Pezani Chitonthozo kwa Yehova
“Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake, monga mwa Kristu Yesu.”—AROMA 15:5.
1. Kodi nchifukwa ninji tsiku lililonse limadza ndi kufunika kokulirapo kwa chitonthozo?
TSIKU lililonse limene limapita limadza ndi kufunika kowonjezereka kwa chitonthozo. Monga momwe wolemba Baibulo ananenera zaka zoposa 1,900 zapitazo, “cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zoŵaŵa pamodzi kufikira tsopano.” (Aroma 8:22) M’nthaŵi yathu ino ‘kubuula’ ndi “zoŵaŵa” zawonjezeka kuposa ndi kale lonse. Chiyambire Nkhondo Yadziko I, anthu akumana ndi mavuto osiyanasiyana monga nkhondo, chiwawa, ndi masoka achilengedwe, kaŵirikaŵiri zochititsidwa ndi kuwononga dziko lapansi.—Chivumbulutso 11:18.
2. (a) Kodi ndani ali ndi mlandu waukulu wa kuchititsa masoka a anthu omwe alipo? (b) Kodi ndi mfundo iti imene imatipatsa chitonthozo?
2 Kodi nchifukwa ninji pakhala kuvutika kochuluka kotero m’nthaŵi yathu? Pofotokoza kugwetsedwa kwa Satana kuchokera kumwamba utabadwa Ufumuwo mu 1914, Baibulo limayankha kuti: “Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.” (Chivumbulutso 12:12) Umboni woonekeratu wa kukwaniritsidwa kwa ulosiwo umatanthauza kuti tafika pafupi kwenikweni ndi mapeto a ulamuliro woipa wa Satana. Nkotonthoza chotani nanga kudziŵa kuti posachedwapa moyo padziko lapansi udzabwerera kumkhalidwe wamtendere umene unalipo Satana asanatsogolere makolo athu oyamba m’chipanduko!
3. Kodi ndi liti pamene anthu anali osafunikira chitonthozo?
3 Pachiyambi, Mlengi wa munthu anakonza munda wokongola monga malo okhala a anthu aŵiri oyamba. Mundawo unali m’malo otchedwa Edene, kutanthauza “Chokondweretsa” kapena “Chosangalatsa.” (Genesis 2:8, NW, mawu amtsinde) Ndiponso, Adamu ndi Hava anasangalala ndi thanzi langwiro, ndi chiyembekezo cha kusafa konse. Tangolingalirani za mbali zosiyanasiyana mmene akanakulitsira maluso awo—kulima, zojambula, kumanga, nyimbo. Talingaliraninso za ntchito zonse za kulenga zimene akanaziphunzira pamene anali kukwaniritsa thayo lawo la kugonjetsa dziko lapansi ndi kulipanga kukhala paradaiso. (Genesis 1:28) Ndithudi, moyo wa Adamu ndi Hava ukanakhala wodzazidwa, osati ndi kubuula ndi zoŵaŵa, koma ndi zokondweretsa ndi zosangalatsa. Mwachionekere, iwo sakanafunikira chitonthozo.
4, 5. (a) Kodi nchifukwa ninji Adamu ndi Hava analephera mayeso awo a kumvera? (b) Kodi nchiyani chimene chinachititsa anthu kukhala ofunikira chitonthozo?
4 Komabe, zimene Adamu ndi Hava anafunikira kuchita ndizo kukulitsa chikondi chozama ndi chiyamikiro kwa Atate wawo wakumwamba wokoma mtima. Chikondi choterocho chikanawasonkhezera kumvera Mulungu m’mikhalidwe yonse. (Yerekezerani ndi Yohane 14:31.) Mwachisoni, makolo athu oyambirira onse aŵiri analephera kumvera Mfumu yawo yoyenerera, Yehova. M’malo mwake, anadzilola kukhala pansi pa ulamuliro woipa wa mngelo wochimwayo, Satana Mdyerekezi. Anali Satana amene anayesa Hava kuti achimwe ndi kudya chipatso choletsedwacho. Ndiyeno Adamu anachimwa pamene iyenso anadya chipatso cha mtengowo za umene Mulungu anachenjeza momvekera bwino kuti: “Tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.”—Genesis 2:17.
5 Mwa njira imeneyi, ochimwa aŵiriwo anayamba kufa. Popereka chiweruzo cha imfa, Mulungu anauzanso Adamu kuti: “Nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha iwe; m’kusauka udzadyako masiku onse a moyo wako: minga ndi mitula idzakubalira iwe; ndipo udzadya therere la m’thengo.” (Genesis 3:17, 18) Motero Adamu ndi Hava anataya chiyembekezo cha kusandutsa dziko lapansi losalimidwalo kukhala paradaiso. Atapitikitsidwa mu Edene, anafunikira kugwira ntchito zolimba ndi nyonga kuti apeze chakudya m’nthaka yotembereredwa. Mbadwa zawo, pokhala kuti zinalandira choloŵa cha mkhalidwe wauchimo ndi wakufa umenewu, zinakhala zofunikiradi chitonthozo.—Aroma 5:12.
Lonjezo Lopereka Chitonthozo Likwaniritsidwa
6. (a) Kodi ndi lonjezo lotonthoza lotani limene Mulungu anapereka pamene anthu anagwera m’tchimo? (b) Kodi Lameke anapereka ulosi wotani wonena za chitonthozo?
6 Poweruza amene anasonkhezera munthu kupanduka, Yehova anasonyeza kuti ali ‘Mulungu wa chitonthozo.’ (Aroma 15:5) Iye anachita zimenezo mwa kulonjeza kutumiza “mbewu” imene potsirizira pake idzamasula mbadwa za Adamu ku ziyambukiro zatsoka za chipanduko cha Adamu. (Genesis 3:15) M’kupita kwa nthaŵi, Mulungu anaperekanso zizindikiro za chilanditso chimenechi. Mwachitsanzo, anauzira Lameke, mbadwa yapatali ya Adamu kupyolera mwa mwana wake Seti, kunenera za zimene mwana wa Lameke adzachita: “Yemweyu adzatonthoza mtima wathu pa ntchito zathu zovuta za manja athu, chifukwa cha nthaka imene anaitemberera Yehova.” (Genesis 5:29) Mogwirizana ndi lonjezo limeneli, mnyamatayo anatchedwa Nowa, dzina limene limadziŵika kutanthauza “Kupuma” kapena “Chitonthozo.”
7, 8. (a) Kodi ndi mkhalidwe wotani umene unachititsa Yehova kumva chisoni kuti analenga munthu, ndipo kodi Iye anasankha kuchitaponji? (b) Kodi Nowa anakwaniritsa motani tanthauzo la dzina lake?
7 Mmene zinali motero, Satana ankasonkhanitsa otsatira ake pakati pa ena a angelo akumwamba. Iwowa anavala mathupi aumunthu ndi kudzatenga akazi okongola a mbadwa za Adamu kukhala akazi awo. Maukwati osakhala achibadwa amenewo anawonjezera kuipa kwa chitaganya cha anthu ndi kutulutsa fuko lopanda umulungu la Anefili, “ogwetsa,” omwe anadzaza dziko lapansi ndi chiwawa. (Genesis 6:1, 2, 4, 11; Yuda 6) “Ndipo anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu padziko lapansi . . . Ndipo Yehova anamva chisoni chifukwa anapanga munthu pa dziko lapansi, ndipo anavutika m’mtima mwake.”—Genesis 6:5, 6.
8 Yehova anafuna kuwononga dziko loipalo ndi chigumula cha dziko lonse, koma choyamba anauza Nowa kuti amange chingalawa chopulumutsiramo moyo. Chifukwa chake, fuko la anthu ndi mitundu ya nyama inapulumutsidwa. Nowa ndi banja lake ayenera kuti anapeza mpumulo chotani nanga Chigumulacho chitapita pamene anatuluka m’chingalawacho kuloŵa m’dziko loyeretsedwa! Nkotonthoza mtima chotani nanga kudziŵa kuti temberero pa nthaka linachotsedwa, zikumapangitsa ntchito yaulimi kukhala yopepuka kwambiri! Ndithudi, ulosi wa Lameke unakhaladi woona, ndipo Nowa anakwaniritsa tanthauzo la dzina lake. (Genesis 8:21) Monga mtumiki wokhulupirika wa Mulungu, Nowa anagwiritsiridwa ntchito kudzetsa ‘chitonthozo’ kwa anthu pamlingo winawake. Komabe, chisonkhezero choipa cha Satana ndi angelo ake auchiŵanda sichinathere pa Chigumula, ndipo anthu akupitiriza kubuula m’goli la uchimo, matenda, ndi imfa.
Wamkulu Kuposa Nowa
9. Kodi Yesu Kristu wasonyeza motani kuti ali wothandiza ndi wotonthoza kwa anthu olapa?
9 M’kupita kwa nthaŵi, kumapeto kwa zaka 4,000 za mbiri ya munthu, Mbewu yolonjezedwayo inafika. Atagwidwa ndi chikondi chachikulu pa anthu, Yehova Mulungu anatumiza Mwana wake wobadwa yekha padziko lapansi kudzafa monga dipo kaamba ka anthu ochimwa. (Yohane 3:16) Yesu Kristu akudzetsa chitonthozo chachikulu kwa ochimwa olapa amene akusonyeza chikhulupiriro mu imfa yake ya nsembe. Onse omwe amapatulira miyoyo yawo kwa Yehova ndi kukhala ophunzira obatizidwa a Mwana wake amapeza mpumulo ndi chitonthozo chokhalitsa. (Mateyu 11:28-30; 16:24) Mosasamala kanthu za kupanda ungwiro kwawo, iwo amapeza chimwemwe chachikulu m’kutumikira Mulungu ndi chikumbumtima choyera. Kumakhala kotonthoza chotani nanga kwa iwo kudziŵa kuti ngati apitiriza kusonyeza chikhulupiriro mwa Yesu, adzafupidwa ndi moyo wosatha! (Yohane 3:36; Ahebri 5:9) Ngati iwo achita tchimo lalikulu chifukwa cha kufooka ali ndi nkhoswe, kapena wotonthoza, mwa Ambuye Yesu Kristu woukitsidwayo. (1 Yohane 2:1, 2) Mwa kulapa tchimo loterolo ndi mwa kuchitapo kanthu mwa Malemba kuti asabwerezenso tchimolo, amapeza mpumulo, akumadziŵa kuti ‘Mulungu ali wokhulupirika ndi wolungama, amene amawakhululukira machimo awo.’—1 Yohane 1:9; 3:6; Miyambo 28:13.
10. Kodi timaphunziranji m’zozizwitsa zimene Yesu anachita pamene anali padziko lapansi?
10 Pamene anali padziko lapansi, Yesu anadzetsanso mpumulo mwa kumasula ogwidwa ndi ziŵanda, mwakuchiritsa mtundu uliwonse wa matenda, ndi mwa kuukitsa akufa okondedwa. Inde, zozizwitsa zoterozo zinali ndi phindu lapakanthaŵi chabe, pakuti aja omwe anadalitsidwa mwa njira imeneyo pambuyo pake anakalamba ndi kumwalira. Komabe, Yesu mwakutero anasonyeza madalitso achikhalire amtsogolo amene adzawatsanulira pa anthu onse. Tsopano, pokhala Mfumu yamphamvu yakumwamba, posachedwapa adzachita zoposa kungochotsa chabe ziŵanda. Adzaziponya izo m’phompho pamodzi ndi mtsogoleri wawo, Satana, mumkhalidwe wosachita kanthu. Ndiyeno Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi waulemerero udzayamba.—Luka 8:30, 31; Chivumbulutso 20:1, 2, 6.
11. Kodi nchifukwa ninji Yesu anadzitcha “mwini tsiku la Sabata”?
11 Yesu ananena kuti anali “mwini tsiku la Sabata,” ndipo nthaŵi zambiri iye anachiritsa pa tsiku la Sabata. (Mateyu 12:8-13; Luka 13:14-17; Yohane 5:15, 16; 9:14) Chifukwa ninji? Chabwino, Sabata linali m’Chilamulo cha Mulungu kwa Israyeli ndipo linatumikira monga “mthunzi wa zokoma zilimkudza.” (Ahebri 10:1) Masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito a mkati mwa mlungu amatikumbutsa za zaka 6,000 zapitazo za ukapolo wa munthu mu ulamuliro wotsendereza wa Satana. Tsiku la Sabata kumapeto kwa mlungu limatikumbutsa za mpumulo wopatsa chitonthozo umene anthu adzakhala nawo mkati mwa Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Nowa Wamkulu, Yesu Kristu.—Yerekezerani ndi 2 Petro 3:8.
12. Kodi ndi zochitika zopatsa chitonthozo zotani zimene tikuyembekezera ndi chidwi mtsogolo?
12 Ha, ndi mpumulo wotani nanga umene nzika za dziko lapansi za ulamuliro wa Kristu zidzakhala nawo, pamene potsirizira pake zidzakhala zomasukiratu ku chisonkhezero choipa cha Satana! Chitonthozo china chidzadza pamene adzachiritsidwa matenda akuthupi, a malingaliro, ndi a maganizo. (Yesaya 65:17) Ndiyeno, tangolingalirani za chisangalalo chawo pamene adzayamba kulandira okondedwa kuchokera kwa akufa! M’njira zimenezi Mulungu “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo.” (Chivumbulutso 21:4) Pamene mapindu a nsembe ya dipo ya Yesu akugwiritsiridwa ntchito pang’onopang’ono, nzika zomvera za Ufumu wa Mulungu zidzafikira ungwiro, zikumakhala zomasukiratu ku ziyambukiro zoipa zonse za uchimo wa Adamu. (Chivumbulutso 22:1-5) Pamenepo Satana adzamasulidwa “kanthaŵi.” (Chivumbulutso 20:3, 7) Anthu onse amene mokhulupirika amachirikiza uchifumu woyenera wa Yehova adzafupidwa ndi moyo wosatha. Tangolingalirani chisangalalo chosaneneka ndi mpumulo wa ‘kumasukiratu ku ukapolo wa chivundi.’ Chifukwa chake, anthu omvera adzasangalala ndi “ulemerero wa ana a Mulungu.”—Aroma 8:21.
13. Kodi nchifukwa ninji Akristu onse oona afunikira chitonthozo chimene Mulungu amapereka?
13 Pakali pano, tikupitiriza kubuula ndi kugwidwa m’zoŵaŵa zogwera onse okhala m’dongosolo loipa la Satana. Kuwonjezeka kwa matenda akuthupi ndi nsautso ya m’maganizo zikuvutitsa mitundu yonse ya anthu, kuphatikizapo Akristu okhulupirika. (Afilipi 2:25-27; 1 Atesalonika 5:14) Ndiponso, monga Akristu kaŵirikaŵiri timakumana ndi chitonzo ndi mazunzo omwe Satana amakundika pa ife chifukwa cha “kumvera Mulungu koposa anthu.” (Machitidwe 5:29) Chifukwa chake, kuti tipirire m’kuchita chifuniro cha Mulungu kufikira mapeto a dziko la Satana, tifunikira chitonthozo, chithandizo, ndi nyonga zimene Iye amapereka.
Kumene Tingapeze Chitonthozo
14. (a) Kodi ndi lonjezo lotani limene Yesu anapereka pa usiku wa imfa yake? (b) Kodi chofunika nchiyani kuti tipindule modzala ndi chitonthozo cha mzimu woyera wa Mulungu?
14 Pa usiku wa imfa yake, Yesu ananena momvekera bwino kwa atumwi ake okhulupirika kuti posachedwa adzawasiya ndi kubwerera kwa Atate wake. Zimenezi zinawavutitsa mtima ndi chisoni chachikulu. (Yohane 13:33, 36; 14:27-31) Pozindikira kufunika kwawo chitonthozo cha nthaŵi zonse, Yesu analonjeza kuti: “Ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe [“wotonthoza,” NW] ina, kuti akhale ndi inu ku nthaŵi yonse.” (Yohane 14:16) Yesu pano anali kunena za mzimu woyera wa Mulungu, umene unatsanuliridwa pa ophunzirawo masiku 50 pambuyo pa kuukitsidwa kwake.a Kuwonjezera pa zinthu zina, mzimu wa Mulungu unawatonthoza pokumana ndi mayesero ndi kuwalimbitsa kuti apitirize kuchita chifuniro cha Mulungu. (Machitidwe 4:31) Komabe, chithandizo choterocho sichiyenera kuonedwa monga chinthu chimene chimangofika chokha. Kuti apindule nawo mokwanira, Mkristu aliyense ayenera kupitiriza kupempherera chithandizo chopereka chitonthozo chimene Mulungu amapereka kupyolera mwa mzimu wake woyera.—Luka 11:13.
15. Kodi ndi njira zina ziti zimene Yehova amatipatsira chitonthozo?
15 Njira ina imene Mulungu amaperekera chitonthozo ndiyo mwa Mawu ake, Baibulo. Paulo analemba kuti: “Zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.” (Aroma 15:4) Zimenezi zimasonyeza kuti tifunikira nthaŵi zonse kuphunzira ndi kusinkhasinkha pa zinthu zolembedwa m’Baibulo ndi mabuku ozikidwa pa Baibulo. Tifunikiranso kumafika mokhazikika pamisonkhano yachikristu, kumene malingaliro opereka chitonthozo amafotokozedwa kuchokera m’Mawu a Mulungu. Chimodzi cha zifuno zazikulu za misonkhano imeneyo ndicho kulimbikitsana wina ndi mnzake.—Ahebri 10:25.
16. Kodi makonzedwe a Mulungu opatsa chitonthozo ayenera kutisonkhezera kuti tichitenji?
16 Kalata ya Paulo kwa Aroma imapitiriza kusonyeza zotulukapo zabwino zimene timalandira mwa kugwiritsira ntchito zogaŵira za Mulungu zopereka chitonthozo. “Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo,” analemba motero Paulo, “apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake, monga mwa Kristu Yesu; kuti nonse pamodzi, m’kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu.” (Aroma 15:5, 6) Inde, mwa kugwiritsira ntchito mokwanira mwaŵi wa zogaŵira za Mulungu zopatsa chitonthozo, tidzafanana kwambiri ndi Mtsogoleri wathu wolimbika mtima, Yesu Kristu. Izi zidzatisonkhezera kupitiriza kugwiritsira ntchito kamwa lathu kulemekeza Mulungu m’ntchito yathu yochitira umboni, pamisonkhano yathu, pocheza ndi okhulupirira anzathu, ndi m’mapemphero athu.
M’Nthaŵi za Mayesero Aakulu
17. Kodi Yehova anamtonthoza motani Mwana wake, ndi chotulukapo chotani?
17 Yesu ‘anathedwa nzeru’ ndipo ‘anagwidwa ndi chisoni’ pa usiku wa imfa yake yoŵaŵitsa. (Mateyu 26:37, 38) Motero iye anachoka pa ophunzira ake kamtunda pang’ono kukapempherera thandizo la Atate wake. “Anamveka popeza anawopa Mulungu.” (Ahebri 5:7) Baibulo limanena kuti “anamuonekera [Yesu] mngelo wakumwamba namlimbitsa iye.” (Luka 22:43) Njira yopanda mantha ndi yachimuna imene Yesu anayang’anizirana ndi omutsutsa ili umboni wakuti njira ya Mulungu yotonthozera Mwana wake inali yogwira ntchito koposa.—Yohane 18:3-8, 33-38.
18. (a) Kodi ndi nyengo iti m’moyo wa mtumwi Paulo imene inali ya mayesero aakulu kwenikweni? (b) Kodi tingakhale motani opereka chitonthozo kwa akulu ogwira ntchito zolimba ndi achifundo?
18 Mtumwi Paulo anapyola m’nthaŵi za mayesero aakulu. Mwachitsanzo, utumiki wake mu Efeso unali wodzaza ‘misozi, ndi mayesero anamugwera ndi ziwembu za Ayuda.’ (Machitidwe 20:17-20) Potsirizira pake, Paulo anachoka ku Efeso pambuyo poti ochirikiza mulungu wachikazi Artemi anabutsa chipolowe mumzindamo pa ntchito yake yolalikira. (Machitidwe 19:23-29; 20:1) Pamene Paulo anali paulendo womka kumpoto kumzinda wa Trowa, chinthu china chinamvutitsa maganizo kwambiri. Panthaŵi ina chipolowecho chisanabuke mu Efeso, anali atalandira uthenga wovutitsa maganizo. Magaŵano anali atabuka mumpingo watsopano ku Korinto, ndipo chisembwere chinali kulekereredwa kumeneko. Motero, kuchokera ku Efeso, Paulo analemba kalata ya uphungu wamphamvu pofuna kuwongolera mkhalidwewo. Chimenechi sichinali chinthu chopepuka kwa iye kuchita. “M’chisautso chambiri ndi kuŵaŵa mtima ndinalembera inu ndi misozi yambiri,” iye anavumbula motero pambuyo pake m’kalata yake yachiŵiri. (2 Akorinto 2:4) Mofanana ndi Paulo, akulu achifundo samakupeza kukhala kopepuka kupereka uphungu wa kuwongolera ndi chidzudzulo, chifukwa chakuti kumbali ina amazindikiranso bwino kwambiri za zofooka za iwo eni. (Agalatiya 6:1) Pamenepo, tiyeni tikhale otonthoza kwa atsogoleri athu mwa kulabadira mwachikondi uphungu wozikidwa pa Baibulo.—Ahebri 13:17.
19. Kodi nchifukwa ninji Paulo anapitiriza ulendo kuchokera ku Trowa kumka ku Makedoniya, ndipo potsirizira pake anaupeza motani mpumulo?
19 Pamene anali mu Efeso, Paulo sanangolembera abale m’Korinto koma anatumizanso Tito kuti akawathandize, akumamtuma kuti akabweze lipoti lonena za kulabadira kwawo kalatayo. Paulo anapita ku Trowa ndi chiyembekezo cha kukakumana ndi Tito. Kumeneko Paulo anapeza mipata yabwino ya kupanga ophunzira. Koma zimenezi sizinathetse nkhaŵa yake chifukwa chakuti Tito anali asanafikebe. (2 Akorinto 2:12, 13) Chotero anapitiriza ulendo kumka ku Makedoniya, akumati akakumana ndi Tito komweko. Nkhaŵa ya Paulo inangokulirako pamene anakumana ndi chitsutso chachikulu pa utumiki wake. “Pakudza ife m’Makedoniya,” iye akufotokoza motero, “thupi lathu linalibe mpumulo, koma tinasautsidwa ife monsemo; kunjako zolimbana, m’katimo mantha. Koma Iye amene atonthoza odzichepetsa, ndiye Mulungu, anatitonthoza ife ndi kufika kwake kwa Tito.” (2 Akorinto 7:5, 6) Chinali chitonthozo chotani nanga pamene potsirizira pake Tito anafika kudzauza Paulo za mmene Akorinto analabadirira bwino kalata yake!
20. (a) Mofanana ndi chochitika cha Paulo, kodi ndi njira ina iti yofunika imene Yehova amaperekera chitonthozo? (b) Kodi tidzakambitsirananji m’nkhani yotsatira?
20 Chokumana nacho cha Paulo nchotonthoza kwa atumiki a Mulungu lerolino, ambiri amene akukumananso ndi mayesero amene amawachititsa kukhala “odzichepetsa (“otaya mtima,” Chipangano Chatsopano) kapena “opsinjika.” (Phillips) Inde, ‘Mulungu wa chitonthozo’ amadziŵa zosoŵa za mmodzi ndi mmodzi ndipo akhoza kutigwiritsira ntchito kukhala otonthoza kwa wina ndi mnzake, monga momwe Paulo anapezera chitonthozo ndi lipoti la Tito lonena za mtima wolapa wa Akorinto. (2 Akorinto 7:11-13) M’nkhani yathu yotsatira, tidzakambitsirana za yankho la Paulo lotonthoza mtima kwa Akorinto ndi mmene lingatithandizire kupeza chitonthozo cha Mulungu lerolino.
[Mawu a M’munsi]
a Imodzi ya ntchito zazikulu za mzimu wa Mulungu pa Akristu a m’zaka za zana loyamba inali kuwadzoza monga ana olera auzimu a Mulungu ndi abale a Yesu. (2 Akorinto 1:21, 22) Zimenezi zimangochitika kwa ophunzira a Kristu okwanira 144,000. (Chivumbulutso 14:1, 3) Lerolino, Akristu ochuluka apatsidwa chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso. Ngakhale kuti sali odzozedwa, iwonso amalandirako chithandizo ndi chitonthozo cha mzimu woyera wa Mulungu.
Kodi Mungayankhe?
◻ Kodi zinachitika motani kuti anthu afunikire chitonthozo?
◻ Kodi Yesu wasonyeza motani kukhala wamkulu kuposa Nowa?
◻ Kodi nchifukwa ninji Yesu anadzitcha “mwini tsiku la Sabata”?
◻ Kodi Mulungu amapereka motani chitonthozo lerolino?
[Mapu/Chithunzi patsamba 10]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Paulo anapeza chitonthozo chachikulu m’lipoti la Tito lonena za Akorinto
MAKEDONIYA
Filipi
GIRISI
Korinto
ASIYA
Trowa
Efeso