Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 2/8 tsamba 14-15
  • Pamene Umbeta Uli Mphatso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pamene Umbeta Uli Mphatso
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chopinga ku Chimwemwe?
  • Mphatso ya Munthu Payekha
  • Muzigwiritsa Ntchito Mwanzeru Nthawi Imene Simuli pa Banja
    Nsanja ya Olonda—2011
  • ‘Ilandireni’
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Umbeta—Khomo la Ntchito Yopanda Chocheukitsa
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Umbeta—Njira Yopatsa Mphoto ya Moyo
    Nsanja ya Olonda—1987
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 2/8 tsamba 14-15

Lingaliro la Baibulo

Pamene Umbeta Uli Mphatso

‘NDILI wosukidwa,’ akudandaula motero mkazi wina Wachikristu amene wakhala mkazi wamasiye kwa zaka zingapo. ‘Ndakhala ndikuyembekezera kupeza wokwatirana naye. Kukhala wotanganitsidwa kumathandiza. Kukhala ndi mabwenzi kumathandiza. Koma ndikufunabe kukwatiwa.’

Pamene muli wofunitsitsadi kukwatira koma kufunafuna kwanuko wokwatirana naye sikuphula kanthu, umbeta sumaoneka konse kukhala mphatso—kungamveke monga ngati munaikidwa m’ndende ya malingaliro amene amakuchititsani kukhala wovutika maganizo ndi wopsinjika. Kapena ngati muli kale ndi banja lanulanu koma muli mbeta, mungakhale ndi thayo lonse la kupeza zofunika zonse za ana anu.

Chotero, mwina simungaone mkhalidwe wanu waumbeta kukhala mphatso. Komabe, ena amaona umbeta kukhala kanthu kamtengo wapatali kwambiri, ndipo amasankha kukhala okha. Chotero kodi umbeta ndi mphatso, ndipo ngati uli mphatso, ndi liti pamene uli wotero ndipo chifukwa ninji? Kodi Baibulo limanenanji?

Chopinga ku Chimwemwe?

Ukwati ungakhale magwero a chisangalalo chachikulu. (Miyambo 5:18, 19) Ena “amakhulupirira kuti njira yopita ku ukwati ndiyo yokha yofikitsa ku chimwemwe ndi chikhutiro,” ikuthirira ndemanga motero Los Angeles Times. Kodi chikalata cha ukwati ndicho “tikiti” yoloŵera ku chimwemwe?

Katswiri wina wa zamaganizo, Ruth Luban, akunena kuti, malinga ndi kunena kwa Los Angeles Times: “Akazi [ndi amuna] angadabwe ndi ukulu wa chikhutiro chimene angapeze pamene aleka kukhala ndi moyo wosakhutira woyembekezera kuti mwamuna [kapena mkazi] adzawawonjola ku moyo wokhala okha.” Inde, umbeta si chinthu chimene chimapinga panjira ya ku moyo wachimwemwe ndi wokhutiritsa. Anthu ambiri osudzulana angavomereze kuti ukwati suli msewu wotsimikizirika wa ku chimwemwe. Chimwemwe chenicheni chili chipatso cha unansi wabwino ndi Mulungu. Chotero, Mkristu angathe kukhala wachimwemwe kaya ndi mbeta kapena wokwatira.—Salmo 84:12; 119:1, 2.

Kuwonjezera pa kutchula zopinga zochititsidwa ndi munthu mwini, Marie Edwards ndi Eleanor Hoover, m’buku lawo lakuti The Challenge of Being Single, akusonyeza chopinga china ku chimwemwe—kuvutitsidwa ndi anthu. Iwo akuti “lingaliro nlakuti ngati suli wokwatira ukudwala nthenda yamkati, yosadziŵika, ya malingaliro. . . . Ndithudi, chinachake ncholakwika mwa iwe.”

Ngakhale mabwenzi okhala ndi cholinga chabwino mosadziŵa angavutitse kwambiri anthu osakwatira mwa kufunsa modandaula kuti, ‘Kodi mudzakwatira liti?’ kapena, ‘Kodi nchifukwa ninji mwamuna wokongola ngati inu simunapezebe mkazi?’ Ngakhale kuti mawu otere anganenedwe moseka, iwo ‘angapyoze ngati lupanga,’ akumachititsa malingaliro opweteka kapena manyazi.—Miyambo 12:18.

Mphatso ya Munthu Payekha

Mtumwi Paulo anali wosakwatira panthaŵi imene anali kuyendayenda monga mmishonale. Kodi zinali motero chifukwa chakuti anali wotsutsa ukwati? Kutalitali. Mtumwi Paulo anali mbeta chifukwa chakuti anasankha kukhala wosakwatira kaamba ka “uthenga wabwino.”—1 Akorinto 7:7; 9:23.

Paulo anali wokhoza kukhala wasakwatira, komabe anazindikira kuti si aliyense amene angakhale monga iye. Iye anati: “Munthu yense ali nayo mphatso yake ya iye yekha kwa Mulungu, wina chakuti, wina chakuti.”—1 Akorinto 7:7.

Umbeta ungakhale msewu wa ku chimwemwe, ngakhale kuti mwina siumene munafuna kuyendamo. Ndithudi, ukwati ukuphatikizidwa pa mphatso zambiri zolandiridwa kwa Yehova. Koma Baibulo limasonyeza kuti umbeta nawonso ungakhale “mphatso”—ngati mungathe “kulandira ichi.” (Mateyu 19:11, 12; 1 Akorinto 7:36-39) Pamenepa, kodi mapindu ena a umbeta ngotani?

Paulo ananena kuti okwatirana amadera nkhaŵa za ‘kukondweretsa’ anzawo a muukwati, pamene osakwatira amadera nkhaŵa “zinthu za Ambuye.” Zimenezi zimasonyeza limodzi la mapindu aakulu koposa a umbeta—mpata wa kutumikira Yehova ‘popanda chocheukitsa.’—1 Akorinto 7:32-35.

Baibulo silimanena kuti munthu wosakwatira amakhala alibiretu zocheukitsa. Komabe, munthu wokhala yekha kwakukulukulu amakhala ndi zocheukitsa zocheperapo kuposa amene amasamalira banja, chifukwa chakuti amangolingalira za iye yekha popanga chosankha. Mwachitsanzo, pamene Mulungu analangiza Abrahamu kuchoka ku Harana ndi kusamukira ku dziko la Kanani, Baibulo limati: “Abramu anatenga Sarai mkazi wake, ndi Loti mwana wa mphwake, ndi chuma chawo chimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala m’Harana; natuluka kumka ku dziko la Kanani.” (Genesis 12:5) Ngakhale kuti mkhalidwe wa banja la Abrahamu sunamulepheretse, mosakayikira iye anathera nthaŵi yochuluka akukonzekeretsa banja lake kaamba ka ulendowo.

Yerekezerani kusamuka kwa Abrahamu ndi kuja kwa mtumwi Paulo. Pamene Paulo ndi Sila analalikira mbiri yabwino mumzinda wa Tesalonika, gulu la anthu okwiya linawaukira. Usiku umenewo, abale anatulutsa mwamsanga Paulo ndi Sila kuwathaŵitsira ku Bereya. Panthaŵi ina, mu Trowa, Paulo anaona masomphenya akuti ‘aolokere ku Makedoniya kuja, nakawathangate iwo.’ Tsopano pamene anangoona masomphenyawo, anamka ku Makedoniya. Mwachionekere, kukhala wopanda mkazi kwa Paulo kunampatsa ufulu wokulirapo wa kuyenda m’nyengo yaifupi ya nthaŵi, chinthu chimene chikanakhala chovutirapo kwa banja.—Machitidwe 16:8-10; 17:1-15.

Phindu lina limene umbeta umadzetsa ndilo ufulu wokulirapo wa kudzisankhira zinthu. Pamene mukhala nokha, kusankha malo okhalako, chimene mudzadya ndi nthaŵi imene mudzadya, kapena ngakhale nthaŵi imene mudzagona kaŵirikaŵiri kumakhala kopepukirapo. Ufulu umenewu umakhudzanso zinthu zauzimu. Pamakhala nthaŵi yochulukirapo ya kuchita phunziro laumwini la Mawu a Mulungu, kukhala ndi phande mu utumiki wapoyera, ndi kugwiritsira ntchito mipata ya kuthandiza anthu ena.

Chotero, kaya muli mbeta chifukwa cha kusankha kutero kapena chifukwa cha mikhalidwe, khalani wofunitsitsa kugwiritsira ntchito nthaŵi yanu mwanzeru. Mudzakhala ndi moyo wachimwemwe chokulirapo ngati mugwiritsira ntchito umbeta wanu kuthandiza ena. (Machitidwe 20:35) Ngati mukhumba ukwati, musadzikhomere m’ndende ya kuvutika ndi malingaliro kapena kukhala ndi moyo monga ngati munthu wosakwanira chifukwa chakuti ‘wapamtimayo’ sanafikebe. Khalani wotanganitsidwa mu utumiki wa Mulungu, ndipo monga momwe Paulo ananenera, mungapeze kuti umbeta ungakhale mphatso.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena