Achinyamata—Kanani Mzimu wa Dziko
“Sitinalandira ife mzimu wa dziko lapansi, koma mzimu wa kwa Mulungu.”—1 AKORINTO 2:12.
1, 2. (a) Kodi pali kusiyana kotani pakati pa achinyamata a dziko ndi achinyamata a m’mipingo ya Mboni za Yehova? (b) Kodi n’chiyamikiro chotani chomwe chikuperekedwa kwa Mboni zachinyamata?
“ACHINYAMATA athu alibe chidwi chenicheni pa moyo. Podziona kukhala opanda pake iwo amapanduka.” Umu ndi mmene inanenera nyuzipepala ina ku Australia yotchedwa The Sun-Herald. Nyuzipepalayo inapitiriza kunena kuti: “Zolembedwa za m’khothi zimasonyeza kuŵirikiza kofikira 22 peresenti [kuposa chaka chatha] kwa achinyamata oonekera m’khothi pamilandu ya kuvulaza wina koopsa . . . Ana akudzipha okha pamlingo woŵirikiza katatu poyerekeza ndi zaka zapakati pa ma 1960 . . . Ndipo kusiyana kwa maganizo a anthu achikulire ndi achinyamata kukukulirakulira mwakuti achinyamata ochulukirachulukira nthaŵi zonse akumwerekera ndi mankhwala ozunguza bongo, uchidakwa ndi kudzipha okha.” Komabe, mkhalidwe umenewu suli m’dziko limodzi lokha ayi. Kuzungulira dziko lonse lapansi, makolo, aphunzitsi, ndi akatswiri panthenda za maganizo ndi thanzi la thupi akudandaula ndi mkhalidwe wa achinyamata.
2 Pali kusiyana kwakukulu kwambiri pakati pa achinyamata ambiri lerolino ndi achinyamata akhalidwe labwino m’mipingo ya Mboni za Yehova! Sikuti iwo ali angwiro ayi. Iwonso amalimbana ndi “zilakolako za unyamata.” (2 Timoteo 2:22) Koma unyinji wa achinyamata ameneŵa alimba mtima pomamatira khalidwe labwino ndi kukana kugonja pa zonyengerera za dzikoli. Ndi mtima wonse, tikukuyamikirani achinyamata nonsenu amene mukupambana pankhondo yolimbana ndi ‘machenjera’ a Satana! (Aefeso 6:11) Monga mtumwi Yohane, tikukakamizika kukuuzani kuti: ‘Takulemberani, anyamata [ndi atsikana], popeza muli amphamvu, ndi mawu a Mulungu akhala mwa inu, ndipo mwam’laka woipayo.’—1 Yohane 2:14.
3.Kodi liwu lakuti “mzimu” lingatanthauzenso chiyani?
3 Komabe, kuti mupitirize kupambana pankhondo yanu yolimbana ndi woipayo, muyenera kuyesetsa mwamphamvu kukana chimene Baibulo limatcha “mzimu wa dziko.” (1 Akorinto 2:12) Malinga n’kunena kwa buku lina lomasulira Chigiriki, “mzimu” ungatanthauze “maganizo kapena chisonkhezero chimene chimadzaza ndi kulamulira moyo wa munthu aliyense.” Mwachitsanzo, ngati muona kuti munthu wina n’ngwa mtima wapachala, munganene kuti ali ndi “mzimu” woipa. “Mzimu” wanu kapena maganizo ndiwo amasonkhezera zinthu zimene mumasankha; mzimuwo ndiwo umalimbikitsa zimene mumachita ndi zimene mumanena. Chofunika kudziŵa n’chakuti, “mzimu” umenewu ukhoza kuonekera mwa munthu mmodzi kapenanso gulu la anthu lingaonetse mzimu umenewu. Mtumwi Paulo analembera gulu la Akristu kuti: “Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Kristu chikhale pamodzi ndi mzimu wanu.” (Filemoni 25) Choncho, ndi mzimu wotani nanga umene dzikoli limaonetsa? Popeza kuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo,” Satana Mdyerekezi, sizingatheke kuti mzimu wa dziko n’kukhala wabwino. Zingatero ngati?—1 Yohane 5:19.
Kudziŵa Mzimu wa Dziko
4, 5. (a) Kodi ndi mzimu wotani umene unalamulira anthu a mumpingo wa Aefeso asanakhale Akristu? (b) Kodi ndani ali “mkulu wa ulamuliro wa mpweya,” ndipo “mpweyawo” n’chiyani?
4 Paulo analemba kuti: “Ndipo inu, anakupatsani moyo, pokhala munali akufa ndi zolakwa, ndi zochimwa zanu, zimene munayendamo kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga [“mpweya,” NW], wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera; amene ife tonsenso tinagonera pakati pawo kale, m’zilakolako za thupi lathu, ndi kuchita zifuniro za thupi, ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo chibadwire, monganso otsalawo.”—Aefeso 2:1-3.
5 Asanaphunzire njira yachikristu, Akristu a ku Efeso mosadziŵa ankatsatira “mkulu wa ulamuliro wa mpweya,” Satana Mdyerekezi. “Mpweya” umenewo si malo enieni kumene Satana ndi ziŵanda zake amakhalako ayi. Pamene Paulo analemba mawuŵa, Satana Mdyerekezi ndi ziŵanda zake anali kupitabe kumwamba. (Yerekezani ndi Yobu 1:6; Chivumbulutso 12:7-12.) Liwu lakuti “mpweya” limatanthauza mzimu, kapena maganizo, amene amalamulira dziko la Satana. (Yerekezani ndi Chivumbulutso 16:17-21.) Mofanana ndi mpweya wotizingawu, mzimu umenewu ulinso paliponse.
6. Kodi “ulamuliro wa mpweya” n’chiyani, ndipo ukugwira motani ntchito pa achinyamata ambiri?
6 Koma kodi “ulamuliro wa mpweya” umenewo n’chiyani? Mwachionekere, imeneyi ndi mphamvu yaikulu imene “mpweya” umenewu uli nayo pa anthu. Paulo anati mzimu umenewu ‘umachita [kapena umagwira ntchito] mwa ana a kusamvera.’ Choncho, mzimu wa dziko umabala mzimu wa kusamvera ndi wa chipanduko, ndipo chisonkhezero cha mabwenzi ndi njira imodzi imene ulamuliro umenewu umagwirira ntchito. Mtsikana wina amene ndi Mboni anati: “Pamene uli kusukulu, aliyense amakulimbikitsa kukhala wopandukako pang’ono. Anyamata ndi atsikana amakulemekeza ngati nthaŵi zina umachitako zinthu zopulupudza.”
Mikhalidwe Yoonetsa Mzimu wa Dziko
7-9. (a) Tchulani mikhalidwe ina imene imaonetsa mzimu wa dziko mwa achinyamata lerolino. (b) Kodi mwaona ina ya mikhalidwe imeneyi kwanuko?
7 Kodi ndi mikhalidwe ina yotani imene imaonetsa mzimu wa dziko pakati pa achinyamata lero? Kusaona mtima limodzi ndi mzimu wopanduka. Lipoti la m’magazini ina linanena kuti 70 peresenti ya ophunzira m’makalasi oyambirira ndi omaliza m’makoleji, anati anachitapo chinyengo pamene anali kusekondale. Malankhulidwe achipongwe, amwano, ndi otukwana n’ngofalanso kwambiri. N’zoona kuti nthaŵi zina pofuna kusonyeza mkwiyo wolungama, Yobu ndi mtumwi Paulo anagwiritsapo ntchito mawu amene ena anganene kuti ndi mwano. (Yobu 12:2; 2 Akorinto 12:13) Komabe, mawu amwano oipitsitsa amene amatuluka pakamwa pa achinyamata ambiri lerolino kaŵirikaŵiri amakhala nkhanza yeniyeni.
8 Kumwerekera m’zosangalatsa ndi umboni winanso wa mzimu wa dziko. Makalabu ausiku a achinyamata, madansi amene nthaŵi zambiri amachezera usiku wonse,a ndi mitundu ina ya zosangalatsa zosadziletsa n’zofala kwambiri. Komanso kuvala ndi kudzikongoletsa kopambanitsa kwafalanso kwambiri. Pali zovala zina zikuluzikulu zopanda saizi, masitayelo odabwitsa, monga kuboola ziwalo zina za thupi, masitayelo a achinyamata ambiri lerolino oonetsa mzimu wa dziko wachipanduko. (Yerekezani ndi Aroma 6:16.) Mkhalidwe wina woonetsa mzimu wa dziko ndi kukondetsa chuma. Malinga n’kunena kwa magazini ina ya zamaphunziro, “amalonda amakopa achinyamata paliponse ndi maluso awo otsatsa malonda komanso zinthu zokongola zimene amapanga.” Pamene achinyamata ku United States amaliza sukulu yawo yasekondale, amakhala ataonera malonda okwanira 360,000 otsatsidwa pawailesi yakanema. Inunso achinyamata anzanu angakuumirizeni kuti mugule zina mwa zinthuzo. Mtsikana wina wazaka 14 anati: “Nthaŵi zonse aliyense amafunsa kuti, ‘Kodi juzi yako, jekete, kapena jini yako dzina lake n’chiyani?’”
9 Kuyambira m’nthaŵi za m’Baibulo, nyimbo zosayenera zakhala chida chimene Satana wachigwiritsa ntchito polimbikitsa khalidwe lonyansa. (Yerekezani ndi Eksodo 32:17-19; Salmo 69:12; Yesaya 23:16.) Choncho n’zosadabwitsa kuona kuti nyimbo zolaula, za mawu otukwana, ndi onena zaupandu n’zofala. Komanso, chiwerewere ndicho khalidwe linanso losonyeza mzimu wonyansa wa dziko. (1 Akorinto 6:9-11) Nyuzipepala yotchedwa The New York Times inati: “Kwa achinyamata ambiri kugonana kwakhala ngati chiyeneretso cha unyamata . . . Ophunzira aŵiri mwa atatu alionse a m’makalasi omalizira kusekondale anachitapo chiwerewere.” Nkhani ina m’nyuzipepala yotchedwa The Wall Street Journal inatchula umboni wosonyeza kuti ana amisinkhu ya pakati pa 8 ndi 12 “akuyamba kuloŵerera m’nkhani ya chiwerewere.” Amene posachedwapa anali mlangizi pasukulu ina anati: “Tikuyamba kuona ana angapo a m’kalasi 6 akutenga pakati.”b
Kukana Mzimu wa Dziko
10. Kodi achinyamata ena ochokera m’mabanja achikristu agonja motani ku mzimu wa dziko?
10 Mwatsoka, achinyamata ena achikristu agonja ku mzimu wa dziko umenewo. Mtsikana wina wachijapani anavomereza kuti: “Pamaso pa makolo anga ndi Akristu ena ndinkaonetsa khalidwe labwino. Koma ndinalinso ndi moyo wina.” Mtsikana wina wa ku Kenya anati: “Kwa nthaŵi yotalikirapo ndithu ndinakhala ndi moyo wachipha maso, umene unaphatikizapo kupita kumaphwando, kumadansi, ndi kukhala ndi mabwenzi oipa. Ndinkadziŵa kuti zimene ndinkachitazo zinali zolakwa, koma ndinangonyalanyaza ndikumaganiza kuti m’kupita kwa nthaŵi ndisiya. Koma sindinasiye ayi. Zinthu zinangoipiraipira.” Wachinyamata winanso wa ku Germany anati: “Vuto linayambira pokhala ndi anzanga akudziko. Kenako ndinayamba kusuta. Cholinga chinali choti ndikhaulitse makolo anga, koma ndinadzikhaulitsa ndekha.”
11. Kodi Kalebi anakhoza bwanji kutsutsa malingaliro a unyinji pamene azondi khumi aja anadzanena zinthu zochititsa mantha?
11 Komabe, n’kotheka kuukana mzimu wa dziko, inde kuutsutsa kotheratu. Taganizani za chitsanzo chakale cha Kalebi. Pamene azondi khumi amantha aja anadzanena zoipa zokhazokha za Dziko Lolonjezedwa, iye, limodzi ndi Yoswa, sanachite mantha ndipo anakana kutsatira malingaliro a unyinji. Iwo molimba mtima analengeza kuti: “Dziko tapitamo kulizonda, ndilo dziko lokometsetsa ndithu. Yehova akakondwera nafe, adzatiloŵetsa m’dzikomo, ndi kutipatsa ilo; ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.” (Numeri 14:7, 8) Kodi chinalimbitsa mtima Kalebi n’chiyani kuti aimirire ndi kutsutsa ochulukawo? Yehova anati za Kalebi: “Anali nawo mzimu wina [“wosiyana,” NW].”—Numeri 14:24.
Kuonetsa “Mzimu Wosiyana”
12. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kuonetsa “mzimu wosiyana” pankhani ya kalankhulidwe?
12 Lerolino, pamafunika kulimba mtima ndi nyonga kuti wina aonetse “mzimu wosiyana,” kapena maganizo osiyana ndi a dzikoli. Njira imodzi imene mungachitire chimenecho ndiyo kupeŵa mawu achipongwe ndi onyoza. Mawu achingelezi amene tamasulira kuti “mawu achipongwe” akuchokera ku mneni wachigiriki wotanthauza “kukhadzula mnofu ngati agalu.” (Yerekezani ndi Agalatiya 5:15.) Monga mmene galu amagwiritsira ntchito mano ake pokhadzula mnofu ku fupa, ndimmenenso “nthabwala” zachipongwe zimachotsera ulemu wa munthu wina. Koma Akolose 3:8 akukulimbikitsani kuti ‘mutaye zonsezo: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka m’kamwa mwanu.’ Ndipo Miyambo 10:19 imati: “Pochuluka mawu zolakwa sizisoŵeka; koma wokhala chete achita mwanzeru.” Ngati wina akunyozani, khalani wodziletsa kotero kuti ‘mum’tembenuzire tsaya lina,’ mwina mwa kulankhula ndi wokunyozaniyo mseri, koma mofatsa ndi mwamtendere.—Mateyu 5:39; Miyambo 15:1.
13. Kodi achinyamata angaonetse motani kaonedwe koyenera ka zinthu zakuthupi?
13 Njira ina yosonyezera “mzimu wosiyana” ndiyo kukhala ndi kaonedwe koyenera ka zinthu zakuthupi. N’zoona kuti n’kwachibadwa kufuna kukhala ndi zinthu zabwino. Chifukwa ngakhale Yesu anali ndi chovala chimodzi chamtengo wapatali. (Yohane 19:23, 24) Komabe, ngati nthaŵi zonse mumakhala ndi chilakolako chofuna kukhala ndi zinthu, kenako n’kumavuta makolo anu kuti akugulireni zinthu zimene sangathe, kapena ngati mumangofuna kufanana ndi anzanu, mwina mzimu wa dziko wayamba kukulamulirani. Baibulo limati: “Chilichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi.” Inde, musagonje ku ulamuliro wa mzimu wa dziko wokondetsa zinthu zakuthupi! Phunzirani kukhutira ndi zimene muli nazo.—1 Yohane 2:16; 1 Timoteo 6:8-10.
14. (a) Kodi anthu a Mulungu m’masiku a Yesaya anali ndi kaonedwe kosayenera kotani ka zosangalatsa? (b) Kodi ndi ngozi zotani zimene Akristu ena achinyamata akumana nazo m’makalabu ndi m’mapwando a dziko?
14 Kuika zosangalatsa m’malo ake n’kofunikanso. Mneneri Yesaya analengeza kuti: “Tsoka kwa iwo amene adzuka m’mamaŵa kuti atsate zakumwa zaukali; amene achezera usiku kufikira vinyo awaledzeretsa! Ndipo zeze ndi mngoli, ndi lingaka ndi chitoliro, ndi vinyo, zili m’mapwando awo; koma iwo sapenyetsa ntchito ya Yehova; ngakhale kuyang’ana pa machitidwe a manja ake.” (Yesaya 5:11, 12) Chomvetsa chisoni n’chakuti Akristu ena achinyamata akhala akuchita nawo mapwando omwerekera amenewo. Pamene gulu lina la Akristu achinyamata anafunsidwa kulongosola zimene zimachitika kumakalabu ausiku, mlongo wina wachitsikana anati: “Ndewu zimachitika nthaŵi zonse. Nthaŵi zina zimandikhudza inenso.” Mbale wina wachinyamata anawonjezera kuti: “Kumakhala kumwa, kusuta, ndi zina zotero.” Mbale winanso wachinyamata anavomereza kuti: “Kumeneko anthu amaledzera. Amachita ngati zitsiru zenizeni! Mankhwala ozunguza bongo amakhalanso komweko. Zoipa zina zosaneneka zimangoti pwirikiti kumeneko. Ngati upita kumeneko ndi maganizo oti ukabwerako bwino, udzanong’oneza bondo.” N’chifukwa chake Baibulo limatchula njiru, kapena “mapwando osadziletsa,” kukhala pakati pa “ntchito za thupi.”—Agalatiya 5:19-21; Aroma 13:13.
15. Kodi Baibulo limapereka kaonedwe kabwino kotani ka zosangalatsa?
15 Sikuti mukapeŵa zosangalatsa zowonongazo, basi moyo wanu udzangokhala wosakondweretsa ndi wonyong’onya ayi. Ifetu timalambira “Mulungu wa ulemerero [“wachimwemwe,” NW],” amene amafuna kuti inunso musangalale ndi unyamata wanu! (1 Timoteo 1:11; Mlaliki 11:9) Koma Baibulo limachenjeza kuti: “Wokonda zoseketsa [“zosangalatsa,” Lamsa] adzasauka.” (Miyambo 21:17) Inde, ngati mutenga zosangalatsa kukhala chinthu chachikulu koposa m’moyo wanu, mudzasauka mwauzimu. Choncho tsatirani malangizo a Baibulo posankha zosangalatsa. Zilipo zinthu zambiri zimene mungasangalale nazo, zimenenso zingakuthandizeni m’malo mokuwonongani.c—Mlaliki 11:10.
16. Kodi Akristu achinyamata angaonetse motani kuti ali osiyana ndi ena pankhani ya kavalidwe, kapesedwe, ndi nyimbo zimene amasankha?
16 Kukhala kwanu ndi mavalidwe aulemu ndi kapesedwe kabwino, komanso kukana masitayelo a dziko, kudzakupangitsani kuoneka wosiyana ndi ena. (Aroma 12:2; 1 Timoteo 2:9) Ngakhalenso posankha nyimbo zabwino. (Afilipi 4:8, 9) “Ndili ndi nyimbo zimene ndimadziŵa kuti ndiyenera kuzitaya,” anavomereza choncho Mkristu wina wachinyamata, “koma zimamveka zokoma kwabasi!” Mnyamata winanso ananena mofananamo kuti: “Mbuna yanga yaikulu ndi nyimbo, chifukwa ndimazikonda zedi. Ngati ndiona kuti m’nyimbomo muli mbali ina yoipa, kapena ngati makolo anga andichenjeza za nyimboyo, ndimakhala pankhondo yoti ndichotseko mtima wanga chifukwa pansi pa mtima ndimaikonda kwabasi.” Achinyamatanu, ‘musakhale osadziŵa machenjerero [a Satana].’ (2 Akorinto 2:11) Iyeyo amagwiritsa ntchito nyimbo poyesetsa kupandutsa Akristu achinyamata kuti am’siye Yehova! Nkhani zosiyanasiyana zatuluka m’zofalitsa za Watch Tower zofotokoza nyimbo zowononga khalidwe zimene pachingelezi amazitcha rap, heavy metal, ndi nyimbo zina za rock.d Komabe, n’kosatheka kuti zofalitsa za Watch Tower zilankhulepo pa mtundu wina uliwonse watsopano wa nyimbo zimene zingatuluke. Chotero, muyenera kugwiritsa ntchito “kulingalira” ndi “kuzindikira” posankha nyimbo.—Miyambo 2:11.
17. (a) Kodi por·neiʹa n’chiyani, ndipo amaphatikizapo machitidwe otani? (b) Kodi chifuniro cha Mulungu n’chiyani ponena za makhalidwe?
17 Chomalizira, muyenera kukhala woyera m’makhalidwe anu. Baibulo limalimbikitsa kuti: “Thaŵani dama.” (1 Akorinto 6:18) Liwu loyambirira lachigiriki limene anamasulira kuti dama, por·nei’a, limatanthauza mchitidwe uliwonse wosaloleka wogwiritsa ntchito ziwalo zogonanira kunja kwa ukwati. Zimenezo zikuphatikizapo kugonana m’kamwa ndi kuseŵeretsana ziwalo zogonanira. Akristu achinyamata ena achitapo mchitidwe umenewu, akumaganiza kuti limenelo silinali dama kwenikweni. Komabe, Mawu a Mulungu amanena momveka bwino kuti: “Pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu, chiyeretso chanu, kuti mudzipatule kudama; yense wa inu adziŵe kukhala nacho chotengera chake m’chiyeneretso ndi ulemu.”—1 Atesalonika 4:3, 4.
18. (a) Kodi wachinyamata angaleŵe motani chidetso cha mzimu wa dziko? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?
18 Inde, ndi thandizo la Yehova, mukhoza kupeŵa chidetso cha mzimu wa dzikoli! (1 Petro 5:10) Komabe, nthaŵi zambiri Satana amabisa misampha yake yakuphayo, ndipo nthaŵi zina pangafunikiredi luntha lenileni kuti muzindikire ngozi imene ilipo. Cholinga cha nkhani yathu yotsatira ndi kuthandiza achinyamata kuti akulitse luso lawo lozindikira zinthu.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mumve zambiri onani nkhani yakuti “Achinyamata Akufunsa Kuti—Kodi Madansi a Rave ndi Zosangulutsa Zabwino?” mu Galamukani! ya January 8, 1998.
b Ana a zaka pafupifupi 11.
c Kuti muone zina zosangalala nazo, onani masamba 296 mpaka 303 m’buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza.
d Onani Nsanja ya Olonda ya April 15, 1993.
Mafunso Obwereramo
◻ Kodi “mzimu wa dziko” n’chiyani, ndipo ukukhala bwanji “ulamuliro” pa anthu?
◻ Ndi mikhalidwe yotani imene imaonetsa mzimu wa dziko pakati pa achinyamata lerolino?
◻ Kodi Akristu achinyamata angaonetse motani “mzimu wosiyana” m’nkhani za kalankhulidwe ndi zosangalatsa?
◻ Kodi Akristu achinyamata angaonetse motani “mzimu wosiyana” m’nkhani za makhalidwe ndi nyimbo?
[Chithunzi patsamba 9]
Achinyamata ambiri amasonyeza mwa makhalidwe awo kuti akulamulidwa ndi “ulamuliro” wa mzimu wa dziko
[Chithunzi patsamba 10]
Sankhani bwino nyimbo zimene mukonda
[Chithunzi patsamba 11]
Kukana mzimu wa dziko kumafuna kulimba mtima