Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 11/1 tsamba 20-25
  • Pamene Mtendere wa mu Ukwati Wawopsyezedwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pamene Mtendere wa mu Ukwati Wawopsyezedwa
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Uphungu Wouziridwa wa Paulo
  • Maziko a Chilekaniro
  • Kachitidwe ka Nzeru?
  • Gwirirani Ntchito Kuthetsa Mavuto
  • M’nyumba Zogawanika
  • Sungirirani Mtendere monga Banja Logwirizana
  • Kodi Mungatani Kuti Banja Lanu Liziyenda Bwino?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Kodi Mulungu Wakuitanani mu Mtendere?
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Musataye Mtima Ngati Banja Lanu Silikuyenda Bwino
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Ngati Ukwati Ukufuna Kusweka
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 11/1 tsamba 20-25

Pamene Mtendere wa mu Ukwati Wawopsyezedwa

“Mkazi asasiye mwamuna wake; . . . mwamuna asalekane naye mkazi.”​—1 AKORINTO 7:10, 11.

1. Nchiyani chomwe chinali chifuno cha Yehova ponena za ukwati?

YEHOVA MULUNGU anagwirizanitsa anthu aŵiri oyamba mu ukwati ndipo anafuna kuti chomangira cha thupi limodzi chimenechi chiyenera kukhala kosatha. Chinayenera kukhala chigwirizano chodalitsidwa chomwe chikatulukamo m’chimwemwe chawo ndi kutulutsa mbadwa zolungama, zonse ku ulemerero wa Mulungu.​—Genesis 1:27, 28; 2:24.

2. Ndi nsonga imodzi iti yomwe imatsogolera ku kuthetsa kwa zomangira za ukwati?

2 Kakonzedwe kabwino ka ukwati kameneko kanasokonezedwa ndi kuligalira kodziimira pawokha ndi chimo. (Genesis 3:1-19; Aroma 5:12) M’chenicheni, mzimu wa kudziimira paokha uli umodzi wa zinthu zomwe zimatsogolera ku kuwononga zomangira za ukwati lerolino. Chotero, mu United States mkati mwa 1985, panali zisudzulo 5​—kuyerekezedwa ndi maukwati 10.2​—pa anthu 1,000. Mu 1986 ripoti lochokera ku Moscow linasonyeza kuti kokha 37 peresenti ya maukwati mu Soviet Union amatha zaka zitatu ndipo kuti 70 peresenti amatha mkati mwa zaka khumi.

3. (a) Nchiyani chomwe chingapangitse kuwombana kwa mu ukwati? (b) M’chigwirizano ndi ukwati, ndani amene ali wakuswa mtendere wamkulu?

3 Mzimu wa kudziimira paokha ungapangitse mkwiyo wa mu ukwati. Iwo umatsenderezanso kukula kwauzimu, popeza kuti “chipatso cha chilungamo chifesedwa mumtendere kwa iwo akuchita mtendere.” (Yakobo 3:18) Koma ndani amene ali wakuswa mtendere wamkulu? Satana. Ndipo chiri chomvetsa chisoni chotani nanga pamene aliyense wa atumiki a Mulungu “alola malo kaamba ka Mdyerekezi” ndipo chotero kulephera kusangalala ndi nyumba za mpumulo ndi mtendere!​—Aefeso 4:26, 27.

4. Pamene okwatirana Achikristu ali ndi mavuto okulira a mu ukwati, nchiyani chimene iwo ayenera kuzindikira ndipo nchiyani chimene ayenera kuchita?

4 Pamene okwatirana Achikristu awona kulekana monga yankho lokha ku mavuto awo a mu ukwati, iwo ali m’ngozi ya kukhoterera ku zipangizo za Satana, ndipo pali chinachake cholakwika moipa mwauzimu. (2 Akorinto 2:11) Maprinsipulo a Mulungu sakugwiritsiridwa ntchito mokwanira ndi mmodzi kapena ndi onse aŵiriwo. (Miyambo 3:1-6) Chotero iwo ayenera mwamsanga kupanga zoyesayesa za pemphero kuthetsa kusiyana kwawo. Ngati izi zikuwonekera kukhala zosagwirizanitsika, akulu a mumpingo angafikiridwe. (Mateyu 18:15-17) Ngakhale kuti amuna amenewa sali opatsidwa lamulo kuuza akhulupiriri anzawo kwenikweni chimene ayenera kuchita ponena za mavuto awo a mu ukwati, iwo angatsogoze chisamaliro ku chimene Malemba amanena.​—Agalatiya 6:5.

5. Ndi pa maziko otani pamene chisudzulo limodzi ndi kuthekera kwa kukwatiranso wina wake kuli kovomerezeka mwa Malemba?

5 Ngati mkhalidwe wa mu ukwati uli woipa kwambiri kotero kuti okwatirana Achikristu afikira ngakhale pa kulingalira chisudzulo, akulu angaloze kuti chisudzulo ndi kukwatiranso ziri zolandirika mwa Malemba kokha ngati mnzake wa mu ukwati wa wina wachita “dama.” Liwu limeneli limakuta chigololo ndi mitundu ina ya unansi woipa wa kugonana ndi kusayeruzika. (Mateyu 19:9; Aroma 7:2, 3; onani Nsanja ya Olonda, March 15, 1983, tsamba 31, Chingelezi.) Komabe, bwanji ngati “dama” silinachitidwe koma mtendere wa mu ukwati wawopsyezedwa mowopsya? Nchiyani chimene Malemba amanena ponena za kulekana kwa lamulo kapena kwenikweni?

Uphungu Wouziridwa wa Paulo

6. (a) Ndi iti yomwe iri nsonga yaikulu ya uphungu wa Paulo pa 1 Akorinto 7:10, 11? (b) Ndimotani mmene okwatirana Achikristu ayenera kuthetsera mavuto aukwati?

6 M’kuyesayesa kuthandiza okwatirana Achikristu amene zomangira za ukwati wawo zawopsyezedwa, akulu angatsogoze chisamaliro ku mawu a mtumwi Paulo: “Koma okwatitsidwawo ndiwalamulira, si ine ayi koma Ambuye, kuti mkazi asasiye mwamuna; komanso ngati amsiya, akhale wosakwatiwa kapena ayanjanitsidwenso ndi mwamunayo; ndipo mwamuna asalekane naye mkazi.” (1 Akorinto 7:10, 11) Okwatira Achikristu ayenera kukhala okhoza kukhazikitsa mavuto awo, akumalola kaamba ka kupanda ungwiro kwaumunthu. Palibe vuto limene liyenera kukhala lokulira kotero kuti silingathe kuthetsedwa mwa kupemphera mofunitsitsa, kugwiritsira ntchito maprinsipulo a Baibulo, ndi kusonyeza chikondi chomwe chiri chipatso cha mzimu wa Mulungu.​—Agalatiya 5:22; 1 Akorinto 13:4-8.

7. (a) Ngati okwatirana Achikristu alekana, nchiyani chomwe chiri mkhalidwe wawo wa m’Malemba? (b) Kulekana kwa Akristu aŵiri okwatirana kungakhale ndi chotulukapo chotani pa mwaŵi wa utumiki?

7 Koma bwanji ngati okwatirana Achikristu alekana? Iwo ayenera “kukhala osakwatira kapena ayanjanitsidwenso.” Kusiyapo kokha ngati liri funso la chisudzulo chopezedwa pa maziko a “dama,” palibe aliyense wa iwo amene mwa Malemba ali waufulu kukwatiranso. M’chiyang’aniro cha ichi ndi “kuchuluka kwa dama,” chikakhala chabwino kwa iwo “kuyanjananso” mosachedwa. (1 Akorinto 7:1, 2) Siiri ntchito ya akulu kulamulira kuti mwamuna ndi mkaziyo athetse kulekana kwawo, koma iwo sangayeneretsedwe kaamba ka mwaŵi wina wa utumiki chifukwa cha mavuto awo a ukwati. Mwachitsanzo, ngati mwamuna “sadziŵa kuweruza nyumba yake ya iye yekha,” iye mwachidziŵikire akusoweka kuthekera kwa “kusungampingo wa Mulungu” monga woyang’anira.​—1 Timoteo 3:1-5, 12.

8. Ndi iti yomwe iri nsonga ya uphungu wa Paulo pa 1 Akorinto 7:12-16?

8 Chigogomezero chikuikidwa pa kusungirira ukwati ngakhale ngati mnzawo wa mu ukwati mmodzi yekha ali wokhulupirira. Paulo analemba kuti: “Ngati mbale wina ali naye mkazi wosakhulupirira, ndipo iye avomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye; ndipo mkazi amene ali naye mwamuna wosakhulupirira, navomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye mwamunayo. . . . Koma ngati wosakhulupirirayo achoka, achoke; m’milandu yotere samangidwa ukapolo mbaleyo kapena mlongoyo, koma Mulungu watiitana ife mumtendere. Pakuti udziŵa bwanji mkazi iwe, ngati udzapulumutsa mwamunayo? Kapena, udziŵa bwanji mwamuna iwe, ngati udzapulumutsa mkaziyo?” (1 Akorinto 7:12-16) Ngati wosakhulupirirayo asankha kuchoka, Mkristuyo adzamulola iye kupita. Koma wokhulupirirayo, akumayembekezera kuti wosakhulupirirayo angapindulidwe ku Chikristu, sadzayambitsa kulekanako. Amayi a Timoteo, Yunike, mwachidziŵikire anakhala ndi mwamuna wawo wosakhulupirira koma anapereka malangizo auzimu kwa mwana wawo.​—2 Timoteo 1:5; 3:14, 15.

Maziko a Chilekaniro

9, 10. (a) M’chiyang’aniro cha 1 Timoteo 5:8, ndi ati omwe ali maziko amodzi a kulekana kwa okwatirana? (b) Nchiyani chomwe akulu oikidwa ayenera kuchita ngati mwamuna Wachikristu azengedwa mlandu wa kukana kuchirikiza mkazi wake ndi ana?

9 Mawu a Paulo pa 1 Akorinto 7:10-16 amalimbikitsa anthu okwatirana kukhala pamodzi. Komabe, ena, pambuyo pa kuyesera mwamphamvu kusungirira unansi wawo waukwati, potsirizira pake agamulapo kuti, m’chikumbumtima chonse, iwo alibe chosankha koma kulekana. Nchiyani chomwe chingakhale maziko kaamba ka sitepi loterolo?

10 Kusachirikiza kodzifunira kuli maziko amodzi a chilekaniro. Pamene mulowa mu ukwati, mwamuna amatenga thayo la kupereka kaamba ka mkazi wake ndi ana alionse omwe angakhale nawo. Mwamuna yemwe sapereka kaamba ka ziwalo za banja lake “wakana chikhulupiriro ndipo aipa koposa wosakhulupirira.” (1 Timoteo 5:8) Chotero kulekana kuli kothekera ngati pali kusachirikiza kodzifunira. Ndithudi, akulu oikidwa ayenera kupereka kulingalira kosamalitsa ku mlandu wakuti Mkristu akukana kuchirikiza mkazi wake ndi banja. Kukana kouma mutu kuchirikiza banja la wina kungatulukemo m’kuchotsedwa.

11. Ndi ati omwe ali maziko ena a kulekana, koma nchiyani chomwe chingapangitse mkhalidwewo kukhala wopiririka?

11 Kuipsya konkitsa kwakuthupi kuli maziko ena a chilekaniro. Tangolingalirani kuti mnzamu wa mu ukwati wosakhulupirira kaŵirikaŵiri amaledzera, kukhala waukali, ndi kupangitsa kuvulaza kwa kuthupi kwa wokhulupirirayo. (Miyambo 23:29-35) Kupyolera m’pemphero ndi mwa kusonyeza chipatso cha mzimu wa Yehova, wokhulupirirayo angakhale wokhoza kuchinjiriza kuwukira koteroko ndi kupanga mkhalidwewo kukhala wopiririka. Koma ngati nsonga yafikirikwa kumene umoyo ndi moyo wa mnzanu wa mu ukwati woipsyidwayo uli kwenikweni m’ngozi, kulekana kungakhale kovomerezeka mwa Malemba. Kachiŵirinso, akulu a mu mpingo ayenera kuyang’ana m’milandu ya kuipsyidwa kwa kuthupi pamene akristu aŵiri alowetsedwa mu ukwati wovutitsidwa, ndipo kachitidwe ka kuchotsa kangayenere kutengedwa.​—Yerekezani ndi agalatiya 5:19-21; Tito 1:7.

12. (a) Ndimotani mmene uzimu wa wokhulupirirayo ungakhalire ndi chiyambukiro pa funso la kulekana? (b) Nchiyani chomwe chalingaliridwa ngati mkhalidwe wopanda umoyo wauzimu uli m’nyumba Yachikristu?

12 Kuikidwa m’ngozi kotheratu kwauzimu nakonso kungapereke maziko a kulekana. Wokhulupirirayo m’nyumba yogawanikana mwachipembedzo ayenera kuchita chirichonse chothekera kutenga mwaŵi wa makonzedwe auzimu a Mulungu. Koma kulekana kuli kovomerezeka ngati chitsutso cha mnzanu wa mu ukwati wosakhulupirirayo (mwinamwake kuphatikizapo kuletsa kwa kuthupi) kuchipangitsa icho mowona mtima kukhala chosatheka kutsatira kulambira kowona ndipo m’chenicheni kuika m’ngozi uzimu wa wokhulupirirayo. Komabe, bwanji ngati mkhalidwe woipa wauzimu ulipo kumene okwatirana onse aŵiri ali okhulupirira? Akulu ayenera kupereka chithandizo, koma makamaka mwamuna wobatizidwayo afunikira kugwirirapo ntchito mwakhama kukonza mkhalidwewo. Ndithudi, ngati mnzanu wa mu ukwati wobatizidwa akuchita ngati wampatuko ndipo akuyesera kuletsa mnzake wa mu ukwati kutumikira Yehova, akulu ayenera kusamalira nkhaniyo mogwirizana ndi Malemba. Ngati kuchotseda kuchitika m’nkhani yokhudza kuikidwa m’ngozi kotheratu kwauzimu, kusachirikiza kodzifunira, kapena kuipsya kwa kuthupi konkitsa, Mkristu wokhulupirikayo yemwe akafuna chilekaniro cha lamulo sadzakhala akutsutsana ndi uphungu wa Paulo wonena za kutengera wokhulupirirayo ku bwalo lamilandu.​—1 Akorinto 6:1-8.

13. Ndi pansi pa mikhalidwe yotani pamene kulekana kwa okwatirana kungaperekedwe?

13 Ngati mikhalidwe iri yonkitsa, chotero, kulekana kungaperekedwe. Koma kuneneza konyengezera mwachidziŵikire sikuyenera kugwiritsiridwa ntchito kuti mupeze chilekaniro. Akristu alionse omwe akalekana ayenera kukhala ndi thayo laumwini kaamba ka kachitidwe koteroko ndipo ayenera kuzindikira kuti tonsefe tidzapereka kuŵerengera kwa Yehova.​—Ahebri 4:13.

Kachitidwe ka Nzeru?

14. (a) Ndi vuto lotani limene kulekana kuli kothekera kupangitsa? (b) Ndimotani mmene kulekana kungayambukirire ana?

14 Kulingalira kwa pemphero kuyenera kuperekedwa ku mavuto omwe kulekana kuli kothekera kuyambitsa. Mwachitsanzo, banja la kholo limodzi kaŵirikaŵiri silimapereka zimene mabanja a makolo aŵiri angachite m’kulinganizika ndi chilango. Ndipo kulekana kungakhale ndi chiyambukiro kwa ana mofanana ndi chija cha chisudzulo, ponena za chimene magazini ya India Today inasimba kuti: “Sheena, wokhala ndi maso a akulu omwe akuwoneka kukhala akuwona dziko lonse, ali ndi zaka zisanu ndi chimodzi. Makolo ake anasudzulana zaka ziŵiri zapitazo pambuyo pa kumenyera koipitsitsa kwa m’bwalo lamilandu. Mwamsanga pambuyo pake, atate ake anakwatira mkazi wina. Kwa chaka chimodzi iye anali ndi kuwukiridwa koipa kwa phumu ndipo mokhazikika anali kuyamwa chala chake cha manthu. Iye amakhala ndi amayi ake mu south Delhi. Mayiyo akuti: ‘Chisoni changa chasamukira kwa Sheena. . . . Iye amawalakalaka atate ake. . . . Iye ali wachikulire koposa ana ambiri a msinkhu wake. Koma iye ali ndi kuwulika kwa kulira kosalamulirika kumeneku, ngati kuti iye akufuna kuchotsa chinachake mwa iyemwini. Sukulu inali vuto. Ana angakhale ankhalwe chotero. Kaŵirikaŵiri, iye amathaŵira m’dziko lopeka: iye amapanga nthano yonena za tonsefe pamodzi tikupita kwa mabwenzi ake.’ “

15. Ndi chiyambukiro chotani chimene kulekana kungakhale nako pa mwamuna kapena mkazi Wachikristu?

15 Kaŵirikaŵiri, kulekana sikumagwira ntchito bwino kaamba ka mwamuna ndi mkazi Wachikristu. Iwo mwamsanga amaphunzira kuti popanda mnzawo wa mu ukwati kapena ana pamakhala chosoweka chokhalirira. Zosafunikira kunyalanyazidwa ziri zitsenderezo zotulukapo kuchokera m’kulekana. Kodi chikakhala chothekera usamalira kaamba ka nkhani kuchokera ku kawonedwe ka za chuma kapena mwa njira ina yake? Ndipo bwanji ngati chitsenderezo cha kulekana chitulukapo kugwera mu mkhalidwe woipa? Yesu ananena kuti: “Nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake.” (Mateyu 11:19) Makamaka pamene okwatirana aŵiri onsewo ali Akristu, chomwe chagwiriridwa ntchito kupyolera m’kulekana nthaŵi zina chatsimikizira kukhala chopanda nzeru koposa.

Gwirirani Ntchito Kuthetsa Mavuto

16. Okwatirana Achikristu omwe amapeza mtendere wawo wa mu ukwati kukhala wowopsyezedwa ayenera kuchita chiyani?

16 Okwatirana Achikristu omwe amapeza mtendere wawo wa mu ukwati kukhala wowopsyezedwa mokulira ayenera kukambitsirana kusiyana kwawo m’njira yopindulitsa awo omwe akutumikira Mulungu. Ndipo iwo ndithudi amafunikira kupanga zilolero kaamba ka kupanda ungwiro. (Afilipi 2:1-4) Koma nchiyani chinanso chimene chingachitidwe?

17. Ndimotani mmene kusonyeza nzeru m’chigwirizano ndi zinthu za kuthupi kungathandizire ku mtendere wa ukwati?

17 Kusonyeza nzeru m’chigwirizano ndi zinthu za kuthupi kungathandizire ku mtendere wa mu ukwati. Kuti tichitire chitsanzo: Pambuyo pa kulingalira kawonedwe kotsutsa ka mkazi wake, mwamuna angagamule, mosasamala kanthu za chimenecho, kuti chiri chanzeru kwa banja lake kusamukira kwina kwake. Ichi chingawoneke kukhala choyenera kaamba ka zifukwa za chuma, koma chingatheketsenso banjalo kupititsa patsogolo zikondwerero za Ufumu mwa kutumikira kumene kusowa kuli kokulirapo. (Mateyu 6:33) Mkazi wake Wachikristu sangayanje kusamukako chifukwa chakuti akakhala akusiya kumbuyo makolo ake kapena malo omuzinga ozolowereka. Koma iye akakhala wanzeru kugwirizana kotheratu ndi mwamuna wake, yemwe ali mutu wa banja ndipo ali ndi thayo la kugamulapo kumene banja lake liyenera kukhala. Kuwonjezerapo, kugonjera kwake ndi kugwirizana kwachikondi kudzathandizira ku mtendere wa banja.​—Aefeso 5:21-24.

18. Ndi mwaŵi wotani umene okwatirana achikristu ali nawo wa kuchitira zinthu pamodzi?

18 Mtendere wa banja umakula ndipo mavuto amawoneka kukhala osawopsya kwenikweni pamene okwatirana achitira zinthu pamodzi. Mwachitsanzo, okwatirana Achikristu ali ndi mwaŵi wochulukira wa kugwirira ntchito limodzi mu utumiki wa m’munda. Ngati iwo achita ichi mokhazikika ndi kutenga ana awo limodzi nawo, banja lonse lidzapindula. Pangakhalenso mwaŵi wosiyanasiyana wa kulimbitsira chomangira cha ukwati mwa kugawana m’machitachita ena opindulitsa makamaka awo osangalalidwa ndi mmodzi wa mu ukwati kapena winayo.

19. Ndi umutu wa mtundu wotani umene ungapititse patsogolo mtendere wa banja?

19 Umutu wochitidwa moyenerera udzalimbikitsa zomangira za ukwati. Ndithudi, mwamuna wachikulire Wachikristu sadzakhala wolamulira wa nkhalwe. M’malomwake, ‘iye adzakonda mkazi wake ndipo sadzamuwawira mtima.’ Yehova amamuyembekezera iye kusonyeza umutu wachikondi. (Akolose 3:18, 19) M’kubwezera, umutu woterowo umapititsa patsogolo mtendere wabanja.

M’nyumba Zogawanika

20, 21. Ndimotani mmene kulingalira kungatsimikizire kukhala kopindulitsa pamene mtendere wawopsyezedwa m’nyumba yogawanikana mwachipembedzo?

20 Kukhala wolingalira kumathandiza m’kuthetsa mavuto a mu ukwati pakati pa okwatirana Achikristu. (Afilipi 4:5) Koma kulingalira kulinso kofunika kwambiri ngati mtendere wawopsyezedwa m’nyumba yogawanikana mwachipembedzo. Ngati mwamuna wosakhulupirira ayesera kuletsa mkazi wake Wachikristu kutumikira Yehova, iye angakalamire kulingalira ndi iye, mwa machenjera akumaloza kuti iye amampatsa iye ufulu wa chipembedzo ndipo iye mwanzeru ayenera kulandira kachitidwe kofananako. (Mateyu 7:12) Ngakhale kuti iye ayenera kukhala wogonjera kwa mwamuna wosakhulupirira, chifuno cha Mulungu chiyenera kuchitidwa pamene pali kuwombana. (1 Akorinto 11:3; Machitidwe 5:29) Ndithudi, kupezeka pa misonkhano Yachikristu nthaŵi zitatu pa mlungu sikuli konkitsa. Koma mkazi wokhulupirirayo angachipeze icho kukhala chanzeru kukhala panyumba pa madzulo ena ndi kuika ndandanda yokulira ya utumiki wa m’munda mkati mwa maora pamene mwamuna wake akugwira ntchito ndipo ana ali ku sukulu. Molingalira ndi kukonzekera kwabwino, iye safunikira “kuleka kuchita chabwino.”​—Agalatiya 6:9.

21 Kulingalira kumafutukukira ku nkhani zinanso. Mwachitsanzo, munthu ali ndi kuyenera kwa kuchita kachitidwe ka chipembedzo chinachake. Koma chikakhala cholingalira ndi chanzeru kwa mkazi Wachikristu kusaika maBaibulo ake ndi zothandizira phunziro la Baibulo kumene mwamuna wotsutsa mwamphamvuyo angaletse. Kuwombana kungapewedwe ngati zofalitsidazo ziikidwa pakati pa zinthu zake zaumwini ndipo aphunzira izo mwamseri. Ndithudi, iye sayenera kugonjera kuchoka ku maprinsipulo olungama.​—Mateyu 10:16.

22. Nchiyani chomwe chingachitidwe ngati kusokonezeka kwa mtendere wa banja kwazikidwa pa malangizo a chipembedzo a ana?

22 Ngati kusokonezeka kwa mtendere wa m’banja kuzikidwa pa malangizo a chipembedzo a ana, mkazi wokhulupirirayo mochenjera angakonze kukhala ndi iwo akutsagana naye ku misonkhano ndi mu utumiki wa m’munda. Koma ngati mwamuna wosakhulupirirayo ndi atate aletsa chimenechi, iye angaphunzitse anawo maprinsipulo a Baibulo kotero kuti pamene iwo akula ndi kuchoka pa nyumba, ali ndi kuthekera kwa kulondola kulambira kowona. Ngati mwamuna ali wokhulupirira, monga mutu wa banja, iye ali ndi thayo la m’Malemba la kulera ana monga Akristu. Chotero iye ayenera kuphunzira Baibulo ndi iwo, kuwatenga iwo ku misonkhano, ndi kuwaphunzitsa mu utumiki wa m’munda. (Aefeso 6:4) Mwachibadwa, iye ayenera kukhala wachifundo, wachikondi, ndipo wolingalira m’kuchta ndi mkazi wake wosakhulupirira.

Sungirirani Mtendere monga Banja Logwirizana

23. Ngati mtendere wa mu ukwati wawopsyezedwa, nchiyani chomwe chingatsimikizire kukhala chothandiza?

23 Popeza anthu okwatirana ali “thupi limodzi,” iwo ayenera kukhalira limodzi mu mtendere m’chigwirizano ndi kakonzedwe ka Mulungu kaamba ka anthu okwatirana, makamaka ngati aŵiri onsewo ali Akristu. (Mateyu 19:5; 1 Akorinto 7:3-5) Koma ngati mtendere wa m’banja wawopsyezedwa m’nkhani yanu, bwereranimo mwapemphero m’nsonga za m’Malemba zomwe zangotchulidwa kumenezo. Chingakhalenso chothandiza kulingalira m’mbuyo ku nthaŵi ya kutomerana kwanu. Ndi mwamphamvu chotani nanga mmene nonse aŵirinu munayeserera kuchita chomwe chinali cholondola ndi kuyala maziko kaamba ka kugwirizana kwa chimwemwe! Kodi tsopano mungayese zoyesayesa zofananazo mkusungirira ukwati wanu pamodzi?

24. Ndi mkhalidwe wotani umene akristu ayenera kukhala nawo kulinga ku ukwati?

24 Akristu ogwirizana mu ukwati ali ndi mphatso yodabwitsa kuchokera kwa Mulungu​—ukwati wawo! Ngati mukhalirira ku malumbiro a ukwati ndi kusungirira umphumphu kwa Yehova, kutsogolo kwanu kuli dziko latsopano lolungama mu limene kulekana kowawitsa mtima ndi chisudzulo sizikakhalanso mliri wa mtundu wa anthu. Chotero sonyezani chiyamikiro kaamba ka ukwati monga “chingwe cha nkhosi zitatu” chophiphiritsira, ndi Yehova monga mbali yokulira ya icho. (Mlaliki 4:12) Ndipo lolani kuti ziwalo zonse za m’banja lanu logwirizana zisangalale ndi dalitso la chimwemwe cha banja m’nyumba ya mpumulo ndi mtendere.

Ndi Ati Omwe Ali Mayankho Anu?

◻ Ndimotani mmene mungatsanzirire uphungu wa Paulo pa 1 Akorinto 7:10-16?

◻ Ndi ziti zomwe ziri zifukwa zoyenerera kaamba ka kulekana kwa anthu okwatirana?

◻ Ndimotani mmene Akristu angathetsere mavuto pamene mtendere wa ukwati wawopsyezedwa?

◻ M’nyumba zogawanikana mwachipembedzo, ndimotani mmene kulingalira kungathandizire ku mtendere?

[Chithunzi patsamba 23]

Okwatirana Achikristu amene mtendere wawo wa mu ukwati wawopsyezedwa ayenera kukambitsirana mavuto awo m’njira yopindulitsa awo otumikira Yehova

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena