-
Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
7. Ufumu wa Mulungu uli ndi malamulo abwino kwambiri
Maboma a anthu amapanga malamulo omwe amayenera kuthandiza ndi kuteteza nzika zawo. Nawonso Ufumu wa Mulungu uli ndi malamulo amene nzika zake zimayenera kuwatsatira. Werengani 1 Akorinto 6:9-11, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi mukuganiza kuti zinthu zidzakhala bwanji padzikoli aliyense akamadzatsatira malamulo a Mulungu?a
Yehova amayembekezera kuti nzika za Ufumu wake zizitsatira malamulo ake, kodi mukuganiza kuti zimene Yehova amafunazi n’zoyenera? N’chifukwa chiyani mukutero?
Ndi mfundo iti imene ikusonyeza kuti anthu amene satsatira malamulo amenewa atha kusintha?—Onani vesi 11.
Maboma amakhazikitsa malamulo n’cholinga chofuna kuthandiza ndi kuteteza nzika zawo. Ufumu wa Mulungu uli ndi malamulo abwino kwambiri omwe amathandiza ndi kuteteza nzika zake
-
-
Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kugonana?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
PHUNZIRO 41
Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kugonana?
Anthu ambiri amaona kuti nkhani zokhudza kugonana ndi zoumitsa pakamwa. Komabe, Baibulo likamanena zokhudza kugonana, limanena zinthu mosapita m’mbali, koma mwaulemu. Ndipo zimene limanena n’zothandiza kwambiri. Zimenezi ndi zomveka chifukwa Yehova ndi amene anatilenga. Choncho amadziwa bwino zimene zingatithandize kuti tizikhala ndi moyo wabwino. Iye amatiuza zimene tiyenera kuchita kuti tizimusangalatsa ndiponso zimene zingatithandize kuti tizisangalala ndi moyo kuyambira panopa mpaka kalekale.
1. Kodi maganizo a Yehova ndi otani pa nkhani ya kugonana?
Kugonana ndi mphatso yochokera kwa Yehova yomwe anapereka kwa anthu okwatirana kuti azisangalala nayo. Mphatsoyi simangothandiza anthu kuti azibereka ana basi, koma imawathandizanso kuti azisonyezana chikondi n’kumasangalala. N’chifukwa chake Mawu a Mulungu amati: “Usangalale ndi mkazi wapaunyamata wako.” (Miyambo 5:18, 19) Yehova amayembekezera kuti Akhristu okwatirana azikhala okhulupirika m’banja, choncho sangachite chigololo.—Werengani Aheberi 13:4.
2. Kodi chiwerewere n’chiyani?
Baibulo limatiuza kuti “adama [achiwerewere] . . . sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:9, 10) Olemba Baibulo ena amene analilemba m’Chigiriki anagwiritsa ntchito mawu akuti por·neiʹa ponena za chiwerewere. Mawuwa amanena za (1) kugonanaa kwa anthu amene sali pabanja, (2) kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha, komanso (3) kugonana ndi nyama. Timasangalatsa Yehova komanso timakhala ndi moyo wabwino tikamayesetsa “kupewa dama” kapena kuti chiwerewere.—1 Atesalonika 4:3.
FUFUZANI MOZAMA
Onani zimene mungachite kuti mupewe chiwerewere komanso phindu limene mungapeze ngati mutayesetsa kukhalabe ndi makhalidwe oyera.
3. Muziyesetsa kupewa chiwerewere
Yosefe, yemwe anali munthu wokhulupirika, anakana kugonana ndi mzimayi yemwe ankamunyengerera kuti achite naye zachiwerewere. Werengani Genesis 39:1-12, kenako mukambirane mafunso awa:
N’chifukwa chiyani Yosefe anakana kuchita chiwerewere?—Onani vesi 9.
Kodi mukuganiza kuti Yosefe anachita zinthu mwanzeru? N’chifukwa chiyani mukutero?
Kodi masiku ano achinyamata angatsanzire bwanji Yosefe pa nkhani yokana kuchita chiwerewere? Onerani VIDIYO.
Yehova amafuna kuti tonsefe tiziyesetsa kupewa chiwerewere. Werengani 1 Akorinto 6:18, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi ndi zinthu ziti zomwe zingapangitse munthu kuchita chiwerewere?
Kodi mungatani kuti mupewe kuchita chiwerewere?
4. Yesetsani kuti musagonje pa mayesero
N’chiyani chingapangitse kuti munthu agonje mosavuta akamayesedwa kuti achite chiwerewere? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.
Kodi m’bale wamuvidiyoyi anachita chiyani atazindikira kuti zinthu zina zimene amaganiza ndi kuchita zikanachititsa kuti asiye kukhala wokhulupirika kwa mkazi wake?
Ngakhale Akhristu okhulupirika amafunika kuchita khama kuti asamaganizire zinthu zoipa. Kodi mungatani kuti musamaganizire zinthu zachiwerewere? Werengani Afilipi 4:8, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi ndi zinthu ziti zimene tiyenera kumaziganizira?
Kodi kuwerenga Baibulo komanso kukhala ndi zochita zambiri potumikira Yehova kungatithandize bwanji kuti tipewe mayesero?
5. Mfundo za Yehova zimatithandiza kukhala ndi moyo wabwino
Yehova amafuna kuti zinthu zizitiyendera bwino. Iye amatiuza zimene tingachite kuti tikhale ndi makhalidwe oyera komanso ubwino wochita zimenezi. Werengani Miyambo 7:7-27 kapena onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.
Kodi mnyamatayu anachita chiyani chomwe chikanatha kumulowetsa m’mayesero?—Onani Miyambo 7:8, 9.
Lemba la Miyambo 7:23, 26, limasonyeza kuti kuchita chiwerewere kukhoza kutibweretsera mavuto aakulu. Ndiye kodi tingapewe mavuto ati tikamayesetsa kukhala ndi makhalidwe oyera?
Kodi kukhala ndi makhalidwe oyera kungatithandize bwanji kuti tizisangalala ndi moyo panopa mpaka kalekale?
Anthu ena amaona kuti zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kugonana kwa amuna komanso akazi okhaokha, ndi kukhwimitsa zinthu. Koma zimenezi si zoona chifukwa Yehova amatikonda ndipo amafuna kuti tonse tizisangalala ndi moyo panopa mpaka kalekale. Kuti zimenezi zitheke, tiziyesetsa kutsatira mfundo zake. Werengani 1 Akorinto 6:9-11, kenako mukambirane funso ili:
Kodi kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha ndi khalidwe lokhalo limene Mulungu amadana nalo?
Kuti tizisangalatsa Mulungu, tonsefe tiyenera kuyesetsa kusintha moyo wathu. Kodi kuchita zimenezi n’kothandizadi? Werengani Salimo 19:8, 11, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi Yehova anachita bwino kutipatsa mfundo zamakhalidwe abwino kapena anangokhwimitsa zinthu? N’chifukwa chiyani mukutero?
Yehova wathandiza anthu ambiri kuti asiye makhalidwe oipa. Inunso angakuthandizeni
ZIMENE ENA AMANENA: “Palibe vuto kugonana ndi wina aliyense amene ukufuna, bola ngati mukukondana.”
Kodi inuyo mungamuuze zotani munthu wotereyu?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Kugonana ndi mphatso yochokera kwa Yehova ndipo imathandiza kuti mwamuna ndi mkazi wake azisangalala.
Kubwereza
Kodi kuchita chiwerewere kumaphatikizaponso kuchita zinthu ziti?
N’chiyani chingatithandize kuti tipewe kuchita chiwerewere?
Kodi timapindula bwanji tikamatsatira mfundo za Yehova zamakhalidwe abwino?
ONANI ZINANSO
Onani chifukwa chake Yehova amafuna kuti mwamuna ndi mkazi azimanga kaye banja lawo asanatengane.
Onani chifukwa chimene Baibulo likamaphunzitsa kuti kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha n’kolakwika, silitanthauza kuti tizidana ndi anthu amene amachita zimenezi.
“Kodi Kugonana Kwa Amuna Kapena Akazi Okhaokha N’kolakwika?” (Nkhani yapawebusaiti)
Onani mmene malamulo a Mulungu pa nkhani zokhudza kugonana amatitetezera.
“Kodi Kugonana M’kamwa Kumakhaladi Kugonana?” (Nkhani yapawebusaiti)
Munkhani yakuti, “Anandilandira Mwaulemu Kwambiri,” onani zimene zinathandiza munthu wina kusiya khalidwe logonana ndi amuna anzake n’cholinga choti azisangalatsa Mulungu.
“Baibulo Limasintha Anthu” (Nsanja ya Olonda, April 1, 2011)
a Zimenezi zikuphatikizapo kuchita zinthu monga chiwerewere, kugonana m’kamwa, kugonana kobibira komanso kuseweretsa maliseche a munthu wina ndi cholinga chofuna kudzutsa kapena kukhutiritsa chilakolako cha kugonana.
-
-
Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Mowa?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
PHUNZIRO 43
Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Mowa?
Anthu padzikoli amakhala ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya mowa. Ena amasankha kumwa mowa ndi anzawo akamacheza. Pomwe ena amasankha kuti asamamwe mowa. Anthu enanso amamwa mowa n’kufika poledzera. Ndiye kodi Baibulo limanena zotani pa nkhani ya mowa?
1. Kodi kumwa mowa n’kulakwa?
Baibulo silinena kuti kumwa mowa n’kulakwa. M’malomwake, likamanena za zinthu zabwino zambiri zimene Mulungu watipatsa, limatchulanso za “vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu.” (Salimo 104:14, 15) Ndipotu, amuna ndi akazi ena okhulupirika otchulidwa m’Baibulo ankamwa mowa.—1 Timoteyo 5:23.
2. Kodi Baibulo limapereka malangizo otani kwa amene asankha kumwa mowa?
Yehova amaletsa kumwa mowa mwauchidakwa komanso kuledzera. (Agalatiya 5:21) Mawu ake amati: “Usakhale pakati pa anthu omwa vinyo kwambiri.” (Miyambo 23:20) Choncho tikasankha kumwa mowa, ngakhale tili patokha, sitiyenera kumwa wambiri mpaka kufika polephera kuganiza bwino, kulephera kulankhula ndi kuchita zinthu zanzeru kapenanso kufika powononga thanzi lathu. Komabe, ngati zikutivuta kumwa mowa modziletsa, tingachite bwino kungosiyiratu.
3. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza zimene anthu ena anasankha pa nkhani ya mowa?
Munthu aliyense ayenera kusankha yekha ngati akufuna kumamwa mowa kapena ayi. Munthu wina akasankha kumwa mowa mosapitirira malire, tisamamuweruze. Komanso ngati wina wasankha kusamwa mowa, tisamamukakamize kuti ayambe kumwa. (Aroma 14:10) Komabe, tingasankhe kusamwa mowa ngati ena angakhumudwe kapena ngati kumwa mowa kungabweretse mavuto kwa anthu ena. (Werengani Aroma 14:21.) Timayesetsa kupewa kuchita zinthu ‘zopindulitsa ife tokha basi,’ koma timachita ‘zopindulitsanso anthu ena.’—Werengani 1 Akorinto 10:23, 24.
FUFUZANI MOZAMA
Onani mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni kusankha kumwa mowa kapena ayi komanso kuchuluka kwa mowa womwe mungamamwe. Onaninso zomwe mungachite ngati muli ndi vuto lomwa mowa mosadziletsa.
4. Mungasankhe kumwa mowa kapena ayi
Kodi maganizo a Yesu anali otani pa nkhani ya mowa? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tione chozizwitsa choyamba chimene Yesu anachita. Werengani Yohane 2:1-11, kenako mukambirane mafunso awa:
Malinga ndi zimene tawerengazi, kodi maganizo a Yesu ndi otani pa nkhani ya mowa, nanga amawaona bwanji anthu amene amasankha kumwa mowa?
Popeza Yesu saona kuti kumwa mowa n’kulakwa, kodi Mkhristu ayenera kumuona bwanji munthu amene wasankha kumwa mowa?
Ngakhale kuti Mkhristu ali ndi ufulu wosankha kumwa mowa, pa nthawi zina, singakhale nzeru kuchita zimenezi. Werengani Miyambo 22:3, kenako onani mmene mfundo zotsatirazi zingakuthandizireni kudziwa ngati muyenera kumwa mowa kapena ayi:
Ngati mukufunika kuyendetsa galimoto kapena kugwiritsa ntchito mashini enaake.
Ngati ndinu woyembekezera.
Ngati dokotala wakuuzani kuti musamwe mowa.
Ngati mumamwa mowa mosadziletsa.
Ngati lamulo lam’dziko lanu likukuletsani kumwa mowa.
Ngati muli ndi munthu amene wasankha kusamwa mowa chifukwa chakuti m’mbuyomo ankamwa mowa mosadziletsa.
Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kudziwa ngati ndi zoyenera kukhala ndi mowa paphwando la ukwati kapena pa zochitika zina? Kuti mudziwe zoyenera kuchita, onerani VIDIYO.
Werengani Aroma 13:13 ndi 1 Akorinto 10:31, 32. Pambuyo powerenga lemba lililonse, mukambirane funso ili:
Kodi kugwiritsa ntchito mfundo yamulembali kungakuthandizeni bwanji kusankha zinthu zimene zingasangalatse Yehova?
Mkhristu aliyense amasankha yekha kumwa mowa kapena ayi. Ngakhale mkhristu yemwe amamwa mowa, nthawi zina angasankhe kusamwa
5. Ganizirani kuchuluka kwa mowa womwe mungamwe
Ngati mwasankha kumwa mowa, muzikumbukira mfundo iyi: Ngakhale kuti Yehova saletsa kumwa mowa, koma amaletsa kumwa mowa mwauchidakwa. N’chifukwa chiyani zimenezi zili choncho? Werengani Hoseya 4:11, 18, kenako mukambirane funso ili:
N’chiyani chingachitike ngati munthu atamwa mowa wambiri?
N’chiyani chingatithandize kuti tisamwe mowa wambiri? Tiyenera kuzindikira malire athu n’kupewa kumwa mowa mopitirira muyezo. Werengani Miyambo 11:2, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani muyenera kudziikira malire a mowa womwe muyenera kumamwa?
6. N’chiyani chimene chingathandize munthu kusiya kumwa mowa mopitirira malire?
Onani zomwe zinathandiza munthu wina kusiya kumwa mowa mopitirira malire. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi Dmitry ankatani akaledzera?
Kodi anakwanitsa kusiya kumwa mowa kamodzin’kamodzi?
N’chiyani chinamuthandiza kuti asiyiretu kumwa mowa mwauchidakwa?
Werengani 1 Akorinto 6:10, 11, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi Baibulo limanena zotani pa nkhani ya kumwa mowa mwauchidakwa?
N’chiyani chikusonyeza kuti munthu yemwe amamwa mowa mopitirira malire akhoza kusintha?
Werengani Mateyu 5:30, kenako mukambirane funso ili:
Pamene Yesu amanena za kudula dzanja ankatanthauza kuti tiyenera kulolera kusiya kuchita zinazake ndi cholinga choti tisangalatse Yehova. Kodi mungatani ngati zikukuvutani kusiya kumwa mowa mwauchidakwa?a
Werengani 1 Akorinto 15:33, kenako mukambirane funso ili:
Kodi n’chiyani chimene chingakuchitikireni ngati mumacheza ndi anthu omwe amakonda kumwa mowa wambiri?
MUNTHU WINA ANGAKUFUNSENI KUTI: “Kodi kumwa mowa n’kulakwa?”
Kodi mungamuyankhe bwanji?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Mowa ndi mphatso imene Yehova anatipatsa kuti tizisangalala. Koma iye safuna kuti tizimwa mowa wambiri kapena kuledzera.
Kubwereza
Kodi Baibulo limanena zotani pa nkhani ya mowa?
Kodi kumwa mowa wambiri kumabweretsa mavuto otani?
Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza zimene anthu ena anasankha pa nkhani ya mowa?
ONANI ZINANSO
Kodi achinyamata angasankhe bwanji zinthu mwanzeru pa nkhani ya mowa?
Onani njira zimene muyenera kutsatira kuti muthane ndi vuto lomwa mowa mosadziletsa.
“Khalani ndi Maganizo Oyenera Pankhani ya Kumwa Mowa” (Nsanja ya Olonda, January 1, 2010)
Kodi Mkhristu ayenera kuchita nawo mwambo wowombanitsa mabotolo kapena matambula azakumwa?
“Mafunso Ochokera kwa Owerenga” (Nsanja ya Olonda, February 15, 2007)
Munkhani yakuti, “Ndinali Mbiyang’ambe,” onani zimene zinathandiza munthu wina kuti asiye kumwa mowa mwauchidakwa.
a Anthu amene mowa unawalowerera kwambiri angafunike thandizo lachipatala kuti akwanitse kusiya. Ndipotu madokotala ambiri amanena kuti anthu amene anali ndi vuto limeneli sayenera kumwa mowa n’komwe.
-
-
Kodi Mukachita Tchimo Lalikulu Muyenera Kutani?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
Ngakhale kuti mumakonda kwambiri Yehova ndiponso mumayesetsa kupewa kuchita zinthu zomwe zingamukhumudwitse, nthawi zina mukhoza kulakwitsa zinazake. Komabe machimo ena amakhala aakulu kuposa ena. (1 Akorinto 6:9, 10) Ngati mwachita tchimo lalikulu musataye mtima ndipo musaiwale kuti Yehova sanasiye kukukondani. Iye ndi wofunitsitsa kukukhululukirani komanso kukuthandizani kuti musinthe.
1. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Yehova atikhululukire?
Anthu amene amakonda Yehova amadzimvera chisoni kwambiri akazindikira kuti achita tchimo lalikulu. Komabe Yehova amawatonthoza ndi lonjezo lakuti: “Ngakhale machimo anu atakhala ofiira kwambiri, adzayera kwambiri.” (Yesaya 1:18) Tikalapa mochokera pansi pa mtima, Yehova sakumbukiranso machimo athu ndipo amatikhululukira ndi mtima wonse. Ndiye timasonyeza bwanji kuti talapa? Timadzimvera chisoni kwambiri chifukwa cha zimene tachitazo, sitimazibwerezanso, kenako timapempha Yehova kuti atikhululukire. Komanso timachita khama kuti tisiye kuchita kapena kuganizira zinthu zoipa zimene zinachititsa kuti tichite tchimo. Kuonjezera pamenepa, timayesetsa kutsatira mfundo za Yehova za makhalidwe abwino pa moyo wathu.—Werengani Yesaya 55:6, 7.
2. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji akulu kuti atithandize tikachimwa?
Tikachita tchimo lalikulu Yehova amatiuza kuti ‘tiitane akulu a mpingo.’ (Werengani Yakobo 5:14, 15.) Akuluwa amakonda Yehova ndi nkhosa zake. Iwo anaphunzitsidwa bwino mmene angatithandizire n’cholinga choti tikhalenso pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.—Agalatiya 6:1.
Kodi akulu amatithandiza bwanji tikachita tchimo lalikulu? Akulu awiri kapena atatu amagwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba potithandiza kuzindikira kuti zomwe tachitazo ndi zolakwika. Iwo amatipatsa malangizo ndi kutilimbikitsa n’cholinga chotithandiza kuti tipewe kudzachitanso tchimolo. Pofuna kuteteza mpingo kuti ukhalebe woyera, akulu amachotsa mumpingo munthu yemwe wachita tchimo lalikulu koma sanasonyeze mtima wolapa kuti munthuyo asasokoneze ena.
FUFUZANI MOZAMA
Onani zimene mungachite kuti muziyamikira zimene Yehova amachita potithandiza tikachita tchimo lalikulu.
3. Kuulula machimo athu kumatithandiza kuti tikhalenso pa ubwenzi ndi Yehova
Tikachita tchimo lililonse Yehova amakhumudwa. Choncho tingachite bwino kuulula kwa iyeyo. Werengani Salimo 32:1-5, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani tiyenera kuulula machimo athu kwa Yehova m’malo momubisira?
Tikaulula machimo athu kwa Yehova tiyeneranso kuuza akulu ndipo kuchita zimenezi kumathandiza kuti zinthu ziyambirenso kutiyendera bwino. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.
Muvidiyoyi, kodi akulu anathandiza bwanji Canon kuti abwerere kwa Yehova?
Tizimasuka pofotokozera akulu za tchimo lathu ndipo tiziwauza zoona zokhazokha. Iwo amafuna kutithandiza. Werengani Yakobo 5:16, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani akulu savutika kutithandiza tikawauza zoona zokhazokha zokhudza tchimo lathu?
Muziulula machimo anu kwa Yehova, muziuza akulu zoona zokhazokha komanso muzivomereza chilango chochokera kwa Yehova chomwe amachipereka mwachikondi
4. Yehova amasonyeza chifundo kwa anthu ochimwa
Ngati munthu amene wachita tchimo lalikulu sakufuna kulapa komanso kutsatira mfundo za m’Malemba amachotsedwa mumpingo ndipo sitiyenera kumacheza naye. Werengani 1 Akorinto 5:6, 11, kenako mukambirane funso ili:
Monga mmene chofufumitsa chimafufumitsira mtanda wonse, kodi kucheza ndi munthu wochimwa yemwe sanalape kungakhudze bwanji mpingo wonse?
Potsanzira mmene Yehova amasonyezera chifundo kwa anthu ochimwa, akulu amayesetsa kuthandiza anthu amene amachotsedwa mumpingo. Anthu ambiri omwe anachotsedwa mumpingo anabwerera chifukwa cha chilango chomwe anapatsidwa. Ngakhale kuti kuchotsedwa mumpingo ndi kowawa, kunawathandiza kuzindikira kuti zomwe anachita zinali zolakwika.—Salimo 141:5.
Kodi mmene Yehova amachitira zinthu ndi anthu ochimwa zimasonyeza bwanji kuti amawamvetsa, ndi wachifundo ndiponso ndi wachikondi?
5. Yehova amakhululukira munthu amene walapa
Yesu anagwiritsa ntchito fanizo lomwe limatithandiza kumvetsa mmene Yehova amamvera munthu wochimwa akalapa. Werengani Luka 15:1-7, kenako mukambirane funso ili:
Kodi fanizoli likukuphunzitsani chiyani zokhudza Yehova?
Werengani Ezekieli 33:11, kenako mukambirane funso ili:
Kodi munthu ayenera kuchita chiyani posonyeza kuti walapadi?
Mofanana ndi m’busa, Yehova amasamalira mwachikondi nkhosa zake
ZIMENE ENA AMANENA: “Ndikuopa kuti ndikaulula tchimo langa kwa akulu andichotsa mumpingo.”
Kodi munthu amene ali ndi maganizo amenewa mungamuuze zotani?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Ngati munthu wachita tchimo lalikulu n’kulapa mochokera pansi pa mtima komanso watsimikiza mtima kuti sadzachitanso tchimolo, Yehova amamukhululukira.
Kubwereza
N’chifukwa chiyani tiyenera kuulula machimo athu kwa Yehova?
Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Yehova atikhululukire machimo athu?
Ngati tachita tchimo lalikulu, n’chifukwa chiyani tiyenera kupempha akulu kuti atithandize?
ONANI ZINANSO
Onani mmene Yehova anasonyezera munthu wina chifundo chotchulidwa pa Yesaya 1:18.
Kodi akulu amathandiza bwanji munthu amene wachita tchimo lalikulu?
“Mmene Tingasonyezere Chikondi ndi Chifundo Wina Akachita Tchimo” (Nsanja ya Olonda, August, 2024)
Onani mmene anthu osalapa amasonyezedwera chikondi komanso chifundo.
“Kodi Akulu Angathandize Bwanji Anthu Amene Achotsedwa Mumpingo?” (Nsanja ya Olonda, August, 2024)
Munkhani yakuti, “Ndinazindikira Kuti Ndiyenera Kubwerera kwa Yehova,” onani chifukwa chake munthu wina anaona kuti Yehova wamuthandiza kubwerera kwa iye.
“Baibulo Limasintha Anthu” (Nsanja ya Olonda, April 1, 2012)
-