Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Nzeru Ili Ndi Odzichepetsa”
    Nsanja ya Olonda—2000 | August 1
    • Paulo​—‘Mtumiki’ Komanso ‘Mdindo’

      4. Kodi Paulo anasangalala ndi madalitso apadera otani?

      4 Paulo anali munthu wotchuka kwambiri pakati pa Akristu oyambirira, ndipotu m’pomveka. M’kati mwa utumiki wake, anayenda makilomita ochuluka panyanja ndi pamtunda pomwe ndipo anayambitsa mipingo yambirimbiri. Komanso, Yehova anadalitsa Paulo ndi masomphenya ndi mphatso ya kulankhula m’malilime. (1 Akorinto 14:18; 2 Akorinto 12:1-5) Mulungu anauziranso Paulo kulemba makalata 14 omwe tsopano ali mbali ya Malemba Achigiriki Achikristu. Mwachionekere, tingatero kuti ntchito yomwe Paulo anagwira inaposa ya atumwi ena onse.​—1 Akorinto 15:10.

      5. Kodi Paulo anasonyeza motani kuti sanali kudziona ngati wapamwamba?

      5 Popeza kuti Paulo anali mtsogoleri wantchito zachikristu, mwina ena angayembekeze kuti anali kusangalala chifukwa cha kutchukako, ngakhalenso kuonetsera udindo wake modzitama. Koma Paulo sanachite zimenezo popeza kuti anali wodzichepetsa. Anadzitcha “wamng’ono wa atumwi,” akumawonjezera kuti: “Ndine wosayenera kutchedwa mtumwi, popeza ndinalondalonda Eklesia wa Mulungu.” (1 Akorinto 15:9) Paulo yemwe kale anali wozunza Akristu, sanaiŵale kuti kunali kokha mwa chisomo kuti anatha kupanga ubwenzi ndi Mulungu, makamakanso kusangalala ndi mwayi wapadera wa utumiki. (Yohane 6:44; Aefeso 2:8) Choncho Paulo sanadzimve kuti zomwe ankachita mwachipambano muutumiki zinam’panga kukhala wapamwamba kwa ena.​—1 Akorinto 9:16.

      6. Kodi Paulo anasonyeza motani kudzichepetsa pochita ndi Akorinto?

      6 Kudzichepetsa kwa Paulo kunali kuonekera makamaka momwe anali kuchitira ndi Akorinto. Zikuoneka kuti ena a iwo ankakonda kwambiri omwe anali kuŵalingalira kuti anali oyang’anira otchuka kuphatikizapo Apolo, Kefa, ndi Paulo yemwe. (1 Akorinto 1:11-15) Koma Paulo sanapemphe Akorintowo kuti adzim’tamanda kapena kutengerapo mwayi pa kukopeka kwawoko. Pamene anali kuŵachezera, sanalankhule kwa iwo “ndi kuposa kwa mawu, kapena kwa nzeru.” M’malo mwake, ponena za iye mwini ndi anzake Paulo anati: “Chotero munthu atiyese ife, monga atumiki a Kristu, ndi adindo a zinsinsi za Mulungu.”a​—1 Akorinto 2:1-5; 4:1.

      7. Kodi Paulo anasonyeza motani kudzichepetsa ngakhale popereka uphungu?

      7 Paulo anasonyezanso kudzichepetsa popereka uphungu wamphamvu ndi malangizo. Iye anachonderera Akristu anzakewo “mwa zifundo za Mulungu” ndinso “mwa chikondi” osati chifukwa cha kukula kwa udindo womwe anali nawo monga mtumwi. (Aroma 12:1, 2; Filemoni 8, 9) Kodi Paulo anachitiranji zimenezi? Chifukwa chake n’chakuti analidi kudziona monga wantchito ‘wothandizana’ ndi abale akewo, osati monga ‘wochita ufumu pa chikhulupiriro chawo.’ (2 Akorinto 1:24) Mosakayika kunali kudzichepetsa kwa Pauloku komwe kunathandiza kuti akhale wokondedwa kwambiri ndi mipingo yachikristu ya m’zaka za zana loyamba.​—Machitidwe 20:36-38.

  • “Nzeru Ili Ndi Odzichepetsa”
    Nsanja ya Olonda—2000 | August 1
    • a Mawu achigiriki otembenuzidwa kuti “atumiki” angaimire kapolo wopalasa ngalawa yaikulu pogwiritsa ntchito zopalasira zakunthungo m’ngalawamo. Mosiyana ndi zimenezo, “adindo” angapatsidwe maudindo ambiri, mwinamwake kuyang’anira munda waukulu. Komabe, kwa olamulira ambiri, mdindo sanali kum’siyanitsa ndi mtumiki wopalasa ngalawayo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena