Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rs tsamba 170-tsamba 174
  • Kudziimira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kudziimira
  • Kukambitsirana za m’Malemba
  • Nkhani Yofanana
  • Tchimo
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Moyo Wokhutiritsa—N’chifukwa Chiyani Uli Wosoŵa Choncho?
    Moyo Wokhutiritsa—Mmene Mungaupezere
  • Mzimu Wochirikiza Dongosolo Lakale Liripo’li
    Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo!
  • Ziyembekezo za Paradaiso Ziri Zotsimikizirika Mosasamala Kanthu za Kusamvera kwa Anthu
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Kukambitsirana za m’Malemba
rs tsamba 170-tsamba 174

Kudziimira

Tanthauzo: Mkhalidwe mu umene munthu saali, kapena samadzinenera kukhala, wodalira pa ena, samagonjera ku chitsogozo chawo kapena chisonkhezero. Pokhala atapatsidwa ufulu wa kudzisankhira, anthu ali ndi chikhumbo chachibadwa cha mlingo wakutiwakuti wa kudziimira. Komabe, chitachitidwa mopitirira muyezo, chikhumbochi chimadzutsa kusamvera, ngakhale chipanduko.

Pamene anthu akankhira pambali miyezo ya Baibulo, kodi iwo amapezadi ufulu?

Aroma 6:16, 23: “Kodi simudziŵa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake akumvera iye, mukhalatu akapolo ake a yemweyo muli kumvera iye; kapena auchimo kulinga ku imfa, kapena aumvero kulinga ku chilungamo? . . . Mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.”

Agal. 6:7-9: “Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta. Pakuti wakufesera kwathupi la iye yekha, chochokera m’thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa mzimu, chochokera m’mzimu adzatuta moyo wosatha. Koma tisaleme pa kuchita zabwino.”

Mkhalidwe wachisembwere: “Wachiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha.” (1 Akor. 6:18) “Wochita chigololo ndi mkazi . . . akuwononga moyo wake.” (Miy. 6:32) (Ponena za mathanyula, wonani Aroma 1:24-27.) (Panthaŵiyo, maunansi achisembwerewo, angawonekere kukhala osangalatsa. Koma amatsogolera kunthenda zonyansa, mimba zosafunika, kutaya mimba, nsanje, chikumbumtima chovutitsidwa, kusokonezeka maganizo, ndipo ndithudi mkwiyo wa Mulungu, pa amene ziyembekezo zathu za moyo wamtsogolo zimadalira.)

Kufunafuna zinthu zakuthupi: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri ndi chitayiko. Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi chapandalama; chimene ena pochikhumba, anasokera, nataya chikulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.” (1 Tim. 6:9, 10) “Ndidzati kwa moyo wanga, Moyo iwe, uli nacho chuma chambiri chosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere. Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani? Atero iye wakudziunjikira chuma mwini yekha wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu.” (Luka 12:19-21) (Chuma chakuthupi sichimabweretsa chimwemwe chokhalitsa. Kaŵirikaŵiri zoyesayesa za kupeza chuma zachititsa mabanja opanda chimwemwe, thanzi lofooka, chivulazo chauzimu.)

Kumwa zakumwa zoledzeretsa kopambanitsa: “Ndani ali ndi chisoni? Ndani ali ndi makangano? Ndani ang’ung’udza? Ndani alasidwa chabe? Ndani afiira maso? Ngamene achedwa pali vinyo, napita kukafunafuna vinyo wosanganizidwa. Pa chitsiriziro chake aluma ngati njoka, najompha ngati mamba.” (Miy. 23:29, 30, 32) (Poyamba kumwa kungawonekere kukhala kukuthandiza munthuyo kuiŵala mavuto, koma iko sikumaŵathetsa. Pamene moŵa umthera, mavutowo amakhalapobe, kaŵirikaŵiri ena atawonjezeredwa. Pamene zimwedwa mopambanitsa, zakumwa zoledzeretsa zimawononga ulemu wamunthu, thanzi lake, moyo wabanja lake, unansi wake ndi Mulungu.)

Kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa maganizo: Wonani tsamba 248-254, pamutu wakuti “Mankhwala.”

Mayanjano oipa: Ngati kagulu kena kanakuuzani kuti kanadziŵa njira ya kupezera ndalama popanda kugwira ntchito kwambiri, kodi mukanapita nako? “Usayende nawo m’njira; Letsa phazi lako ku mayendedwe awo; pakuti mapazi awo athamangira zoipa, Afulumira kukhetsa mwazi.” (Miy. 1:10-19) Ngati munthu saali wolambira Yehova, koma akuwonekera kukhala wabwinodi, kodi mukanamuwona monga bwenzi loyenerera? Sekemu anali mwana wamwamuna wa kalonga Wachikanani, ndipo Baibulo limanena kuti anali “wolemekezedwa woposa onse apabanja la atate wake,” koma iye “anamtenga [Dina] nagona naye, namuipitsa.” (Gen. 34:1, 2, 19) Kodi chenicheni chakuti anthu ena sangakhulupirire chowonadi chimene munaphunzira m’Mawu a Mulungu chimapanga kusiyana kwa inu? “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akor. 15:33) Kodi ndimotani mmene Yehova angalingalirire ngati munasankha anthu amene samamkonda kukhala mabwenzi anu? Kwa mfumu ya Yuda imene inachita zimenezo, wolankhulira Yehova anati: “Chifukwa cha ichi ukugwereni mkwiyo wochokera kwa Yehova.”—2 Mbiri 19:1, 2.

Kodi ndani amene anasonkhezera anthu kukhala aufulu kupanga zosankha zawo popanda kuŵerengera malamulo a Mulungu?

Gen. 3:1-5: “Ndipo njoka [imene inagwiritsiridwa ntchito ndi Satana monga cholankhulira; wonani Chivumbulutso 12:9] . . . inati kwa mkaziyo. Eya! Kodi anatitu Mulungu, usadye mitengo yonse ya m’mundamu? Mkaziyo ndipo anati kwa njoka, Zipatso za mitengo ya m’mundamu tidye, Koma zipatso za mtengo umene uli mkati mwa munda, Mulungu anati, Musadye umenewu, musakhudze umenewu, mungadzafe. Njokayo ndipo inati kwa mkaziyo, Kufa simudzafai; chifukwa adziŵa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziŵa zabwino ndi zoipa.”

Kodi ndimzimu wotani umene umasonkhezera munthu pamene anyalanyaza chifuniro cha Mulungu kuti akhutiritse zikhumbo zake?

Aef. 2:1-3: “Ndipo inu, [Mulungu] anakupatsani moyo, pokhala munali akufa ndi zolakwa, ndi zochimwa zanu, zimene munayendamo kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino [limene Satana ali wolamulira wake], monga mwa mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera; amene ife tonsenso tinagonera pakati pawo kale, m’zilakolako zathupi lathu, ndi kuchita zifuniro zathupi, ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo chibadwire, monga otsalawo.”

Kodi ndimakhalidwe odziimiira otani amene ali ofunika kuti awo odzinenera kukhala akutumikira Mulungu apeŵe?

Miy. 16:18: “Kunyada kutsogolera kukuwonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera ku kuphunthwa.”

Miy. 5:12: “Ndi kuti, Bwanji ndinada mwambo, mtima wanga ndi kunyoza chidzudzulo!” (Mkhalidwe wotero ungatsogolere munthuyo m’mavuto aakulu, monga momwe mawu apatsogolo ndi pambuyo akusonyezera.)

Num. 16:3: “Ndipo anasonkhana motsutsana pa Mose ndi Aroni [amene Yehova anali kugwiritsira ntchito monga oyang’anira anthu ake] nanena nawo, Mukula mphamvu inu, pakuti khamu lonse nlopatulika, onsewa, ndipo Yehova ali pakati pawo; mudzikuza bwanji pamsonkhano wa Yehova?”

Yuda 16: “Amenewo ndi odandaula, oderera, akuyenda monga mwa zilakolako zawo (ndipo pakamwa pawo alankhula zazikuluzikulu), akutama anthu chifukwa cha kupindula nako.”

3 Yoh. 9: “Diotrofe uja, wofuna kukhala wamkulu wa iwo, satilandira ife.”

Miy. 18:1: “Wopanduka afunafuna chifuniro chake, nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.”

Yak. 4:13-15: “Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena maŵa tidzapita kuloŵa kumudzi wakutiwakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, ndi kupindula nawo; inu amene simudziŵa chimene chidzagwa maŵa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuwonekera kanthaŵi, ndi pamenepo ukanganuka. Mukadanena inu, Akalola Mulungu, ndipo tikakhala ndi moyo, tidzachita kakutikakuti.”

Pamene chikhumbo cha munthu cha kudzimiira chimtsogolera ku kutsanzira dziko lokhala kunja kwa Mpingo Wachikristu, kodi amaloŵa mu ulamuliro wayani? Ndipo kodi Mulungu amawona motani zimenezi?

1 Yoh. 2:15; 5:19: “Musakonde dziko lapansi kapena za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichiri mwa iye.” “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.”

Yak. 4:4: “Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi ladziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena