Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • N’chiyani Chingatithandize Kuti Tizisankha Zinthu Mwanzeru?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • 5. Muzilemekeza zikumbumtima za anthu ena

      Anthu amene ndi osiyana amasankhanso zinthu mosiyana. Ndiye tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza zikumbumtima za anthu ena? Taganizirani zochitika ziwiri izi:

      Chochitika choyamba: Mlongo amene anazolowera kuphoda wasamukira mumpingo wina umene alongo amumpingomo amaona kuti kuphoda si koyenera.

      Werengani Aroma 15:1 ndi 1 Akorinto 10:​23, 24, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

      • Malinga ndi mavesiwa, kodi mlongoyo angasankhe kuchita chiyani? Nanga inuyo mungatani ngati muli ndi munthu wina amene chikumbumtima chake sichikumulola kuchita zimene inuyo chikumbumtima chanu chikukulolani kuchita?

      Chochitika chachiwiri: M’bale akudziwa bwino kuti Baibulo silimaletsa kumwa mowa mosapitirira malire, koma iyeyo wasankha kuti asamamwe mowa n’komwe. Kenako m’baleyo waitanidwa kuphwando ndipo akuona kuti abale ena akumwa mowa.

      Werengani Mlaliki 7:16 ndi Aroma 14:1, 10, kenako mukambirane mafunso awa:

      • Malinga ndi mavesiwa, kodi m’baleyu angasankhe kuchita chiyani? Nanga inuyo mungatani ngati mwaona munthu wina amene chikumbumtima chake chikumulola kuchita zimene inuyo chikumbumtima chanu sichikukulolani kuchita?

      Kodi ndi zinthu ziti zimene zingathandize munthu kusankha zinthu mwanzeru?

      Mzimayi akupemphera.

      1. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kusankha zoyenera kuchita.​​​—Yakobo 1:5.

      Mzimayi yemweyu akufufuza pogwiritsa ntchito Baibulo, mabuku athu komanso kompyuta.

      2. Muzifufuza m’Baibulo, mabuku ndi zinthu zina zimene gulu lathu limafalitsa kuti mupeze mfundo zimene zingakuthandizeni. Mukhozanso kulankhulana ndi Akhristu okhwima mwauzimu.

      Mzimayi yemweyu akuganiza.

      3. Muziganizira mmene zosankha zanu zingakhudzire chikumbumtima chanu komanso zikumbumtima za anthu ena.

  • Tizivala Ndi Kudzikongoletsa Moyenera
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • 2. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira abale ndi alongo athu tikamasankha zomwe tikufuna kuvala?

      N’zoona kuti tili ndi ufulu wosankha zimene tikufuna kuvala, komabe ndi bwino kuganizira mmene kavalidwe kathu kangakhudzire anthu ena. Timapewa kukhumudwitsa ena ndipo timayesetsa “kuwakondweretsa pa zinthu zabwino zowalimbikitsa.”​—Werengani Aroma 15:1, 2.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena