Kuzindikira Kukuchinjirizeni
“Kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakuchinjiriza.”—MIYAMBO 2:11.
1. Kodi kuzindikira kungatichinjirize ku chiyani?
YEHOVA akufuna kuti musonyeze kuzindikira. Chifukwa ninji? Chifukwa amadziŵa kuti kudzakuchinjirizani ku ngozi zosiyanasiyana. Miyambo 2:10-19 imayamba ndi mawu akuti: “Pakuti nzeru idzaloŵa m’mtima mwako, moyo wako udzakondwera ndi kudziŵa, kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakuchinjiriza.” Kukuchinjirizani ku chiyani? Ku zinthu zonga “njira yoipa,” aja osiya njira yoongoka, ndi anthu okhotetsa mayendedwe awo.
2. Kodi kuzindikira nchiyani, ndipo Akristu makamaka amafuna kuzindikira kotani?
2 Mwina mukukumbukira kuti kuzindikira ndiko luso la maganizo limene iwo amasiyanitsira chinthu china ndi chinzake. Munthu wozindikira amaona kusiyana kwa malingaliro kapena zinthu ndipo amaganiza bwino. Monga Akristu, timafuna makamaka kuzindikira kwauzimu kozikidwa pa chidziŵitso cholongosoka cha Mawu a Mulungu. Pamene tiphunzira Malemba, timachita monga ngati tikukumba miyala yomangira kuzindikira kwauzimu. Zimene timaphunzira zingatithandize kupanga zosankha zimene zimakondweretsa Yehova.
3. Kodi kuzindikira kwauzimu tingakupeze motani?
3 Pamene Mulungu anafunsa Mfumu Solomo ya Israyeli dalitso limene iye anafuna, wolamulira wachichepereyo anati: “Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa.” Solomo anapempha kuzindikira, ndipo Yehova anampatsa iye pamlingo waukulu. (1 Mafumu 3:9; 4:30) Kuti tipeze kuzindikira, tifunikira kupemphera, ndipo tiyeneranso kuphunzira Mawu a Mulungu mothandizidwa ndi zofalitsa zounikira zogaŵiridwa kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Zimenezi zidzatithandiza kukhala ndi kuzindikira kwakukulu kwauzimu kwakuti tidzakhala ‘akulu misinkhu m’chidziŵitso,’ okhoza “kusiyanitsa [kapena, kuzindikira] chabwino ndi choipa.”—1 Akorinto 14:20; Ahebri 5:14.
Kuzindikira Nkofunika Kwambiri
4. Kodi kukhala ndi diso “langwiro” kumatanthauzanji, ndipo lingatithandize bwanji?
4 Ndi kuzindikira koyenera, tingachite mogwirizana ndi mawu a Yesu Kristu akuti: “Muthange mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake [cha Mulungu], ndipo zonse zimenezo [zakuthupi] zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:33) Yesu anatinso: “Nyali ya thupi ndiyo diso lako; pamene paliponse diso lako lili langwiro thupi lako lonse liunikidwanso monsemo.” (Luka 11:34) Diso ndilo nyali yophiphiritsira. Diso “langwiro” limaona bwino, limasumika bwino. Ndi diso lotero, tingasonyeze kuzindikira ndi kuyenda popanda kukhumudwa mwauzimu.
5. Ponena za malonda, kodi tiyenera kukumbukiranji za cholinga cha mipingo yachikristu?
5 M’malo mokhala ndi diso langwiro, ena avutitsa moyo wawo ndi wa ena mwa machitachita okopa amalonda. Koma tiyenera kukumbukira kuti mpingo wachikristu ndiwo “mzati ndi mchirikizo wa choonadi.” (1 Timoteo 3:15) Monga mizati ya nyumba, mpingo umachirikiza choonadi cha Mulungu, osati malonda a munthu aliyense. Mipingo ya Mboni za Yehova siinakhazikitsidwe kuti ikhale malo ochirikiza zinthu zamalonda, katundu, kapena mautumiki. Tiyenera kupeŵa kukambitsirana nkhani zaumwini zamalonda pa Nyumba ya Ufumu. Kuzindikira kumatithandiza kuona kuti Nyumba za Ufumu, Maphunziro a Buku a Mpingo, misonkhano yadera, ndi yazigawo ya Mboni za Yehova zili malo a kuyanjana kwachikristu ndi makambitsirano auzimu. Ngati tikugwiritsira ntchito maunansi auzimu kuchirikizira malonda amtundu uliwonse, kodi zimenezo sizingasonyeze kusoŵeka kwa chiyamikiro cha miyezo yauzimu? Musagwiritsire ntchito anthu pampingo kupezerapo phindu la ndalama.
6. Kodi nchifukwa ninji katundu wamalonda ndi mautumiki ake sitiyenera kuzigulitsa kapena kuzisatsira pamisonkhano ya mpingo?
6 Ena agwiritsira ntchito maunansi ateokrase kusatsa zothandizira thanzi kapena zothandizira kukongola, mankhwala amavitameni, mautumiki amafoni, mirimo yomangira, zamaulendo, maprogramu a makompyuta ndi zipangizo zake, ndi zina zotero. Komatu, misonkhano ya mpingo siili malo ogulitsirako kapena osatsirako katundu wamalonda kapena mautumiki ake. Tikhoza kuzindikira pulinsipulo lofunika panopo ngati tikumbukira kuti Yesu “anatulutsa onse m’kachisimo, ndi nkhosa ndi ng’ombe; nakhuthula ndalama za osinthanawo, nagubuduza magome; nati kwa iwo akugulitsa nkhunda, Chotsani izi muno; musamayesa nyumba ya Atate wanga nyumba ya malonda.”—Yohane 2:15, 16.
Bwanji Nanga za Kuikiza Ndalama?
7. Nchifukwa ninji pafunika kuzindikira ndi kusamala pankhani ya kuikiza ndalama?
7 Zonse ziŵiri kuzindikira ndi kusamala zifunika pamene mukulingalira zoikiza ndalama m’malonda. Tinene kuti wina afuna kubwereka ndalama ndipo akupanga malonjezo otere: “Ndikutsimikizani kuti mudzapanga ndalama.” “Simudzataya kalikonse. Mudzapindulatu.” Samalani pamene wina apereka malonjezo otero. Angakhale akulota kapena ali wosaona mtima, pakuti nthaŵi zambiri kuikiza ndalama sikotsimikizika ayi. Kunena zoona, anthu osyasyalika opanda khalidwe akwangwanutsa ena mumpingo. Zimenezi zimatikumbutsa za “anthu osapembedza” amene anakwaŵira m’tseri kuloŵa mumpingo wa m’zaka za zana loyamba ‘nasandutsa chisomo cha Mulungu chikhale chilakolako chonyansa.’ Iwo anali ngati zimiyala zojenya za pansi pa madzi zimene zikanatumbula ndi kupha osambira. (Yuda 4, 12) Zoona, zolinga za onyenga zimasiyana, koma nawonso amalalira a mumpingo.
8. Kodi chachitika nchiyani m’malonda ooneka ngati aphindu?
8 Ngakhale Akristu okhala ndi zolinga zabwino agaŵana ndi ena chidziŵitso cha malonda ooneka ngati aphindu, ndipo iwo, limodzi ndi aja amene anatsatira chitsanzo chawo, ataya ndalama zimene anaikiza. Chifukwa chake, Akristu ambiri ataya mathayo awo mumpingo. Malonda olemeretsa msangawo atakhala chinyengo, amene amapindula ndi wonyenga yekhayo basi, amenenso amathaŵa nthaŵi yomweyo. Kodi kuzindikira kungamthandize motani munthu kupeŵa mikhalidwe yotero?
9. Kodi nchifukwa ninji pafunika kuzindikira popenda zonena za ena za kuikiza ndalama?
9 Kuzindikira kumapereka lingaliro la kukhoza kumvetsa chinthu chosadziŵika bwino. Timafunika luso limeneli kuti tipende zimene wina akunena pa zakuikiza ndalama. Akristu amakhulupirirana, ndipo ena angaganize kuti abale ndi alongo awo auzimu sangaloŵe m’malonda angozi amene angawononge chuma cha okhulupirira anzawo. Koma chifukwa chokha chakuti mwini malonda ndi Mkristu sindicho chitsimikizo chakuti amachita bwino m’zamalonda kapena kuti malonda ake adzayenda bwino.
10. Kodi nchifukwa ninji Akristu ena amafuna maloni kwa okhulupirira anzawo, ndipo chingachitikire ndalama zoikizazo nchiyani?
10 Akristu ena amafuna maloni a malonda kwa okhulupirira anzawo chifukwa chakuti mabungwe omveka okongoletsa ndalama sangayese kuwakongoletsa ndalama za malonda awo angozi. Ambiri apusitsidwa kukhulupirira kuti mwa kungoikiza ndalama zawo, adzalemera msanga ndiponso popanda kugwiritsa ntchito kapena mwinamwake popanda ntchito iliyonse. Ena amakopeka ndi malonda a kuikiza ndalamawo chifukwa cha chikoka chake, nataya ndalama zomwe anasunga kwa moyo wonse! Mkristu wina anaikiza ndalama zambiri m’malonda, pokhulupirira kuti adzalandira phindu lokwanira 25 peresenti m’milungu iŵiri chabe. Anataya ndalama zake zonsezo pamene kampaniyo inalengeza kuti yalephera kubweza ngongole! M’malonda ena, wogula malo, kumangapo nyumba ndi kuzigulitsa anakongola ndalama zochuluka kwa ena mumpingo. Analonjeza mapindu ochuluka kopambanitsa koma malonda ake anagwa nataya ndalama zobwerekazo.
Pamene Malonda Alephereka
11. Kodi Paulo anapereka uphungu wotani pa umbombo ndi chikondi cha pandalama?
11 Kulephereka kwa malonda pakati pa Akristu kwagwiritsa ena mwala ndipo kwatayitsa ngakhale mkhalidwe wauzimu wa ena amene analoŵa m’malonda angozi. Kulephera kulola kuzindikira kuwachinjiriza kwadzetsa chisoni ndi kuipidwa. Umbombo wakola anthu ambiri. ‘Chisiriro, chisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima,’ analemba motero Paulo. (Aefeso 5:3) Ndipo anachenjeza nati: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko. Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama; chimene ena pochikhumba, anasokera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.”—1 Timoteo 6:9, 10.
12. Ngati Akristu achita malonda wina ndi mnzake, kodi makamaka afunikira kukumbukira chiyani?
12 Ngati Mkristu akhala ndi chikondi cha pandalama, angadzivulaze kwambiri mwauzimu. Afarisi anali kukonda ndalama, ndipo umenewu ndiwo mkhalidwe wa anthu ambiri masiku ano otsiriza. (Luka 16:14; 2 Timoteo 3:1, 2) Komabe, moyo wa Mkristu uyenera kukhala “wosakonda chuma.” (Ahebri 13:5) Inde, Akristu angachite malonda wina ndi mnzake kapena kuyamba malonda pamodzi. Komabe, pamene achita zimenezo, makambitsiranowo ndi kumvana siziyenera kuphatikizidwa pamodzi ndi zochitika za mpingo. Ndipo kumbukirani: Ngakhale pakati pa abale auzimu, nthaŵi zonse lembani pa pepala mapangano a malonda. Imene ingakuthandizeni kwambiri pambaliyi ndi nkhani yakuti “Zilembeni!” yofalitsidwa mu Galamukani! wachingelezi wa February 8, 1983, masamba 13 mpaka 15.
13. Kodi mungaigwiritsire ntchito motani Miyambo 22:7 pamalonda?
13 Miyambo 22:7 imatiuza kuti: “Wokongola ndiye kapolo wa womkongoletsa.” Kaŵirikaŵiri kumakhala kopanda nzeru kwa ife kudziika ife eni kapena mbale wathu m’malo a kapolo. Pamene wina atipempha kuti timkongoletse ndalama za malonda, kungakhale kwanzeru kulingalira ngati iye akhoza kubwezera ndalamayo. Kodi ali ndi mbiri ya kukhulupirika ndi kudalirika? Ndithudi, tiyenera kudziŵa kuti kupereka loni imeneyo kungatanthauzenso kutaya ndalamayo chifukwa malonda ambiri atsopano amalephera. Pangano lokha si chitsimikizo chakuti malonda adzayenda bwino. Ndipotu sikuli kwanzeru kwa aliyense kuika pangozi m’malonda ndalama zambiri zimene sangafune kutaya.
14. Nchifukwa ninji tifunikira kusonyeza kuzindikira ngati takongoletsa ndalama Mkristu mnzathu amene malonda ake sanayende bwino?
14 Tifunikira kusonyeza kuzindikira ngati takongoletsa Mkristu ndalama za malonda ndipo ndalamazo zawonongeka, ngakhale panalibe kusaona mtima. Ngati kusayenda bwino kwa malonda sikunali chifukwa cha wokhulupirira mnzathu amene anakongola ndalama, kodi tinganene kuti anatilakwira? Ayi, chifukwa chakuti tinapereka loniyo mwaufulu, mwinamwake takhala tikulandira phindu lake, ndipo palibe kusaona mtima kulikonse kumene kwachitika. Popeza kuti panalibe kusaona mtima, tilibe chifukwa chosumira mlandu wokongolayo. Kodi ndi ubwino wanji umene kusumira mlandu kungamchitire Mkristu mnzathu woona mtimayo amene anachita kulengeza mwalamulo kuti analephera kubweza ngongole chifukwa malonda ake olongosoka sanayende bwino?—1 Akorinto 6:1.
15. Kodi ndi zinthu ziti zofunika kuzilingalira ngati wina walengeza mwalamulo kuti walephera kubweza ngongole?
15 Nthaŵi zina anthu akaona kuti malonda awo sakuyenda bwino amafuna mpumulo mwa kulengeza mwalamulo kuti alephera kubweza ngongole. Popeza Akristu samanyalanyaza ngongole, ena chikumbumtima chawo chawasonkhezera kuyesa kubwezera ngongole zofafanizidwazo ngati amene anawakongoletsa angavomereze, ngakhale pambuyo poti amasulidwa mwalamulo pangongole zina. Koma bwanji ngati wokongolayo wataya ndalama za mbale wake ndiyeno akhalabe ndi moyo wapamwamba ndithu? Kapena bwanji ngati wokongolayo wapeza ndalama zobwezera ngongoleyo koma nkunyalanyaza mangawa ake andalama kwa mbale wakeyo? Zimenezo zitachitika, zimakayikitsa ziyeneretso zake za kutumikira pamalo athayo mumpingo.—1 Timoteo 3:3, 8; onani Nsanja ya Olonda ya September 15, 1994, masamba 30-1.
Bwanji Ngati Pali Chinyengo?
16. Kodi tingachitenji ngati tiganiza kuti wina watinyenga pamalonda?
16 Kuzindikira kumatithandiza kudziŵa kuti si kuikiza konse kumene kumadzetsa mapindu. Nanga bwanji ngati pali chinyengo? Chinyengo ndicho “kuchenjeretsa dala, kukwangwanutsa, kapena kupotoza choonadi ndi cholinga cha kusonkhezera wina kulepa chinthu chake chamtengo wapatali kapena kupereka chimene mwalamulo nchake.” Yesu Kristu analongosola njira zimene munthu angatsatire pamene aganiza kuti wolambira mnzake wamnyenga. Malinga ndi Mateyu 18:15-17, Yesu anati: “Ngati mbale wako akuchimwira iwe, pita, numlangize panokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako. Koma ngati samvera, onjeza kutenga ndi iwe wina mmodzi kapena aŵiri, kuti atsimikizidwe mawu onse pakamwa pa mboni ziŵiri kapena zitatu. Ndipo ngati iye samvera iwo, uuze mpingo; ndipo ngati iye samveranso mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.” Fanizo limene Yesu anapereka pambuyo pake limasonyeza kuti iye anali kuganiza za machimo okhudza nkhani za ndalama, kuphatikizapo chinyengo.—Mateyu 18:23-35.
17, 18. Ngati wodzitcha Mkristu watinyenga, kodi kuzindikira kungatichinjirize motani?
17 Inde, sipangakhale maziko a m’Malemba otsatirira njira yolongosoledwa pa Mateyu 18:15-17 ngati palibe umboni kapena ngakhale lingaliro lakuti pali chinyengo. Komano, bwanji ngati wodzitcha Mkristu anatinyengadi? Kuzindikira kudzatichinjiriza kuti tisachite chinthu chimene chingapereke chithunzi choipa pampingo. Paulo analangiza Akristu anzake kulola kuipsidwa ngakhale kunyengedwa m’malo mopitira mbale kukhoti.—1 Akorinto 6:7.
18 Abale athu ndi alongo athu enieni saali ‘odzala ndi chinyengo chonse ndi chenjerero lonse,’ monga wamatsenga uja Baryesu. (Machitidwe 13:6-12) Chotero tigwiritsire ntchito kuzindikira pamene ndalama zathu zatayika m’malonda a okhulupirira anzathu. Ngati tikuganiza zowasumira mlandu, tiyenera kulingalira za zimene zingachitikire ife enife, munthuyo kapena anthuwo, mpingo, ndi akunja. Kufunafuna malipo kungawononge nthaŵi yathu yochuluka, nyonga, ndi chuma china. Kungangolemeza maloya ndi akatswiri ena. Nzachisoni kuti Akristu ena alepa mathayo ateokrase chifukwa cha kutanganidwa kwambiri ndi zinthu zimenezi. Mosakayika, kuchenjenekedwa kwathu mwanjirayi kumakondweretsa Satana, koma timafuna kukondweretsa mtima wa Yehova. (Miyambo 27:11) Komabe, kuvomereza kwathu kutayikidwako kungatipeŵetse chisoni ndipo nthaŵi yathu yochuluka ndi ya akulu yomwe ingasungike. Kudzatithandiza kusunga mtendere wa mpingo ndiponso kudzatilola kufunafuna Ufumu choyamba.
Kuzindikira Popanga Zosankha
19. Kodi kuzindikira kwauzimu ndi pemphero zingatichitirenji popanga zosankha zovuta?
19 Kupanga zosankha m’zandalama kapena m’zamalonda kumavuta kwambiri. Koma kuzindikira kwauzimu kungatithandize kupenda zinthu zonse ndi kupanga zosankha zanzeru. Ndiponso, kudalira Yehova mwa pemphero kungatipatse “mtendere wa Mulungu.” (Afilipi 4:6, 7) Ndiwo bata ndi kudekha mtima zimene zimadza ndi unansi waumwini wolimba ndi Yehova. Ndithudi, mtendere umenewu ungatithandize kukhalabe okhazikika pamene tifunikira kupanga zosankha zovuta.
20. Kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchitanji pankhani za malonda ndi za mpingo?
20 Titsimikizetu mtima kusalola mikangano ya malonda kusokoneza mtendere wathu kapena wa mpingo. Tiyenera kukumbukira kuti mpingo wachikristu ulipo kutithandiza ife mwauzimu, osati kutumikira monga malo a malonda. Nthaŵi zonse, nkhani za malonda siziyenera kuphatikizidwa pamodzi ndi zochitika za mpingo. Tiyenera kugwiritsira ntchito kuzindikira ndi kusamala pamene tikuloŵa m’zamalonda. Ndipo tiyeni nthaŵi zonse tikhale ndi lingaliro loyenera pankhani zotero, ndi kufunafuna zinthu za Ufumu choyamba. Ngati malonda a olambira anzathu sanayende bwino, tiyesetsetu kuchita zokomera onse ophatikizidwamo.
21. Kodi tingagwiritsire ntchito bwanji kuzindikira ndi kuchita mogwirizana ndi Afilipi 1:9-11?
21 M’malo motanganidwa kwambiri ndi nkhani zandalama ndi zinthu zina zosafunika kwenikweni, ife tonse tilozetsetu mtima wathu kukuzindikira, kupempherera chitsogozo cha Mulungu, ndi kuika zinthu za Ufumu patsogolo. Mogwirizana ndi pemphero la Paulo, ‘chikondi chathu chisefukire chiwonjezere m’chidziŵitso [cholongosoka] ndi kuzindikira konse kuti tiyese zinthu zosiyana osalakwa [titsimikizire zinthu zofunika kwambiri osakhumudwitsa ena]’ kapena ife eni. Tsopano, popeza Kristu Mfumu ali pa mpando wake wachifumu kumwamba, tiyeni tisonyeze kuzindikira kwauzimu m’mbali iliyonse ya moyo wathu. Ndipotu ‘tidzale nacho chipatso cha chilungamo, chimene chili mwa Yesu Kristu, kuchitira Mulungu,’ Ambuye Mfumu Yehova, “ulemerero ndi chiyamiko.”—Afilipi 1:9-11.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi kuzindikira nchiyani?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuzindikira nkofunika kwambiri m’nkhani zamalonda pakati pa Akristu?
◻ Kodi kuzindikira kungatithandize bwanji ngati tiganiza kuti wokhulupirira mnzathu watinyenga?
◻ Kodi kuzindikira kuli ndi ntchito yanji popanga zosankha?
[Chithunzi patsamba 18]
Kuzindikira kudzatithandiza kutsatira uphungu wa Yesu wa kufunafuna Ufumu choyamba
[Zithunzi patsamba 20]
Nthaŵi zonse lembani mapangano a malonda