wankhondo wa Aisrayeli. Ndimo mmene mwaukali anayankhira pamene Mbenjamini wotchedwa Simeyi mwaudani anali kumunyozera mbuye wake Mfumu Davide.​—2 Samueli 16:5-9.

Abisai anali ndi malingaliro amene anthu ambiri lerolino amakhala nawo​—pulinsipulo la kubweza moto. Inde, Abisai anafuna kuti Simeyi avutike chifukwa cha chipongwe chimene anachitira Davide.

Komabe, kodi Davide anachitanji? Davide anamuletsa Abisai, nati: “Mlekeni.” Ngakhale kuti Davide anali wosalakwa pa zimene Simeyi anali kumunenera, iye modzichepetsa anakana chiyeso choti abwezere. M’malo mwake, iye anasiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova.​—2 Samueli 16:10-13.

Davide atabwereranso pa mpando wachifumu pambuyo pothaŵa kuukira kosaphula kanthu kwa mwana wake, Simeyi anali mmodzi wa anthu amene anali oyambirira kudzamuchingamira ndi kupempha kuti awakhululukire. Abisai anafunanso kumupha, koma Davide sanalolenso.​—2 Samueli 19:15-23.

Pachochitika chimenechi, Davide anaimira Yesu Kristu bwino kwambiri, munthu yemwe mtumwi Petro analemba za iye kuti: “Amene pochitidwa chipongwe sanabwezera chipongwe . . . koma anapereka mlandu kwa Iye woweruza kolungama.”​—1 Petro 2:23.

Lerolino, Akristu akulangizidwa kukhala “odzichepetsa; osabwezera choipa ndi choipa.” (1 Petro 3:8, 9) Mwa kutsatira zimene anachita Davide ndi Yesu Kristu, ifenso ‘tingamagonjetse choipa ndi chabwino.’​—Aroma 12:17-21.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena