Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 4/15 tsamba 10-15
  • Kupeza Mtendere ndi Mulungu mwa Kudzipereka ndi Ubatizo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupeza Mtendere ndi Mulungu mwa Kudzipereka ndi Ubatizo
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Maziko Kaamba ka Mtendere
  • Kulandira “Chizindikiro”
  • Ubatizo​—Kaamba ka Yani?
  • Kulaka Zipsinjo
  • Ubatizo Umatithandiza kuti Tikhale pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Mmene Ubatizo Ungatipulumutsire Ife
    Nsanja ya Olonda—1989
  • N’chifukwa Chiyani Tifunika Kubatizidwa?
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kukwaniritsa Zimene Zimafunika Paubatizo Wachikristu
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 4/15 tsamba 10-15

Kupeza Mtendere ndi Mulungu mwa Kudzipereka ndi Ubatizo

“Ndipo Yehova ananena naye, ‘. . . koma musayandikira munthu aliyense ali nacho chizindikiro.’”​—EZEKIELI 9:4, 6.

1, 2. (a) Kodi nchifukwa ninji anthu sali pa mtendere ndi Mulungu? (b) Kodi nchifukwa ninji chiri chofunika kwa onse kupeza mtendere wote rowo?

KUPEZA mtendere ndi Mulungu? Koma nchifukwa ninji? Anthu ochepa amadzilingalira iwo eni kukhala otsutsana ndi Mulungu. Kodi icho chiri chothekera ngakhale kuli tero, kukhala mdani weniweni wa Mulungu ndi kukhala osazindikira icho? Mtumwi Paulo ana longosola kwa Akristu mu zana loyamba: “Inde, pakati pawo ife tonse panthawi ina tinadzisungira mogwirizana ndi zikhumbo zathupi lathu, ndi kumachita zinthu zofunidwa ndi thupindi maganizo, ndipo mwachibadwa tinali ana a mkwiyo mofanana ndi ena onse.”​—Aefeso2:3, NW.

2 Mofananamo lerolino, ngakhale kuti mungakhale osangalatsidwa m’kukondweretsa Mulungu, tchimo lacholowa kuchokera kwa Adamu limayambukira kayang’anidwe kanu ndipo lingakupangitseni inu kulondola “zinthu zokhumbidwa ndi thupi.” Ngakhale ngati muli munthu amene akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova kapena wachichepere wosabatizidwa amene makolo anu ali Mboni, khalidwe lozikidwa pa inumwini la ‘chita monga ndikufunira’ lingawonekere mokulira m’moyo wanu ndi kupitiriza kukuchotsani inu kuchokera kwa Mulungu. Munthu amene amasunga njira yoteroyo ali ‘kudzikundikira mkwiyo iyemwini.’ (Aroma 2:5; Akolose 1:21; 3:5-8) Mulungu adzasonyeza mkwiyo wake kotheratu mkati mwa “tsiku lamkwiyo ndi lakuvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu” lomayandikira mwamsanga. (Aroma 1:28-2:6) Kodi ndimotani mmene mungapezere mtendere ndi Mulungu ndi kupulumuka “tsiku lamkwiyo limeneli”?

Maziko Kaamba ka Mtendere

3. Kodi ndimotani mmene Mulungu anaperekeramaziko kaamba ka chiyanjanitso?

3 Yehova anapanga chiyambi cha kufuna kuthandiza. “Iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiwombolo chifukwa cha machimo athu.” (1 Yohane 4:10) Imfa ya nsembe ya Yesu imawombola, kunena kuti, kutonthoza kapena kukwaniritsa chilungamo cha Yehova. Ichi chimapereka maziko alamulo kaamba ka kukhululukira machimo ndipo pambuyo pake, kaamba kakuchotsa kotheratu kwa udani pakati pa Mulungu ndi munthu. Inde, chiri chotheka kukhala “oyanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake,” monga mmene analembera mtumwi Paulo.​—Aroma 5:8-10.

4. Kodi ndi masomphenya oyenerera otani amene anaperekedwa kwa Ezekieli, ndipo nchifukwa ninji ali ofunika kwa ife?

4 Koma kuti tipindule mwaumwini kuchokera ku nsembe ya Kristu, tiyenera kutenga masitepi ena ake. Awa asonyezedwa mu masomphenya achitsanzo operekedwa kwa mneneri Ezekieli. Masomphenya amene akukwaniritsidwa mkati mwa nthawi yathu pamene “tsiku lamkwiyo” la Mulungu tin pafupi kwambiri. Gulu lakupha la Mulungu lachitiridwa chithunzi mumasomphenya ndi amuna azida asanu ndi mmodzi. Amuna amenewa asanapereke mkwiyo wa Mulungu, mwamuna wachisanu ndi chiwiri, atanyamula zolembera, akuuzidwa: “ ‘Pita pakati pa mzinda, . . . nulembe chizindikiro pa mphumi zawo za anthu akuusa moyo ndi kutira chifukwa cha zonyansa zonse zichitidwa pakati pake.’ Nati kwa enawo [amuna azida asanu ndi mmodzi] ndirikumva ine; ‘Pita pakati pa mzinda kumutsata iye ndi kukantha. . . . Koma musayandikira munthu atiyense alinacho chizindikiro.’ ”​—Ezekieti 9:1-6.

5. Kodi nchiyani chimene chimatsogolera ku kulapa?

5 Anthu ‘oikidwa chizindiro’ chachinjirizo amenewo anali odwala chifukwa chakuti anthu odzinenera kuti akulambira Mulungu wowona ‘anadzaza dziko ndi chiwawa’ ndipo anadzilowetsa m’mkhatidwe woipa wakugonana, kulambira mafano, ndi mtundu wina uliwonse wa khatidwe loipa. (Ezekieti 8:5-18; Yeremiya 7:9) Mofananamo lerolino, awo amene ‘akaikidwa chizindikiro’ ayenera kuphunzira choyamba, kudzera muphunziro la Baibulo, kuti awone makhalidwe a Mulungu kukhala amtengo wapatali ndi kukhala oipidwa mu mtima, inde,‘kuusa moyo ndi kulira,’ pa ziphunzitso ndi machitachita omwe samlemekeza iye. Mwinamwake chifukwa chakusazindikira ena anadzilowetsa m’kuchita zoipa kapena kugwirizanitsidwa ndi zimenezo mwakupereka chirikizo lawo. Komabe, tsopano iwo ayamba kuwona machitachita oterowo monga mmene Mulungu amawonera​—ndi kunyansidwa! (Aroma 1:24-32; Yesaya 2:4; Chivumbulutso 18:4; Yohane 15:19) Chiyamikiro chowonjezereka chimenechi chimatsogolera kusitepi loyamba lakupeza mtendere ndi Mulungu: kulapa. Mtuniwi Petro anafulumiza: “Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa [osati zamkwiyoj zochokera ku nkhope ya Yehova.” (Machitidwe 3:19, NW) Ndi kotsitsimula chotani nanga mmene kukhululukidwa koteroko, kuliri!

Kulandira “Chizindikiro”

6. Kodi ndi pa zifukwa ziti pamene anthu ena anaikidwira chizindikiro mkati mwa nthawi za kale?

6 Kuti tipulumutsidwe kuchokera ku mkwiyo wa Mulungu, awo amene ‘akuusa moyo ndi kutira’ ayenera kuikidwa chizindikiro pa mphumi pawo. (Ezekieti 9:4) Mu nthawi zakale akapolo kawirikawiri anali kuikidwa chizindikiro pa mphumi pawo kuti azindikirike bwino. Zizindikiro zosiyanasiyana pa mphumi ndi pena pali ponse zingawonetse kuti munthu analambira mtundu wina wa mulungu.a (Yerekezani ndi Yesaya 44:5) Chotero, mtsiku lathu, kodi nchiyani chimene chiri chizindikiro chapadera, chopatsa moyo chomwe mwachiwonekere chimazindikiritsa eni ake monga olambira owona ndi akapolo a Yehova?

7. Kodi nchiyani chimene chiri chizindikiro chophiphiritsira?

7 Chizindikiro chophiphiritsa chiri chitsimikiziro, monga ngati kuti chasonyezedwa pa mphumi yanu yosaphimbidwa, (1) kuti ndinu wophunzira wodzipereka, wobatizidwa wa Yesu Kristu ndi (2) kutimwavalaumunthu watsopano Wachikristu. (Aefeso 4:20-24) Popeza awo amene ‘aikidwa chizindikiro’ ayenera choyamba kudzipereka, tiyenera kudziwa nchiyani chimene icho chimaphatikizamo. Yesu analongosola: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule [mtengo wozunzirapo wake NW],nanditsate ine.”​—Marko8:34.

8, 9. (a) Kodi nchiyani chimene chimatanthauza ‘kudzikaniza iyemwini’? (b) Kodi ndimotani mmene mungafanizire chimene kudzipereka kumafunikira?

8 Liwu la Chigriki lotanthauzidwa “kudzikaniza” limatanthauza “kukana kotheratu” kapena “kusiya.” Chotero, ‘kudzikaniza inu mwmi’ kumatanthauza koposa kudzimana inu eni chosangulutsa china chake kapena kumwelekera tsopano ndi mtsogolo. Mmalo mwake, chimatanthauza kukhala ofunitsitsa kunena ayi kwa inu mwini pamene chifika kukulola moyo wanu kulamuliridwa ndi zokhumba zanu zaumwini ndi zikhumbo zachipambano. Timathandizidwa kuwona tanthauzo la mawu a Yesu mwakuzindikira ndimotani mmene mbali imeneyi yatanthauzidwira m’zinenero zosiyanasiyana: “Kusiya kuchita zimene mtima wa munthu umafuna” (Tzeltal, Mexico), “osadzikhalira kwa iwe mwini” (K’anjobal, Guatemala) ndi “kudzitembenukira” (Javanese, Indonesia)Inde, ichi chimatanthauza kudzipereka kodzipatulira, osati chabe kudzipereka komwe kungapangidwe ku zinthu zambiri.

9 Mkristu wotchedwa Susan, yemwe poyambirira anali wodzidalira, akulongosola chimene kudzipereka kunatanthauza kwa iye: “Ndinali kudzipereka ine mwini wathunthu kwa wina wake. Yehova tsopano amalingalira njira yanga, kundiuza ine chimene ndingachite, ndi kukhazikitsa zoyambirira zanga.” Kodi muli wofunitsitsa kupanga kudzipereka kodzipatulira kofananako kuchita chifuniro cha Yehova Mulungu? Kumbukirani, chizindikiro chophiphiritsa chimakuzindikiritsani inu monga ‘okhalira moyo’ kwa Mulungu, monga kapolo wachimwemwe kwa Mbuye wake.​—Yerekezani ndi Eksodo 21:5, 6; Aroma 14:8.

10. Kodi ndi nkhani zotani zimene wina ayenera kuzilingalira asanapange kudzipereka?

10 Ndani wa inu amene akufuna kupanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, nawerengera mtengo wake, awone ngati ali nazo zakuimaliza?” Anafunsa Yesu. (Luka 14:28) Chotero kodi muli wofunitsitsa: Kupezeka pa misonkhano Yachikristu mokhazikika? (Ahebri 10:25) Kusunga khalidwe labwino lapamwamba la makhalidwe abwino lokhazikitsidwa ndi Mulungu kaamba ka atumiki ake? (1 Atesalonika 4:3, 4, 7) Kukhala ndi kugawanamo kotheratu mu ntchito yolalikira Ufumu monga momwe mungathere? Kuika chifuniro cha Mulungu poyamba pamene musankha ntchito kapena kukhazikitsa zonulirapo zamoyo? (Mateyu 6:33; Mlaliki 12:1) Kusamalira kaamba ka mathayo anu abanja? (Aefeso 5:22-6:4; 1 Timoteo 5:8) Pamene mwapanga kudzipereka kwaumwini m’pemphero, sitepi lotsatira limathandiza ena kudziwa ichi mwapoyera.

Ubatizo​—Kaamba ka Yani?

11. Kodi nchiyani chimene ubatizo umaphiphiritsira, ndipo nchiyani chimene chimakwaniritsidwa ndi iwo?

11 Yesu analamulira kuti otsatira ake ayenera kubatizidwa. (Mateyu 28:19, 20) Iwo anayenera kumizidwa kotheratu m’madzi ndi kuturutsidwa kuchokera mu iwo. Mofanana ndi kuikidwa mmanda ndi kuukitsidwa, ichi chimaimira bwino kufa kwa munthuyo ku njira yamoyo yozikidwa pa iye mwini ndi kukhala atasankhidwa kukhalanso ndi moyo kuchita chifuniro cha Mulungu. Mwaubatizo mumadzizindikiritsa inu eni monga mmodzi wa Mboni za Yehova m’chigwirizano ndi mipingo yadziko lonse ya Mulungub Ubatizo umayeneretsa chigwirizano chotheratu chopangidwa ndi Mulungu. (Yerekezani ndi Eksoao 19:3-8) Moyo wanu uyenera kukhala m’chigwirizano ndi malamulo ake. (Masalmo 15; 1 Akorinto 6:9-11) Ubatizo, womwe umakukazikitsani inu monga minisitala wa Mulungu, umawunikiranso “chifunsiro chopangidwa kwa Mulungu kaamba ka chikumbumtima chabwino” chifukwa mumadziwa kuti midi pa mtendere ndi Mulungu.​—1 Petro 3:21.

12. Ndi liti pamene ana amachinjirizidwa ndi “chizindikiro cha kholo lawo?

12 Kodi ngakhale achichepere ayenera kulingalira zaubatizo? Chabwino, kumbukiranikuti Yehova anauuza amuna azida asanu ndimmodzi mu masomphenya: “Iphanitu nkhalamba, mnyamata ndi namwali, makanda, ndi akazi; koma musayandikira munthu aliyense ali nacho chizindikiro.” (Ezekieli 9:6) Komabe, ana achichepere kwambiri omwe sangapange kudzipereka adzachinjirizidwa ndi “chizindikiro” cha kholo ngati khololo likukalamira kubweretsa anawo ku kukonda Yehova ndipo ngati iwo momvera amavomereza. (1 Akorinto 7:14) Ngakhale kuli tero, ngati mwana ali wanzeru zokwanira kupanga chosankha chaumwini ndipo wafika ku nsonga kumene iye “amadziwa kuchita chimene chiri chabwino,” musalingalire kuti iye adzapitirizabe kunthawi yosatha pansi pa kuyenerera kwa “chizindikiro” cha makolo ake.​—Yakobo 4:17.

13. Kodi ndi zolingalira ziti zomwe zingasonyeze kukonzekera kwa wachichepere kaamba ka ubatizo?

13 Asanapange kudzipereka, wachichepere ayenera kukhala ndi chidziwitso chokwanira kumvetsetsa zimene zikuphatikizidwamo ndipo ayenera kufunafuna unansi waumwini ndi Mulungu. Iye ayenera kumvetsetsa ndi kumamatira ku maprinsipulo a Baibulo, kudziwa kuti iye adzawerengeredwa kaamba ka kuphophonya kuli konse kuchokera pamenepo. Iye ayeneranso kukhala ndi zokumana nazo zokwanira mkugawana chikhulupiriro chake ndi ena ndi kudziwa kuti iyi iri mbali yofunika kwambiri ya kulambira kowona; iye mowonadi ayenera kufuna kutumikira Yehova. Mwachibadwa, iye sakafunikira kuyembekezeredwa kusonyeza ukulu wa achikulire, koma kupita kwake patsogolo kwauzimu kuyenera kukhala moyenerera kokhazikika.

14. Kodi nchifukwa ninji wachichepere mmodzi analingalira ubatizo wake kukhala chinjirizo?

14 Ngati wina ‘wawerengera mtengo,’ sichimamuika iye patsoka kupanga kudzipereka adakali wachichepere. Ndi chifupifupi Akristu onse achatsopano, pambuyo paubatizo chiyamikiro chimazama. “Kubatizidwa ndidakali wachichepere chinali chitetezero kaamba ka ine,” analongosola motero David. “Pamene ndinali kukula, ndinazindikira ndimotani mmene a zaka 13 mpaka 19 osabatizidwa mu mpingo anadzimverera kukhala aufulu kuchokera ku ulamuliro wa akulu ndipo monga chotulukapo chake chinathera ku khalidwe lawo loipa. Koma nthawi zonse ndinakumbukira kuti ndinapereka moyo wanga kwa Mulungu. Moyo wanga unali utatengedwa kale, chotero sindikanatsatira ana a zaka 13 mpaka 19 oterowo.”

15. (a) Kodi timadziwa motani kuti chiri chothekera kaamba ka achichepere kusunga kawonekedwe kosamalitsa ka kulambira kowona? (b) Kodi ndimotani mmene makolo angathandizire bwino koposa?

15 ‘Bwanji, ngakhale kuli tero, ngati mwana wanga wamwamuna kapena wamkazi abatizidwa pamene akali wachichepere ndipo kenaka ndikuzilala?’ Makolo ena amadabwa. Mwachiwonekere, wachichepere sayenera kubatizidwa kokha kuti asangalatse makolo kapena chifukwa chakuti mabwenzi ena atero. Komabe, Yosefe, Samueli, Mfumu Yosiya, ndi Yesu pamene anali achichepere a zaka 13 mpaka 19 onse anali ndi kawonedwe kosamalitsa ka kulambiridwa kwa Mulungu ndi kumamatira ku iko. (Genesis 37:2; 39:1-3; 1 Samueli 1:24-28; 2:18-21; 2 Mbiri 34:3; Luka 2:42-49) Mu nthawi za makono, Mkristu wotchedwa Jean anabatizidwa pamene anali kokha ndi zaka khumi. Pamene anafunsidwa zaka zingapo pambuyo pake ngati iye ana mvetsetsadi sitepilo, Jean anayankha: “Ndinadziwa kuti timakonda Yehova, ndinayamikira zimene Yesu anachita kaamba ka ife, ndipo ndinafuna kutumikira Yehova.” Iye watumikira mokhulupirika kwa zaka 40 kuyambira pamene anabatizidwa. Wachichepere aliyense ali munthu pa iyemwini; palibe wina aliyense angaike malire a msinkhu. Makolo ayenera kukalamira kufikira mtima wa mwana wawo, kumthandiza iye kukulitsa kudzipereka kwa umulungu.c Iwo sayenera kokha kuika pamaso pa ana awo mwawi wa kudzipereka ndi ubatizo komanso ayenera kulimbikitsa iwo kukhala alambiri osagwedezeka.

Kulaka Zipsinjo

16. Nchifukwa ninji choposa chidziwitso cha m’mutu chiri chofunikira?

16 Pamene chidziwitso cha Baibulo chiri chofunika, “chizindikiro” chimaphatikizapo kuposa nzeru ya m’mutu. Mwachitsanzo, masomphenya operekedwa kwa Ezekieli, akulu amene anaphedwa kaamba ka kupereka lubani kwa milungu yabodza anali ndi chidziwitso chofala cha mawu olembedwa a Yehova. Koma khalidwe lawo kuseri kwa zitseko linasonyeza kuti iwo sanali olambira owona. (Ezekieli 8:7-12; 9:6) Chotero, kuti “muikidwe chizindikiro” kaamba ka chipulumuko kumafunikira kuvala “umunthu watsopano womwe unalengedwa [mchigwirizano ndi chifuniro. NW] cha Mulungu m’chilungamo chenicheni ndi [kukhulupirika, NW].”​—Aefeso 4:22-24.

17. (a) Kodi ndi zipsinjo zotani zimene zimaletsa ena kubatizidwa? (b) Kodi ndimotani mmene uphungu wa pa Yakobo 4:8 ungagwiritsidwire ntchito?

17 Chipsinjo chonyansa chiri chisonkhezero chathupi lanu lochimwa. (Aroma 8:7, 8) Ena safuna kubatizidwa chifukwa chosatha kuletsa kufooka kwina kwamphamvu kwa thupi, kapena chifukwa chofuna kudzilowetsa mu zosangulutsa zoipa zadziko. (Yakobo 4:1, 4) Anthu oterowo akusowa unansi wapadera. Mawu a Mulungu akulangiza: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m’manja ochimwa inu; yeretsani mitima, amitima iwiri inu.” (Yakobo 4:8) Kachitidwe kosankha kakufunikira. Monga chitsanzo, mwamuna wina yemwe anayamba kuphunzira Baibulo anali atamwerekera ku kachasu ndi mankhwala kwa zaka 16 ndipo anali wodwala kwambiri chifukwa cha chimenechi. Ndi kufunitsitsa iye analaka zizolowezi zoipa zimenezi. “Koma kokha pamene ndinali kupita patsogolo kulinga ku kudzipereka, mkazi wina anayamba kundipempha kuti ndigone naye. Chinalidi chiyeso chenicheni,” iye anatero. “Ngakhale kuti mkaziyo anaganiza kuti ndinali wamisala, ndinamuuza iye: ‘Ndikuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndipo sindingachite chimenecho.’ ” Kodi nchiyani chimene chinafulumiza yankho lake? “Ndinali nditawona chimene Yehova anali atachita kaamba ka moyo wanga mwakundithandiza ine kusiya kumwa kachasu. Iye anandithandiza ine munjira zinanso. Ichi chinapitiriza kundiyandikitsa ine kwa iye. Sindingamukhumudwitse iye.” Mwamuna ameneyu wakula moyandikira kwa Mulungu.

18. Kodi nchiyani chimene chiri mfungulo ku kulaka zokhumudwitsa?

18 Chomwe chimafunika sikuchuluka kotani kumene mumadziwa koma miimakonda mochuluka chotani zimene mumadziwa. Masalmo 119:165 amanena kuti: “Akukonda [osati kokha kudziwa] chilamulo chanu ali nawo mtendere wambiri; ndipo alibe chokhumudwitsa.” Mfungulo iri kukonda chilamulo cha Mulungu, kuyamikira mozama mtengo wake m’moyo wanu.​—Yesaya 48:17, 18.

19, 20. (a) Kodi ndi zokhumudwitsa zotani zimene ziyenera kulakidwa, ndipo kodi ndi chitsimikiziro chotani chimene tiri nacho? (b) Kulaka zokhumudwitsa mwachipambano kudzaturukamo nchiyani?

19 Komabe, zipsinjo zina kapena zokhumudwitsa zingabuke. “Chovuta kwambiri kwa ine,” anatero mbale wotchulidwa pamwambapo, “anali mantha a anthu. Ndinali ndi ‘mabwenzi’ akudziko omwe ndinali kumwa nawo. Chinali chinthu chovuta kwambiri kwa ine kuwauza iwo kuti ndinali kudula mayanjano awo chifukwa ndinali kupereka moyo wanga kwa Mulungu.” (Miyambo 29:25) Ena ayang’anizana ndi chitonzo cha ziwalo zabanja. Mboni yobatizidwa posachedwa, yomwe inalaka chitsutso cha mwamuna wake, inawona: “Mmalo mwavuto limodzi lalikulu, panali timavuto tina tambiri tomwe ndinayenera kulaka limodzi panthawi.”Mokhulupirika kulaka chipsinjo chirichonse pamene chibwera chidzalimbikitsa mtima wanu. Khalani otsimikiziridwa kuti palibe chipsinjo chomwe sichingalakidwe ndi awo amene amakonda chilamulo cha Mulungu!​—Luka 16:10.

20 Pamene mukupambana pa chokhumudwitsa chirichonse, mudzapeza “mtendere wambiri.” (Masalmo 119:165) Inde, “udzayenda m’njira yako wosawopa. . . udzagona tulo tokondweretsa. Usawope zowopsya zodzidzimutsa, ngakhale zikadza zopasula oipa, pakuti Yehova adzalimbitsa mtima wako, nadzasunga phazi lako lingakodwe.”​—Miyambo 3:23-26.

[Mawu a M’munsi]

a Chifupifupi zaka 150 pambuyo pa masomphenya a Ezekieli, wolemba mbiri wa Chigriki Herodotus, pozindikira kuti zizindikiro pa anthu odzipereka kwa mulungu Hercules zinapereka kwa iwo chlnjirizo, analemba: “Ngati kapolo wa munthu wina aliyense apeza chinjirizo [mu kachisi wa Hercules], ndipo chizinddoro chopatulika chiikidwa pa iye, chotero kudzipereka iye mwini kwa mulungu, sichiri chalamulo kupha munthu ameneyo.

b Posachedwapa mafunso awiri operekedwa kwa anthu aubatizo anapepukitsidwa kotero kuti anthuwo angayankhe ndi kugwirizana kotheratu kwa zimene zikuphatikizidwamo mkulowa mu unansi wathithithi ndi Mulungu ndi gulu lake la padziko lapansi.

c Onani “Phunzirani Muli ndi Kupembedza Mulungu Monga Chonulirapo Chanu” mu kope lathu la February 1, 1986.

Nsonga Zakapendedwe

◻ Kodi ndimotani mmene Mulungu amatithandizira ife kupeza mtendere ndi iye?

◻ Kodi nchiyani chimene chiri chizindikiro chophiphiritsira chopatsa moyo?

◻ Kodi nchiyani chimene chiri chizindikiro cha kudzipereka ndi ubatizo?

◻ Kodi ndi zokhumudwitsa zotani zimene ziyenera kukumanizidwa, ndipo kodi izo zingalakidwe motani?

[Bokisi pa tsamba 13]

Kumizidwa kapena Kuwaza Madzi?

Mbiri ya ubatizo wa Yesu imatchula “kuturuka kwake m’madzi.” (Marko 1:10) Kuti Yesu anamizidwa chiri chogwirizana ndi tanthauzo la liwu la Chigriki lotanthauzidwa kuti ubatizo (ba’pti-sma). Iri linachokera ku liwu lakuti bapti’zo, lomwe limatanthauza “nyika, miza.” Nthawi zina linali kugwiritsiridwa ntchitokulongosola kumila kwa sitima ya m’madzi. Wolemba wa mu zana lachiwiri Lucian amagwiritsira ntchito liwu lofanana nalo kulongosola munthu wina akumiza mnzake: “Kumuvuwaza iye pansi kwambiri [bapti’zon-ta] kotero kuti iye sangathe kutulukanso.” The New International Dictionary of New Testament Theology likumaliza kuti: “Mosasamala kanthu za zitsimikizo zotsutsa, chikuwoneka kuti baptizo, ponse pawiri mu Chiyuda ndi m’malemba a Chikristu, mwachibadwa amatanthauza ’kumiza’, ndipo kuti ngakhale pamene linakhala liwu logwiritsidwa ntchito kaamba ka ubatizo, lingaliro lakumiza linatsalira.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena