Kodi Tilambire Mulungu Uti?
MOSIYANA ndi zinyama, anthufe tinapangidwa ndi luso lakulambira. Kameneka kali kapangidwe kathu kachibadwidwe. Tirinso ndi nzeru ya makhalidwe abwino, chikumbumtima chimene chimatitsogoza ponena za chimene chiri chabwino ndi choipa. M’njira zosiyanasiyana tonsefe timatsatira chikumbumtima chimenecho, ndipo potero, ambiri amayang’ana kwa mulungu kapena milungu kaamba ka chitsogozo.
M’zaka za zana limodzi kapena aŵiri zapitazo, anthu ena anzeru zakudziko atsutsa kukhalako kwa Mulungu wamphamvuyonse ndi Mlengi. Mu 1844, Karl Marx analengeza kuti chipembedzo chiri “mankhwala oletsa ululu a anthu.” Pambuyo pake, Charles Darwin anayambitsa nthanthi ya chisinthiko. Ndiyeno panadza kupanduka kwa Bolshevik. Kusakhulupirira Mulungu kunakhala lamulo lovomerezedwa laboma Kum’maŵa kwa Ulaya, ndipo kunanenedwa kuti chipembedzo chikatha ndi mbadwo wa 1917. Koma osakhulupirira Mulungu amenewo sakanatha kusintha njira imene anthu anapangidwira. Ichi chikuwonekera ndi kudzukanso kwa chipembedzo Kum’maŵa kwa Ulaya panthaŵi ino.
Komabe, monga momwe Baibulo limanenera, iriko yambiri “yonenedwa milungu, kapena m’mwamba, kapena pa dziko lapansi, monga iriko milungu yambiri, ndi ambuye ambiri.” (1 Akorinto 8:5) M’mibadwo yonseyi anthu alambira milungu yambirimbiri. Pakhala milungu ya kubala, ya chikondi, ya nkhondo, ya vinyo ndi ya kuledzera. M’chipembedzo cha Chihindu chokha, milungu imafika ku chiŵerengero cha mamiliyoni.
Milungu yokhala itatuitatu inali yambiri m’Babulo, Asuri, ndi Igupto, limodzinso ndi m’maiko Achibuda. Chikristu Chadziko nachonso chiri ndi Utatu wake “wopatulika.” Chisilamu, chikumakana Utatu, “chiribe mulungu koma Allah.” Ndiponso, ngakhale awo amene amaseka lingaliro la Mulungu wamphamvuyonse wosawoneka, ali ndi milungu yawo. Mwachitsanzo, pa Afilipi 3:19, Baibulo limanena za anthu amene anyengedwa ndi zolondola zakuthupi kuti: ‘Mulungu wawo ndiyo mimba yawo.’
Anthu ambiri amalambira mulungu kapena milungu ya dziko kapena chitaganya chimene anabadwiramo. Ichi chimadzutsa mafunso. Kodi mitundu yonse yakulambira imatsogolera kumalo amodzimodziwo—mofanana ndi misewu yonka pamwamba pa phiri? Kapena kodi misewu yambiri yachinsinsi ya chipembedzo imapita kutsoka—mofanana ndi njira zopita ku phompho lakuya? Kodi pali njira zambiri zoyenera zolambirira kapena kodi pali imodzi yokha? Kodi pali milungu yambiri yofunikira kutamandidwa kapena kodi pali Mulungu Wamphamvuyonse mmodzi yekha yemwe amayenerera kudzipereka kwathu kotheratu ndi kulambira?
Kubuka kwa Milungu Yonyenga
Tifunikira kusanthula mosamalitsa mafunso apamwambawa. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti bukhu lolembedwa kale koposa la chipembedzo, Baibulo, limafotokoza mmene mulungu wonyenga, ananyengera makolo athu oyambirira kuloŵa m’njira yosakaza mwakugwiritsira ntchito njoka. Tikuvutikabe ndi zotulukapo za machenjera ake kufikira lerolino. (Genesis 3:1-13, 16-19; Salmo 51:5) Yesu, “Mwana wa Mulungu,” analankhula za mulungu wopanduka ameneyo kukhala “mkulu wa dziko ili lapansi.” Mmodzi wa atumwi a Yesu anamutcha “mulungu wa dongosolo lino la zinthu.” (Yohane 1:34; 12:31; 16:11; 2 Akorinto 4:4, NW) Pa Chivumbulutso mutu 12, vesi 9, akulongosoledwa kukhala ‘njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse.’ Ulamuliro wadziko wa chipembedzo chonyenga ukulamuliridwa ndi Satana.
Satana ndiye wonyenga wamkulu. (1 Timoteo 2:14) Iye amagwiritsira ntchito mwamachenjera chikhumbo chobadwa nacho cha anthu cha kulambira mwakuchilikiza milungu yamitundu yambiri—mizimu ya makolo, mafano, zifanizo, ndi mafano a Namwali Mariya. Iye amachilikizanso kulambira milungu yaumunthu, monga ngati olamulira amphamvu, akazembe ankhondo olakika, ndi ngwazi za akanema ndi maseŵera. (Machitidwe 12:21-23) Tingachite bwino kukhala amaso, otsimikiza mtima kufunafuna ndi kulambira Mulungu wowona yekha, amene kwenikwenidi ‘sakhala patali ndi yense wa ife.’—Machitidwe 17:27.
Pamenepo, kodi Mulungu wapadera ameneyu yemwe tifunikira kumlambira ndiye yani? Zaka 3,000 zapitazo, wamasalmo wa Baibulo anamfotokoza kukhala “Wam’mwambamwamba . . . , Wamphamvuyonse . . . , Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira,” ndipo anamuitana ndi dzina lake laulemerero—“Yehova.” (Salmo 91:1, 2) Poyamba, Mose anati za iye: “Yehova Mulungu wathu, Yehova ndiye mmodzi.” (Deuteronomo 6:4) Ndipo mneneri Yesaya anamgwira mawu Mulungu mwini kukhala akunena kuti: “Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.”—Yesaya 42:8.
Yehova Mulungu akufuna kudzachotsera dzina lake chitonzo chonse chomwe mulungu wonyenga Satana walipaka. Iye anasonyeza mwafanizo mmene akachitira chimenechi m’chaka cha 1513 B.C.E., pamene anagwiritsira ntchito mneneri wake Mose kulanditsa anthu a Israyeli ku chitsenderezo cha Aigupto. Pachochitika chimenecho, Mulungu anagwirizanitsa dzina lake lakuti Yehova ndi mawu aŵa: “Ine ndine yemwe ndiri ine.” (Eksodo 3:14, 15) Akadzilemekeza yekha motsutsana ndi Farao wa Igupto, koma choyamba anauza wolamulira woipayo kuti: ‘Chifukwa chake ndakuimika kuti ndikuonetse mphamvu yanga, ndi kuti alalikire dzina langa pa dziko lonse lapansi.’—Eksodo 9:16.
Mkhalidwe uli wofanana lerolino. Mofanana ndi Farao wakale, mulungu wa dziko lino, Satana, amanyoza Yehova Mulungu ndipo mwamachenjera amamenya nkhondo yauzimu ndi anthu amene amakonda chilungamo ndi chowonadi. (Aefeso 6:11, 12, 18) Kachiŵirinso, Mulungu akufuna kulemekeza dzina lake mosasamala kanthu za chitsutso cha Satana. Komabe, asanasonyeze mphamvu yake mwakuwononga Satana ndi ntchito zake zonse, Yehova akutumiza olambira ake kulengeza dzina Lake padziko lonse lapansi. Kupereka umboni wa dzina lake kumeneku kuli mbali yofunika ya kulambira kowona.
Moyenerera, Mulungu iyemwini wanena kuti olambira ameneŵa akakhala mboni zake, Mboni za Yehova, “anthu amene ndinadzilengera ndekha, kuti aonetse matamando anga.” (Yesaya 43:10-12, 21) Kodi ndimotani mmene amaonetsera matamando a Yehova? Amalalikira ndi kuphunzitsa poyera ndi kunyumba ndi nyumba, kulengeza mbiri yabwino yakuti Ufumu wa Yehova, wolamulidwa ndi Mwana wake, Yesu Kristu, udzabweretsa madalitso amuyaya kwa anthu omvera padziko lapansili. Chotero, amalambira Mulungu ‘osaleka,’ monga momwe anachitira Akristu owona m’zaka za zana loyamba. (Machitidwe 5:42; 20:20, 21) Kodi alandira dalitso la Mulungu m’zimenezi? Masamba otsatiraŵa adzayankha.