Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • be phunziro 15 tsamba 131-tsamba 134 ndime 4
  • Kuoneka Bwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuoneka Bwino
  • Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Nkhani Yofanana
  • Tizivala Ndi Kudzikongoletsa Moyenera
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kuvala Moyenera Kumasonyeza Kuti Tikulemekeza Mulungu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Kodi Mavalidwe Anu Amalemekeza Mulungu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • N’chifukwa Chiyani Timavala Bwino Tikamapita Kumisonkhano Yathu?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
Onani Zambiri
Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
be phunziro 15 tsamba 131-tsamba 134 ndime 4

PHUNZIRO 15

Kuoneka Bwino

Kodi muyenera kuchita motani?

Valani zoyera, zaudongo, ndi zosonyeza ulemu. Tsitsi lipesedwe mwaukhondo. Kaimidwe kanunso kaonetse kuti muli ndi chidwi.

N’chifukwa chiyani kuli kofunikira?

Maonekedwe anu angakhudze mmene ena amaonera chikhulupiriro chanu chachikristu ndi moyo umene mumauonetsa.

MAONEKEDWE anu amanena zambiri za inu. Pamene Yehova amaona zimene zili m’mtima wa munthu, kaŵirikaŵiri anthufe timaonera pa “chooneka ndi maso.” (1 Sam. 16:7) Pamene mwavala mwaudongo ndi kupesa bwino, ena amaona kuti mumadzilemekeza, ndipo amamvetsera mukawalankhula. Mavalidwe anu abwino amaperekanso chithunzi chabwino cha chipembedzo chanu ndipo omvera anu amalemekeza Mulungu amene mumam’pembedza.

Malangizo Oyenera Kuwatsatira. Baibulo silipereka malamulo ambiri pankhani ya maonekedwe a munthu. Koma limapereka mfundo za makhalidwe abwino zoyenera zomwe zingatithandize kusankha zinthu mwanzeru. Chachikulu pa zonse ndi mfundo yakuti ‘tichite zonse ku ulemerero wa Mulungu.’ (1 Akor. 10:31) Kodi ndi mfundo za makhalidwe abwino zotani zimene zingatithandize pankhani ya maonekedwe athu?

Yoyamba, Baibulo limatilangiza kukhala aukhondo, m’thupi ndi zovala. M’Chilamulo chake kwa Israyeli, Yehova anapereka malangizo pankhani ya ukhondo. Mwachitsanzo, pamene ansembe anali pantchito yawo, anafunikira kusamba ndi kuchapa zovala zawo panthaŵi zoikika. (Lev. 16:4, 24, 26, 28) N’zoona kuti Akristu sasunga Chilamulo cha Mose, koma mfundo za makhalidwe abwino zomwe zili mmenemo zimagwirabe ntchito. (Yoh. 13:10; Chiv. 19:8) Makamaka pamene tikupita kumalo olambirira kapena mu utumiki wa kumunda, matupi athu, mpweya wa m’kamwa, ndi zovala zathu ziyenera kukhala zaukhondo kuti ena asakhumudwe nafe. Awo amene amakamba nkhani kapena kupereka zitsanzo pamaso pa mpingo ayenera kupereka chitsanzo chabwino pambali imeneyi. Kusamalira maonekedwe athu kumapereka ulemu kwa Yehova ndi gulu lake.

Yachiŵiri, Baibulo limatilangiza kukhala odzichepetsa ndi odziletsa. Mtumwi Paulo analangiza akazi achikristu kuti “adziveke okha . . . manyazi (“kudzichepetsa,” NW) ndi chidziletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golidi kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali; komatu (umo mokomera akazi akuvomereza kulemekeza Mulungu).” (1 Tim. 2:9, 10) Kudzichepetsa ndi kudziletsa n’zofunikanso pamavalidwe ndi mapesedwe a amuna.

Munthu wodzichepetsa amapewa kukhumudwitsa ena popanda chifukwa. Amapeŵanso kudzionetsera. Kudziletsa kumapatsa nzeru, kapena kuzindikira bwino. Munthu amene amasonyeza makhalidwe ameneŵa amachita zinthu mosamala chifukwa amalemekeza miyezo yaumulungu. Sikuti pokhala ndi makhalidwe ameneŵa sitiyenera kutchena ayi, koma amatithandiza kukhala osamala m’mavalidwe athu ndi kupeŵa masitaelo opambanitsa a kavalidwe ndi kapesedwe. (1 Yoh. 2:16) Timafuna kutsatira mfundo za makhalidwe abwino zimenezi kaya tili pamalo olambirira, mu utumiki wa kumunda, kapena m’zochitika zina. Ngakhale zovala zathu za masiku onse ziyeneranso kusonyeza kudzichepetsa ndi kudziletsa kwathu. Kusukulu kapena kuntchito, timakhala ndi mipata yolalikira mwamwayi. Ngakhale kuti sitingavale mmene timavalira kumisonkhano yaing’ono ndi yaikulu, zovala zathu zikhalebe zaudongo ndi zoyenera.

N’zoona kuti sitivala mofanana. Ndipo sitiyembekezeka kutero. Anthufe tili ndi makonda osiyana, ndipo zimenezo n’zoyenera. Koma malangizo a Baibulo tiyenera kuwatsatira nthaŵi zonse.

Mtumwi Petro anasonyeza kuti chofunika koposa kapesedwe ka tsitsi kapena chovala chakunja ndicho chovala cha “munthu wobisika wa mtima.” (1 Pet. 3:3, 4) Ngati mitima yathu idzala ndi chimwemwe, chikondi, mtendere, chifundo, ndi chikhulupiriro chozama, zimenezi zidzakhala kwa ife ngati zovala zauzimu zimene zimalemekezadi Mulungu.

Yachitatu, Baibulo limatifulumiza kuti tione ngati maonekedwe athu ndi oyenera. Pa 1 Timoteo 2:9, pakutchulidwa “chovala choyenera.” Ngakhale kuti mtumwi Paulo anatchula chovala cha akazi, mfundo yake imagwiranso ntchito kwa amuna. Chinthu choyenera chimakhala chaudongo ndi chadongosolo. Kaya tili opeza bwino m’zachuma kapena ayi, tikhoza kumaoneka audongo.

Mbali imodzi ya maonekedwe imene anthu amaona msanga ndi tsitsi lathu. Lizikhala laudongo ndi lokonzedwa bwino. Mmene anthu amakonzera tsitsi lawo zimadaliranso chikhalidwe cha kwawoko ndi chibadwa. Pa 1 Akorinto 11:14, 15, timapezapo uphungu wa mtumwi Paulo wonena za kakonzedwe ka tsitsi, umene mwachionekere unakhudza mbali ziŵirizo. Komabe, ngati mwamuna akonza tsitsi lake mofuna kuoneka ngati mkazi, kapena mkazi mofuna kuoneka ngati mwamuna, amakhala akuphwanya mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo.—Deut. 22:5.

Kwa amuna, maonekedwe audongo angaphatikizepo kupala ndevu mwaudongo. Kumadera kumene anthu ambiri amaona ndevu zapamlomo wapamwamba (ena amati kapitolosi) kukhala zoyenera, aliyense amene angamasunge ndevuzo ayenera kumazidulira mwaudongo.

Yachinayi, maonekedwe athu asaonetse kukonda dziko ndi njira zake. Mtumwi Yohane anachenjeza kuti: “Musakonde dziko lapansi, kapena za m’dziko lapansi.” (1 Yoh. 2:15-17) Zilakolako zoipa zambiri zimaonetsa mzimu wa dzikoli. Mwa zimenezo Yohane anatchula chilakolako cha thupi lochimwa ndi kudzitama ndi chuma. Malemba amachenjezanso za mzimu wachipanduko, kapena kusamvera olamulira. (Miy. 17:11; Aef. 2:2) Zilakolako ndi maganizo oterowo kaŵirikaŵiri zimaonekera m’njira imene anthu amavalira ndi mmene amakonzera tsitsi lawo. Chifukwa cha zimenezo, maonekedwe awo angakhale onyazitsa, odzutsa chilakolako chonyansa, odzikongoletsa monyanyira, anyankhalala, kapena osasamala m’zochita zawo. Ife monga atumiki a Yehova, timapeŵa masitaelo osonyeza njira zodana ndi Chikristu zoterozo.

M’malo motsanzira dzikoli, tiyeni titengere chitsanzo chabwino cha kavalidwe ndi kapesedwe ka amuna ndi akazi okhwima mwauzimu a mumpingo wachikristu! Anyamata omwe ali ndi cholinga chomadzakamba nkhani za onse m’tsogolo aziyang’anitsitsa mmene amavalira amene amakamba nkhanizo. Tonse tingatengere chitsanzo cha awo amene atumikira zaka zambiri mu utumiki wothandiza anthu.—1 Tim. 4:12; 1 Pet. 5:2, 3.

Yachisanu, pofuna kusankha chinthu choyenera, tikumbukire kuti “Kristunso sanadzikondweretse yekha.” (Aroma 15:3) Nkhaŵa yaikulu ya Yesu inali kuchita chifuniro cha Mulungu. Yesu anatsogozanso kuthandiza ena m’malo mwa zofuna zake. Pankhani ya masitaelo a mavalidwe ndi mapesedwe, kodi tiyenera kuchitanji ngati chinachake chikhala chokhumudwitsa anthu a kumene tikutumikira pakali pano? Kutengera mzimu wodzichepetsa umene Kristu anasonyeza kungatithandize kusankha zinthu mwanzeru. Mtumwi Paulo analangiza kuti: “Osapatsa chokhumudwitsa konse m’chinthu chilichonse.” (2 Akor. 6:3) Pachifukwa chimenecho, tiyenera kupeŵa masitaelo a tsitsi kapena zovala zimene zingatseke makutu a anthu amene timawalalikira.

Kaimidwe. Maonekedwe abwino amakhudzanso kaimidwe koyenera. N’zoona kuti timanyamula matupi athu m’njira zosiyanasiyana poima ndi poyenda, ndipo sitikunena kuti tizichita mofanana. Komabe, Baibulo limasonyeza kuti kuima mowongoka kumaonetsa kuti munthuyo n’ngodzilemekeza ndipo akulankhula mwachidaliro. (Lev. 26:13; Luka 21:28) Ngakhale ndi choncho, chifukwa chogwira ntchito yoŵerama kwa zaka zambiri kapena chifukwa cha ukalamba kapena kufooka kwina kwa thupi, mbale kapena mlongo sangathe kuima mowongoka kapena angafune kuyedzamira chinachake. Koma kwa omwe amatha kutero, kuima mowongoka polankhula kwa ena n’kwabwino kuti tisasonyeze mphwayi kapena mantha. Ndiponso, ngakhale kuti sikulakwa kuika manja nthaŵi zina pasitandi yolankhulirapo, sikumapereka chithunzi chabwino kwa omvera.

Zida za Ntchito Zosamalika. Si maonekedwe athu okha amene ayenera kukhala audongo ndi aulemu, komanso zida zathu zantchito ya utumiki wa kumunda ziyenera kukhala zosamalika.

Ganizirani za Baibulo lanu. Sikuti tonse tingagule Baibulo latsopano pamene lakale liyamba kutha. Komabe, kaya Baibulo lathu takhala nalo kuyambira liti, lizioneka kuti timalisamala bwino.

Pali njira zambiri zolongedzera mabuku m’chola chanu cha mu umboni, koma chiyenera kukhala chaudongo. Kodi munaonapo mapepala akugwa m’Baibulo pamene wofalitsa wina anafuna kuŵerenga Baibulo kwa mwininyumba kapena pamene mbale wina anali kukamba nkhani mumpingo? Zimenezo zinakujejemetsani, si choncho kodi? Ngati mapepala osungidwa m’Baibulo ndiwo amadodometsa anthu, ndiye kuti kuwasungira pamalo ena kungakhale mbali ina yosamalira bwino zida zanu zantchito. Dziŵaninso kuti m’madera ena, kukhazika pansi Baibulo kapena mabuku ena auzimu ndi kunyozera kwambiri.

Maonekedwe abwino azikhala chinthu chofunika kwa ife. Amakhudzanso mmene anthu ena amationera. Koma mfundo yaikulu ndi yakuti, tisamale maonekedwe athu kuti ‘tikakometsere chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu m’zinthu zonse.’—Tito 2:10.

MAFUNSO OPENDERA MAONEKEDWE ANU

  • Kodi chilichonse n’choyera?

  • Kodi maonekedwe anu amaonetsa kudzichepetsa ndi kulingalira bwino?

  • Kodi chilichonse chaikidwa m’malo?

  • Nanga tsitsi lanu n’losamalika?

  • Kodi pali chilichonse chokhudza maonekedwe anu chimene chingaonetse kukonda dziko?

  • Kodi pangakhale chifukwa chimene mungaganizire kuti maonekedwe anu angakhumudwitse ena?

ZOCHITA: Kamodzi patsiku kwa mlungu wathunthu, zilibe kanthu kuti mwakonzekera kuchitanji, dzipendeni pa mndandandawo wakuti “Mafunso Opendera Maonekedwe Anu,” patsamba 132.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena