-
Achinyamata, Sankhani Kutumikira YehovaNsanja ya Olonda—2006 | July 1
-
-
Masiku Ano Munthu Sabadwa Ali Wodzipereka
3, 4. Kodi n’chiyani chimene chingathandize ana amene makolo awo ndi odzipereka kuti adzipereke mwa kufuna kwawo?
3 Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amaona ana aang’ono kukhala oyera ngakhale ngati kholo limodzi ndi limene lili Mkristu wokhulupirika. (1 Akorinto 7:14) Kodi ndiye kuti ana ngati amenewo ndi atumiki odzipereka a Yehova chifukwa cha zimenezi? Ayi. Koma ngakhale zili choncho, ana oleredwa ndi makolo odzipereka kwa Yehova amalandira maphunziro amene angathandize anawo kudzipereka okha kwa Yehova. Mfumu Solomo yanzeru inalemba kuti: “Mwananga, sunga malangizo a atate wako, usasiye malamulo a mako. . . . Adzakutsogolera ulikuyenda, ndi kukudikira uli m’tulo. Ndi kulankhula nawe utauka. Pakuti malangizo ndi nyali, malamulo ndi kuunika; ndi zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo.”—Miyambo 6:20-23.
-
-
Achinyamata, Sankhani Kutumikira YehovaNsanja ya Olonda—2006 | July 1
-
-
Senzani Udindo Wanu
12. (a) Ngakhale kuti makolo angaphunzitse ana awo, kodi n’chiyani chimene iwo sangachitire ana awowo? (b) Kodi ndi liti pamene mwana amakhala ndi udindo woyankha kwa Yehova pa zosankha zimene amapanga?
12 Nthawi imafika pamene ananu mumasiya kukhala otetezeka chifukwa cha kukhulupirika kwa makolo anu. (1 Akorinto 7:14) Wophunzira Yakobo analemba kuti: “Kwa iye amene adziwa kuchita bwino, ndipo sachita, kwa iye kuli tchimo.” (Yakobo 4:17) N’zosatheka kuti makolo atumikire Mulungu chifukwa cha ana awo kapena ana kutumikira Mulungu chifukwa cha makolo awo. (Ezekieli 18:20) Kodi mwaphunzira za Yehova ndi zolinga zake? Kodi mwafika pa msinkhu woti mukumvetsa zimene mwaphunzira ndipo mungakhale pa ubwenzi wanuwanu ndi iye? Ngati mwatero, kodi si pake kuganiza kuti Mulungu akuona kuti mutha kusankha nokha kum’tumikira?
-